Penyererani Chiphunzitso Chanu Nthaŵi Zonse
“Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”—1 TIMOTEO 4:16.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani aphunzitsi achangu akufunika mwamsanga lerolino?
“MUKANI, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Chifukwa cha lamulo limeneli la Yesu Kristu, Akristu onse ayenera kuyesetsa kukhala aphunzitsi. Aphunzitsi achangu akufunika kuti athandize anthu oona mtima kukhala ndi chidziŵitso chonena za Mulungu nthaŵi isanathe. (Aroma 13:11) Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Lalikira mawu; chita nawo panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Zimenezi zimafuna kuphunzitsa ponse paŵiri mumpingo ndi kunja kwa mpingo. Ndithudi, ntchito yolalikira yeniyeniyo ikuphatikizapo zambiri zoposa kungolengeza uthenga wa Mulungu. Kuphunzitsa kogwira mtima n’kofunika kuti anthu achidwi akhale ophunzira.
2 Tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Maganizo a anthu asintha chifukwa cha mafilosofi adziko ndi ziphunzitso zonyenga. Ambiri “maganizo awo ali mumdima” ndipo “sazindikiranso makhalidwe.” (Aefeso 4:18, 19, NW) Ena ali ndi chisoni chachikulu m’mitima mwawo. Inde, anthu alidi “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Ngakhale zili choncho, mwa kugwiritsa ntchito luso la kuphunzitsa, tingathandize anthu oona mtima kusintha moyenera.
Aphunzitsi Mumpingo
3. (a) Kodi ntchito yophunzitsa imene Yesu anatipatsa ikuphatikizapo chiyani? (b) Kodi ndani amene ali ndi udindo waukulu wophunzitsa mumpingo?
3 Mwa makonzedwe a phunziro la Baibulo lapanyumba, anthu miyandamiyanda akulandira malangizo mwachindunji. Komano, atabatizidwa, achatsopanowo ayenera kuthandizidwabe kuti akhale “ozika mizu ndi otsendereka.” (Aefeso 3:17) Pamene tichita ntchito imene Yesu anatipatsa yolembedwa pa Mateyu 28:19, 20 ndi kutsogolera atsopano ku gulu la Yehova, iwo amapindula mwa kuphunzitsidwa mumpingo mwenimwenimo. Malinga n’kunena kwa Aefeso 4:11-13, amuna aikidwa kuti atumikire monga “abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu.” Nthaŵi zina, luso lawo la kuphunzitsa limaloŵetsapo kufunika kwa ‘kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza ndi kuleza mtima konse.’ (2 Timoteo 4:2) Ntchito ya aphunzitsi inali yofunika kwambiri moti, polembera Akorinto, Paulo anaika aphunzitsi pambuyo pa atumwi ndi aneneri.—1 Akorinto 12:28.
4. Kodi kukhoza kwathu kuphunzitsa kumatithandiza motani kumvera uphungu wa Paulo wolembedwa pa Ahebri 10:24, 25?
4 Zoonadi, si Akristu onse amene akutumikira monga akulu, kapena oyang’anira. Komabe, onse akulimbikitsidwa kufulumizana “ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25) Kuchita zimenezo pamisonkhano kumafuna ndemanga zokonzedwa bwino, zochokera pansi pa mtima zimene zingamangirire ndi kulimbikitsa ena. Ofalitsa Ufumu achidziŵitso ‘angafulumize ena ku ntchito zabwino’ mwa kugaŵana chidziŵitso chawo ndi luso lawo ndi achatsopano pogwira nawo ntchito mu utumiki wakumunda. Malangizo othandiza kwambiri angaperekedwe pazochitika zimenezi ndi pazochitika wamba. Mwachitsanzo, akazi achikulire akulimbikitsidwa kukhala “akuphunzitsa zokoma.”—Tito 2:3.
Osonkhezeredwa Kukhulupirira
5, 6. (a) Kodi Chikristu choona chimasiyana motani ndi kulambira konyenga? (b) Kodi akulu amawathandiza motani achatsopano popanga zosankha zabwino?
5 Choncho Chikristu choona n’chosiyana kwambiri ndi zipembedzo zonyenga, zambiri zimene zimafuna kulamulira maganizo a anthu awo. Pamene Yesu anali padziko lapansi, atsogoleri achipembedzo ankafuna kulamulira mbali iliyonse ya moyo wa anthu mwa miyambo yopondereza yopangidwa ndi anthu. (Luka 11:46) Nthaŵi zambiri atsogoleri achipembedzo a m’Dziko Lachikristu achitanso chimodzimodzi.
6 Koma kulambira koona ndiko “utumiki wopatulika” umene timauchita ndi “mphamvu [yathu] ya kulingalira.” (Aroma 12:1, NW) Atumiki a Yehova ‘n’ngosonkhezedwa mtima.’ (2 Timoteo 3:14) Nthaŵi zina, otsogolera angafunikire kuika zitsogozo ndi njira zina zoyendetsera bwino mpingo. Komabe, m’malo mofuna kupangira zosankha Akristu anzawo, akulu amawaphunzitsa “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Kwenikweni, akulu amachita zimenezi mwa kupatsa mpingo “mawuwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino.”—1 Timoteo 4:6.
Kupenyerera Chiphunzitso Chanu
7, 8. (a) Kodi anthu osakhala ndi maluso apadera amatha bwanji kutumikira monga aphunzitsi? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti kuyesayesa kwa munthu aliyense payekha n’kofunika kuti akhale mphunzitsi wabwino?
7 Koma tsono tiyeni tipitirize kukambirana za ntchito yathu yophunzitsa. Kodi umafunika kukhala ndi maluso apadera, maphunziro apadera, kapena nzeru zina zake kuti uchite nawo ntchitoyi? Iyayi. Ambiri amene akuchita ntchito imeneyi yophunzitsa padziko lonse lapansi ndi anthu wamba osakhala ndi maluso apadera. (1 Akorinto 1:26-29) Paulo anafotokoza kuti: “Tili nacho chuma ichi [utumiki] m’zotengera zadothi [matupi opanda ungwiro], kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7) Chipambano chachikulu cha ntchito yolalikira Ufumu padziko lonse lapansi ndiwo umboni wa mphamvu ya mzimu wa Yehova!
8 Ngakhale zili motero, munthu aliyense payekha amayenera kuyesetsa kuti akhale “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Kodi munthu amapenyerera motani chiphunzitso chake, kaya mumpingo kapena kunja kwa mpingo? Kodi kuchita zimenezo kumafuna kuphunzira maluso ena ake kapena njira zina zophunzitsira?
9. Kodi chofunika kwambiri kuposa maluso achibadwa n’chiyani?
9 Mosakayikira Yesu anasonyeza luso lodabwitsa la kuphunzitsa mu Ulaliki wake wa pa Phiri wotchukawo. Atamaliza kuyankhula, “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Inde, palibe aliyense wa ife amene angaphunzitse monga momwe Yesu anaphunzitsira. Komabe, sitifunikira kuchita kukhala okamba mwaluso kuti tikhale aphunzitsi abwino. Inde, malinga n’kunena kwa Yobu 12:7, ngakhale “nyamazo” ndi “mbalame” zimaphunzitsa mosayankhula kalikonse! Pamodzi ndi maluso achibadwa amene tingakhale nawo, chofunika kwambiri n’chakuti ndife “anthu otani”—mikhalidwe imene tili nayo ndiponso zizoloŵezi zimene takulitsa zimene ophunzira angatsanzire.—2 Petro 3:11; Luka 6:40.
Ophunzira a Mawu a Mulungu
10. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani monga wophunzira wa Mawu a Mulungu?
10 Mphunzitsi wabwino wa choonadi cha m’Malemba ayenera kukhala wophunzira wa Mawu a Mulungu. (Aroma 2:21) Yesu Kristu anapereka chitsanzo chabwino koposa pambaliyi. Mu utumiki wake, Yesu anatchula kapena kufotokoza malingaliro ofanana ndi opezeka m’theka la mabuku a m’Malemba Achihebri.a Kudziŵa kwake bwino Mawu a Mulungu kunaonekera pamene anali wazaka 12, pamene anamupeza “[atakhala] pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.” (Luka 2:46) Atakula, Yesu anali ndi chizoloŵezi chopita ku sunagoge, kumene Mawu a Mulungu anali kuŵerengedwa.—Luka 4:16.
11. Kodi mphunzitsi ayenera kukulitsa zizoloŵezi zabwino zotani za kuphunzira?
11 Kodi mumaŵerenga Mawu a Mulungu mwakhama? Mwa kukumba m’Mawuwo mpamene “[m]udzazindikira kuopa Yehova ndi kumudziŵadi Mulungu.” (Miyambo 2:4, 5) Chotero kulitsani zizoloŵezi zabwino pophunzira. Yesani kuŵerenga chigawo cha Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Salmo 1:2) Khalani ndi chizoloŵezi choŵerenga kope lililonse la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mukangoilandira. Mvetserani kwambiri pamisonkhano ya mpingo. Phunzirani kufufuza mosamala. Mwa kuphunzira ‘kulondola mosamalitsa zinthu zonse,’ mungapeŵe kukokomeza ndi kuphophonya pophunzitsa.—Luka 1:3.
Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu kwa Amene Akuphunzitsidwa
12. Kodi Yesu anali kuwaona motani ophunzira ake?
12 Mkhalidwe winanso wofunika kwambiri ndiwo kaonedwe kabwino ka awo amene mukuphunzitsa. Afarisi ankanyansidwa ndi anthu amene anali kumvetsera Yesu. “Khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa,” iwo anatero. (Yohane 7:49) Koma Yesu anali kuwakonda ndi kuwalemekeza kwambiri ophunzira ake. Iye anati: “Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) Zimenezi zinasonyeza mmene ophunzira a Yesu ayenera kuchitira ntchito yawo yophunzitsa.
13. Kodi Paulo anali kumva bwanji ponena za anthu amene anali kuphunzitsa?
13 Mwachitsanzo, Paulo sanaone ophunzira ake monga ophunzira basi. Anauza Akorinto kuti: “Mungakhale muli nawo aphunzitsi zikwi khumi mwa Kristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Kristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.” (1 Akorinto 4:15) Nthaŵi zina pochenjeza awo amene ankaphunzitsa, Paulo anafika pogwetsa misozi! (Machitidwe 20:31) Anasonyezanso kuleza mtima ndi kukoma mtima kwakukulu. Choncho anauza Atesalonika kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha.”—1 Atesalonika 2:7.
14. Kodi n’chifukwa chiyani kuwaderadi nkhaŵa ophunzira athu a Baibulo kuli kofunika kwambiri? Perekani chitsanzo.
14 Kodi mukutsanzira Yesu ndi Paulo? Chikondi chenicheni pa ophunzira athu chingathandize kwambiri ngati tili opereŵera pa maluso ena achibadwa. Kodi ophunzira athu a Baibulo amaona kuti timaderadi nkhaŵa? Kodi timathera nthaŵi pofuna kuwadziŵa bwino? Pamene mkazi wina wachikristu anavutika kuthandiza wophunzira wake kuti apite patsogolo mwauzimu, anafunsa mokoma mtima kuti: “Kodi pali zimene zikukudetsani nkhaŵa?” Mkaziyo anayamba kunena zakukhosi, kufotokoza nkhaŵa zake zambiri. Atakambirana mwachikondi moteromo mpamene mkazi wophunzirayo anasintha. Zikatere, malingaliro a m’Malemba ndi mawu otonthoza ndi olimbikitsa n’ngofunika. (Aroma 15:4) Koma nali chenjezo: Wophunzira Baibulo angamapite patsogolo mwamsanga koma angakhalebe ndi makhalidwe osakhala achikristu omwe afunikira kuleka. Choncho sikungakhale kwanzeru kukhala ndi munthu wotero paubwenzi wathithithi. Payenera kukhala malire oyenera achikristu.—1 Akorinto 15:33.
15. Kodi ndi motani mmene tingasonyezere ulemu kwa ophunzira athu a Baibulo?
15 Kulemekeza ophunzira athu kumaphatikizapo kusayesa kulamulira moyo wawo. (1 Atesalonika 4:11) Mwachitsanzo, tikhoza kumaphunzitsa mkazi amene akukhala ndi mwamuna amene sanakwatirane naye mwalamulo. Mwina wabala naye ana. Atakhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu, mkaziyo angafune kuwongolera kaimidwe kake pamaso pa Yehova. (Ahebri 13:4) Kodi akwatirane naye mwamunayo mwalamulo kapena amusiye? Mwina ifeyo tili ndi nkhaŵa yaikulu yakuti kukwatiwa ndi mwamuna wopanda chidwi ndi zinthu zauzimu kungasokoneze kupita patsogolo kwa mkaziyo m’tsogolo. Komanso, mwina tingamvere chisoni anawo ndipo tingaganize kuti zingakhale bwino kuti akwatirane naye. Mulimonse mmene zingakhalire, n’kupanda ulemu ndi kusoŵa chikondi kuloŵerera m’moyo wa wophunzirayo ndi kuyesa kumukakamiza kutsatira malingaliro athu pankhani ngati zimenezo. Ndipotu ndi wophunzirayo amene adzayang’anizana ndi zotsatirapo za chosankhacho. Chotero, kodi sikungakhale bwino kuphunzitsa wophunzira wotere kugwiritsa ntchito ‘mphamvu zake za kuzindikira’ ndi kudzisankhira chimene ayenera kuchita?—Ahebri 5:14, NW.
16. Kodi akulu angasonyeze motani chikondi ndi ulemu ku gulu la Mulungu?
16 N’kofunika kwambiri kuti akulu makamaka azisonyeza chikondi ndi ulemu ku gulu la nkhosa. Polembera Filemoni, Paulo anati: “Ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu m’Kristu kukulamulira chimene chiyenera, koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi.” (Filemoni 8, 9) Nthaŵi zina, mumpingo mungakhale zochitika zokhumudwitsa. Mwina pangafunikirenso kukhwimitsa zinthu. Paulo analimbikitsa Tito kuti ‘awadzudzule mokalipa [olakwa], kuti akakhale olama m’chikhulupiriro.’ (Tito 1:13) Ngakhale zitatero, oyang’anira ayenera kusamala kuti sakulankhula mosakoma mtima ku mpingo. “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu,” analemba motero Paulo, “komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza.”—2 Timoteo 2:24; Salmo 141:3.
17. Kodi Mose analakwa chiyani, ndipo n’chiyani chimene akulu angaphunzirepo?
17 Nthaŵi zonse oyang’anira ayenera kumadzikumbutsa kuti akuchita ndi “gulu la Mulungu.” (1 Petro 5:2) Ngakhale kuti Mose anali wofatsa, iye anaiŵala mfundo imeneyi nthaŵi ina yake. Aisrayeli “anaŵaŵitsa mzimu wake, ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yake.” (Salmo 106:33) Mulungu anakwiya kwambiri ndi kuvutitsa gulu Lake kumeneku, ngakhale kuti gululo linalidi lolakwa. (Numeri 20:2-12) Akakumana ndi zovuta zofananazo lerolino, akulu ayenera kuyesetsa kuphunzitsa ndi kulangiza mwanzeru ndi mokoma mtima. Abale athu amalabadira bwino kwambiri pamene atengedwa monga anthu ofuna chithandizo, osati monga anthu amene sangawongolere. Akulu afunikira kukhala ndi chiyembekezo chabwino chimene Paulo anali nacho pamene anati: “Tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.”—2 Atesalonika 3:4.
Kuwathandiza pa Zosoŵa Zawo
18, 19. (a) Kodi tiyenera kuwathandiza motani ophunzira Baibulo okhala ndi mavuto ena pophunzira? (b) Kodi tingathandize motani ophunzira ovutika kumvetsa nkhani zina?
18 Mphunzitsi wabwino amakhala wofunitsitsa kusintha malinga ndi luso la wophunzirayo ndi zimene amatha kuchita. (Yerekezani ndi Yohane 16:12.) M’fanizo la Yesu la matalente, mbuye wawo anapereka udindo “kwa iwo onse monga [mwa] nzeru zawo.” (Mateyu 25:15) Tingatsatire njira imeneyo pamene tikuchititsa maphunziro a Baibulo. N’zoona kuti timafuna kumaliza chofalitsa chofotokoza Baibulo m’nthaŵi yaifupi. Komanso ndi zoona kuti si onse amene amatha kuŵerenga bwino kapena kumvetsa malingaliro atsopano mwamsanga. Choncho, tiyenera kuzindikira bwino pamene tingasunthire pamfundo ina pophunzira ngati ofuna kuphunzirawo akuvutika kuphunzira mofulumira. Chofunika kwambiri kuposa kumaliza phunziro mwamsanga ndicho kuthandiza wophunzirayo kumvetsa lingaliro la zimene akuphunzira.—Mateyu 13:51.
19 Zingakhalenso chimodzimodzi ndi ophunzira Baibulo amene akuvutika kumvetsa nkhani zina, monga Utatu kapena maholide achipembedzo. Pamene kuli kwakuti nthaŵi zambiri kuphatikizapo mfundo zina zofufuzidwa m’Baibulo pa maphunziro athu n’kosafunikira, nthaŵi zina tingaziphatikizepo ngati zimenezi zingakhale zopindulitsa kwambiri. Kusamala n’kofunika kuti tisachedwetse mosayenera kupita patsogolo kwa wophunzira.
Khalani Wokhudzidwa Mtima!
20. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani posonyeza kukhudzika mtima ndi chikhulupiriro pamene anali kuphunzitsa?
20 “Khalani achangu mumzimu,” anatero Paulo. (Aroma 12:11) Inde, kaya tikuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba kapena tili ndi mbali pamsonkhano wa mpingo, tiyenera kuchita zimenezo ndi changu ndiponso mokhudzika mtima. Paulo anauza Atesalonika kuti: “Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu [“chikhulupiriro chachikulu,” NW].” (1 Atesalonika 1:5) Chotero, Paulo ndi anzake anapereka “[osati] Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo [wawo].”—1 Atesalonika 2:8.
21. Kodi tingakhalebe okhudzika mtima motani pantchito yathu yophunzitsa?
21 Timakhudzikadi mtima titakhulupirira zedi kuti ophunzira athu a Baibulo afunikira kumva zimene tikufuna kunena. Tisamaone ntchito iliyonse yophunzitsa monga ntchito wamba. Ndithudi mlembi Ezara anasamala kuphunzitsa kwake. “Adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli.” (Ezara 7:10) Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi mwa kukonzekera bwino ndi kusinkhasinkha za kufunika kwa zinthu zophunziridwazo. Tiyeni tipemphere kwa Yehova kuti atidzaze ndi chikhulupiriro. (Luka 17:5) Kukhudzika mtima kwathu kungathandize ophunzira Baibulo kukulitsa chikondi chenicheni cha choonadi. Komanso, kupenyerera chiphunzitso chathu kungaphatikizepo kugwiritsa ntchito maluso ena a kuphunzitsa. Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza ena mwa malusowa.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 1071, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani lerolino pakufunika aphunzitsi aluso achikristu?
◻ Kodi tingakulitse zizoloŵezi zabwino zotani pophunzira?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani chikondi ndi ulemu kwa amene tikuwaphunzitsa zili zofunika kwambiri?
◻ Kodi tingawathandize motani ophunzira athu a Baibulo pa zosoŵa zawo?
◻ Kodi n’chifukwa chiyani kukhudzika mtima ndi chikhulupiriro zili zofunika kwambiri pophunzitsa ena?
[Chithunzi patsamba 10]
Aphunzitsi abwino ali ophunzira abwino a Mawu a Mulungu
[Chithunzi patsamba 13]
Khalani ndi chidwi chenicheni mwa ophunzira Baibulo