Yehova Ndi “Mulungu Amene Amapatsa Mtendere”
“Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi nonsenu.”—AROMA 15:33.
1, 2. Kodi m’machaputala 32 ndi 33 a Genesis muli nkhani yotani ndipo zotsatira zake zinali zotani?
TAGANIZIRANI izi. Munthu ndi mchimwene wake anali atatsala pang’ono kukumana ku Penueli pafupi ndi chigwa cha Yaboki, kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Anthuwo anali Esau ndi Yakobo ndipo anali atatenga nthawi yaitali osaonana. Zaka 20 m’mbuyomu, Esau anagulitsa ukulu wake kwa m’bale wake Yakobo. Esau atamva kuti Yakobo akubwera, anapita kukamuchingamira ali ndi amuna 400. Yakobo atamva zimenezi, anaopa poganiza kuti m’bale wake akumusungirabe chakukhosi ndipo akufuna kumupha. Choncho Yakobo anatumiza anyamata ake kuti akapereke mphatso ya ziweto kwa m’bale wakeyo. Anatumiza ziwetozo m’magulumagulu. Anyamatawo akakumana ndi Esau kuti amupatse gulu la ziweto, ankamuuza kuti ziwetozo ndi mphatso yochokera kwa Yakobo. Ziweto zonse pamodzi zinali zoposa 550.
2 N’chiyani chinachitika atakumana? Yakobo anayenda molimba mtima kupita kwa Esau ndipo anagwada n’kumaweramitsa nkhope yake pansi mpaka maulendo 7. Yakobo asanachite zimenezi, anali atachita kale chinthu chofunika kwambiri. Anali atapemphera kwa Yehova kuti amuteteze kwa Esau. Kodi Yehova anayankha pemphero lake? Inde anayankha. Baibulo limanena kuti: “Esau anathamanga kudzakumana naye, ndipo anamukumbatira ndi kum’psompsona.”—Gen. 32:11-20; 33:1-4.
3. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Yakobo ndi Esau?
3 Nkhani ya Yakobo ndi Esau ikusonyeza kuti tiyenera kuyesetsa kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tithetse mavuto amene angasokoneze mtendere mu mpingo wachikhristu. Yakobo anayesetsa kukhazikitsa mtendere ndi Esau ngakhale kuti Yakoboyo sanalakwire m’bale wake. Esau ndi amene ananyoza ukulu wake n’kuugulitsa kwa m’bale wake Yakobo pousinthanitsa ndi mbale ya chakudya. (Gen. 25:31-34; Aheb. 12:16) Komabe zimene Yakobo anachita pokumana ndi Esau zimasonyeza kuti tiyenera kuchita zambiri pofuna kusunga mtendere ndi abale athu achikhristu. Zimasonyezanso kuti tikapempha Mulungu woona kuti atithandize poyesetsa kukhazikitsa mtendere, amatidalitsa. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zimene zimatithandiza kudziwa mmene tingakhazikitsire mtendere. Tsopano tiyeni tikambirane zitsanzo zina.
Chitsanzo Chapamwamba Kwambiri Choyenera Kutsatira
4. Kodi Mulungu anachita chiyani kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa?
4 Yehova ndi chitsanzo chapamwamba kwambiri pa nkhani ya kukhazikitsa mtendere. Iye ndi “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Aroma 15:33) Taganizirani zinthu zambiri zimene Yehova wachita kuti tikhale naye pa mtendere. Popeza kuti tinatengera uchimo wa makolo athu Adamu ndi Hava, ndife oyenera kulandira “malipiro a uchimo.” (Aroma 6:23) Koma Yehova anatisonyeza chikondi chachikulu kwambiri. Iye anatumiza Mwana wake wokondedwa kuti achoke kumwamba n’kubadwa monga munthu wangwiro padziko kuti atipulumutse. Mwanayo anamvera Atate ake ndi mtima wonse. Iye analolera kuphedwa ndi adani a Mulungu. (Yoh. 10:17, 18) Mulungu woona anaukitsa mwana wake wokondedwa ndipo mwanayo anapereka kwa Atate wake moyo wake wangwiro umene anaupereka nsembe padziko lapansi. Mulungu anagwiritsa ntchito nsembe ya dipo imeneyi kuti apulumutse anthu ochimwa ku imfa yosatha.—Werengani Aheberi 9:14, 24.
5, 6. Kodi magazi a Yesu amene anakhetsedwa amathandiza bwanji kukonza ubwenzi wa pakati pa anthu ochimwa ndi Mulungu?
5 Kodi nsembe ya dipo imene Mwana wa Mulungu anapereka imathandiza bwanji kukonza ubwenzi wa pakati pa anthu ochimwa ndi Mulungu umene unawonongeka? Lemba la Yesaya 53:5 limanena kuti: “Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo, ndipo chifukwa cha zilonda zake ifeyo tachiritsidwa.” Chifukwa cha zimenezi, anthu omvera angakhale pa mtendere ndi Mulungu m’malo mokhala adani ake. Baibulo limanenanso kuti: “Kudzera mwa [Yesu], tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu.”—Aef. 1:7.
6 Baibulo limanena kuti: “Kunamukomera Mulungu kuti zinthu zonse zikhale mwa [Khristu] ndipo zidzazemo bwino.” Izi zili choncho chifukwa chakuti Khristu ali ndi udindo waukulu kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Koma kodi cholinga cha Yehova n’chiyani? Cholinga chake n’chakuti “agwirizanitsenso zinthu zina zonse ndi iyeyo, pokhazikitsa mtendere mwa magazi” a Yesu Khristu amene anakhetsedwa. “Zinthu zina zonse” zimene Mulungu akuzigwirizanitsa ndi iyeyo kuti akhale nazo pa mtendere ndizo “zinthu zakumwamba” ndiponso “zinthu zapadziko lapansi.” Kodi zinthu zimenezi ndi ziti?—Werengani Akolose 1:19, 20.
7. Kodi “zinthu zakumwamba” ndiponso “zinthu zapadziko lapansi” zimene zikugwirizanitsidwa ndi Mulungu ndi ziti?
7 Dipo limachititsa kuti Akhristu odzozedwa amene ‘ayesedwa olungama’ monga ana a Mulungu, ‘akhale pa mtendere ndi Mulungu.’ (Werengani Aroma 5:1.) Iwo amatchedwa “zinthu zakumwamba” chifukwa chakuti ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba ndipo “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi” n’kumatumikira monga ansembe a Mulungu. (Chiv. 5:10) Koma “zinthu zapadziko lapansi” zikuimira anthu olapa amene adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi.—Sal. 37:29.
8. Kodi chitsanzo cha Yehova chingakuthandizeni bwanji pakakhala mavuto mu mpingo?
8 Paulo anayamikira kwambiri zimene Yehova watichitira. Posonyeza kuyamikiraku, iye analembera Akhristu odzozedwa a ku Efeso kuti: “Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka, . . . anatikhalitsa amoyo pamodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa m’machimo (pakuti inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu).” (Aef. 2:4, 5) Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padziko lapansi, timayamikira kwambiri chifundo ndiponso kukoma mtima kwa Mulungu. Timayamikira kwambiri tikaganizira zinthu zonse zimene Yehova wachita pofuna kuti anthu akhale naye pa mtendere. Pakachitika zinthu zimene zingasokoneze mtendere ndiponso mgwirizano mu mpingo, kuganizira chitsanzo cha Mulungu kungatithandize kukhazikitsa mtendere.
Tizitsatira Zitsanzo za Abulahamu ndi Isaki
9, 10. Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakonda kukhala pa mtendere ndi anthu?
9 Ponena za Abulahamu, Baibulo limati: “‘Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama,’ choncho anatchedwa ‘bwenzi la Yehova.’” (Yak. 2:23) Abulahamu ankayesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu ndipo izi zikusonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Mwachitsanzo, ziweto zake zitayamba kuchuluka, abusa ake ankakangana ndi abusa a Loti yemwe anali mwana wa mchimwene wake. (Gen. 12:5; 13:7) Kuti athetse vutoli, Abulahamu anayenera kusiyana ndi Loti. Kodi Abulahamu anatani zinthu zitavuta choncho? Iye sanaganize kuti chifukwa chakuti anali wamkulu ndiponso anali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu ndi woyenera kuuza Loti zochita. M’malomwake, anasonyeza kuti anafuna kukhala pa mtendere ndi Loti.
10 Abulahamu anauza Loti kuti: “Chonde, pasakhale mkangano uliwonse pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa abusa anga ndi abusa ako, pajatu ndife pachibale. Tiye tipatukane. Ukhoza kutenga mbali iliyonse ya dzikoli. Iwe ukapita kumanzere, ine ndipita kumanja, koma iwe ukapita kumanja, ine ndipita kumanzere.” Loti anasankha dera limene linali lachonde kwambiri, koma Abulahamu sanakwiye ndi zimene Loti anachita. (Gen. 13:8-11) Patapita nthawi, Loti atagwidwa ndi adani, Abulahamu anathamanga kukamulanditsa.—Gen. 14:14-16.
11. Kodi Abulahamu anachita chiyani kuti akhale mwamtendere ndi Afilisiti?
11 Taganiziraninso zimene Abulahamu anachita kuti akhale pa mtendere ndi Afilisiti amene ankakhala nawo m’dziko la Kanani. Afilisitiwo “analanda mwachiwawa” chitsime chimene antchito a Abulahamu anakumba ku Beere-seba. Ngakhale kuti m’mbuyomo Abulahamu anagonjetsa mafumu anayi populumutsa Loti, pa nthawiyi anasankha kusachita kapena kulankhula chilichonse. Patapita nthawi, mfumu ya Afilisiti inapita kwa Abulahamu kuti ikachite naye pangano la mtendere. Iye anapempha Abulahamu kuti alonjeze zoti adzakomera mtima ana a mfumuyo. Abulahamu atalonjeza zimenezi m’pamene anauza mfumuyo za chitsime chimene chinalandidwa chija. Mfumuyi inadabwa kwambiri ndi zimenezi ndipo inabwezera Abulahamu chitsimecho. Abulahamu anapitiriza kukhala mwamtendere ndi anthu m’dziko lachilendoli.—Gen. 21:22-31, 34.
12, 13. (a) Kodi Isaki anatengera bwanji chitsanzo cha bambo ake? (b) Kodi Yehova anadalitsa bwanji zimene Isaki anachita pofuna kusunga mtendere?
12 Nayenso Isaki, yemwe anali mwana wa Abulahamu, ankakonda mtendere. Umboni wake umaonekera pa zimene anachita ndi Afilisiti. Pothawa njala, Isaki ndi banja lake anasamuka kudera louma la Beere-lahai-roi ku Negebu n’kupita kudera lachonde ku Gerari. Derali linali la Afilisiti. Kumeneko, Yehova anamudalitsa ndi zokolola ndiponso ziweto zambiri. Ndiyeno, Afilisiti anayamba kum’chitira kaduka. Iwo sankafuna kuti Isaki zinthu zimuyendere bwino ngati mmene zinalili ndi bambo ake Abulahamu. Choncho Afilisitiwo anakwirira zitsime zimene antchito a Abulahamu anakumba m’derali. Kenako, mfumu ya Afilisiti inauza Isaki kuti: “Utichokere kwathu kuno.” Kuti asunge mtendere ndi Afilisiti, Isaki anamvera n’kuchoka.—Gen. 24:62; 26:1, 12-17.
13 Isaki atasamuka, abusa ake anakakumbanso chitsime china. Abusa achifilisiti anayamba kunena kuti madziwo ndi awo. Mofanana ndi bambo ake, Isaki sanakangane nawo za chitsimecho. M’malomwake, iye anauza abusa ake kuti akumbe chitsime china. Koma Afilisiti ananenanso kuti ndi chawo. Kuti asunge mtendere, Isaki ndi banja lake ananyamula katundu wawo yense n’kusamukiranso kudera lina. Kumeneko antchito ake anakumba chitsime chimene Isake anachipatsa dzina loti Rehoboti. Patapita nthawi, anasamukira kudera lachonde kwambiri la Beere-seba. Kumeneko Yehova anamudalitsa n’kumuuza kuti: “Usaope, chifukwa ndili nawe. Ndidzakudalitsa ndi kuchulukitsa mbewu yako chifukwa cha Abulahamu mtumiki wanga.”—Gen. 26:17-25.
14. Kodi Isaki anasonyeza bwanji kuti ankafuna kusunga mtendere pamene mfumu ya Afilisiti inabwera kudzachita naye pangano la mtendere?
14 Isaki akanatha kuteteza zitsime zonse zimene antchito ake anakumba kuti apitirize kuzigwiritsa ntchito. Koma kuti asunge mtendere, iye anasamuka kangapo. Sanafune kulimbana nawo. Kenako mfumu ya Afilisiti inazindikira kuti Yehova anali kudalitsa Isaki pa chilichonse chimene ankachita. Mfumuyo itabwera ndi akuluakulu ena ku Beere-seba kudzachita pangano la mtendere ndi Isaki, inanena kuti: “Ife taona kuti ndithu Yehova ali nawe.” Apanso, Isaki anasonyeza kuti ankafuna kusunga mtendere. Baibulo limanena kuti: “Isaki anawakonzera [alendo akewo] phwando, ndipo iwo anadya ndi kumwa. M’mawa mwake, analawirira kudzuka n’kulumbiritsana. Kenako Isaki anatsanzikana nawo . . . mwamtendere.”—Gen. 26:26-31.
Tizitsatira Chitsanzo cha Yosefe
15. N’chifukwa chiyani abale ake a Yosefe ankalephera kulankhula naye mwamtendere?
15 Yakobo, yemwe anali mwana wa Isaki, anali “munthu wosalakwa.” (Gen. 25:27) Monga tanenera poyamba paja, Yakobo anayesetsa kuti akhale pa mtendere ndi m’bale wake Esau. N’zosakayikitsa kuti Yakobo anatengera chitsanzo cha bambo ake Isaki, yemwe ankakonda mtendere. Nanga bwanji za ana a Yakobo? Pa ana ake 12, Yakobo ankakonda kwambiri Yosefe. Iye ankamvera ndiponso kulemekeza bambo ake moti bambo akewo ankamudalira kwambiri. (Gen. 37:2, 14) Koma abale ake anayamba kumuchitira nsanje kwambiri moti ankalephera kulankhula naye mwamtendere. Ankamuda kwambiri Yosefe mpaka kufika pomugulitsa kuti akhale kapolo. Kenako ananamiza bambo awo kuti Yosefe anaphedwa ndi chilombo.—Gen. 37:4, 28, 31-33.
16, 17. Kodi Yosefe anasonyeza bwanji kuti ankafuna kukhala pa mtendere ndi abale ake?
16 Yehova anamudalitsa Yosefe. Patapita nthawi, Yosefe anakhala nduna yaikulu ya Iguputo. Iye anali wachiwiri kwa Farao. Tsopano ku Kanani kunagwa njala yoopsa, ndipo abale ake a Yosefe anapita ku Iguputo kukagula chakudya. Iwo sanazindikire Yosefe chifukwa cha zovala za ku Iguputo zimene anavala. (Gen. 42:5-7) Zikanakhala zosavuta kuti Yosefe abwezere abale ake pa zoipa zimene anachitira iyeyo ndi bambo awo. Koma m’malo mobwezera, iye anayesetsa kuti akhale nawo pa mtendere. Ataona kuti iwo alapa, Yosefe anadzidziwikitsa kwa iwo. Iye anati: “Musadzimvere chisoni kapena kudzipsera mtima kuti munandigulitsa kuno. Mulungu ndiye ananditumiza patsogolo panu kuti ndidzapulumutse miyoyo yanu.” Kenako Yosefe anayamba kupsompsona abale ake onsewo n’kumalira akuwakumbatira.—Gen. 45:1, 5, 15.
17 Yakobo atamwalira, abale ake a Yosefe anaganiza kuti tsopano Yosefe akhoza kuwabwezera. Atauza Yosefe zimenezi, iye “analira kwambiri” n’kuyankha kuti: “Musachite mantha. Ine ndipitiriza kukugawirani chakudya limodzi ndi ana anu.” Apa Yosefe anasonyezanso kuti ankakonda mtendere. Iye “anawalimbikitsa n’kuwatsimikizira” kuti sadzawabwezera.—Gen. 50:15-21.
“Zinalembedwa Kuti Zitilangize”
18, 19. (a) Kodi mwaphunzira chiyani pa zitsanzo zimene takambirana m’nkhaniyi? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Paulo analemba kuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Kodi taphunzira chiyani pa chitsanzo chapamwamba kwambiri cha Yehova ndiponso pa zimene Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Yosefe anachita?
19 Kuganizira zimene Yehova wachita pofuna kukonza ubwenzi wa pakati pa iye ndi anthu ochimwa kungatilimbikitse kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhale pa mtendere ndi anthu ena. Chitsanzo cha Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Yosefe chimasonyeza kuti makolo akhoza kuthandiza kwambiri ana awo. Nkhanizi zimasonyezanso kuti Yehova amadalitsa anthu akamayesetsa kukhala pa mtendere ndi anzawo. M’pake kuti Paulo ananena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Werengani Aroma 15:33; 16:20.) Koma n’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti tiyenera kuyesetsa kukhala pa mtendere ndi anthu ndipo tingachite bwanji zimenezi? M’nkhani yotsatira tidzakambirana mayankho a mafunso amenewa.
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• Kodi Yakobo atatsala pang’ono kukumana ndi Esau anachita chiyani pofuna kuti akhale naye pa mtendere?
• Kodi zimene Yehova anachita kuti anthu akhale naye pa mtendere zimakulimbikitsani kuchita chiyani?
• Kodi mwaphunzira chiyani pa chitsanzo cha Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Yosefe?
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi mukudziwa chinthu chofunika kwambiri chimene Yakobo anachita pofuna kuti akhalenso pa mtendere ndi Esau?