Kalata ya Yakobo
3 Abale anga, pasakhale aphunzitsi ambiri pakati panu, podziwa kuti tidzalandira chiweruzo chokhwima.+ 2 Paja tonsefe timapunthwa* nthawi zambiri.+ Ngati munthu sapunthwa pa mawu, ndiye kuti ndi wangwiro ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse. 3 Tikamangirira zingwe pakamwa pa mahatchi kuti azitimvera, timatha kulamuliranso matupi awo onse. 4 Ganiziraninso za ngalawa. Ngakhale kuti ndi zazikulu kwambiri ndipo zimayenda mokankhidwa ndi mphepo zamphamvu, munthu amene akuziyendetsa amaziwongolera ndi thabwa lalingʼono kwambiri kuti zipite kumene iye akufuna.
5 Lilime nalonso ndi kachiwalo kakangʼono, koma limadzitama kwambiri. Taganizirani mmene kamoto kakangʼono kamayatsira nkhalango yaikulu. 6 Lilimenso ndi moto.+ Pa ziwalo zonse za thupi lathu, lilime ndi lodzaza ndi zinthu zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse+ komanso limayatsa moyo wonse wa munthu* ndipo lili ndi moto wa Gehena.* 7 Anthu angathe kuweta mtundu uliwonse wa nyama zakutchire, mbalame, nyama zokwawa ndiponso zamoyo zamʼnyanja ndipo akhala akuchita zimenezi. 8 Koma palibe munthu amene angathe kuweta lilime. Lilime ndi losalamulirika ndipo limavulaza komanso ndi lodzaza ndi poizoni wakupha.+ 9 Lilime timaligwiritsa ntchito potamanda Yehova,* amene ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu amene analengedwa “mʼchifaniziro cha Mulungu.”+ 10 Pakamwa pamodzi pomwepo pamatuluka mawu otamanda komanso otemberera.
Abale anga, nʼzosayenera kuti zinthu zizichitika mwa njira imeneyi.+ 11 Kodi kasupe angatulutse madzi abwino* komanso madzi owawa padzenje limodzi? 12 Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu ungabereke maolivi, kapena kodi mtengo wa mpesa ungabereke nkhuyu?+ Ngakhale kasupe wa madzi amchere sangatulutse madzi abwino.
13 Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu? Ngati alipo asonyeze zimenezi pochita zinthu zabwino pa moyo wake. Azichita zinthu zonse mofatsa, lomwe ndi khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru. 14 Koma ngati mʼmitima yanu muli nsanje yaikulu+ ndi kukonda mikangano,*+ musadzitame+ chifukwa kuchita zimenezo nʼkunamizira choonadi. 15 Imeneyi si nzeru yochokera kumwamba, koma ndi yapadziko lapansi,+ yauchinyama ndiponso yauchiwanda. 16 Chifukwa pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano,* pamakhalanso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.+
17 Koma nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+ 18 Komanso, chilungamo ndi chipatso chimene anthu obweretsa mtendere+ amafesa mumtendere.+