Yehova Amalalikira ‘za Chimaliziro Kuchokera Pachiyambi’
“Ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.”—YESAYA 46:10.
1, 2. Kodi kugonjetsedwa kwa Babulo n’kodabwitsa motani, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wotani?
GULU la nkhondo la adani likuyenda usiku mwakachetechete, m’mphepete mwa mtsinje wa Firate pa ulendo wawo wopita mu mzinda wamphamvu wa Babulo. Litayandikira mzindawo, likuona zodabwitsa. Chipata cha zitseko ziwiri cholowera mumzindawo angochisiya chili pululu! Gululo likukwera kumtunda, n’kulowa mumzindawo. Posakhalitsa likugonjetsa mzindawo. Koresi, mtsogoleri wa gulu la adanilo, nthawi yomweyo akuyamba kulamulira mzinda wogonjetsedwawo ndipo pambuyo pake akupereka lamulo lomasula Aisrayeli amene anatengedwa ukapolo. Aisrayeli masauzande ambirimbiri amene anatengedwa ukapolo akubwerera kwawo ku Yerusalemu kukayambiranso kulambira Yehova.—2 Mbiri 36:22, 23; Ezara 1:1-4.
2 Zimenezi zinachitika pakati pa chaka cha 539 ndi 537 B.C.E. ndipo akatswiri a mbiri yakale atsimikizira kuti zinachitikadi. Koma chodabwitsa n’chakuti zimenezi zinali zitadziwika kale zaka 200 zisanachitike. Yehova anauzira mneneri wake Yesaya kuti alongosole mmene mzinda wa Babulo udzagwere zaka zambiri chonchi m’tsogolo. (Yesaya 44:24–45:7) Sikuti Mulungu anangoneneratu zimene zidzachitike panthawi yogonjetsa Babulo koma anatchulanso dzina la mtsogoleri amene adzagonjetse mzindawo.a Yehova anauza Aisrayeli, omwe anali mboni zake pa nthawiyo, kuti: “Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.” (Yesaya 46:9, 10a) Inde, Yehova ndi Mulungu wotha kudziwiratu zimene zidzachitike m’tsogolo.
3. Kodi tikambirana mayankho a mafunso ati?
3 Kodi Mulungu amadziwiratu zonse zodzachitika m’tsogolo? Kodi Yehova amadziwiratu zimene aliyense wa ife achite pa moyo wake? Kapena tifunse kuti, kodi Mulungu analemberatu tsogolo lathu lonse? M’nkhani ino ndi yotsatirayo tikambirana mayankho a Baibulo a mafunso amenewa ndi mafunso enanso.
Yehova Ndi Mulungu wa Ulosi
4. Kodi Gwero la maulosi olembedwa m’Baibulo ndani?
4 Popeza kuti Yehova amatha kudziwa zam’tsogolo, anauzira aneneri ake m’nthawi za m’Baibulo kuti alembe maulosi ambiri, moti ifeyo timadziwiratu zimene Yehova akufuna kuchita. Yehova anati: “Zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.” (Yesaya 42:9) Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri umene anthu a Mulungu ali nawo.
5. Kodi munthu amene wadziwiratu zimene Yehova achite m’tsogolo amakhala ndi udindo wotani?
5 Mneneri Amosi anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” Kudziwiratu zam’tsogolo kumeneku kunawapatsanso udindo. Taonani chitsanzo chokhudza mtima kwambiri chimene Amosi ananena pambuyo pa mawu amenewa. Iye anati: “Mkango ukabangula, ndani amene saopa?” Mkango ukabangula, anthu ndi nyama zimene zamva kubangulako zimadziwiratu choyenera kuchita, moteronso aneneri monga Amosi anadziwiratu kuti ayenera kulalikira mawu a Yehova. “Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?”—Amosi 3:7, 8.
“Mawu” a Yehova Salephera
6. Kodi “uphungu” wa Yehova unakwaniritsidwa motani pa nkhani ya kugonjetsedwa kwa Babulo?
6 Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova anati: “Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Yesaya 46:10b) “Uphungu” wa Mulungu, kapena kuti chifuniro chake chokhudza Babulo, chinali choti aitane Koresi kuchoka ku Perisiya kuti akagonjetse Babulo n’kuchotseratu ufumuwo. Yehova analengeza cholinga chimenechi zaka zambiri zimenezi zisanachitike. Monga taonera kale, zimenezi zinakwaniritsidwadi mosalephera m’chaka cha 539 B.C.E.
7. N’chifukwa chiyani sitikayika kuti “mawu” a Yehova amakwaniritsidwa nthawi zonse?
7 Pafupifupi zaka 400 Koresi asanagonjetse Babulo, Mfumu Yehosafati ya ku Yuda inaukiridwa ndi magulu ankhondo awiri, a Amoni ndi a Moabu. Mfumuyi inapemphera mosakayika, kuti: “Yehova, Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m’Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.” (2 Mbiri 20:6) Yesaya naye anadalira Yehova chifukwa anati: “Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?” (Yesaya 14:27) Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, inapenga ndipo pambuyo pake itachiritsidwa, inavomereza modzichepetsa kuti: “Palibe woletsa dzanja [la Mulungu], kapena wakunena naye, Muchitanji?” (Danieli 4:34, 35) Inde, Yehova anatsimikizira anthu ake kuti: “Mawu anga . . . sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:11) Tisakayike ngakhale pang’ono kuti “mawu” a Yehova amakwaniritsidwa nthawi zonse. Zivute zitani chifuniro cha Mulungu chimakwaniritsidwa.
‘Chifuniro cha Muyaya’ cha Mulungu
8. Kodi ‘chifuniro cha muyaya’ cha Mulungu n’chiyani?
8 M’kalata imene analembera Akristu a ku Efeso, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu ali ndi ‘chifuniro cha muyaya.’ (Aefeso 3:11, NW) Sikuti chifuniro chimenechi chili ngati pulani imene Mulungu amakonza pofuna kuchita zinazake. Koma chimatanthauza zimene Yehova anatsimikiza mumtima mwake pofuna kukwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga anthu ndi dzikoli. (Genesis 1:28) Kuti timvetse mfundo yoti chifuniro chakechi sichingalephereke, tiyeni tione ulosi woyamba wolembedwa m’Baibulo.
9. Kodi lemba la Genesis 3:15 limagwirizana bwanji ndi chifuniro cha Mulungu?
9 Lonjezo la pa Genesis 3:15 limasonyeza kuti Adamu ndi Hava atangochimwa, Yehova anatsimikiza mtima kuti mkazi Wake wophiphiritsira adzabala mbewu, kapena kuti mwana wamwamuna. Komanso Yehova anaoneratu zimene zidzachitike chifukwa cha udani wa pakati pa mkazi ameneyu ndi Satana ndiponso pakati pa mbewu ziwiri zodanazo. Ngakhale kuti m’tsogolo mwake Yehova analola kuti Mbewu ya mkazi wa Mulungu ailalire chitendene chake, panthawi imene Mulungu anaika, Mbewuyi idzalalira mutu wa chinjoka, kapena kuti Satana Mdyerekezi. Koma zonsezi zisanachitike, panachitika zinthu zosiyanasiyana zokhudza kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu kudzera mumzera wosankhidwa wa banja limene Yesu anadzabadwiramo monga Mesiya wolonjezedwa.—Luka 3:15, 23-38; Agalatiya 4:4.
Zimene Yehova Amakonzeratu
10. Kodi Yehova anakonzeratu pachiyambi kuti Adamu ndi Hava adzachimwe? Longosolani.
10 Ponena za udindo umene Yesu anakwaniritsa pa chifuniro cha Mulungu, mtumwi Petro analemba kuti: “[Yesu] anazindikiratu [anadziwikiratu, NW] lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi, chifukwa cha inu.” (1 Petro 1:20, 21) Kodi Yehova anakonzeratu pachiyambi kuti Adamu ndi Hava adzachimwe kuti potero padzafunike nsembe ya dipo ya Yesu Kristu? Ayi. Mawu akuti “lisanakhazikike” akumasulira mawu a m’Chigiriki omwe amatanthauza “kudzala mbewu.” Kodi pali ‘mbewu iliyonse imene inadzalidwa,’ kapena kuti mwana aliyense amene anakhalako Adamu ndi Hava asanachimwe? Ayi. Adamu ndi Hava anabereka ana atachimwira kale Mulungu. (Genesis 4:1) Motero Adamu ndi Hava atapanduka, koma asanakhale ndi mwana, Yehova anakonzeratu zoti kudzabwera “mbewu.” Imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu kunatipatsa mphatso yachikondi ya dipo, imene idzachotse uchimo wobadwa nawo ndipo zoipa zonse zimene Satana amachita zidzathetsedwa.—Mateyu 20:28; Ahebri 2:14; 1 Yohane 3:8.
11. Kodi Yehova anakonzeratu chiyani pofuna kukwaniritsa chifuniro chake?
11 Mulungu anakonzeratunso chinthu china pokwaniritsa chifuniro chake. Zimenezi zikusonyezedwa ndi mawu amene Paulo analemba kwa Aefeso, akuti Mulungu ‘adzasonkhanitsa pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.’ Kenaka, potchula “za kumwamba,” kapena kuti anthu amene anasankhidwa kuti akalamulire ndi Kristu, Paulo analongosola kuti: “Tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake.” (Aefeso 1:10, 11) Inde, Yehova anakonzeratu kuti anthu owerengeka adzakhale mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi wa Mulungu ndipo pamodzi ndi Kristu iwo adzapatsa anthu madalitso obwera ndi dipo la Kristu. (Aroma 8:28-30) Mtumwi Paulo, anatchula anthu amenewa kuti “mtundu woyera mtima.” (1 Petro 2:9) Mtumwi Yohane anali ndi mwayi wouzidwa chiwerengero cha anthuwa, omwe adzalamulire pamodzi ndi Kristu. Chiwerengero chake ndi 144,000. (Chivumbulutso 7:4-8; 14:1, 3) Pothandiza Mfumu Kristu, iwo amatumikira ‘moyamikiritsa ulemerero wa Mulungu.’—Aefeso 1:12-14.
12. Kodi timadziwa bwanji kuti anthu 144,000 sanasankhidwiretu pawokhapawokha?
12 Kukonzeratu kuti padzakhale anthu 144,000 sikutanthauza kuti anthu enaake anasankhidwiratu ndi Mulungu kuti adzam’tumikire mokhulupirika m’njira imeneyi. N’zoona kuti mawu olimbikitsa a m’Malemba Achigiriki Achikristu analembedwa makamaka pofuna kuthandiza ndiponso kulimbikitsa odzozedwa kuti apitirize kukhala okhulupirika ndi kuti ayesetse kukhalabe oyenerera chiyembekezo chawo chopita kumwamba. (Afilipi 2:12; 2 Atesalonika 1:5, 11; 2 Petro 1:10, 11) Yehova anadziwiratu kuti anthu 144,000 adzakhala oyenerera kuchita cholinga chake. Koma sanadziwiretu anthuwo pawokhapawokha, chifukwa zimenezo zimadalira zimene munthu aliyense m’gululi angasankhe kuchita m’moyo wake.—Mateyu 24:13.
Zimene Yehova Amadziwiratu
13, 14. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake zodziwiratu m’tsogolo mogwirizana ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani amatero?
13 Popeza Yehova ndi Mulungu wa maulosi ndiponso ali ndi chifuniro chake, kodi amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zodziwiratu zinthu zam’tsogolo? Choyamba tidziwe kuti njira zonse za Mulungu ndi za choonadi, chilungamo, ndiponso chikondi. Polemba kalata kwa Akristu achihebri a m’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo anatsimikizira kuti lumbiro ndiponso lonjezo la Mulungu ndizo “zinthu ziwiri zosasinthika, mmene Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:17, 18) M’kalata imene analembera wophunzira Tito, Paulo analongosolanso mfundo imeneyi ponena kuti Mulungu ndi “wosanama.”—Tito 1:2.
14 Komanso, ngakhale kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, iye sachita zinthu zopanda chilungamo. Mose ananena kuti Yehova ndi “Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Chilichonse chimene Yehova amachita chimakhala chogwirizana ndi makhalidwe ake okoma. Zochita zake zonse zimagwirizana ndendende ndi makhalidwe ake aakulu omwe ndi chikondi, nzeru, chilungamo, ndi mphamvu.
15, 16. Kodi Yehova anamuuza Adamu kuti angasankhe kuchita zotani m’munda wa Edene?
15 Taganizirani mmene mfundo zonsezi zikugwirizanirana ndi zimene zinachitika mu Edene zija. Popeza Yehova ndi Tate wachikondi, anapereka chilichonse chofunikira kwa anthu amene anawalenga. Anam’patsa Adamu mphamvu zomatha kuganiza, kuona zinthu mwanzeru, ndi kudziwa njira yabwino yochitira zinthu. Mosiyana ndi nyama zimene Yehova analenga, zomwe zimangochita zinthu mosaganizira, Adamu ankatha kusankha zoyenerera kuchita. Motero, Mulungu anayang’ana pansi ali kumpando wake wachifumu ndipo “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”—Genesis 1:26-31; 2 Petro 2:12.
16 Mmene Yehova ankam’patsa Adamu lamulo loti asadye “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa,” anamuuza zonse zoyenerera kuti asankhe zochita. Yehova anamulola Adamu kudya zipatso za “mitengo yonse ya m’munda” kupatulapo mtengo umodzi wokha ndipo anamuchenjeza kuti akadya umenewo afa. (Genesis 2:16, 17) Anamulongosolera Adamu zimene zichitike ngati atadya zipatso za mtengowo. Ndiye kodi Adamu anatani?
17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zoti adziwiretu?
17 N’zoonekeratu kuti Yehova anasankha kusadziwa zimene Adamu ndi Hava achite, ngakhale kuti Yehovayo amatha kudziwiratu chilichonse chisanachitike. Motero, sikuti pamenepa nkhani yagona poti Yehova angathe kuoneratu zam’tsogolo, koma poti iye amatha kusankha kutero kapena ayi. Kuphatikizanso apo, tinganene kuti poti Yehova ndi Mulungu wachikondi, sizikanatheka kuti akonzeretu mwadala zoti Adamu ndi Hava adzapanduke, poti kuchita zimenezi ndi nkhanza chifukwa pali zosautsa zambirimbiri zimene zabwera ndi kupanduka kumeneku. (Mateyu 7:11; 1 Yohane 4:8) Motero, Yehova amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zoti adziwiretu.
18. N’chifukwa chiyani Yehova sali woperewera m’njira inayake ngakhale kuti amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zoti adziwiretu?
18 Kodi tingati Yehova n’ngoperewera m’njira inayake chifukwa choti amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zoti adziwiretu? Ayi. Mose anati Yehova ndi “Thanthwe.” Ndipo anapitiriza kunena kuti: “Ntchito yake ndi yangwiro.” Si Yehova amene ayenera kuimbidwa mlandu chifukwa cha mavuto obwera ndi kuchimwa kwa anthu. Mavuto amene tikukumana nawowa anachokera pa kusamvera kwa Adamu. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Deuteronomo 32:4, 5; Aroma 5:12; Yeremiya 10:23.
19. Kodi ndi mafunso otani amene afotokozedwa m’nkhani yotsatira?
19 Pa zimene takambiranazi, taona kuti Yehova alibe chisalungamo chilichonse. (Salmo 33:5) M’malo mwake, zimene Yehova amatha kuchita, makhalidwe ake, ndiponso miyezo yake, zimakhala zogwirizana ndi chifuniro chake. (Aroma 8:28) Popeza Yehova ndi Mulungu wa maulosi, iye amalalikira ‘za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale amanena zinthu zimene zisanachitidwe.’ (Yesaya 46:9, 10) Taonanso kuti amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zoti adziwiretu. Ndiye kodi zimenezi zikutikhudza bwanji ifeyo. Kodi tingatani kuti tizisankha kuchita zinthu zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu wachikondi? Ndipo kodi ndi madalitso otani amene kuchita zimenezi kudzatibweretsere? Nkhani yotsatira yafotokoza mafunso amenewa.
[Mawu a M’munsi]
a Onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse, tsamba 28, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi ndi zitsanzo zakale ziti zimene zimatsimikizira kuti “mawu” a Mulungu salephera?
• Kodi Yehova anakonzeratu chiyani mogwirizana ndi ‘chifuniro chake cha muyaya’?
• Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake zodziwiratu zinthu zam’tsogolo?
[Chithunzi patsamba 22]
Yehosafati anadalira Yehova
[Chithunzi patsamba 23]
Mulungu ananeneratu za imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi Yehova anali atakonzeratu zimene Adamu ndi Hava anachita?