Achimwemwe Tsopano ndi Kosatha
“Kalani inu okondwa ndi Kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.”—YESAYA 65:18.
1. Kodi kulambira koona kwakhudza motani anthu pazaka mazana ambiri?
M’ZAKA mazana ambirimbiri, makamu osaŵerengeka apeza chimwemwe chochuluka potumikira Mulungu woona, Yehova. Davide anali mmodzi wa awo amene anali achimwemwe m’kulambira koona. Baibulo limasimba kuti pamene likasa la chipangano linabweretsedwa ku Yerusalemu, “Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe.” (2 Samueli 6:15) Chimwemwe chotero potumikira Yehova sichili chabe chinthu chakale ayi. Mungakhale nacho. Ndipo mungapeze chimwemwe chatsopano!
2. Kuwonjezera pa kukwaniritsidwa koyamba kwa Yesaya chaputala 35 pa Ayuda obwerera, kodi ndani lerolino amene akuphatikizidwa m’kukwaniritsidwa kwina?
2 M’nkhani yoyamba, tinapenda kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wosangalatsa wolembedwa mu Yesaya chaputala 35. Pachifukwa chabwino tingatche umenewu ulosi wa kubwezeretsedwa chifukwa chakuti ndi mmene unakwaniritsidwira kwa Ayuda akalewo. Uwo ukukwaniritsidwa mofananamo m’nthaŵi yathu. Motani? Aha, kuyambira kwa atumwi a Yesu ndi ena pa Pentekoste wa 33 C.E., Yehova wakhala akuchita zinthu ndi Aisrayeli auzimu. Ameneŵa ndi anthu odzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu amene amakhala mbali ya amene mtumwi Paulo amatcha “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Aroma 8:15-17) Kumbukiraninso kuti pa 1 Petro 2:9, Akristu ameneŵa akutchedwa “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.” Petro akupitiriza kutchula ntchito yopatsidwa kwa Israyeli wauzimu: “Kuti mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.”
Kukwaniritsidwa Kwake m’Nthaŵi Yathu
3, 4. Kodi mkhalidwe unali wotani pamene Yesaya chaputala 34 anakwaniritsidwa m’nthaŵi yamakono?
3 Panali nthaŵi ina kuchiyambi cha zaka za zana lino pamene otsalira a Israyeli wauzimu padziko lapansi sanapitirize kukhala okangalika polengeza uthenga umenewo. Sanali kukondwa mokwanira ndi kuunika kodabwitsako kwa Mulungu. Kwenikweni, anali mumdima waukulu. Kodi zimenezo zinachitika liti? Ndipo kodi Yehova Mulungu anachitapo chiyani?
4 Zinachitika m’nyengo ya Nkhondo Yadziko I, Ufumu wa Mulungu waumesiya utangokhazikitsidwa kumene kumwamba mu 1914. Amitundu, pochirikizidwa ndi atsogoleri achipembedzo a matchalitchi a m’maiko osiyanasiyana, anakwiyirana. (Chivumbulutso 11:17, 18) Ndithudi, Mulungu anatsutsiratu Dziko Lachikristu limodzi ndi kagulu ka atsogoleri ake achipembedzo odzikweza kameneko monga momwe anachitira ndi mtundu wa Edomu wodzikuzawo. Chifukwa chake, Dziko Lachikristu, Edomu wophiphiritsira, akuyembekezera kukumana ndi kukwaniritsidwa kwamasiku ano kwa Yesaya chaputala 34. Kukwaniritsidwa kumeneku kochitika mwa chiwonongeko chachikhalire nkotsimikizirika monga momwedi kunalili kukwaniritsidwa kwake koyamba pa Edomu wakale.—Chivumbulutso 18:4-8, 19-21.
5. Kodi ndi kukwaniritsidwa kotani kumene Yesaya chaputala 35 wakhala nako m’nthaŵi yathu?
5 Bwanji nanga za chaputala 35 cha ulosi wa Yesaya, ndi kugogomezera kwake chimwemwe? Nachonso chakwaniritsidwa m’nthaŵi yathu. Motani? Chakwaniritsidwa mwa kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu kuchoka mu ukapolo winawake. Tiyeni tipende maumboni mu imene kwenikweni ili mbiri yamakono yateokrase, imene yachitika m’moyo wa ambiri amene akali amoyo.
6. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti otsalira a Israyeli wauzimu analoŵa mu mkhalidwe waukapolo?
6 Kwa nthaŵi yaifupi mkati mwa nyengo ya Nkhondo Yadziko I, otsalira a Israyeli wauzimu sanadzisunge ali oyera kotheratu ndiponso sanali ogwirizana kwambiri ndi chifuniro cha Mulungu. Ena a iwo anachitidwa maŵanga ndi ziphunzitso zolakwa ndipo anagonja mwa kusaima kwenikweni kumbali ya Yehova pamene anakakamizidwa kuchirikiza mitundu yomenya nkhondoyo. M’zaka za nkhondozo, anakumana ndi zizunzo za mtundu uliwonse, mabuku awo ofotokoza Baibulo akumaletsedwa m’malo ambiri. Potsiriza, abale ena odziŵika kwambiri anaimbidwa mlandu naponyedwa m’ndende pazifukwa zonama. Poona zimene zinachitika kumbuyoku sikovuta kuona kuti, m’lingaliro lina, anthu a Mulungu, m’malo mokhala omasuka, anali mumkhalidwe waukapolo. (Yerekezerani ndi Yohane 8:31, 32.) Iwo analibiretu maso auzimu. (Aefeso 1:16-18) Anali osakhoza kulankhula kwambiri kutamanda Mulungu, choncho anakhala osabala zipatso mwauzimu. (Yesaya 32:3, 4; Aroma 14:11; Afilipi 2:11) Kodi mukuona mmene zimenezi zikufananirana ndi mkhalidwe wa Ayuda akale okhala mu ukapolo ku Babulo?
7, 8. Kodi ndi kubwezeretsedwa kotani kumene otsalira amakono anaona?
7 Koma kodi Mulungu anasiya atumiki ake amakono mumkhalidwe umenewo? Ayi, iye anali wotsimikiza kuwabwezeretsa, monga momwe Yesaya ananeneratu. Chifukwa chake ulosi umodzimodziwo wa m’chaputala 35 ukukwaniritsidwa mwapadera m’nthaŵi yathu, mwa kubwezeretsedwa kwa otsalira a Israyeli wauzimu kukhalanso olemera ndi athanzi m’paradaiso wauzimu. Pa Ahebri 12:12, Paulo anamasulira Yesaya 35:3 mophiphiritsira, akumachirikiza kumasulira kwathu kwauzimu chigawo chimenechi cha ulosi wa Yesaya.
8 M’nyengo ya pambuyo pa nkhondo, otsalira odzozedwa a Israyeli wauzimu anatuluka mu ukapolo, titero kunena kwake. Yehova Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu Kristu, Koresi Wamkulu, kuwamasula. Chotero, otsalirawo anali okhoza kuchita ntchito yomanganso, yofanana ndi ntchito ya otsalira akale a Ayuda, amene anabwerera kudziko lawo kukamanganso kachisi weniweni ku Yerusalemu. Ndiponso, Aisrayeli auzimu ameneŵa m’nthaŵi yamakono anakhoza kuyamba kulima ndi kupanga paradaiso wauzimu wokongola mochititsa kaso, munda wa Edene wophiphiritsira.
9. Kodi zinthu zonga zija zofotokozedwa pa Yesaya 35:1, 2, 5-7 zinachitika motani m’nthaŵi yathu?
9 Polingalira zimenezo, tiyeni tipendenso Yesaya chaputala 35, choyamba tikumayang’ana mavesi 1 ndi 2. Malo amene anaoneka ngati ouma anayambadi kuphukira zomera ndi kukhala obala ngati madambo akale a Saroni. Ndiyeno, taonani mavesi 5 mpaka 7. Otsalirawo, amene oŵerengeka okha akali ndi moyo ndi okangalika mu utumiki wa Yehova, maso awo a mtima anatsegulidwa. Iwo anakhoza kuona bwino tanthauzo la zimene zinachitika mu 1914 ndi pambuyo pake. Ndipo zimenezo zitikhudza ambirife amene tili a “khamu lalikulu,” otumikira tsopano limodzi ndi otsalirawo.—Chivumbulutso 7:9.
Kodi Muli Mbali ya Kukwaniritsidwako?
10, 11. (a) Kodi mwaphatikizidwa motani m’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 35:5-7? (b) Kodi inu panokha mukumva motani pa masinthidwe ameneŵa?
10 Mwachitsanzo, tiyeni tinene za inu mwini. Musanayambe kuyanjana ndi Mboni za Yehova, kodi munali kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse? Ngati munali kutero, kodi munadziŵa zinthu zochuluka motani? Mwachitsanzo, tsopano mukudziŵa choonadi chonena za mkhalidwe wa akufa. Mwachionekere mukhoza kusonyeza wina wofuna kudziŵa za nkhaniyo mavesi oyenera mu Genesis chaputala 2, Mlaliki chaputala 9, ndi Ezekieli chaputala 18, ndi mavesi enanso ambiri. Inde, inu mwachionekere mumamvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani zambiri. Kunena mwachidule, Baibulo nlomveka kwa inu, ndipo mungafotokoze zambiri kwa ena ponena za ilo, monga momwedi mwakhala mukuchitira.
11 Komabe, ife aliyense payekha tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zonse zimene ndidziŵa ponena za choonadi cha Baibulo ndinaziphunzira motani? Ndisanayambe kuphunzira ndi anthu a Yehova, kodi ndinali wokhoza kupeza mavesi onse amene angotchulidwa kumenewo? Kodi ndinawamvetsa ndi kudziŵa bwino tanthauzo lake?’ Mwinamwake yankho loona mtima pamafunso ameneŵa nlakuti ayi. Chonde musakhumudwe ndi mawu awa, koma tikhoza kunena kuti inu kwenikweni munali akhungu pamavesi ameneŵa ndi tanthauzo lake. Sichoncho nanga? Iwo analimo m’Baibulo, koma inu simunali kuwaona kapena kuzindikira tanthauzo lake. Nanga kodi maso anu anatsegulidwa motani mwauzimu? Mwa zimene Yehova wachita pokwaniritsa Yesaya 35:5 pa otsalira odzozedwa. Ndiyeno, maso anu anatsegulidwa. Simulinso mumdima wauzimu. Mutha kuona.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:17, 18.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti ino si nthaŵi ya machiritso ozizwitsa akuthupi? (b) Kodi chitsanzo cha Mbale F. W. Franz chinasonyeza motani mmene Yesaya 35:5 akukwaniritsidwira m’nthaŵi yathu?
12 Ophunzira akhama a Baibulo ndi zochita za Mulungu pazaka mazana ambiri akudziŵa kuti ino si nyengo ya machiritso ozizwitsa akuthupi m’mbiri. (1 Akorinto 13:8-10) Chotero sitimayembekezera kuti Yesu Kristu adzatsegula maso akhungu kuti atsimikizire kuti ndiye Mesiya, Mneneri wa Mulungu. (Yohane 9:1-7, 30-33) Ndiponso sakuchititsa onse ogontha kumvanso. Pamene Frederick W. Franz, mmodzi wa odzozedwa ndi pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, anayandikira zaka zake za 100, anali pafupi kufa maso ndipo anali kugwiritsira ntchito chipangizo chothandizira kumva. Kwa zaka zingapo sanali kuona moti nkuŵerenga; komabe, kodi ndani amene akanaganiza kuti iye anali wakhungu kapena wogontha m’lingaliro la Yesaya 35:5? Maso ake akuthwa auzimu anali dalitso kwa anthu a Mulungu padziko lonse lapansi.
13. Kodi ndi kusintha kotani kapena kubwezeretsedwa kumene anthu amakono a Mulungu anaona?
13 Bwanji nanga za lilime lanu? Odzozedwa a Mulungu angakhale anali osalankhula pamene anali mu ukapolo wawo wauzimu. Koma pamene Mulungu anasintha mkhalidwewo, malilime awo anayamba kuimba mosangalala pa zimene anadziŵa ponena za Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa ndi malonjezo ake amtsogolo. Iwo angakhale atakuthandizani inunso kumasula lilime lanu. Kodi munalankhula kangati kwa ena za choonadi cha Baibulo kumbuyoku? Mwinamwake nthaŵi ina munaganiza kuti, ‘Ndimakonda kuphunzira, koma sindingapite konse kukalankhula ndi anthu osawadziŵa.’ Koma kodi si zoona kuti ‘lilime la wosalankhula likuimba’ tsopano?—Yesaya 35:6.
14, 15. Kodi ambiri ayenda motani pa “Njira Yopatulika” m’nthaŵi yathu?
14 Ayuda akale amene anamasulidwa ku Babulo anali ndi ulendo wautali kubwerera kudziko lawo. Kodi zimenezo zikufanana ndi chiyani m’nthaŵi yathu? Eya, tayang’anani pa Yesaya 35:8: “Kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa [N]jira [Y]opatulika; audyo sadzapita mmenemo.”
15 Chiyambire kumasulidwa kwawo mu ukapolo wauzimu, otsalira a odzozedwa, amene tsopano akutsagana ndi mamiliyoni a nkhosa zina, atuluka m’Babulo Wamkulu pakhwalala lophiphiritsira, njira yoyera yopatulika yopita ku paradaiso wauzimu. Tikuchita zonse zomwe tingathe kuti tiyenerere Njira Yopatulikayo ndi kukhalabe mmenemo. Talingalirani za inu mwini. Kodi miyezo yanu ya makhalidwe ndi mapulinsipulo amene mumatsatira sizili zapamwamba kwambiri tsopano kuposa pamene munali kudziko? Kodi simumayesayesa zolimba kugwirizanitsa kulingalira kwanu ndiponso khalidwe lanu ndi Mulungu?—Aroma 8:12, 13; Aefeso 4:22-24.
16. Kodi timasangalala ndi mikhalidwe yotani pamene tiyenda pa Njira Yopatulika?
16 Pamene mupitiriza kuyenda m’Njira Yopatulika imeneyi, inu kwenikweni simumada nkhaŵa ndi anthu onga zilombo. Zoona, kudziko muyenera kukhala watcheru kuti anthu aumbombo kapena oipa asakudyeni wamoyo mophiphiritsira. Anthu ambirimbiri amachita ndi ena molusa. Anthu a Mulungu ali osiyana ndi amenewo chotani nanga! Inde, inu muli m’malo otetezereka. Zoonadi, Akristu anzanu sali angwiro; nthaŵi zina wina amalakwa kapena kutikhumudwitsa. Koma mukudziŵa kuti abale anu sakuyesa kukuvulazani dala kapena kukulikwirani. (Salmo 57:4; Ezekieli 22:25; Luka 20:45-47; Machitidwe 20:29; 2 Akorinto 11:19, 20; Agalatiya 5:15) M’malo mwake, iwo amakukondani; akuthandizani; afuna kutumikira nanu.
17, 18. Kodi paradaiso tsopano alipo m’lingaliro lotani, ndipo zimenezi zimatikhudza motani?
17 Chotero, tingapende Yesaya chaputala 35, tikumaganiza za kukwaniritsidwa kwamakono kwa mavesi 1 mpaka 8. Kodi sikoonekeratu kuti tapeza kale chimene moyenera chikutchedwa paradaiso wauzimu? Sali wangwiro ayi—osati pakali pano. Koma alidi paradaiso, pakuti mmenemu tayamba kale ‘kuona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu,’ malinga ndi zimene vesi 2 likunena. Ndipo zotulukapo zake nzotani? Vesi 10 limati: “Oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pamitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.” Inde, kutuluka kwathu m’chipembedzo chonyenga ndi kulondola kwathu kulambira koona m’chiyanjo cha Mulungu kumatipatsa chimwemwe.
18 Chimwemwe chogwirizana ndi kulambira koona chimangowonjezereka, sichoncho nanga? Mumaona achatsopano akupanga masinthidwe nakhazikika m’choonadi cha Baibulo. Mumaona achichepere akukula mumpingo ndi kupita patsogolo mwauzimu. Pali maubatizo, pamene mumaona anthu amene mumadziŵa akubatizidwa. Kodi zimenezo si zifukwa zokhalira achimwemwe, chimwemwe chochulukadi lerolino? Inde, tili ndi chimwemwe chachikulu pokhala ndi ena amene akugwirizana nafe mu ufulu wathu wauzimu ndi m’mikhalidwe yaparadaiso!
Kukwaniritsidwa Kumene Kukali Mtsogolo!
19. Kodi Yesaya chaputala 35 akutipatsa chiyembekezo chabwino chotani?
19 Kufikira pano zimene takambitsirana pa Yesaya chaputala 35 zimakhudza kukwaniritsidwa kwake koyamba konena za kubwerera kwa Ayuda ndiponso kukwaniritsidwa kwake kwauzimu komwe kukuchitika lerolino. Koma si zokhazo ayi. Pali zina zambiri. Zikukhudza lonjezo la Baibulo la kubwezeretsedwa kulinkudzako kwa mikhalidwe yakuthupi yaparadaiso padziko lapansi.—Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:4, 5.
20, 21. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera ndiponso kwa Malemba kukhulupirira kuti kudzakhalanso kukwaniritsidwa kwina kwa Yesaya chaputala 35?
20 Sikungakhale koyenera kwa Yehova kupereka mafotokozedwe ochititsa chidwi a paradaiso komano nkulola kuti akwaniritsidwe mwauzimu chabe. Ndithudi, sitikunena kuti kukwaniritsidwa kwauzimuko nkosafunika. Ngakhale ngati paradaiso wakuthupi angakhazikitsidwe, ife sitingakhutire naye ngati pakati pa malo okongolawo ndi nyama zamtendere tazingidwa ndi anthu oipa mwauzimu, anthu ochita ngati zilombo zolusa. (Yerekezerani ndi Tito 1:12.) Inde, paradaiso wauzimu ayenera kuyambirira, pakuti ndiye wofunika koposa.
21 Komano, Paradaiso amene akudzayo sadzangokhala chabe wa zinthu zauzimu zimene tikusangalala nazo tsopano ndi zambiri zimene tidzasangalala nazo mtsogolo. Tili ndi chifukwa chabwino choyembekezera kukwaniritsidwa kwake kwakuthupi kwa maulosi onga Yesaya chaputala 35. Chifukwa ninji? Eya, m’Yesaya chaputala 65, Yesaya ananeneratu za “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Mtumwi Petro anagwira mawu lembalo pofotokoza zimene zidzatsatira tsiku la Yehova. (Yesaya 65:17, 18; 2 Petro 3:10-13) Petro anali kusonyeza kuti mbali zimene Yesaya anafotokoza zidzakhalakodi pamene “dziko lapansi latsopano” lidzakhalako. Zimenezo zikuphatikizapo mafotokozedwe amene mukudziŵa—kumanga nyumba ndi kukhalamo; kuoka minda yamphesa ndi kudya zipatso zake; kusangalala kwa nthaŵi yaitali ndi ntchito ya manja athu; mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzakhala pamodzi; ndipo dziko lonse lapansi silidzasakazidwa. M’mawu ena, moyo wautali, nyumba zosungika, chakudya chochuluka, ntchito yokhutiritsa, ndi mtendere pakati pa nyama zokhazokha ndi pakati pa nyama ndi anthu.
22, 23. Kodi nchifukwa chotani chokhalira achimwemwe chimene chidzakhalako pakukwaniritsidwa kwa mtsogolo kwa Yesaya chaputala 35?
22 Kodi chiyembekezo chimenecho sichimakudzazani ndi chimwemwe? Chiyeneradi kutero, popeza Mulungu anatilenga kuti tikhale motero. (Genesis 2:7-9) Chotero, kodi ulosi wa pa Yesaya chaputala 35 umene tikupendawu umatanthauzanji? Umatanthauza kuti tili ndi chifukwa china chofuulira ndi chimwemwe. Zipululu zenizeni ndi malo ouma zidzaphuka, zikumatikondweretsa. Ndiyeno anthu amaso abluu kapena ofiirira, kapena amaonekedwe ena abwino, koma amene tsopano ali akhungu, adzapenyanso. Akristu anzathu amene ali ogontha, ngakhale ife amene timavutika kumva, tidzamva bwinobwino. Kudzakhala kosangalatsa chotani nanga kugwiritsira ntchito mphamvu zimenezo kumvetsera Mawu a Mulungu akuŵerengedwa ndi kumasuliridwa, limodzinso ndi kumvetsera kulira kwa mphepo m’mitengo, kumva mwana akuseka, kumva nyimbo za mbalame!
23 Kudzatanthauzanso kuti opunduka, kuphatikizapo aja odwala kusweka malungo tsopano lino, adzayendayenda osamva kuŵaŵa. Udzakhala mpumulo wotani nanga! Ndiyeno mitsinje idzatumphuka m’zipululu. Tidzaona madzi akuŵinduka ndi kumva nthubwinthubwi yake. Tidzakhoza kupita kumeneko ndi kugwira udzu wobiriŵira ndi milulu. Adzakhaladi Paradaiso wobwezeretsedwa. Nanga bwanji za chimwemwe cha kukhala pafupi ndi mkango kapena nyama ina yofanana nawo popanda mantha? Sitifunikira kuyamba nkomwe kufotokoza zimenezo, pakuti ife tonse mokondwa talingalirapo kale za mkhalidwewo.
24. Kodi nchifukwa ninji mukuvomereza mawu a Yesaya 35:10?
24 Yesaya akutilonjeza kuti: “Oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pamitu yawo.” Chotero, tikuvomerezadi kuti tili ndi chifukwa chofuulira ndi chimwemwe. Chimwemwe pa zimene Yehova wayamba kale kuchitira anthu ake m’paradaiso wathu wauzimu, ndi chimwemwe pa zimene tikuyembekezera m’Paradaiso wakuthupi yemwe ali pafupi kwambiri. Ponena za anthu achimwemwe—ponena za ife—Yesaya akulemba kuti: “Iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”—Yesaya 35:10.
Kodi Mwazindikira?
◻ Kodi ndi kukwaniritsidwa kwachiŵiri kuti kumene Yesaya chaputala 35 wakhala nako?
◻ Kodi nchiyani chimene chimafanana mwauzimu ndi masinthidwe ozizwitsa amene Yesaya analosera?
◻ Kodi mwatengamo mbali motani m’kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yesaya chaputala 35 amatipatsa chiyembekezo cha mtsogolo?
[Chithunzi patsamba 15]
Ndende ya mu Raymond Street ku Brooklyn, New York kumene abale asanu ndi aŵiri odziŵika anatsekeredwa mu June 1918
[Chithunzi patsamba 16]
Ngakhale kuti Mbale Franz anali pafupi kufa maso pazaka zake zaukalamba, maso ake auzimu anali akuthwa
[Zithunzi patsamba 17]
Kukula kwauzimu ndi kupita patsogolo ndiko zifukwa zokhalira achimwemwe