Deuteronomo
32 “Tamverani kumwamba inu, ndipo ine ndilankhula,
Dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.
2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,
Mawu anga adzatsika ngati mame,
Ngati mvula yowaza pa udzu,
Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.
3 Chifukwa ndidzalengeza dzina la Yehova.+
Anthu inu, lengezani za ukulu wa Mulungu wathu!+
5 Iwo ndi amene achita zinthu zoipa.+
Iwo si ana ake, ali ndi vuto ndi iwowo.+
Iwo ndi mʼbadwo wopotoka maganizo komanso wachinyengo!+
Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+
Amene anakupangani ndi kukukhazikitsani monga mtundu?
7 Kumbukirani masiku akale,
Ganizirani zaka za mibadwo ya mʼmbuyo.
Funsani bambo anu ndipo akuuzani,+
Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozerani.
8 Pamene Wamʼmwambamwamba anapereka cholowa ku mitundu ya anthu,+
Pamene analekanitsa ana a Adamu,*+
Anaika malire a anthu ena onse+
Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+
11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera chisa chake,
Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,
Mmene chimatambasulira mapiko ake, kuti chitenge anawo,
Nʼkuwanyamula pamapiko ake,+
12 Ndi Yehova yekha amene anapitiriza kumutsogolera,*+
Panalibe mulungu wachilendo amene anali naye.+
Anamudyetsa uchi wochokera mʼthanthwe,
Ndi mafuta ochokera mʼmwala wa nsangalabwi.
14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ngʼombe ndi mkaka wa nkhosa,
Pamodzi ndi nkhosa zabwino kwambiri,*
Komanso nkhosa zamphongo za ku Basana ndi mbuzi zamphongo,
Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa.*+
Ndipo munamwa vinyo wochokera mʼmagazi a mphesa.*
15 Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake.
Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+
Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+
Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake.
17 Iwo ankapereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+
Anapereka nsembe kwa milungu imene sankaidziwa,
Kwa milungu yatsopano yongobwera kumene,
Komanso kwa milungu imene makolo anu sankaidziwa.
Umene udzayaka mpaka kukafika pansi penipeni pa Manda,*+
Ndipo udzapsereza dziko lapansi ndi zokolola zake,
Komanso udzayatsa maziko a mapiri.
23 Ndidzawonjezera masoka awo,
Mivi yanga yonse ndidzaigwiritsa ntchito pa iwo.
Ndipo adzavutika ndi kutentha thupi koopsa komanso adzawonongedwa nʼkutheratu.+
Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali+
Komanso njoka zapoizoni za mʼfumbi.
25 Kunja, lupanga lidzawasandutsa anamfedwa.+
Mʼnyumba, anthu adzagwidwa ndi mantha+
Zimenezi zidzachitikira mnyamata, namwali,
Mwana wamngʼono ndi munthu wa imvi.+
26 Ndikanatha kunena kuti: “Ndidzawabalalitsa,
Ndidzachititsa kuti anthu asakumbukirenso za iwo,”
Iwo anganene kuti: “Tapambana chifukwa cha mphamvu zathu,+
Si Yehova amene wachita zonsezi.”
29 Zikanakhala bwino ngati akanakhala anzeru,+ chifukwa akanaganizira mozama zimenezi.+
Akanaganizira kuti ziwathera bwanji.+
30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,
Kapena anthu awiri angathamangitse bwanji anthu 10,000?+
Nʼzosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+
Komanso ngati Yehova atawapereka.
31 Chifukwa thanthwe lawo si lofanana ndi Thanthwe lathu,+
Ndipo adani athu akudziwa bwino zimenezi.+
32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,
Ndi kuminda ya mʼmapiri a ku Gomora.+
Zipatso zawo za mphesa ndi zapoizoni
Ndipo ndi zowawa.+
33 Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka,
Ndi poizoni woopsa wa mamba.
35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+
Zimenezi zidzachitika pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo likadzaterereka,+
Chifukwa tsiku la tsoka lawo layandikira,
Ndipo zowagwera zifika mofulumira.’
36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+
Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake+
Akadzaona kuti mphamvu zawo zatha,
Komanso kuti kwangotsala anthu ovutika ndi ofooka.
37 Ndiyeno iye adzanena kuti, ‘Ili kuti milungu yawo,+
Thanthwe limene anathawirako,
38 Milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo,*
Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+
Ibwere kudzakuthandizani.
Ikhale malo anu othawirako.
Ndimapha komanso ndimapereka moyo.+
40 Ndakweza dzanja langa kumwamba
Ndipo ndikulumbira kuti: “Ine, Mulungu wamuyaya, ndikulumbira pa dzina langa,”+
41 Ndikanola lupanga langa lonyezimira,
Nʼkukonzekeretsa dzanja langa kuti lipereke chiweruzo,+
Ndidzabwezera adani anga,+
Ndipo ndidzapereka chilango kwa amene amadana nane.
42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,
Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,
Ndi magazi a anthu ophedwa komanso ogwidwa,
Ndiponso mitu ya atsogoleri a adani.’
43 Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake,+
Chifukwa adzabwezera magazi a atumiki ake,+
Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+
Komanso adzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”*
44 Ndiyeno Mose anabwera nʼkulankhula mawu onse a nyimbo iyi anthu onse akumva,+ iye pamodzi ndi Hoshiya*+ mwana wa Nuni. 45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46 anawauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse okuchenjezani amene ndikulankhula nanu lero,+ kuti muuze ana anu kuti azionetsetsa kuti akuchita zimene mawu onse a Chilamulo ichi akunena.+ 47 Chifukwa amenewa si mawu opanda pake kwa inu, koma angakuthandizeni kukhala ndi moyo.+ Mukamatsatira mawu amenewa mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kuti mukalitenge kukhala lanu.”
48 Yehova analankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49 “Kwera mʼphiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili mʼdziko la Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa Aisiraeli kuti likhale lawo.+ 50 Kenako ukafera paphiri limene ukufuna kukwerali nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako,* mofanana ndi Aroni mʼbale wako amene anafera paphiri la Hora+ nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake. 51 Izi zili choncho chifukwa awirinu simunakhale okhulupirika kwa ine pakati pa Aisiraeli kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini, chifukwa simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli.+ 52 Iwe udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa mʼdziko limene ndikupereka kwa Aisiraeli.”+