Musaleme Kuthamanga Makani a Moyo!
“Tithamange Mwachipiriro Makaniwo Adatiikira.”—Ahebri 12:1.
1, 2. Kodi ndi zochitika zochititsa chidwi zotani zimene zasangalatsa atumiki a Yehova m’masiku ano otsiriza?
TIKUKHALA m’nthaŵi zochititsa chidwi ndiponso zovuta. Zaka zoposa 80 zapitazo, mu 1914, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu wakumwamba. “Tsiku la Ambuye” pamodzi ndi “nthaŵi ya chitsiriziro” ya dongosolo lino la zinthu zinayamba. (Chivumbulutso 1:10; Danieli 12:9) Kuyambira pamenepo makani a Mkristu othamangira moyo akhala aliŵiro kwambiri. Atumiki a Mulungu alimbikira mwamphamvu kuyendera limodzi ndi galeta la Yehova lakumwamba, gulu lake lakumwamba, limene likuyenda mosaima kuti likwaniritse zifuno za Yehova.—Ezekieli 1:4-28; 1 Akorinto 9:24.
2 Kodi anthu a Mulungu apeza chimwemwe pamene ‘akuthamanga makani’ kumka kumoyo wosatha? Ndithudi! Iwo asangalala kuona kusonkhanitsidwa kwa otsala a abale a Yesu, ndipo ngokondwa poona kuti kusindikiza chizindikiro komaliza kwa otsalira a 144,000 kwatsala pafupi kutha. (Chivumbulutso 7:3, 4) Ndiponso, iwo ngokondwa pozindikira kuti Mfumu yoikidwa ndi Yehova yaponya zenga lake kuti imwete “dzinthu za dziko.” (Chivumbulutso 14:15, 16) Ndipo zotuta zake nzochuluka chotani nanga! (Mateyu 9:37) Pakali pano, anthu oposa mamiliyoni asanu asonkhanitsidwa—“khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Palibe anganene kuti khamulo lidzakhala lalikulu motani pomalizira pake, popeza palibe munthu angakhoze kuliŵerenga.
3. Kodi tiyenera kukulitsabe mzimu wokondwera mosasamala kanthu za chiyani?
3 Zoonadi, Satana akuyesetsa kutipunthwitsa kapena kutibweza mmbuyo pamene tili paliŵiro m’makaniwa. (Chivumbulutso 12:17) Ndipo kupitirizabe kuthamanga kwakhala kovuta pakati pa nkhondo, njala, miliri, ndi zovuta zina zonse zosonyeza kuti tili m’nthaŵi yamapeto. (Mateyu 24:3-9; Luka 21:11; 2 Timoteo 3:1-5) Ngakhale kuti zili choncho, mitima yathu njosangalala koposa pamene tikuyandikira mapeto a makaniwa. Tikuyesetsa kusonyeza mzimu umene Paulo analimbikitsa Akristu anzake a m’tsiku lake kukhala nawo: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.”—Afilipi 4:4.
4. Kodi Akristu a ku Filipi anasonyeza mzimu wotani?
4 Sitingakayike kuti Akristu amene Paulo analembera mawu amenewo anali kukondwera ndi chikhulupiriro chawo, popeza kuti Paulo anawauza kuti: “Pitirizani kukondwera mwa Ambuye.” (Afilipi 3:1, NW) Anthu a mumpingo wa Afilipi anali ooloŵa manja ndiponso achikondi amene anatumikira mwachangu ndiponso mochokera pansi pamtima. (Afilipi 1:3-5; 4:10, 14-20) Koma si Akristu onse a m’zaka za zana loyamba amene anali ndi mzimu umenewo. Mwachitsanzo, Akristu ena achiyuda amene Paulo analembera buku la Ahebri anali kudetsa nkhaŵa.
“Kusamaliradi Zimene Tidazimvazi”
5. (a) Kodi Akristu achihebri anali ndi mzimu wotani pamene mpingo woyamba wachikristu unapangidwa? (b) Fotokozani mzimu umene Akristu ena achihebri anali nawo cha ku ma 60 C.E.
5 Mumpingo woyamba wachikristu m’mbiri ya dziko munali Ayuda achibadwa ndi otembenukira kuchiyuda ndipo unakhazikitsidwa ku Yerusalemu mu 33 C.E. Kodi iwo anali ndi mzimu wotani? Munthu amangofunika kuŵerenga machaputala oyambirira a buku la Machitidwe kuti adziŵe za kusonkhezereka kwawo kochokera mumtima ndi chimwemwe chawo, ngakhale pakati pa chizunzo. (Machitidwe 2:44-47; 4:32-34; 5:41; 6:7) Komabe, m’kupita kwa zaka makumi ambiri, zinthu zinasintha, ndipo mwachionekere Akristu ambiri achiyuda anachepetsa liŵiro lawo pamakani a moyo. Pofotokoza mkhalidwe wawo cha ku ma 60 C.E., buku lina limati: “Unali mkhalidwe wa mphwayi ndi kutopa, wa ziyembekezo zosakwaniritsidwa, ziyembekezo zochedwa kukwaniritsidwa, kunyalanyaza ndiponso kupanda chikhulupiriro. Iwo anali Akristu koma chiitano chawo anachiona kukhala chopanda pake.” Kodi Akristu odzozedwa analoŵamo bwanji mumkhalidwewu? Kusanthula mbali za kalata ya Paulo yopita kwa Ahebri (yolembedwa cha mu 61 C.E.) kudzatithandiza kuyankha funso limenelo. Kusanthula zimenezi kudzathandiza tonsefe lerolino kupeŵa kuloŵa mumkhalidwe wofananawo wa kufooka kwauzimu.
6. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kulambira m’Chilamulo cha Mose ndi kulambira kozikidwa pa kukhulupirira Yesu Kristu?
6 Akristu achihebri anachokera m’Chiyuda, malambiridwe amene ankanena kuti akulabadira Chilamulo chimene Yehova anapereka kudzera mwa Mose. Chilamulo chimenecho chiyenera kuti chinapitirizabe kukopa Akristu ambiri achiyuda, mwinamwake chifukwa chakuti kwa zaka mazana ambiri ndicho chinali njira yokha yolambirira Yehova, ndipo linali dongosolo lochititsa chidwi la kulambira, lokhala ndi ansembe, kupereka nsembe nthaŵi ndi nthaŵi, ndi kachisi wotchuka padziko lonse ku Yerusalemu. Chikristu nchosiyana ndi zimenezo. Icho chimafuna lingaliro lauzimu, monga la Mose, amene “anapenyerera chobwezera cha mphotho” yakutsogolo ndiponso “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.” (Ahebri 11:26, 27) Akristu ambiri achiyuda mwachionekere analibe lingaliro lauzimu limeneli. Iwo anali kungothamanga mokayikakayika m’malo mothamanga ndi chifuno.
7. Kodi dongosolo limene tachokamo lingakhudze motani mmene tikuthamangira makani a moyo?
7 Kodi pali mkhalidwe wofananawo lerolino? Zoonadi, zinthu zasintha. Komabe, Akristu achokera m’dongosolo la zinthu lodzitukumula kwadzaoneni. Dziko likupereka mwaŵi wosangalatsa, koma panthaŵi imodzimodziyo, likusenzetsa anthu mitolo yolemera. Ndiponso, ambiri a ife tikukhala m’maiko mmene anthu ochuluka ali ndi mzimu wokayikakayika ndi mmene munthu aliyense payekha amafuna kusamala zake zokha. Ngati tidzilekerera kuti tisonkhezeredwe ndi dongosolo limeneli, ‘maso a mitima yathu’ angachite khungu mosavuta. (Aefeso 1:18) Kodi tingathamange bwino motani makani a moyo ngati sitithanso kuzindikira bwino kumene tikupita?
8. Kodi Chikristu nchokwezeka kuposa kulambira kwa Chilamulo m’njira zina zotani?
8 Kuti asonkhezere Akristu achiyuda, Paulo anawakumbutsa za kukwezeka kwa dongosolo lachikristu mosiyana ndi Chilamulo cha Mose. Nzoona kuti pamene mtundu wa Israyeli wakuthupi unali anthu a Yehova otsatira Chilamulo, Yehova analankhula nawo kudzera mwa aneneri ouziridwa. Komano, akutero Paulo, lero akulankhula “[mwa, NW] Mwana amene anamuika woloŵa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi a m’mwamba omwe.” (Ahebri 1:2) Ndiponso, Yesu ndiye wamkulu pa mafumu ‘anzake’ onse a mumzere wa Davide. Iye ndi wamkulu kuposa ndi angelo omwe.—Ahebri 1:5, 6, 9.
9. Kodi nchifukwa ninji ifeyo, monga Akristu achiyuda a m’tsiku la Paulo, tifunikira “kusamaliradi” zimene Yehova akunena?
9 Motero, Paulo analangiza Akristu achiyuda kuti: “Tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.” (Ahebri 2:1) Ngakhale kuti kuphunzira za Kristu kunali dalitso lalikulu, panali zambiri zofunikira. Iwo anayenera kupereka chisamaliro chachikulu pa Mawu a Mulungu kuti alimbane ndi chisonkhezero cha dziko lachiyuda lowazinga. Ifenso tiyenera “kusamaliradi” zimene Yehova akunena chifukwa chakuti tazingidwa ndi mabodza osatha a dzikoli. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumakhala ndi phunziro labwino ndi kukhala ndi ndandanda yabwino ya kuŵerenga Baibulo. Monga momwe Paulo akunenera pambuyo pake m’kalata yake yopita kwa Ahebri, zikutanthauzanso kufika pamisonkhano nthaŵi zonse ndi kulengeza chikhulupiriro chathu kwa ena. (Ahebri 10:23-25) Zinthu zimenezi zidzatithandiza kukhalabe atcheru mwauzimu kuti tipitirizebe kuona chiyembekezo chathu chaulemerero. Ngati tidzaza maganizo athu ndi malingaliro a Yehova, sitidzafooka kapena kugwa ndi chilichonse chimene dzikoli lingatichite.—Salmo 1:1-3; Miyambo 3:1-6.
“Dandauliranani Nokha”
10. (a) Kodi nchiyani chingachitikire amene sasamaliradi Mawu a Yehova? (b) Kodi ‘tingadandaulirane tokha’ motani?
10 Ngati sitipereka chisamaliro chachikulu pa zinthu zauzimu, malonjezo a Mulungu nawonso sangaoneke kukhala enieni. Zimenezi zinachitika ngakhale m’zaka za zana loyamba pamene mipingo inali ndi Akristu odzozedwa okhaokha ndipo atumwi ena anali adakali amoyo. Paulo anachenjeza Ahebri kuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo; komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo.” (Ahebri 3:12, 13) Mawu a Paulo akuti “tapenyani” akugogomezera kufunika kwa kukhala atcheru. Pali ngozi! Kusoŵa chikhulupiriro—“uchimo”—kungayambike m’mitima mwathu, ndipo tingalekane ndi Mulungu m’malo moyandikana naye. (Yakobo 4:8) Paulo akutilimbikitsa kuti ‘tidandaulirane tokha.’ Tikufunikira chikondi cha pa mayanjano a abale. “Wopanduka [wodzipatula, NW] afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Kufunika kwa mayanjano ameneŵa kumasonkhezera Akristu lerolino kuti nthaŵi zonse azifika pamisonkhano yampingo, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo.
11, 12. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhutiritsidwa ndi kungodziŵa ziphunzitso zoyambirira zachikristu?
11 Pambuyo pake m’kalata yake, Paulo akupereka uphungu wofunika kwambiri uwu wakuti: “Mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusoŵanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. . . . Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:12-14) Mwachionekere, Akristu ena achiyuda analephera kukula m’kumvetsa kwawo. Iwo sanali kulandira msanga kuunika kowonjezereka kokhudzana ndi Chilamulo ndi mdulidwe. (Machitidwe 15:27-29; Agalatiya 2:11-14; 6:12, 13) Ena ayenera kuti anakondabe miyambo yakale monga kusunga Sabata mlungu uliwonse ndi Tsiku la Chitetezo limenelo lapachaka lochititsa kukhudzika mtima.—Akolose 2:16, 17; Ahebri 9:1-14.
12 Ndiye chifukwa chake, Paulo akuti: “Polekana nawo mawu a chiyambidwe cha Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu.” (Ahebri 6:1) Wochita mpikisano wothamanga mtunda wautali amene amasamala kwambiri zimene amadya amatha kupirira makani aatali ndi othetsa mphamvu amenewo. Mofananamo, Mkristu amene amasamala kwambiri za zakudya zauzimu zopatsa thanzi—amene samangolekezera pa “mawu a chiyambidwe” oyambirira—adzatha kuthamanga makaniwo mpaka kuwamaliza. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 4:7.) Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kukulitsa chidwi chofuna kudziŵa “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama” kwa choonadi, ndi kupita patsogolo ku uchikulire.—Aefeso 3:18, 19.
“Chikusoŵani Chipiriro”
13. Kodi Akristu achihebri anali atasonyeza motani chikhulupiriro chawo poyambirira?
13 Pentekoste wa 33 C.E. atangopita, Akristu achiyuda anaima molimbika mosasamala kanthu za chitsutso choopsa. (Machitidwe 8:1) Mwinamwake nzimene Paulo anali kulingalira pamene analemba kuti: “Tadzikumbutsani masiku akale, mmenemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zoŵaŵa.” (Ahebri 10:32) Kupirira mokhulupirika kumeneku kunasonyeza chikondi chawo pa Mulungu ndipo kunawapatsa ufulu wa kulankhula naye. (1 Yohane 4:17) Paulo akuwalimbikitsa kuti asataye ufuluwo chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro. Akuwalimbikitsa kuti: “Chikusoŵani [“mufunikira,” NW] chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. Pakuti katsala kanthaŵi kakang’onong’ono. Ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.”—Ahebri 10:35-37.
14. Kodi ndi zenizeni ziti zimene ziyenera kutithandiza kupirira ngakhale kuti tatumikira Yehova zaka zambirimbiri?
14 Nanga ifeyo lerolino? Ambiri a ife tinali achangu titangophunzira choonadi chachikristu. Kodi changucho tikali nacho? Kapena kodi ‘tataya chikondi chathu choyamba’? (Chivumbulutso 2:4) Kodi changu chathu chazizira, mwinamwake tataya mtima pang’ono kapena tatopa ndi kuyembekezera Armagedo? Taimani kaye, ndipo ganizirani. Choonadi chikali chochititsa chidwi monga momwe chinalili poyamba. Yesu akali Mfumu yathu yakumwamba. Tikuyembekezerabe moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso, ndipo tikali paunansi wathu ndi Yehova. Ndipotu musaiŵale kuti: “Wakudzayo adzafika, wosachedwa.”
15. Monga Yesu, kodi Akristu ena apirira motani chizunzo choŵaŵa?
15 Chotero, mawu a Paulo olembedwa pa Ahebri 12:1, 2 ngoyenerera kwambiri: “Titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” Pali zinthu zambiri zimene atumiki a Mulungu apirira m’masiku ano otsiriza. Monga Yesu amene anali wokhulupirika mpaka imfa yopweteka, ena mwa abale ndi alongo athu apirira mokhulupirika chizunzo choipitsitsa—kukhala m’ndende, kuzunzidwa, kugonedwa mokakamiza, ngakhale imfa. (1 Petro 2:21) Kodi sitimawakonda kuchokera mumtima titalingalira za kukhulupirika kwawo?
16, 17. (a) Kodi Akristu ochuluka amalimbana ndi zovuta zotani pachikhulupiriro chawo? (b) Kodi ndi kukumbukira chiyani kumene kudzatithandiza kuthamangabe pamakani a moyo?
16 Komabe, mawu otsatira a Paulo amakhudza ochuluka: “Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo.” (Ahebri 12:4) Ngakhale zili choncho, njira ya choonadi njovuta kwa tonsefe m’dongosolo lino. Ena amafooka chifukwa cha ‘ochimwa otsutsana nawo’ kuntchito yakuthupi kapena kusukulu, kupirira kunyozedwa kapena kukana chikakamizo choti achimwe. (Ahebri 12:3) Chifukwa cha chiyeso champhamvu, ena ataya kutsimikiza mtima kwawo pa kusunga makhalidwe apamwamba oikidwa ndi Mulungu. (Ahebri 13:4, 5) Ampatuko asokoneza mkhalidwe wauzimu wa ena angapo amene amamvetsera mabodza awo oipitsitsa. (Ahebri 13:9) Kusiyana malingaliro kwachititsa ena kutaya chimwemwe chawo. Kukondetsa zosangulutsa ndi zochita za panthaŵi yakupuma kwafooketsa Akristu ena. Ndipo ambiri amamva kukhala otsenderezeka ndi mavuto a m’dongosolo lino la zinthu.
17 Zoonadi, pamikhalidwe yonseyi palibe mkhalidwe uliwonse wofuna ‘kukana kufikira mwazi.’ Ndipo ina imakhalapo chifukwa cha kusaganiza bwino kwathu. Koma yonseyo imachititsa chikhulupiriro chathu kukhala chovuta. Ndiye chifukwa chake tiyenera kuyang’ana pa chitsanzo cha Yesu cha kupirira. Tisaiŵaletu kufunika kwa chiyembekezo chathu. Tisataye konse kukhulupirira kwathu kuti Yehova “ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Tikatero, tidzakhala ndi nyonga yauzimu yothamangabe makani a moyo.
Tingathe Kupirira
18, 19. Kodi nzochitika zotani za m’mbiri yakale zimene zimasonyeza kuti Akristu achihebri ku Yerusalemu anamva uphungu wouziridwa wa Paulo?
18 Kodi Akristu achiyuda anatani ataŵerenga kalata ya Paulo? Patapita zaka ngati zisanu ndi chimodzi kalata yopita kwa Ahebri italembedwa, Yudeya anali pankhondo. Mu 66 C.E., gulu lankhondo lachiroma linazinga Yerusalemu, kukwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira.” (Luka 21:20) Komabe, pofuna kuthandiza Akristu amene adzakhala ali m’Yerusalemu panthaŵiyo, Yesu anati: “Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asaloŵemo.” (Luka 21:21) Choncho, kumenya nkhondo ndi Roma kunadzetsa chiyeso: Kodi Akristu achiyudawo adzathaŵamo m’Yerusalemu, chimake cha kulambira kwa Ayuda ndi malo a kachisi waulemereroyo?
19 Mosayembekezereka, ndiponso pachifukwa chosadziŵika, Aromawo anabwerera. Ayuda opembedza ayenera kuti anaona zimenezi kukhala umboni wakuti Mulungu akuchinjiriza mzinda wawo wopatulika. Bwanji ponena za Akristu? Mbiri yakale imatiuza kuti anathaŵa. Kenako, mu 70 C.E., Aroma anabweranso ndi kuwononga Yerusalemu kotheratu, ndipo chiŵerengero chochititsa mantha cha anthu anafa. “Tsiku la Yehova” lonenedweratu ndi Yoweli linafika pa Yerusalemu. Koma Akristu okhulupirika sanalinso mmenemo. Iwo ‘anapulumutsidwa.’—Yoweli 2:30-32; Machitidwe 2:16-21.
20. Kodi kudziŵa kuti “tsiku la Yehova” lalikulu lili pafupi kuyenera kutisonkhezera m’njira zotani?
20 Lerolino, tikudziŵa kuti “tsiku la Yehova” lalikulu linanso lidzafika padongosolo lonse la zinthu lilipoli posachedwapa. (Yoweli 3:12-14) Sitikudziŵa kuti tsikulo lidzafika liti. Koma Mawu a Mulungu akutitsimikiza kuti lidzafikadi! Yehova akunena kuti silidzazengereza. (Habakuku 2:3; 2 Petro 3:9, 10) Choncho, tiyeni ‘tisamaliredi zimene tidazimvazi.’ Tipeŵe kukhala opanda chikhulupiriro, “tchimoli limangotizinga.” Titsimikize mtima kuti tidzapirira kwautali wake wonse. Tiyeni tikumbukire kuti gulu lakumwamba la Yehova longa galeta likupitabe patsogolo. Ilo lidzakwaniritsa chifuno chake. Choncho tonsefe tipitirize kuthamanga ndipo tisatope kuthamanga makani a moyo!
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi kumva chilimbikitso chotani cha Paulo kwa Afilipi kumene kudzatithandiza kupirira pamakani a moyo?
◻ Kodi nchiyani chidzatithandiza kulimbana ndi mkhalidwe wa dzikoli wofuna kutisokoneza?
◻ Kodi tingathandizane motani kuti tipirire pamakaniwa?
◻ Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingachititse Mkristu kuchepetsa liŵiro?
◻ Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize motani kupirira?
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Akristu, monga othamanga, sayenera konse kulola kanthu kalikonse kuwasokoneza
[Chithunzi patsamba 10]
Palibe chimene chingaletse galeta lalikulu la Yehova lakumwamba kuti lisakwaniritse chifuno chake