Kukhala Tate ndi Mkulu—Kukwaniritsa Mbali Zonse Ziŵiri
“Ngati munthu sadziŵa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji mpingo wa Mulungu?”—1 TIMOTEO 3:5.
1, 2. (a) M’zaka za zana loyamba, kodi oyang’anira osakwatira ndi okwatira omwe opanda ana anakhoza motani kutumikira abale awo? (b) Kodi Akula ndi Priskila anali chitsanzo chotani kwa okwatirana ambiri a lerolino?
OYANG’ANIRA mumpingo wachikristu woyambirira anali amuna osakwatira kapena amuna okwatira opanda ana, kapena amuna okhala ndi banja ndi ana. Mosakayikira, ena mwa Akristu amenewo anakhoza kutsatira chilangizo cha mtumwi Paulo chimene anapereka m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, chaputala 7, cha kusakwatira. Yesu anali atanena kuti: “Pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu Wakumwamba.” (Mateyu 19:12) Amuna osakwatira oterowo, onga Paulo, ndipo mwinamwake enanso mwa anzake oyenda nawo, anali omasuka kuyenda maulendo okathandiza abale awo.
2 Baibulo silimanena kuti kaya Barnaba, Marko, Sila, Luka, Timoteo, ndi Tito anali okwatira kapena ayi. Ngati anali okwatira, mwachionekere anali omasuka mokwanira ku mathayo a banja kwakuti anali okhoza kuyenda maulendo aatali ku mautumiki osiyanasiyana. (Machitidwe 13:2; 15:39-41; 2 Akorinto 8:16, 17; 2 Timoteo 4:9-11; Tito 1:5) Ayenera kuti ankayenda ndi akazi awo, monga Petro “monganso atumwi ena,” amene akuoneka kuti anatenga akazi awo popita ku malo ndi malo. (1 Akorinto 9:5) Akula ndi Priskila ali chitsanzo cha okwatirana omwe anali ofunitsitsa kusamuka, akumatsatira Paulo kuchokera ku Korinto kumka ku Efeso, ndiyeno ku Roma, ndi kubwereranso ku Efeso. Baibulo silimanena ngati kuti iwo anali ndi ana. Utumiki wawo wodzipereka kaamba ka abale awo unapangitsa “mipingo yonse ya . . . anthu amitundu” kuyamikira. (Aroma 16:3-5; Machitidwe 18:2, 18; 2 Timoteo 4:19) Lerolino, alipodi anthu ambiri okwatirana omwe, mofanana ndi Akula ndi Priskila, akhoza kutumikira mipingo ina, mwinamwake mwa kusamukira kumene kuli kusoŵa kokulira.
Kukhala Tate ndi Mkulu
3. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti akulu ambiri a m’zaka za zana loyamba anali amuna okwatira okhala ndi mabanja?
3 Zikuoneka kuti m’zaka za zana loyamba C.E., akulu achikristu ochuluka anali amuna okwatira okhala ndi ana. Pamene Paulo anandandalika ziyeneretso zofunika kwa mwamuna amene “akhumba udindo wa woyang’anira,” ananena kuti Mkristu woteroyo ayenera kukhala “woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nawo ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.”—1 Timoteo 3:1, 4.
4. Kodi nchiyani chinali chofunika kwa akulu okwatira okhala ndi ana?
4 Monga momwe taonera, woyang’anira analibe chomukakamiza kukhala ndi ana, kapena ngakhale kukwatira. Koma ngati anali wokwatira, kuti ayeneretsedwe kukhala mkulu kapena mtumiki wotumikira, Mkristu anafunikira kuchita umutu woyenera ndi wachikondi pa mkazi wake ndi kudzisonyeza kukhala wokhoza kuphunzitsa ana ake kukhala ogonjera. (1 Akorinto 11:3; 1 Timoteo 3:12, 13) Chifooko chachikulu chilichonse pa kusamalira banja lake chinapangitsa mbale kusayenerera mathayo apadera mumpingo. Chifukwa ninji? Paulo akufotokoza kuti: “Ngati munthu sadziŵa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji mpingo wa Mulungu?” (1 Timoteo 3:5) Ngati a m’banja lake anali kukana kugonjera ku uyang’aniro wake, kodi ena angalabadire motani kwa iye?
“Wokhala Nawo Ana Okhulupirira”
5, 6. (a) Kodi nchofunika chotani kwa ana chimene Paulo anatchula kwa Tito? (b) Kodi nchiyani chikuyembekezeredwa kwa akulu omwe ali ndi ana?
5 Polangiza Tito za kuika oyang’anira m’mipingo ya ku Krete, Paulo anati: “Ngati wina ali wopanda chirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nawo ana okhulupirira, [opanda chinenezo cha makhalidwe onyansa kapena cha kusamvera, NW]. Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chirema, ngati mdindo wa Mulungu.” Kodi chiyeneretso cha ‘kukhala nawo ana okhulupirira’ chimatanthauzanji kwenikweni?—Tito 1:6, 7.
6 Mawu akuti “ana okhulupirira” akunena za achichepere omwe anapatulira kale miyoyo yawo kwa Yehova ndi kubatizidwa kapena achichepere omwe akupita patsogolo kulinga ku kudzipatulira ndi ubatizo. Ziŵalo za mpingo zimayembekezera ana a akulu kukhala odzisunga ndi omvera. Kuyenera kukhala koonekera kuti mkulu akuyesa kwenikweni kumangirira chikhulupiriro cha ana ake. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Koma bwanji ngati wachichepere amene anaphunzitsidwa zimenezo akana kutumikira Yehova kapena ngati achita cholakwa chachikulu?
7. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli koonekeratu kuti Miyambo 22:6 siimapereka lamulo losasinthika? (b) Ngati mwana wa mkulu sasankha kutumikira Yehova, kodi nchifukwa ninji zimenezo mwa izo zokha sizidzachititsa mkuluyo kulandidwa mathayo ake?
7 Nkoonekeratu kuti mwambi wogwidwa mawu pamwambapa sukukhazikitsa lamulo losasinthika. Sukufafaniza lamulo la ufulu wa kudzisankhira. (Deuteronomo 30:15, 16, 19) Pamene mwana afika pamsinkhu wa kukhala ndi thayo, ayenera kudzipangira chosankha ponena za kudzipatulira ndi ubatizo. Ngati moonekera bwino mkulu wapereka chithandizo chonse chauzimu chofunikira, chitsogozo ndi chilangizo ndipo wachichepereyo sasankha kutumikira Yehova, tateyo samachotsedwa pa kutumikira monga woyang’anira kokha chifukwa cha zimenezo. Komabe, ngati mkulu ali ndi ana aang’ono angapo omwe akukhala panyumba, ndipo amene mmodzi ndi mmodzi adwala mwauzimu ndi kugwera m’vuto, iye sangaonedwenso kukhala “woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha.” (1 Timoteo 3:4) Mfundo ndi yakuti, kuyenera kukhala koonekeratu kuti woyang’anira akuyesayesa kwenikweni kukhala ndi ‘ana okhulupirira opanda chinenezo cha makhalidwe onyansa kapena kusamvera.’a
Wokwatira “Mkazi Wosakhulupirira”
8. Kodi mkulu ayenera kuchita motani kulinga kwa mkazi wake wosakhulupirira?
8 Ponena za amuna achikristu amene ali ndi akazi osakhulupirira, Paulo analemba kuti: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. . . . Pakuti . . . mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Pakuti udziŵa bwanji . . . mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?” (1 Akorinto 7:12-14, 16) Liwu lakuti “wosakhulupirira” pano silikunena za mkazi wosapembedza koma mkazi wosadzipatulira kwa Yehova. Iye angathe kukhala anali Myuda, kapena wokhulupirira milungu yachikunja. Lerolino, mkulu angakhale wokwatira mkazi wa chipembedzo china, wokayikira Mulungu, kapena ngakhale wokana Mulungu. Ngati mkaziyo akufuna kukhala naye, iye sayenera kumsiya pa chifukwa cha kusiyana zikhulupiriro chabe. Ayenera ‘kukhalabe naye monga mwa chidziŵitso, akumamchitira ulemu monga chotengera chochepa mphamvu,’ akumakhala ndi chiyembekezo cha kupulumutsa mkaziyo.—1 Petro 3:7; Akolose 3:19.
9. M’maiko amene lamulo limapatsa onse aŵiri mwamuna ndi mkazi mphamvu za kuphunzitsa ana awo zikhulupiriro za chipembedzo chawo, kodi mkulu ayenera kuchita motani, ndipo kodi zimenezi zidzayambukira motani mathayo ake?
9 Ngati woyang’anira ali ndi ana, ayenera kuchita umutu wake monga mwamuna ndi tate m’njira yoyenera powalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) M’maiko ambiri lamulo limapatsa okwatirana onse aŵiri mphamvu za kuphunzitsa ana awo chipembedzo. Zikakhala motero, mkazi angafune kugwiritsira ntchito mphamvu zake za kuphunzitsa ana ake zikhulupiriro ndi machitidwe a chipembedzo chake, zimene zingaphatikizepo kupita nawo ku tchalitchi chake.b Ndithudi, ana ayenera kutsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo ponena za kusachita nawo zikondwerero za chipembedzo. Monga mutu wa banja, tate ayenera kugwiritsira ntchito mphamvu zake kumaphunzira ndi ana ake ndi kupita nawo kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu pamene kuli kotheka. Pamene afika pamsinkhu umene angapange zosankha zawo, adzadzisankhira okha njira imene adzailondola. (Yoswa 24:15) Ngati akulu anzake ndi ziŵalo za mpingo ziona kuti iye akuchita zonse zomwe lamulo limamlola kuchita pa kuphunzitsa ana ake moyenera m’njira ya choonadi, sadzachotsedwa pathayo la woyang’anira.
“Woweruza Bwino Nyumba Yake”
10. Ngati mkulu ali ndi banja, kodi thayo lake loyambirira limakhala pati?
10 Ngakhale kwa mkulu amene ali tate amene mkazi wake ndi Mkristu mnzake, siimakhala ntchito yopepuka kugaŵa moyenera nthaŵi yake ndi maganizo ake pakati pa mkazi wake, ana ake, ndi mathayo a mumpingo. Malemba amasonyeza bwino lomwe kuti tate wachikristu ali ndi thayo la kusamalira mkazi wake ndi ana ake. Paulo analemba kuti: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) M’kalata imodzimodziyo, Paulo ananena kuti amuna okwatira amene asonyeza kale kukhala amuna ndi atate abwino ndiwo okha amene ayenera kuvomerezedwa kutumikira monga oyang’anira.—1 Timoteo 3:1-5.
11. (a) Kodi ndi m’njira zotani zimene mkulu ayenera ‘kusunga banja lake la iye yekha’? (b) Kodi zimenezi zingamthandize motani mkulu kukwaniritsa mathayo ake mumpingo?
11 Mkulu ayenera ‘kusunga’ banja lake si mwa zinthu zakuthupi chabe komanso zauzimu ndi zamaganizo. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” (Miyambo 24:27) Motero, pamene woyang’anira akusamalira zosoŵa zakuthupi, zamaganizo, ndi za zosangulutsa za mkazi wake ndi ana, ayeneranso kuwamangirira mwauzimu. Zimenezi zimatenga nthaŵi—nthaŵi imene sadzakhoza kuitayira pa zinthu za mpingo. Koma ili nthaŵi imene ingadzetse phindu lalikulu ponena za chimwemwe cha banja ndi mkhalidwe wake wauzimu. M’kupita kwa nthaŵi, ngati banja lake nlolimba kuuzimu, mkuluyo sangafunikire kuthera nthaŵi yochuluka pakusamalira mavuto a banja. Zimenezi zidzachititsa maganizo ake kukhala omasuka kwambiri moti nkusamalira bwino zinthu za mpingo. Chitsanzo chake monga mwamuna wabwino ndi tate wabwino chidzadzetsanso mapindu auzimu pa mpingo.—1 Petro 5:1-3.
12. Kodi ndi m’mbali iti ya banja mmene atate amene ali akulu ayenera kupereka chitsanzo chabwino?
12 Kuweruza bwino nyumba kumaphatikizapo kuika nthaŵi ya kuchititsa phunziro la banja. Nkofunika kwambiri kuti akulu apereke chitsanzo chabwino pambali imeneyi, pakuti mabanja olimba amapanga mipingo yolimba. Nthaŵi ya woyang’anira siyenera kukhala yochulukidwa nthaŵi zonse ndi mathayo ena autumiki kwakuti akusoŵeratu nthaŵi ya kuphunzira ndi mkazi wake ndi ana. Ngati umu ndi mmene zinthu zakhalira, ayenera kupendanso programu yake. Angafunikire kusintha kapena kuchepetsa nthaŵi imene amaitayira pa zinthu zina, ngakhale kukana mathayo ena nthaŵi zina.
Uyang’aniro Wolinganizika Bwino
13, 14. Kodi ndi uphungu wotani umene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka kwa akulu amene ali ndi banja?
13 Uphungu wonena za kulinganiza bwino mathayo a banja ndi a mpingo suli watsopano. Kwa zaka zambiri “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakhala akupereka uphungu kwa akulu pankhani imeneyi. (Mateyu 24:45) Zaka zoposa 37 zapitazo, Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 15, 1959, masamba 553 ndi 554, inalangiza kuti: “Ndithudi, kodi sitingofunikira kulinganiza bwino zinthu zolira nthaŵi yathu? M’kulinganiza kumeneku, lolani kuti chisamaliro chachikulu chikhale pa zinthu za banja lanu. Kunena zoona, Yehova Mulungu sangafune mwamuna kugwiritsira ntchito nthaŵi yake yonse pantchito za mpingo, pa kuthandiza abale ndi anansi ake kuti apeze chipulumutso, komabe osasamala za chipulumutso cha banja lake. Mkazi ndi ana ali thayo loyambirira la mwamuna.”
14 Nsanja ya Olonda ya November 1, 1986, tsamba 21, inapereka uphungu wakuti: “Kutengamo mbali muuminisitala wakumunda monga banja kudzakuyandikizitsani pamodzi kwambiri, komabe zofunika zapadera za ana zimafunikiritsa kugwiritsiridwa ntchito kwa nthaŵi yanu ya inu mwini ndi nyonga ya maganizo. Chifukwa chake, kukhazikika kuli kofunika kuti mudziŵe kuchuluka kwa nthaŵi imene mungagwiritsire ntchito m’ntchito . . . zampingo, ndipo musamaliranso mwauzimu, mwamaganizo, ndi m’zinthu zakuthupi za ‘a m’banja lanu.’ [Mkristu] ayenera ‘kuyamba kuphunzira kuchitira ulemu choyamba a m’banja la [iye yekha].’ (1 Timoteo 5:4, 8)”
15. Kodi nchifukwa ninji mkulu amene ali ndi mkazi ndi ana afunikira nzeru ndi luntha?
15 Mwambi wa m’Malemba umati: “Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.” (Miyambo 24:3) Inde, kuti woyang’anira akwaniritse mathayo ake ateokrase ndipo panthaŵi imodzimodziyo kumangirira banja lake, afunikiradi nzeru ndi luntha. Mwa Malemba, iye ali ndi mbali zoposa imodzi za uyang’aniro. Banja lake ndi mathayo ake mumpingo zimaloŵetsedwamo. Amafunikira luntha kuti azilinganize bwino zimenezi. (Afilipi 1:9, 10) Iye afunikira nzeru kuti aike zinthu zofunika pamalo oyamba. (Miyambo 2:10, 11) Ngakhale ngati iye akukhumba kwambiri kusamalira mathayo a mpingo, ayenera kuzindikira kuti pokhala mwamuna ndi tate, thayo lake loyambirira lopatsidwa ndi Mulungu ndilo chisamaliro ndi chipulumutso cha banja lake.
Atate Abwino Amakhalanso Akulu Abwino
16. Kodi ndi ubwino wotani umene mkulu amapeza ngati alinso tate?
16 Mkulu amene ali ndi ana odzisungira bwino angakhale thandizo lenileni. Athaphunzira kusamalira bwino banja lake, amakhala wokhoza kuthandiza mabanja ena mumpingo. Amamvetsetsa mavuto awo ndipo akhoza kupereka uphungu umene umasonyeza zokumana nazo zake. Chosangalatsa nchakuti, zikwi zambiri za akulu kuzungulira dziko lonse akuchita bwino kwambiri monga amuna, atate, ndi oyang’anira.
17. (a) Kodi mwamuna amene ali tate ndi mkulunso sayenera kuiŵalanji? (b) Kodi ziŵalo zina za mpingo zingasonyeze motani chifundo?
17 Kuti mwamuna wa banja akhale mkulu, ayenera kukhala Mkristu wokhwima, amene posamalira mkazi wake ndi ana, akhozanso kulinganiza zinthu zake kuti akhale wokhoza kupereka nthaŵi ndi maganizo kwa ena mumpingo. Sayenera kuiŵala kuti ntchito yake yaubusa imayambira panyumba. Podziŵa kuti akulu okhala ndi mkazi ndi ana ali ndi thayo m’banja lawo ndi mumpingo momwe, ziŵalo za mpingo zidzayesa kupeŵa kuwatayitsa nthaŵi yawo yochuluka mosayenera pa izo. Mwachitsanzo, mkulu amene ali ndi ana omwe ayenera kupita kusukulu mmaŵa mwake sangakhoze nthaŵi zonse kumatsalira pambuyo pa misonkhano yamadzulo. Ziŵalo zina za mpingo ziyenera kuzindikira zimenezi ndi kusonyeza chifundo.—Afilipi 4:5.
Tiwachitire Ulemu Akulu Athu
18, 19. (a) Kodi kupenda kwathu 1 Akorinto chaputala 7 kwatikhozetsa kuzindikiranji? (b) Kodi amuna achikristu oterowo tiyenera kuwaona motani?
18 Kupenda kwathu chaputala 7 cha kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto kwatikhozetsa kuona kuti pali amuna osakwatira ambiri omwe mwakutsatira uphungu wa Paulo, akugwiritsira ntchito ufulu wawo kutumikira zinthu za Ufumu. Palinso zikwi zambiri za abale okwatira koma opanda ana, omwe popereka chisamaliro choyenera kwa akazi awo, akutumikiranso monga oyang’anira abwino m’zigawo, m’madera, m’mipingo, ndi m’nthambi za Watch Tower, ndi chichirikizo cha akazi awo choyamikirika kwambiri. Chomaliza, m’mipingo pafupifupi 80,000 ya anthu a Yehova, muli atate ambiri amene samangosamalira mwachikondi akazi awo ndi ana komanso amapeza nthaŵi ya kutumikira abale awo monga abusa osamalira.—Machitidwe 20:28.
19 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu woŵirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” (1 Timoteo 5:17) Inde, akulu amene aweruza m’njira yabwino m’nyumba zawo ndi mumpingo amafunikira chikondi chathu ndi ulemu. Tifunikiradi ‘kuchitira ulemu otereŵa.’—Afilipi 2:29.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya February 1, 1978, masamba 31-2.
b Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 1, 1960, masamba 735-6.
Kubwereramo
◻ Kodi timadziŵa motani kuti akulu ambiri a m’zaka za zana loyamba C.E. anali amuna a mabanja?
◻ Kodi chofunika nchiyani kwa akulu okwatira amene ali ndi ana, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi ‘kukhala ndi ana okhulupirira’ kumatanthauzanji, koma bwanji ngati mwana wa mkulu sasankha kutumikira Yehova?
◻ Kodi ndi m’mbali ziti zimene mkulu ayenera ‘kusamalira banja lake la iye yekha’?
[Chithunzi patsamba 23]
Mabanja olimba amapanga mipingo yolimba