Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi
“Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu.”—SALMO 86:11.
1. Kodi nchiyani makamaka chimene kope loyamba la magazini ano linanena ponena za choonadi?
YEHOVA amatumiza kuunika ndi choonadi. (Salmo 43:3) Amatipatsanso luso la kuŵerenga Mawu ake, Baibulo, ndi kuphunzira choonadi. Kope loyamba la magazini ano—July 1879—linati: “Choonadi, monga momwe lilili duŵa wamba laling’ono m’chipululu cha moyo, nchozingidwa ndipo pafupifupi chotsamwitsidwa ndi zomera zina zomakula kwambiri za chinyengo. Kuti muchipeze muyenera kuyang’anitsitsa nthaŵi zonse. Kuti muone kukongola kwake muyenera kukankhira m’mbali zomera zinazo za chinyengo ndi ziyangoyango zaminga za liuma. Kuti chikhale chanu muyenera kuŵerama ndi kuchitola. Musakhutire ndi duŵa limodzi la choonadi. Duŵa limodzi likanakhala lokwanira sipakanakhalanso ena. Sonkhanitsani mosalekeza, funani ambiri.” Kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kumatikhozetsa kupeza chidziŵitso cholongosoka ndi kuyenda m’choonadi chake.—Salmo 86:11.
2. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Ezara ndi ena anaŵerengera Ayuda Chilamulo cha Mulungu mu Yerusalemu wakale?
2 Malinga a Yerusalemu atamangidwa mu 455 B.C.E., wansembe Ezara ndi ena anaŵerengera Ayuda Chilamulo cha Mulungu. Zimenezi zinatsatiridwa ndi Madyerero a Misasa achimwemwe, kuulula machimo, ndi kuchita “pangano lokhazikika.” (Nehemiya 8:1–9:38) Timaŵerenga kuti: “Naŵerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa choŵerengedwacho.” (Nehemiya 8:8) Ena amalingalira kuti Ayuda sanamve bwino Chihebri ndi kuti anawafotokozera m’Chiaramu. Koma vesilo silimasonyeza za kutanthauzira wamba kwa mawu achinenero. Ezara ndi ena anafotokoza Chilamulocho kotero kuti anthu adziŵe tanthauzo la mapulinsipulo ake ndi kuwagwiritsira ntchito. Zofalitsa zachikristu ndi misonkhano nazonso zimathandizira ‘kutanthauzira’ Mawu a Mulungu. Chimodzimodzinso akulu oikidwa, amene ali ‘odziŵa kuphunzitsa.’—1 Timoteo 3:1, 2; 2 Timoteo 2:24.
Mapindu Okhalitsa
3. Kodi ndi mapindu ena otani amene amapezedwa m’kuŵerenga Baibulo?
3 Pamene mabanja achikristu aŵerenga Baibulo pamodzi, mwachionekere amakhala ndi mapindu okhalitsa. Amadziŵa malamulo a Mulungu ndi kudziŵa zoona ponena za ziphunzitso, nkhani zaulosi, ndi nkhani zina. Ataŵerenga chigawo china cha Baibulo, mutu wa banja ungafunse kuti: Kodi zimenezi ziyenera kutiyambukira motani? Kodi zimenezi zikugwirizana motani ndi ziphunzitso zina za Baibulo? Kodi tingagwiritsire ntchito motani mfundo zimenezi polalikira uthenga wabwino? Banja limapeza chidziŵitso chachikulu pamene liŵerenga Baibulo ngati lifufuza nkhani mwa kugwiritsira ntchito Watch Tower Publications Index kapena maindekisi ena. Mavoliyumu aŵiri a Insight on the Scriptures angafufuzidwemo ndi kupezamo mapindu.
4. Kodi Yoswa anafunikira kugwiritsira ntchito motani malangizo olembedwa pa Yoswa 1:8?
4 Mapulinsipulo otengedwa m’Malemba angatitsogolere m’moyo. Ndiponso, kuŵerenga ndi kuphunzira ‘malembo opatulika kungatipatse nzeru kufikira chipulumutso.’ (2 Timoteo 3:15) Ngati tilola Mawu a Mulungu kutitsogolera, tidzapitiriza kuyenda m’choonadi chake ndipo chikhumbo chathu cholungama chidzakwaniritsidwa. (Salmo 26:3; 119:130) Komabe, tifunikira kufunafuna kuzindikira, monga momwe woloŵa malo a Mose, Yoswa anachitira. “Buku . . . la chilamulo” silinafunikire kuchoka pakamwa pake, ndipo anafunikira kuŵerengamo usana ndi usiku. (Yoswa 1:8) Kusachotsa “buku . . . la chilamulo” pakamwa pake kunatanthauza kuti Yoswa sanafunikire kuleka kuuza ena zinthu zopatsa chidziŵitso zimene ilo linanena. Kuŵerenga Chilamulo usana ndi usiku kunatanthauza kuti Yoswa anafunikira kuchisinkhasinkha, anafunikira kuchiphunzira. Mofananamo mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo “kusamalitsa”—mwakusinkhasinkha—khalidwe lake, utumiki, ndi kuphunzitsa kwake. Monga mkulu wachikristu, Timoteo anafunikira makamaka kukhala wosamala kuona kuti moyo wake unali wachitsanzo chabwino ndi kuti anaphunzitsa choonadi cha m’Malemba.—1 Timoteo 4:15.
5. Kodi nchiyani chimene chikufunika ngati titi tipeze choonadi cha Mulungu?
5 Choonadi cha Mulungu ndicho chuma chamtengo wosayerekezereka. Kuchipeza kumafuna kukumba, kusanthula Malemba kwakhama. Ndi kukhala monga ana ophunzira a Mlangizi Wamkulu kokha kumene tingapeze nako nzeru ndi kufikira pa kuzindikira kuwopa Yehova kwaulemu. (Miyambo 1:7; Yesaya 30:20, 21) Zoonadi, tiyenera kutsimikizira zinthu mwa Malemba. (1 Petro 2:1, 2) Ayuda ku Bereya “anali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu [zonenedwa ndi Paulo] zinali zotero.” Iye anayamikira m’malo mwa kudzudzula Abereya chifukwa cha kuchita zimenezi.—Machitidwe 17:10, 11.
6. Kodi nchifukwa ninji Yesu anatha kusonyeza kuti kusanthula Malemba sikunawathandize Ayuda?
6 Yesu anauza Ayuda ena kuti: “Musanthula m’Malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira ine umboni ndi iwo omwewo; ndipo simufuna kudza kwa ine, kuti mukhale nawo moyo.” (Yohane 5:39, 40) Anasanthula Malemba ndi cholinga chabwino—kuti ameneŵa awatsogolere ku moyo. Indedi, Malembawo anali ndi maulosi a Mesiya amene anasonya kwa Yesu kukhala njira ya moyo. Koma Ayuda anamkana. Motero, kusanthula Malemba sikunawathandize.
7. Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tikulitse kumvetsetsa Baibulo, ndipo chifukwa ninji?
7 Kuti tikulitse kumvetsetsa kwathu Baibulo, tifunikira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. “Mzimu [u]santhula zonse, zakuya za Mulungu zomwe” kuti tidziŵe tanthauzo lake. (1 Akorinto 2:10) Akristu ku Tesalonika anafunikira ‘kuyesa zonse’ pa ulosi uliwonse umene anamva. (1 Atesalonika 5:20, 21) Pamene Paulo analembera Atesalonika (cha ku ma 50 C.E.), mbali yokha ya Malemba Achigiriki imene inali italembedwa kale inali Uthenga Wabwino wa Mateyu. Chotero Atesalonika ndi Abereya akanatha kutsimikiza zinthu zonse, mwachionekere mwa kupenda matembenuzidwe a Septuagint yachigiriki ya Malemba Achihebri. Anafunikira kuŵerenga ndi kuphunzira Malemba, ndipo nafenso tifunikira kutero.
Kofunika kwa Onse
8. Kodi nchifukwa ninji akulu oikidwa afunikira kukhala ndi chidziŵitso chopambana cha Baibulo?
8 Akulu oikidwa afunikira kukhala ndi chidziŵitso chopambana cha Baibulo. Ayenera kukhala ‘okhoza kuphunzitsa’ ndipo ayenera ‘kugwira mawu okhulupirika.’ Woyang’anira Timoteo anafunikira kukhala “wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (1 Timoteo 3:2; Tito 1:9; 2 Timoteo 2:15) Amake, a Yunike, ndi agogo wake aakazi a Loisi anamphunzitsa malembo opatulika kuyambira ukhanda, kuloŵetsa “chikhulupiriro chosanyenga” mwa iye, ngakhale kuti atate wake anali wosakhulupirira. (2 Timoteo 1:5; 3:15) Atate okhulupirira ayenera kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW],” ndipo makamaka akulu amene ali atate ‘okhala nawo ana okhulupirira kapena osasakaza’ ayenera kuchita zimenezi. (Aefeso 6:4; Tito 1:6) Pamenepo, mosasamala kanthu za mikhalidwe yathu, tiyenera kuona mwamphamvu kufunika kwa kuŵerenga, kuphunzira, ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu.
9. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuphunzira Baibulo limodzi ndi Akristu anzathu?
9 Tiyeneranso kuphunzira Baibulo limodzi ndi okhulupirira anzathu. Paulo anafuna kuti Akristu a ku Tesalonika azikambitsirana za uphungu wake. (1 Atesalonika 4:18) Kuti tinole kuzindikira kwathu choonadi, palibe njira ina yabwino kwambiri kuposa ya kugwirizana ndi ophunzira ena odzipereka pa kusanthula Malemba. Mwambiwu ngwoona: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17) Chipangizo chachitsulo chingachite dzimbiri ngati sichikugwiritsiridwa ntchito ndi kunoledwa. Mofananamo, tifunikira kusonkhana nthaŵi zonse ndi kunolana mwa kugaŵana chidziŵitso chimene tapeza m’kuŵerenga, kuphunzira, ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu a choonadi. (Ahebri 10:24, 25) Ndiponso, imeneyi ndiyo njira imodzi yotsimikizirira kuti tikupindula ndi kuŵala kwa kuunika kwauzimu.—Salmo 97:11; Miyambo 4:18.
10. Kodi kuyenda m’choonadi kumatanthauzanji?
10 Pakuphunzira kwathu Malemba, tingapemphere moyenera kwa Mulungu monga momwe wamasalmo anachitira: “Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere.” (Salmo 43:3) Ngati tifuna chiyanjo cha Mulungu, tiyenera kuyenda m’choonadi chake. (3 Yohane 3, 4) Zimenezi zikuphatikizapo kuchita mogwirizana ndi zofunika zake ndi kumtumikira mokhulupirika ndi moona mtima. (Salmo 25:4, 5; Yohane 4:23, 24) Tiyenera kutumikira Yehova m’choonadi, monga momwe chavumbulidwira m’Mawu ake ndi kufotokozedwa momveka m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Zimenezi zimafuna chidziŵitso cholongosoka cha Malemba. Nangano, ndi motani mmene tiyenera kuŵerengera ndi kuphunzira Mawu a Mulungu? Kodi tiyenera kuyamba kuŵerenga kuchokera Genesis chaputala 1, vesi 1, mpaka kumaliza mabuku 66 onse? Inde, Mkristu aliyense amene ali ndi Baibulo lathunthu m’chinenero chake ayenera kuliŵerenga kuyambira ku Genesis kukafika ku Chivumbulutso. Ndipo cholinga chathu poŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zachikristu chiyenera kukhala kuwonjezera kumvetsetsa kwathu zinthu zochuluka za choonadi cha m’Malemba chimene Mulungu wapereka kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika.”
Ŵerengani Mawu a Mulungu Momveka
11, 12. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kuŵerenga Baibulo momveka pamisonkhano?
11 Tingaŵerengere mumtima pamene tili tokha. Komabe, m’nthaŵi zakale, kuŵerenga kwaumwini kunali kuchitidwa momveka. Pamene mdindo wa ku Aitiopiya anali kuyenda pa galeta lake, mlaliki Filipo anamumva akuŵerenga mu ulosi wa Yesaya. (Machitidwe 8:27-30) Liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “ŵerenga” makamaka limatanthauza “kuitana.” Chotero awo amene poyamba satha kuŵerengera mumtima ndi kupeza lingaliro la zimene akuŵerenga sayenera kuzengereza kutchula liwu ndi liwu momveka. Chinthu chachikulu ndicho kuphunzira choonadi mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu olembedwa.
12 Nkopindulitsa kuŵerenga Baibulo momveka pamisonkhano yachikristu. Mtumwi Paulo analimbikitsa wantchito mnzake Timoteo kuti: “Usamalire kuŵerenga [poyera, NW], kuchenjeza, kulangiza.” (1 Timoteo 4:13) Paulo anauza Akolose kuti: “Pamene mudamŵerenga kalata uyu, amŵerengenso mumpingo wa ku Laodikaya, ndi inunso muŵerenge wa ku Laodikaya.” (Akolose 4:16) Ndipo Chivumbulutso 1:3 (NW) chimati: “Wachimwemwe ndi iye amene amaŵerenga momveka ndi aja amene amamva mawu a ulosiwu, ndi amene amasunga zinthu zolembedwamo; pakuti nthaŵi yoikidwiratu yayandikira.” Chotero, wokamba nkhani yapoyera ayenera kuŵerenga mavesi a m’Baibulo kuti achirikize zimene akunena ku mpingo.
Njira ya Kuphunzira Yolondola Mitu ya Nkhani
13. Kodi njira yopita patsogolo kwambiri ya kuphunzira choonadi cha Baibulo njotani, ndipo kodi nchiyani chimene chingatithandize kupeza malemba?
13 Kuphunzira kolondola mitu ya nkhani ndiko njira yopita patsogolo kwambiri ya kuphunzira choonadi cha m’Malemba. Makonkodansi, ondandalika mawu a Baibulo monga mwa alufabeti malinga ndi nkhani yake ya buku, chaputala, ndi vesi, amapangitsa kupeza mavesi ogwirizana ndi nkhaniyo kukhala kosavuta. Ndipo malemba amenewo angagwirizanitsidwe lina ndi linzake chifukwa chakuti Mlembi Wamkulu wa Baibulo samadzitsutsa. Mwa mzimu wake woyera, iyeyo anauzira amuna 40 kulemba Baibulo m’nyengo yoposa zaka mazana 16, ndipo kuliphunzira molondola mitu ya nkhani kwakhala njira yophunzirira choonadi yothandiza nthaŵi yaitali.
14. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuphunzirira pamodzi Malemba Achihebri ndi Achigiriki Achikristu?
14 Kuyamikira kwathu choonadi cha Baibulo kuyenera kutisonkhezera kuŵerenga ndi kuphunzira Malemba Achigiriki Achikristu limodzi ndi Malemba Achihebri. Zimenezi zidzasonyeza mmene Malemba Achigiriki alili ogwirizana ndi chifuno cha Mulungu ndipo zidzaunikira pamaulosi a m’Malemba Achihebri. (Aroma 16:25-27; Aefeso 3:4-6; Akolose 1:26) Yothandiza kwambiri pa zimenezi ndi New World Translation of the Holy Scriptures. Inakonzedwa ndi atumiki a Mulungu odzipatulira amene anagwiritsira ntchito mwaŵi wa chidziŵitso chowonjezereka chimene chilipo chonena za malembo oyambirira a Baibulo ndiponso mbiri yake ndi mawu ake okuluwika. Zofunikanso kwambiri ndizo mabuku othandizira kuphunzira Baibulo amene Yehova wapereka kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”
15. Kodi mungasonyeze motani kuti kuli koyenera kugwira mawu m’malo osiyanasiyana m’Baibulo?
15 Ena anganene kuti, ‘Zofalitsa zanu zimagwira mawu ambirimbiri a m’Baibulo, koma kodi nchifukwa ninji mumagwira mawu m’malo osiyanasiyana?’ Mwa kugwira mawu apo ndi apo m’mabuku 66 a Baibulo, zofalitsazo zimasonkhanitsa umboni wambiri wouziridwa kuti zisonyeze choonadi cha chiphunzitsocho. Yesu mwiniyo anagwiritsira ntchito njira imeneyi ya kulangiza. Pamene anapereka Ulaliki wake wa pa Phiri, anagwira mawu okwanira 21 kuchokera m’Malemba Achihebri. Nkhani imeneyo ili ndi mawu atatu ogwidwa kuchokera mu Eksodo, aŵiri kuchokera mu Levitiko, amodzi kuchokera mu Numeri, asanu ndi amodzi kuchokera mu Deuteronomo, amodzi kuchokera mu Mafumu Wachiŵiri, anayi kuchokera mu Masalmo, atatu kuchokera mu Yesaya, ndi amodzi kuchokera mu Yeremiya. Kodi Yesu anali ‘kuyesa kusonyeza zinthu zilizonse chabe’ mwa kuchita motero? Ayi, “pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi.” Zimenezo zinali choncho chifukwa chakuti Yesu anachirikiza chiphunzitso chake ndi ulamuliro wa Mawu a Mulungu olembedwa. (Mateyu 7:29) Nayenso mtumwi Paulo anachita motero.
16. Kodi Paulo anagwira mawu Malemba ati pa Aroma 15:7-13?
16 M’chigawo cha malemba chopezeka pa Aroma 15:7-13, Paulo anagwira mawu m’zigawo zitatu za Malemba Achihebri—Chilamulo, Aneneri, ndi Masalmo. Anasonyeza kuti Ayuda ndi Akunja adzalemekeza Mulungu, ndipo motero Akristu anayenera kulandira mitundu yonse. Paulo anati: “Mulandirane wina ndi mnzake, monganso Kristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero. Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo, ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa [pa Salmo 18:49], Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu. Ndiponso anena [pa Deuteronomo 32:43], Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso [pa Salmo 117:1], Tamandani [Yehova, NW], inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya [11:1, 10] ati, Padzali muzu wa Jese, ndi iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya mzimu woyera.” Mwa njira imeneyi yolondola mutu wa nkhani, Paulo anasonyeza mmene munthu angagwirire mawu malemba kuti asonyeze choonadi cha Baibulo.
17. Kodi Akristu amachita mogwirizana ndi chitsanzo chiti pogwira mawu m’malo osiyanasiyana m’Baibulo lonse?
17 Kalata youziridwa yoyamba ya mtumwi Petro ili ndi mawu ogwidwa 34 kuchokera m’mabuku khumi m’Chilamulo, Aneneri, ndi Masalmo. M’kalata yake yachiŵiri, Petro akugwira mawu nthaŵi zisanu ndi imodzi kuchokera m’mabuku atatu. Uthenga Wabwino wa Mateyu uli ndi mawu ogwidwa 122 kuchokera ku Genesis kufikira ku Malaki. M’mabuku 27 a Malemba Achigiriki, muli mawu 320 ogwidwa mwachindunji kuchokera mu Genesis kufikira ku Malaki ndiponso zilozero zina zotchula Malemba Achihebri. Mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa ndi Yesu chimenenso atumwi ake anatsatira, pamene Akristu amakono apanga phunziro lolondola mutu wa nkhani ya m’Malemba, amagwira mawu apo ndi apo m’Baibulo lonse limene. Zimenezi makamaka nzoyenerera mu “masiku otsiriza” ano, pamene Malemba ochuluka Achihebri ndi Achigiriki akukwaniritsidwa. (2 Timoteo 3:1) “Kapolo wokhulupirika” amagwiritsira ntchito Baibulo mwa njira imeneyo m’zofalitsa zake, koma samawonjezera kanthu pa Mawu a Mulungu kapena kuchotsapo.—Miyambo 30:5, 6; Chivumbulutso 22:18, 19.
Yendani m’Choonadi Nthaŵi Zonse
18. Kodi nchifukwa ninji tiyenera “kuyenda m’choonadi”?
18 Sitiyenera kuchotsa kanthu kalikonse m’Baibulo, pakuti ziphunzitso zonse zachikristu m’Mawu a Mulungu ndizo “choonadi” kapena “choonadi cha uthenga wabwino.” Kutsatira choonadi chimenechi—‘kuyendamo’—nkofunika kaamba ka chipulumutso. (Agalatiya 2:5; 2 Yohane 4; 1 Timoteo 2:3, 4) Popeza kuti Chikristu chili “njira ya choonadi,” mwa kuthandiza ena kupititsa patsogolo zolinga zake, timakhala “othandizana nacho choonadi.”—2 Petro 2:2; 3 Yohane 8.
19. Kodi ndi motani mmene tingapitirizire “kuyenda m’choonadi”?
19 Ngati titi tipitirize “kuyenda m’choonadi,” tiyenera kuŵerenga Baibulo ndi kudzipezera thandizo lauzimu limene Mulungu akupereka kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika.” (3 Yohane 4) Tichitetu zimenezi kaamba ka ubwino wathu kotero kuti tikhale okhoza kuphunzitsa ena za Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi chifuno cha Mulungu. Ndipo tiyenitu tithokoze kuti mzimu wa Yehova umatithandiza kumvetsa Mawu ake ndi kukhoza kumtumikira m’choonadi.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi mapindu ena okhalitsa a kuŵerenga Baibulo ngotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuphunzira Baibulo ndi okhulupirira anzathu?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kugwira mawu m’malo osiyanasiyana m’Baibulo lonse?
◻ Kodi “kuyenda m’choonadi” kumatanthauzanji, ndipo tingachite motani zimenezo?
[Chithunzi patsamba 17]
Makolo, phunzitsani ana anu Malemba
[Chithunzi patsamba 18]
Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anagwira mawu mbali zosiyanasiyana za Malemba Achihebri