Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nkulakwa Kupeza Ndalama?
“NDITHUDI ndalama ndi chinthu chofunikadi koposa m’dziko.” Ananena motero wolemba maseŵero wachibritishi George Bernard Shaw. Kodi mukuvomerezana naye? Mwina mukulingalira mofanana ndi Tanya wazaka 17, yemwe akuti: “Sindifuna kudzakhala wolemera, kungokhala nazo zokwanira basi.” Avian wachinyamata nayenso amaona ndalama, osati monga chinthu chofunika koposa m’dziko, koma monga chinthu chothandiza kupeza kenakake. Iye akuti: “Ndalama nzofunika kupezera zosoŵa zanga, monga zovala ndiponso zoyendera.”
Kodi mumadziŵa kuti Baibulo nalonso limanena zofananazo? Pa Mlaliki 7:12, limati “ndalama zichinjiriza.” Umphaŵi wanenedwa kukhala “mdani wamkulu wa chimwemwe cha munthu.” Ndipo kukhala ndi ndalama zokwanira kungakuchinjirizeni—pamlingo wina wake—pamavuto amene umphaŵi umabweretsa nthaŵi zambiri. Ndalama zikhozanso kukuthandizani pamavuto a mwadzidzidzi. “Baibulo limati ‘nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimatigwera ife tonse,’” akutero Phyllis wachinyamata. “Sitidziŵa pamene mavuto angatigwere, motero tifunikira kumasunga ndalama.” (Mlaliki 9:11, NW) Ndipo ngakhale kuti ndalama zingaoneke zofunika kwa inu tsopano, zingakhale zofunikanso kwambiri mtsogolo mwanu.
“Kukula kwa Khalidwe la Kukonda Chuma”
Koma ngakhale kuti malingaliro okhala ndi ndalama zokwanira ndi oyenera ndiponso abwino, kwa achinyamata ena ndalama zafika polamulira maganizo awo onse. Pamene achinyamata 160,000 anafunsidwa kuti, “Nchiyani chimene umafuna kwambiri m’moyo?,” 22 peresenti anati, “Kulemera.”
Mosakayika kukonda ndalama kumeneku kwakula chifukwa cha chimene magazini ya Newsweek amachitcha “kukula kwa khalidwe la kukonda chuma” limene lafala padziko lonse. “Ndine munthu wokonda chuma kwambiri ndiponso ndimakonda katundu wopangidwa ndi makampani otchuka,” akutero Martin wazaka 18. “Ndimakhulupirira kwambiri kuti katundu amene wagula amadalira pa kuchuluka kwa ndalama wagulira. Motero, ndimawononga ndalama zambiri pa zomwe ndikufuna.” Martin si wachinyamata yekhayo amene ‘amawononga ndalama zambiri.’ U.S.News & World Report inachita lipoti kuti: “[Mu United States] chaka chatha, achinyamata a zaka zapakati pa 12 ndi 19 anawononga ndalama zambiri zokwanira $109,000,000,000, pogula katundu kuposa kale lonse, chiwonjezeko cha 38 peresenti kuposa mu 1990.”
Koma nanga nkuti kumene achinyamata amapeza ndalama zogulira zovala zonsezo zatsopano, mawailesi apamwamba, ndi makompyuta? Malinga ndi U.S.News & World Report: “Pafupifupi theka la achinyamata a zaka 16 kufika 19 amagwira ntchito zamaola ochepa.” Atazilinganiza bwino, ntchito yogwira pambuyo poŵeruka kusukulu ikhoza kukhala ndi mapindu ake, monga kuphunzitsa wachinyamata kusenza udindo. Komabe, achinyamata ena mwachionekere amanyanyira pankhaniyi. Magazini ya Newsweek inati: “Akatswiri a zamaganizo ndiponso aziphunzitsi amaona mmene ophunzira [ogwira ntchito] amavutikira. Sakhala ndi nthaŵi yokwana ya homuweki, ndipo aphunzitsi amene nthaŵi zonse amaona ophunzira akulimbana nkuti asagone m’kalasi, ndipotu masiku onse, sawayembekezera kuchita zochuluka.”
Ngakhale ndi choncho, ndi achinyamata ogwira ntchito ochepa okha amene amafuna kuleka njira yawo yopezera ndalama. “Sukulu ndi yofunika,” akutero Vanessa wachinyamata, “koma ndalama nzofunikanso. Homuweki singakupatse ndalama.” Kupeza ndalama nkofunika motani kwa inu? Kodi kukhala ndi ndalama zambiri ndicho cholinga chanu chachikulu m’moyo?
‘Kufuna Kukhala Wachuma’
Baibulo limafotokoza mafunso ameneŵa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:9, 10.
Mwachionekere Paulo ankadziŵa zimene ankanena. Asanakhale Mkristu, anali mmodzi wa atsogoleri achipembedzo otchedwa “Afarisi,” amene Baibulo limawatcha “okonda ndalama.” (Luka 16:14) Ngakhale ndi tero, mtumwiyo sananene kuti kupeza ndalama mwa iko kokha nkoipa. M’malo mwake anachenjeza “akufuna kukhala achuma” kapena, monga mmene matembenuzidwe ena amanenera, kwa anthu amene “amalakalaka kukhala olemera.” (Phillips) Koma choipa nchiyani ndi kuchita zimenezo?
Mmene Paulo akunenera, oterowo “amagwa m’chiyesero ndi m’msampha.” Miyambo 28:20 imanena zofananazo pamene imati: “Koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.” Polingalira kuti alibe zokwanira, achinyamata ena amayamba kuba.
Kunena zoona, achinyamata ambiri sangalingalire za kuba. Koma ena amayamba makhalidwe opatsa ngozi. Christianity Today inati: “Akatswiri ena amakhulupirira kuti kutchova juga konkitsa kwakhala chizoloŵezi chomka nchikwera mofulumira kwa achinyamata.” Malo ena ku United States, “pafupifupi 90 peresenti ya achinyamata osakwanitsa zaka 20 anagulapo tikiti ya lotale mosaloledwa ndi lamulo podzafika chaka chawo chomalizira kusekondale.” Achinyamata ena amatembenukira ku njira zosadalirika. “Ntchito zabwino nzovuta kupeza,” akutero Matthew wazaka 16. “Motero ndalama zanga zambiri ndimazipeza mwa kugula ndi kugulitsa zinthu. . . . Nthaŵi zina [ndinali] kugulitsa [mankhwala osokoneza bongo].”
‘Kumira m’Chiwonongeko ndi Chitayiko’
Nzoona kuti, kukhala ndi ndalama kukhoza kupangitsa munthu kudzimva kuti ali pamtendere. Koma momwe Paulo akulongosolera, mkupita kwa nthaŵi, kufunafuna ndalama kukhoza kupangitsa munthu kukhala kapolo wa ‘zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka zomwe zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.’ Inde, ngati chikondi cha pa ndalama chikulamulira maganizo anu, chisiriro, nsanje yambanda, ndiponso zilakolako zina zoipa zikhoza kuzika mizu. (Yerekezerani ndi Akolose 3:5.) Nkhani ya m’magazini ya Teen inanena kuti achinyamata ena akhoza kuyamba kusirira kwambiri magalimoto ndi zovala zomwe achinyamata ena ali nazo “mpaka amatengeka maganizo.” Chisiriro chotero nthaŵi zina “chimakula kufikira poyamba kudzida,” ikupitiriza motero nkhaniyo, “ndipo wachinyamata sathanso kulingalira zina kupatulapo zomwe iye alibe.”
Onani tsopano kuti kukonda chuma ‘sikugwetsera m’chiyesero’ chabe komanso kukhoza ‘kumiza munthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.’ Wothirira ndemanga Baibulo Albert Barnes akuti: “Lingaliro lake lili ngati kumira kwa sitima, pamene zonse zomwe zilimo zamirira limodzi. Kuwonongeka kwake nkotheratu. Pamakhala kutheratu chimwemwe, khalidwe labwino, ndiponso moyo wonse.”—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 1:19.
Choncho, moyenerera Paulo ananena kuti “muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.” Chifukwa cha chimenechi, ambiri “anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” Mwachitsanzo, lingalirani za wachinyamata yemwe timutche Rory. Pausinkhu wa zaka 12 anayamba kutchova juga. “Inali njira yopezera ndalama popanda kuchita chilichonse,” iye akukumbukira motero. Posapita nthaŵi anali ndi ngongole yokwana madola mazanamazana komanso anasiya kusamala mabwenzi, banja, ndi sukulu. “Ndinayesa kuleka,” anavomera motero, koma nthaŵi zonse analephera. Anapitiriza ‘kudzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri’ kufikira pamene anapempha chithandizo pausinkhu wa zaka 19. Motero wolemba nkhani Douglas Kennedy sakukokomeza pamene m’buku lake lotchedwa Chasing Mammon, akutcha kufunafuna ndalama kuti ndi “chokumana nacho chovulaza.”
Kupeza Polekezera
Motero malangizo a Solomo ndi othandiza lerolino monga mmene analili zaka mazana ambiri zapitazo: “Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.” (Miyambo 23:4, 5) Chuma chakuthupi nchosakhalitsa, motero ndikupusa kupanga kufunafuna chuma kukhala chinthu chofunika koposa m’moyo. “Sindifuna kukodwa mumsampha wa kufunafuna chuma,” akutero Mkristu wachitsikana wotchedwa Maureen. “Ndimadziŵa bwino,” iye akutero, “kuti mtengo umene ndingalipire nditakodwa ndi kupeza ndalama ndiwo kusiya zauzimu.”
Ndithudi, ndalama nzofunika. Ndipo kumapeza zokwana kudzakuthandizani kupeza zosoŵa zanu—mwinanso ngakhale kuthandiza ena ndi chuma chakuthupi nthaŵi ndi nthaŵi. (Aefeso 4:28) Phunzirani kugwira ntchito mwamphamvu kuti muzipeza ndalama mwachilungamo. Komanso, phunzirani kusunga, kupanga bajeti, ndi kugwiritsira ntchito ndalama mwanzeru. Koma musapange ndalama kukhala chinthu chofunika kwambiri m’moyo. Yeserani kukhala ndi lingaliro labwino lonenedwa ndi mlembi wa Miyambo 30:8, yemwe anapemphera kuti: “Musandipatse umphaŵi, ngakhale chuma.” Mwakuika zinthu zauzimu poyamba, mudzatha kupeza mtundu wabwino kwambiri wa chuma. Monga momwe Miyambo 10:22 imanenera, “madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”
[Chithunzi patsamba 29]
Achinyamata ambiri amafuna ndalama kuti azilingana ndi mabwenzi awo