Makolo ndi Ana: Ikani Mulungu Pamalo Oyamba!
“Opa[ni] Mulungu, musunge malamulo ake.”—MLALIKI 12:13.
1. Kodi ndi mantha otani amene makolo ndi ana afunika kukhala nawo, ndipo adzawadzetsera chiyani?
ULOSI wonena za Yesu Kristu unati “adzakondwera nako kumuwopa Yehova.” (Yesaya 11:3) Mantha ake makamaka anali ulemu waukulu ndi kuwopa Mulungu, mantha osafuna kukwiyitsa Mulungu popeza anamkonda. Makolo ndi ana afunika kukhala ndi mantha onga a Kristu kwa Mulungu, amene adzakondwera nawo monga zinalili ndi Yesu. Afunika kuika Mulungu pamalo oyamba m’moyo wawo mwa kumvera malamulo ake. Malinga ndi mlembi wina wa Baibulo, “choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.
2. Kodi lamulo lofunika koposa pa Chilamulo linali lotani, ndipo linaperekedwa makamaka kwa ndani?
2 Lamulo lofunika koposa pa Chilamulo chonse, lakuti, tiyenera ‘kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo, ndi mphamvu,’ linaperekedwa makamaka kwa makolo. Zimenezi zikusonyezedwa ndi mawu owonjezera a Chilamulo: “Muziwaphunzitsa mwachangu [mawuwa a kukonda Yehova] kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:4-7; Marko 12:28-30) Motero makolo analamulidwa kuika Mulungu pamalo oyamba mwa kumkonda iwo eni ndi mwa kuphunzitsa ana kuchita zimenezo.
Thayo Lachikristu
3. Kodi Yesu anasonyeza motani kufunika kwake kwa kusamalira ana?
3 Yesu anasonyeza kufunika kwake kwa kusamalira ngakhale ana. Nthaŵi ina chakumapeto kwa utumiki wa Yesu wa pa dziko lapansi, anthu anayamba kudza nawo ana kwa iye. Mwachionekere poganiza kuti Yesu anali wotanganidwa kwambiri wosafunika kumvuta, ophunzira ake anayesa kuwaletsa anthuwo. Koma Yesu anawadzudzula ophunzira ake kuti: “Lolani ana adze kwa ine, ndipo musawaletse.” Ndipo Yesu “anatiyangata,” motero akumasonyeza mwanjira yokhudza mtima kufunika kwake kwa kusamalira ana.—Luka 18:15-17; Marko 10:13-16.
4. Kodi ndayani anapatsidwa lamulo la ‘kuphunzitsa anthu amitundu yonse,’ ndipo zimenezi zinafuna chiyani kwa iwo?
4 Ndiponso Yesu anamveketsa bwino lomwe kuti kuwonjezera pa ana awo, otsatira ake analinso ndi thayo la kuphunzitsa ena. Atamwalira ndi kuukitsidwa, Yesu “anaoneka panthaŵi imodzi kwa abale oposa mazana asanu”—kuphatikizapo makolo ena. (1 Akorinto 15:6) Mwachionekere zimenezi zinachitikira paphiri la ku Galileya kumenenso atumwi 11 anasonkhana. Kumeneko Yesu anawalimbikitsa onse: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:16-20) Palibe Mkristu amene angakhale ndi chifukwa chomveka chonyalanyazira lamulolo! Kuti atate ndi amayi alitsatire afunika kusamalira ana awo kudzanso kuchita ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa poyera.
5. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti atumwi ochuluka, ngati si onse, anali okwatira ndi kutinso mwina anali ndi ana? (b) Kodi mitu ya mabanja inafunika kusamala uphungu wotani?
5 M’mawu ena, ngakhale atumwi anafunika kulinganiza bwino mathayo a banja ndi a kulalikira kudzanso kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu. (Yohane 21:1-3, 15-17; Machitidwe 1:8) Chifukwa chake nchakuti ochuluka a iwo, ngati si onse, anali okwatira. Nchifukwa chake mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye [mlongo monga, NW] mkazi, . . . monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?” (1 Akorinto 9:5; Mateyu 8:14) Atumwi ena angakhalenso anali ndi ana. Olemba mbiri oyambirira, monga Eusebius, amati Petro anali nawo. Makolo onse Achikristu oyambirira anafunika kulabadira uphungu wa Malemba wakuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”—1 Timoteo 5:8.
Thayo Loyamba
6. (a) Kodi akulu Achikristu okhala ndi mabanja ali ndi ntchito yovuta yotani? (b) Kodi thayo loyamba la mkulu nlotani?
6 Akulu Achikristu amene ali ndi mabanja lerolino mkhalidwe wawo uli wonga uja wa atumwi. Ayenera kulinganiza thayo lawo la kusamalira zofunika za banja zauzimu ndi zakuthupi ndi thayo lawo la kulalikira poyera ndi kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu. Kodi ndi ntchito iti imene iyenera kukhala yoyamba? The Watchtower ya March 15, 1964, inati: “Thayo loyamba [la atate] ndilo banja lawo, ndipotu iwo sangatumikire bwino [monga mkulu] ngati sasamalira thayo limeneli.”
7. Kodi atate Achikristu amamuika motani Mulungu pamalo oyamba?
7 Chotero atate ayenera kuika Mulungu pamalo oyamba mwa kutsatira lamulo la ‘kuwalera ana m’maleredwe ndi chilangizo cha Yehova.’ (Aefeso 6:4) Thayo limenelo silingaperekedwe kwa wina, ngakhale ngati atate angakhalenso ndi ntchito ina yoyang’anira zochita mumpingo Wachikristu. Kodi atate otero angasamalire motani mathayo awo—popezera mabanja awo zofunika zakuthupi, zauzimu, ndi chikondi—ndiyeno nthaŵi imodzimodziyo, kuyang’anira mpingo?
Kupereka Chichirikizo Chofunika
8. Kodi mkazi wake wa mkulu angamchirikize motani?
8 Mwachionekere, akulu okhala ndi mathayo abanja angapindule ndi chichirikizo. Watchtower yotchulidwayo inati mkazi Wachikristu angachirikize mwamuna wake. Inati: “Angampeputsire zinthu kuti akonzekere mathayo ake osiyanasiyana, ndi kuthandizira kuti nthaŵi ya mwamuna ndi yake isawonongeke mwa kukhala ndi ndandanda yabwino panyumba, kukonza chakudya panthaŵi yake, kukhala okonzeka kupita ku misonkhano ya mpingo mwamsanga. . . . Motsogozedwa ndi mwamuna wake, mkazi Wachikristu angathandize kwambiri kuphunzitsa ana njira imene ayenera kuyendamo kuti akondweretse Yehova.” (Miyambo 22:6) Inde, mkazi analengedwa kukhala “womthangatira,” ndipo mwamuna wake mwanzeru adzayamikira thandizo lake. (Genesis 2:18) Chichirikizo chake chingamkhozetse kusamalira bwino lomwe banja lake ndi mathayo ake mumpingo.
9. Kodi ndani mumpingo wa ku Tesalonika amene analimbikitsidwa kuthandiza ena mumpingo?
9 Komabe, akazi a akulu Achikristu sindiwo okha angachite zinthu zochirikiza woyang’anira amene ayenera ‘kuŵeta gulu la Mulungu’ ndi kusamaliranso banja lake. (1 Petro 5:2) Ndayaninso angachite zimenezo? Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ku Tesalonika kuchitira ulemu “akulu” mwa iwo. Komabe, popitiriza kufotokozera abale ameneŵa—makamaka aja amene sanali oyang’anira—Paulo analemba kuti: “Tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani [opsinjika mtima, NW]. Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse.”—1 Atesalonika 5:12-14.
10. Kodi thandizo lachikondi la abale onse limakhala ndi chotulukapo chabwino chotani pampingo?
10 Zimakhala bwino chotani nanga pamene abale mumpingo ali ndi chikondi chimene chimawasonkhezera kutonthoza opsinjika mtima, kuchirikiza ofooka, kulangiza osayenda bwino, ndi kukhala oleza mtima pa onse! Abale ku Tesalonika, amene anali atangolandira kumene choonadi cha Baibulo ngakhale kuti anali ndi mavuto ndi mayesero, anatsatira uphungu wa Paulo wa kuchita zimenezi. (Machitidwe 17:1-9; 1 Atesalonika 1:6; 2:14; 5:11) Talingalirani zotulukapo za kulimbitsa mpingo wonse ndi kuugwirizanitsa zimene kumvera kwawo kwa chikondi kunali nazo! Momwemonso, pamene abale lerolino atonthozana, kuchirikizana, ndi kulangizana, zimapeputsa mathayo a kuŵeta a akulu amene kaŵirikaŵiri amakhalanso ndi mabanja oti aziwasamalira.
11. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kunena kuti mawu akuti “abale” anaphatikizapo akazi? (b) Kodi mkazi wachikulire Wachikristu angapereke thandizo lotani kwa mkazi wachichepere lerolino?
11 Kodi “abale” amene mtumwi Paulo anali kulankhulako anaphatikizapo akazi? Inde, pakuti akazi ambiri anakhala okhulupirira. (Machitidwe 17:1, 4; 1 Petro 2:17; 5:9) Kodi akazi otero akanapereka thandizo lotani? Eya, panali akazi aang’ono m’mipingo amene kunali kowavuta kulamulira “zilakolako” (NW) zawo kapena amene anali “opsinjika mtima.” (1 Timoteo 5:11-13) Akazi ena lerolino ali ndi mavuto onga amenewo. Zimene angafune kwambiri ndi munthu womvetsera ndi wachifundo basi. Kaŵirikaŵiri mkazi wachikulire Wachikristu ndiye munthu woyenerera koposa kupereka thandizolo. Mwachitsanzo, angakambirane ndi mkazi wina nkhani zaumwini zimene mwamuna Wachikristu pa iye yekha sakhoza kuzisamalira bwino. Posonyeza phindu la kupereka thandizo lotero, Paulo analemba kuti: “Akazi okalamba akhale . . . akuphunzitsa zokoma; kuti akalangize akazi aang’ono akonde amuna awo, akonde ana awo, akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwawo, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.”—Tito 2:3-5.
12. Kodi ndi chitsogozo chofunika chayani chimene onse mumpingo ayenera kutsatira?
12 Alongo odzichepetsa amakhala dalitso lotani nanga pampingo pamene mofunitsitsa amachirikiza amuna awo ndi akulu omwe! (1 Timoteo 2:11, 12; Ahebri 13:17) Akulu amene ali ndi mathayo abanja amapindula kwambiri pamene onse akufuna kuthandizana mu mzimu wa chikondi ndi pamene onse agonjera chitsogozo cha abusa oikidwa.—1 Petro 5:1, 2.
Makolo, Kodi Mumaika Chiyani Pamalo Oyamba?
13. Kodi atate ambiri amalephera motani m’mabanja awo?
13 Zaka zakumbuyoku wamaseŵero wina wotchuka anati: “Ndaona amuna okhoza akuyendetsa makampani okhala ndi anthu mazana ambiri; amadziŵa kuchita ndi mkhalidwe uliwonse, kulangiza ndi kupereka mfupo m’zabizinesi. Koma bizinesi yaikulu koposa imene akuyendetsa ndiyo banja lawo ndipo amalephera.” Chifukwa? Kodi si chifukwa chakuti amaika bizinesi ndi ntchito zina pamalo oyamba nanyanyala uphungu wa Mulungu? Mawu ake amati: “Mawu awa ndikuuzani . . . muziwaphunzitsa kwa ana anu.” Ndipo anayenera kuchita zimenezi masiku onse. Makolo afunika kupereka nthaŵi yawo yochuluka—ndipo makamaka chikondi ndi chisamaliro chawo.—Deuteronomo 6:6-9.
14. (a) Kodi makolo ayenera kusamalira motani ana awo? (b) Kodi kuphunzitsa ana koyenera kumaphatikizaponji?
14 Baibulo limatikumbutsa kuti ana ali cholandira cha kwa Yehova. (Salmo 127:3) Kodi mumasamalira ana anu monga ngati mukusamalira chuma cha Mulungu, mphatso imene wakuikizani? Mwachionekere mwana wanu adzakondwa mukamfukatira, mukumasonyeza chikondi chanu ndi chisamaliro mwakutero. (Marko 10:16) Koma ‘kuphunzitsa mwana poyamba njira yake’ kumafuna zambiri kuposa kungomfukatira ndi kumpsompsona. Kuti mwana akhale ndi nzeru yopeŵera mbuna za m’moyo, afunikanso chilango chachikondi. Kholo limasonyeza chikondi choona mwa ‘kumyambitsa mwana kumlanga.’—Miyambo 13:1, 24; 22:6.
15. Kodi nchiyani chikusonyeza kufunika kwake kwa chilango cha makolo?
15 Tingaone kufunika kwake kwa chilango cha makolo mwa njira imene phungu wina wa pasukulu anafotokozera ana omwe amafika ku ofesi kwake: “Amamvetsa chisoni, amakhala atondovi, ndi osoŵa chochita. Amakhala akulira polankhula za mmene zinthu zilili. Ambiri—ambiri kuposa amene wina angaganize—ayesa kudzipha, sikuti amakondwa koma zimangowakanika kupirira; nchifukwa chakuti amamva kusakondwa konse, kuti palibe amene amasamala za iwo, ndipo amakhala opsinjika chifukwa chakuti pa usinkhu wawo waung’onowo amakhala ndi thayo lalikulu la ‘kuyang’anira zinthu’ ndipo nkovuta kwambiri.” Anawonjezera: “Kumawawopsa achichepere kuganiza kuti ndiwo akuyendetsa zinthu.” Zoona, ana angayese kuzemba chilango, koma kwenikweni amayamikira zitsogozo ndi ziletso zomwe makolo awo amawaikira. Amakondwa kuti makolo awo amawasamalira kwambiri powaikira ziletso. “Zandipeputsira zinthu kwambiri,” anatero wachinyamata wina amene makolo ake anachita zimenezo.
16. (a) Kodi chimachitika nchiyani kwa ana ena okulira m’mabanja Achikristu? (b) Kodi nchifukwa ninji kupulupudza kwa mwana sikumatanthauza kwenikweni kuti chiphunzitso choperekedwa ndi makolo sichinali bwino?
16 Komabe, ngakhale kuti ali ndi makolo amene amawakonda ndi kuwaphunzitsa bwino, ana ena, monga mwana woloŵerera wa m’fanizo la Yesu, amakana chitsogozo cha makolo nasokera. (Luka 15:11-16) Komabe, zimenezo zokha sizitanthauza kuti makolo sanakwaniritse thayo lawo la kuphunzitsa mwana moyenera, mmene Miyambo 22:6 imalangizira. Mawu a ‘kuphunzitsa mwana poyamba njira yake ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo’ anaperekedwa monga lamulo lachisawawa. Mwachisoni, monga mwana woloŵerera, ana ena ‘amanyoza kumvera makolo.’—Miyambo 30:17.
17. Kodi makolo a ana opulupudza angapeze kuti chitonthozo?
17 Tate wina wa mwana wopulupudza anadandaula kuti: “Ndayesayesa kumfika pamtima. Sindidziŵa chochita chifukwa ndayesa zinthu zambiri. Palibe chimene chathandiza.” Tikhulupirira kuti m’kupita kwa nthaŵi, ana opulupudza otero adzakumbukira chiphunzitso chachikondi chimene analandira ndi kubwerera monga mwana woloŵerera. Komabe, choonadi nchakuti ana ena amapandukabe nachita zinthu zoipa akumapweteka kwambiri makolo awo. Makolo amapeza chitonthozo mwa kudziŵa kuti ngakhale mphunzitsi wamkulu koposa onse okhalako pa dziko lapansi anaona wophunzira wake wa nthaŵi yaitali Yudasi Isikariote akumpereka. Ndipo Yehova mwiniyo mosakayikira anachita chisoni kwambiri pamene ana ake ambiri auzimu anakana uphungu wake napanduka osati chifukwa cha Iye.—Luka 22:47, 48; Chivumbulutso 12:9.
Ananu—Kodi Mudzakondweretsa Yani?
18. Kodi ana angasonyeze motani kuti amaika Mulungu pamalo oyamba?
18 Yehova akulimbikitsa ananu kuti: “Mverani akukubalani mwa Ambuye.” (Aefeso 6:1) Achicheperenu ikani Mulungu pamalo oyamba mwa kuchita zimenezi. Musakhale chitsiru! “Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake,” amatero Mawu a Mulungu. Ndiponso musaganize modzigangira kuti simufunika chilango. Choonadi nchakuti “pali mbadwo umene umadziyesa woyera, komabe sunayeretsedwe litsiro lake.” (Miyambo 15:5; 30:12, American Standard Version) Chotero labadirani chilangizo chaumulungu—‘imvani,’ ‘sungani,’ ‘musaiŵale,’ ‘tcherani makutu,’ “samalirani,”NW, ndipo ‘musasiye’ malamulo ndi mwambo wa makolo.—Miyambo 1:8; 2:1; 3:1; 4:1; 6:20.
19. (a) Kodi ndi zifukwa zamphamvu zotani zimene ana ali nazo za kumvera Yehova? (b) Kodi ana angasonyeze motani kuti akuyamikira Mulungu?
19 Muli ndi zifukwa zamphamvu za kumvera Yehova. Amakukondani, ndipo wapereka malamulo ake, kuphatikizapo lamulo lija lakuti ana azimvera makolo awo, kuti akutetezereni ndi kukuthandizani kukhala ndi moyo wachimwemwe. (Yesaya 48:17) Anaperekanso Mwana wake kudzakuferani kuti mupulumuke ku uchimo ndi imfa ndi kupeza moyo wosatha. (Yohane 3:16) Kodi mumayamikira? Mulungu akupenya ali kumwamba, akumapenda mtima wanu kuona ngati mumamkondadi ndi kuyamikira makonzedwe ake. (Salmo 14:2) Nayenso Satana akupenya, ndipo akutonza Mulungu, akumati simudzamumvera Iye. Mumakondweretsa Satana ndi ‘kumvetsa chisoni’ Yehova pamene simumvera Mulungu. (Salmo 78:40, 41) Yehova akukuchondererani: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga [mwa kundimvera ine]; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Inde, nali funso, Kodi mudzakondweretsa yani, Satana kapena Yehova?
20. Kodi wachichepere wina walimba mtima motani potumikira Yehova ngakhale pamene achita mantha?
20 Sikopepuka kuchita chifuniro cha Mulungu ndi zovuta zimene Satana ndi dziko lake amakudzetserani. Kungakhale kowopsa. Mtsikana wina anati: “Kuwopa kuli ngati kuzizidwa. Mukhoza kukuletsa.” Anafotokoza kuti: “Mukazizidwa, mumavala juzi. Ngati muzizidwabe, mumavalanso ina. Ndipo mumawonjezerapo ina mpaka kuzizirako kutatha ndipo simukuzizidwanso. Chotero kupemphera kwa Yehova pamene mwachita mantha kuli ngati kuvala juzi mutazizidwa. Ngati ndichitabe mantha pambuyo popemphera, ndimapempheranso mobwerezabwereza, mpaka manthawo atatha. Ndipo kumathandiza. Kwandipeŵetsa mavuto!”
21. Kodi Yehova adzatichirikiza motani ngati tiyesetsa kumuika pamalo oyamba m’moyo wathu?
21 Tikayesetsa kuika Mulungu pamalo oyamba m’moyo wathu, Yehova adzatichirikiza. Adzatilimbitsa, akumatipatsa chithandizo cha angelo chitafunika, monga momwedi anachitira kwa Mwana wake. (Mateyu 18:10; Luka 22:43) Makolonu ndi inunso ana, limbani mtima. Khalani ndi mantha onga a Kristu, ndipo mudzakondwera nawo. (Yesaya 11:3) Inde, “opa[ni] Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 12:13.
Kodi Mukhoza Kuyankha?
◻ Kodi ndi mathayo otani amene otsatira Yesu oyambirira anafunika kulinganiza?
◻ Kodi makolo Achikristu ayenera kukwaniritsa thayo lotani?
◻ Kodi pali thandizo lotani kwa akulu Achikristu okhala ndi mabanja?
◻ Kodi ndi ntchito yotani yofunika imene alongo angachite pampingo?
◻ Kodi uphungu ndi chitsogozo zimene ana afunika kulabadira nzotani?
[Chithunzi patsamba 15]
Nthaŵi zambiri mkazi wokhwima Wachikristu angapatse mkazi wachichepere thandizo lofunika
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi makolo okhala ndi ana opulupudza angapeze chitonthozo chotani m’Malemba?