Dziko Labwinopo—Layandikira!
“CHILAKOLAKO champhamvu cha paradaiso chili pakati pa zilakolako zimene zimasautsa anthu maganizo. Chingakhale champhamvu koposa ndi chokhalitsa kuposa zilakolako zonse. Chilakolako chakutichakuti cha paradaiso chimaonekera m’mbali iliyonse ya moyo wachipembedzo,” ikutero The Encyclopedia of Religion.
Mafuko onse amaonekera kukhala ndi chikhumbo chofanana cha kukhala m’dziko labwinopo, monga ngati kuti akulirira dziko loyambirira labwino koposa lomwe kulibeko. Zimenezi zimasonyeza kuthekera kwakuti paradaiso woyambirira analiko, koma kuti? Wopenda maganizo a anthu anganene kuti chikhumbo champhamvu chimenechi chimavumbula chilakolako cha kupeza chisungiko chotayika cha m’mimba mwa nakubala. Komabe, malongosoledwe ameneŵa samakhutiritsa akatswiri amene amapenda mbiri ya chipembedzo.
“Chilakolako Champhamvu cha Paradaiso”—Chifukwa?
Kodi kukhalapo kwa chilakolako champhamvu choterocho, monga momwe ena amanenera, kumangochititsa mavuto ndi kufupika kwa moyo kukhala kopiririka? Kapena kodi pali malongosoledwe ena?
Kodi nchifukwa ninji mtundu wa anthu umalakalaka dziko labwinopo? Baibulo limapereka malongosoledwe amene ali omvekera bwino ndi okhweka: Mtundu wa anthu unachokera ku dziko labwinopo! Paradaiso woyambirira adalikodi. Mawu a Mulungu amamulongosola monga “munda” wokhala pakati pa chigawo chakutichakuti ku Middle East, wodalitsidwa ndi “mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya.” Mulungu anaupereka kuti usamaliridwe ndi anthu okwatirana oyambirira. (Genesis 2:7-15) Anali malo abwino koposa amene anthu akanakhaladi achimwemwe.
Kodi nchifukwa ninji mikhalidwe ya Paradaiso imeneyo sinakhalitse? Chifukwa cha kupanduka kochitidwa poyamba ndi cholengedwa chauzimu ndipo kenako kwa anthu okwatiranawo. (Genesis 2:16, 17; 3:1-6, 17-19) Motero, munthu sanangotaya Paradaiso yekha komanso ungwiro, thanzi, ndi moyo wosatha. Mikhalidwe imene inayamba kukhalapo sinawongolere konse moyo wa anthu. Mosiyana, mkhalidwewu wanyonyotsoka mopitirizabe kufika pamkhalidwe woipa kwambiri umene tikuona lerolino.—Mlaliki 3:18-20; Aroma 5:12; 2 Timoteo 3:1-5, 13.
Kufunafuna Paradaiso —Mbiri ya Lingaliroli
Monga momwe mungayembekezere, “chilakolako champhamvu cha paradaiso” chili ndi mbiri yaitali kwambiri. Anthu a ku Sumer anakumbukira nthaŵi imene kugwirizana kunali pachilengedwe chonse: “Kunalibe mantha, chiwopsezo, munthu analibe mdani. . . . M’chilengedwe chonse, anthu mogwirizana anali kupereka chitamando ndi chinenero chimodzi kwa Enlil,” inanena motero ndakatulo yakale ya ku Mesopotamia. Ena, mofanana ndi Aigupto amakedzana, anayembekezera kufikira dziko labwinopo pambuyo pa imfa yawo. Iwo anakhulupirira kuti moyo wosafa unafika kumalo amene anatchedwa mabwalo a Aaru. Koma poyambapo, chiyembekezo chimenechi chinali chotseguka kwa olamulira okha; amphaŵi sakanalingalira zokhala m’dziko labwino.
M’dera la chipembedzo chosiyana, Ahindu adikirira kufikanso kwa nyengo ya dziko labwinopo (yuga) kwa zaka mazana ambiri. Malinga ndi ziphunzitso za Chihindu, nyengo za yuga zinayi zimabwerezedwabwerezedwa, ndipo pakali panopo tikukhala m’nthaŵi ya nyengo yoipitsitsa. Mwatsoka, nyengo ino ya Kali Yuga (nyengo yamdima), yokhala ndi mavuto ake ndi kuipa, idzakhalako, malinga ndi kunena kwa ena, kwa nyengo yaitali ya zaka 432,000. Komabe, Ahindu okhulupirika akudikirirabe nyengo yamtendere, Krita Yuga.
Kumbali ina, Agiriki ndi Aroma anali kulingalira zofika ku chisumbu chanthanthi cha Zisumbu Zamwaŵi, m’nyanja ya Atlantic. Ndipo olemba ambiri, onga ngati Hesiod, Virgil, ndi Ovid, analankhula za nyengo yamtendere yoyambirira yabwino koposa, akumayembekezera kuti tsiku lina ikabwezeretsedwa. Chakumapeto kwa zaka za zana loyamba B.C.E., wolemba ndakatulo Wachilatini Virgil analosera kuyandikira kwa kufika kwa aetas aurea (nyengo yamtendere) yatsopano ndi yokhalitsa. M’zaka mazana otsatira, “olamulira Achiroma osachepera pa khumi ndi asanu ndi mmodzi ananena kuti kulamulira kwawo kunakhazikitsanso Nyengo Yamtendere,” ikutero The Encyclopedia of Religion. Koma monga momwe tikudziŵira bwino lomwe lerolino, amenewo anali chabe manenanena andale.
A Celt ambiri analakalaka limene analilingalira kukhala dziko loŵala pachisumbu (kapena pa kagulu ka zisumbu) kutsidya la nyanja, kumene anakhulupirira kuti anthu anali kukhala mwachimwemwe kwenikweni. Malinga ndi kunena kwa nthano ina, Mfumu Arthur, ngakhale kuti anavulazidwa kwambiri, anapitiriza kukhala ndi moyo pambuyo popeza chisumbu chabwino kwambiri chotchedwa Avalon.
M’nthaŵi zamakedzana ndi m’Nyengo Yapakati, ambiri analingalira kuti munda wokhala ndi zinthu zosangalatsa zenizeni, munda wa Edene, unalipobe kwinakwake, “pamwamba pa phiri losatheka kulikwera kapena kutsidya kwa nyanja yosatheka kuiwoloka,” akulongosola motero wolemba mbiri Jean Delumeau. Ngakhale kuti wolemba ndakatulo wa ku Italy Dante anakhulupirira za paradaiso wakumwamba, iye analingalira kuti dziko lapansi la paradaiso linalipobe pamwamba pa phiri la Purigatoriyo yake, pandunji penipeni pa mzinda wa Yerusalemu. Ena anakhulupirira kuti unayenera kupezeka ku Asia, Mesopotamia, kapena ku mapiri a Himalayas. Ndipo nthano za m’zaka zapakati zonena za paradaiso wa ku Edene zinali zambiri. Ambiri anakhulupirira kuti pafupi ndi paradaiso ameneyo, panali ufumu wabwino kwambiri wolamuliridwa ndi Wansembe John wopembedzayo. Chifukwa cha kuyandikira kwa paradaiso wapadziko lapansiyo, kunalingaliridwa kuti moyo muufumu wa Wansembe John unali wautali ndi wachimwemwe, magwero osatha a zochuluka ndi chuma. Ena, pokumbukira nthano zamakedzana Zachigiriki, analingalirabe kuti zisumbu za paradaiso zinayenera kupezeka m’nyanja ya Atlantic. Mapu a nyengo yapakati anasonyeza kuti anthu anali otsimikizira kwambiri za kukhalako kwa munda wa Edene, ngakhale kusonyeza malo ake olingaliridwa.
M’zaka za mazana a 15 ndi 16, amalinyero amene anawoloka Atlantic kwenikweni anali kufunafuna dziko limene, panthaŵi imodzimodziyo, linali latsopano ndi lamakedzana. Iwo analingalira kuti kutsidya lina la nyanjayo, akapezako osati Indies yokha komanso munda wa Edene. Mwachitsanzo, Christopher Columbus anafunafuna mundawo pakati pa mapiri akumalo ozizirira ndi maiko akumalo otentha a ku South ndi Central America. Ofufuza malo a ku Ulaya amene anafika ku Brazil anali otsimikizira kuti paradaiso wotayikayo anayenera kukhala kumeneko chifukwa cha kucha bwino kwa kunja ndi kuchuluka kwa chakudya ndi zomera. Komabe, posakhalitsa anakakamizika kuzindikira zenizeni zochititsa chisoni.
Ma Utopia —Kodi Ndimalo Abwino Koposa?
Mmalo mokalimira kupeza dziko labwino koposa m’mbali zina zakutali zadziko lapansi, ena ayesa kulilinganiza. Motero, mu 1516, katswiri Wachingelezi wa chiphunzitso cha umunthu Thomas More analongosola za chisumbu cha Utopia, malo abwino kwambiri, amtendere ndi aakulu osiyana kwambiri ndi dziko loluluzika limene anadziŵa. Ena anayesanso kulinganiza maiko abwinopo, maiko okhala ndi anthu olungama: m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., kunali Plato ndi Lipabuliki lake; mu 1602, kunali bambo wa tchalitchi wa ku Italy Tommaso Campanella ndi mzinda wake wotchedwa Mzinda wa Dzuŵa wolinganizidwa bwino kwambiri; zaka zoŵerengeka zokha pambuyo pake, kunali wanthanthi Wachingelezi Francis Bacon amene analongosola “mkhalidwe wachimwemwe ndi wachipambano” wa Atlantis Yatsopano yake. M’kupita kwa zaka mazana, anthu oganiza a mitundu yonse (kaya okhulupirira chipembedzo kapena ayi) afotokoza maunyinji ambirimbiri a Utopia. Komabe, ngati pali amene anakhulupiriridwa, iwo ndioŵerengeka okha.
Pakhala ngakhale awo amene anayesa kumanga ma Utopia. Mwachitsanzo, mu 1824 Mngelezi wina wachuma, Robert Owen, anasankha zosamukira ku Indiana, U.S.A., kuti akakwaniritse malingaliro ake a Utopia m’mudzi umene anautcha New Harmony. Ali wokhutira maganizo kuti pansi pa mikhalidwe yoyenera, anthu angawongokere, iye anagwiritsira ntchito pafupifupi chuma chake chonse kuyesayesa kukhazikitsa limene analilingalira kukhala dziko latsopano lamakhalidwe abwino. Koma zotulukapo zinasonyeza kuti mikhalidwe yatsopano siili yokwanira kupanga anthu atsopano.
Pafupifupi ziphunzitso zonse zandale zimanenetsa kuti munthu ayenera kulinganiza dziko malinga ndi chidziŵitso chake ndi zimene iye mwini amaganiza kukhala zowona kuti abweretse paradaiso wofunidwayo padziko lapansi. Komabe, mosiyana, zoyesayesa za kukwaniritsa zilakolako zoterozo zachititsa nkhondo ndi zipanduko, monga ngati chipanduko cha French Revolution mu 1789 ndi Bolshevik Revolution mu 1917. Mmalo mobweretsa mikhalidwe ya paradaiso, kaŵirikaŵiri zoyesayesa zimenezi zinatsogolera ku zopweteka ndi kuvutika kowonjezereka.
Zilakolako, zolinganiza, ma Utopia, ndi zoyesayesa za kuzikwaniritsa—zangokhala nkhani yokhumudwitsa mobwerezabwereza. Pakali panopo, ena akulankhula za “loto losakwaniritsidwa” ndi “kutha kwa nyengo ya ma utopia,” kutiitana kuphunzira “kukhala popanda maloto a ma utopia.” Kodi pali chiyembekezo chilichonse cha kuona dziko labwinopo, kapena kodi lidzakhalabe loto chabe?
Akristu ndi Dziko Labwinopo
Dziko latsopano siliri loto chabe—ndichiyembekezo chotsimikizirika! Yesu Kristu, Woyambitsa wa Chikristu, anadziŵa kuti dziko lilipoli silili labwino koposa. Iye anaphunzitsa kuti dziko lapansi lidzakhalidwa ndi anthu odzichepetsa ndi kuti chifuniro cha Mulungu chidzachitika pansi pano. (Mateyu 5:5; 6:9, 10) Iye ndi ophunzira ake omwe anadziŵa kuti dzikoli likulamuliridwa ndi mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, ndi kuti ndiye wochititsa wamkulu wa mavuto ambiri a anthu. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:12) Ayuda okhulupirika anayembekezera tsiku limene Mulungu akachotsera dziko lapansi nkhondo, kupweteka, ndi matenda kotero kuti likhalidwe ndi anthu okonda mtendere ndi chilungamo. Mwa njira yofananayo, Akristu a m’zaka za zana loyamba anayembekezera mwachidaliro kuti dziko lilipoli likaloŵedwa mmalo ndi dongosolo latsopano la zinthu, “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”—2 Petro 3:13; Salmo 37:11; 46:8, 9; Yesaya 25:8; 33:24; 45:18; Chivumbulutso 21:1.
Pamene Yesu Kristu anali wolenjekeka pamtengo wozunzirapo, anabwereza lonjezo la dziko labwinopo kwa wochita zoipa amene anasonyeza mlingo wakutiwakuti wa chikhulupiriro mwa Iye. “[Yesu] ananena naye: ‘Ndithudi ndikukuuza lerolino, Udzakhala nane m’Paradaiso.’” (Luka 23:40-43, NW) Kodi wochita zoipayo anamva mawuwo kukhala akutanthauza chiyani? Kodi Yesu anapereka lingaliro lakuti wochita zoipayo akakhala ‘naye’ kumwamba patsiku lomwelo, monga momwe matembenuzidwe a Baibulo ena a Chikatolika ndi Chiprotesitanti amasonyezera? Ayi, zimenezo sizimene Yesu anatanthauza, popeza kuti pambuyo pa kuuka kwake, Yesu anauza Mariya wa Magadala kuti Iye ‘anali asanakwere kwa Atate.’ (Yohane 20:11-18) Ngakhale kuti anaphunzitsidwa ndi Yesu kwa zaka zitatu ndi theka, asanafike Pentekoste wa 33 C.E. ngakhale atumwi ake sanalingalire za paradaiso wakumwamba. (Machitidwe 1:6-11) Wochita zoipayo anamva zimene unyinji waukulu wa Ayuda okhala panthaŵiyo anamva: Yesu anali kulonjeza dziko labwinopo lomwe lidzabwera padziko lapansi la paradaiso. Katswiri wina wa ku Germany anavomereza kuti: “Chiphunzitso cha kubwezera chilango m’moyo wapambuyo pa imfa sichimapezeka konse m’Chipangano Chakale.”
Mfundo yakuti padzakhala paradaiso padziko lathu lapansi yatsimikiziridwa ndi mtumwi Paulo m’kalata yake kwa Ahebri. Polimbikitsa okhulupirira anzake kuti ‘asamale chipulumutso chachikulu chotero chimene chinayamba kulankhulidwa kudzera mwa Yesu Kristu,’ Paulo akutsimikizira kuti Yehova Mulungu anapatsa Yesu ulamuliro pa “dziko [Chigiriki, oi·kou·meʹne] lilinkudza.” (Ahebri 2:3, 5) M’Malemba Achigiriki Achikristu, liwu lakuti oi·kou·meʹne nthaŵi zonse limanena za dziko lathu lapansi lokhalidwa ndi anthu, osati dziko lakumwamba. (Yerekezerani ndi Mateyu 24:14; Luka 2:1; 21:26; Machitidwe 17:31.) Chotero Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Kristu Yesu udzalamulira dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Amenewo adzakhaladi malo abwino koposa kukhalamo!
Ngakhale kuti Ufumu weniweniwo uli wakumwamba, udzaloŵererabe m’zochitika zapadziko lapansi. Ndi zotulukapo zotani? Matenda, nkhalwe, umphaŵi, ndi imfa zidzaiŵalika. Ngakhale kugwiritsidwa mwala ndi kusakhutira zidzatha. (Chivumbulutso 21:3-5) Baibulo limanena kuti ‘Mulungu adzaoloŵetsa dzanja lake, nadzakwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’ (Salmo 145:16) Mavuto onga ngati ulova ndi kuipitsa adzakhala ndi mankhwala ogwira ntchito ndi okhalitsa. (Yesaya 65:21-23; Chivumbulutso 11:18) Koma koposa zonse, chifukwa cha dalitso la Mulungu, chowonadi, chilungamo, ndi mtendere zidzafunga—mikhalidwe imene ikuonekera kukhala itatheratu!—Salmo 85:7-13; Agalatiya 5:22, 23.
Kodi zonsezi ndi loto, Utopia? Ayi, nthaŵi yowawitsa kwambiri imene tikukhalamo imasonyeza kuti tili mu “masiku otsiriza” a dzikoli ndi kuti dziko latsopano lili pafupi. (2 Timoteo 3:1-5) Kodi mungakonde kukhalamo? Phunzirani mmene zingathekere mwakuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Dziko labwinopo lili pafupi, labwino koposa limene timalingalira. Siliri Utopia—ndilenileni!
[Chithunzi patsamba 7]
Dziko labwinopo—lidzakhala lenileni posachedwapa