Miyambo
3 Usalakelake chakudya chake chokoma,
Chifukwa ndi chakudya chachinyengo.
4 Usadzitopetse pofuna kupeza chuma.+
Leka kuchita zimenezi, mʼmalomwake uzisonyeza kuti ndiwe womvetsa zinthu.*
5 Ukayangʼana pamene panali chumacho, umapeza kuti palibe,+
Chifukwa ndithu chimamera mapiko ngati chiwombankhanga nʼkuulukira mʼmwamba.+
6 Usadye chakudya cha munthu womana.*
Usalakelake chakudya chake chokoma,
7 Chifukwa iye ali ngati munthu amene amakuyangʼanitsitsa kuti adziwe kuchuluka kwa chakudya chimene wadya.
Iye amakuuza kuti: “Idya ndi kumwa,” koma salankhula zimenezo ndi mtima wonse.
8 Mbamu imene wadya udzaisanza
Ndipo mawu ako oyamikira adzangopita pachabe.
12 Yesetsa ndi mtima wonse kumvetsera malangizo ndi kuwagwiritsa ntchito,
Ndipo khutu lako limvetsere mawu anzeru.
13 Mwana usalephere kumupatsa chilango.*+
Ngakhale utamukwapula ndi chikwapu, sangafe.
17 Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+
Koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+
18 Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+
Ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.
19 Mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru,
Ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino.
20 Usakhale mʼgulu la anthu amene amamwa vinyo wambiri.+
Usakhale mʼgulu la anthu amene amadya nyama mosusuka,+
21 Chifukwa chidakwa komanso munthu wosusuka adzasauka,+
Ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.
24 Bambo a munthu wolungama ndithu adzasangalala.
Aliyense amene anabereka mwana wanzeru adzakondwera naye.
25 Bambo ako ndi mayi ako adzasangalala,
Ndipo mayi amene anakubereka adzakondwera.
27 Chifukwa hule lili ngati dzenje lakuya,
Ndipo mkazi wachiwerewere* ali ngati chitsime chachingʼono.+
28 Iye amabisalira anthu panjira ngati wachifwamba.+
Amachititsa kuti chiwerengero cha amuna osakhulupirika chiwonjezereke.
29 Ndi ndani amene akuvutika? Ndi ndani amene ali ndi nkhawa?
Ndi ndani amene ali pa mikangano? Ndi ndani amene ali ndi madandaulo?
Ndi ndani amene ali ndi mabala popanda chifukwa? Ndi ndani amene ali ndi maso ofiira?
31 Usakopeke ndi kufiira kwa vinyo,
Pamene akunyezimira mʼkapu nʼkumatsetserekera kukhosi mwamyaa!
32 Chifukwa pamapeto pake amaluma ngati njoka,
Ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri.
34 Udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja,
Komanso ngati munthu amene wagona pansonga ya mtengo* wa ngalawa.
35 Udzanena kuti: “Andimenya koma sindinamve kupweteka.
Andikuntha koma sindinadziwe chilichonse.
Kodi ndidzuka nthawi yanji?+
Ndikufuna ndikamwenso wina.”