2 Samueli
6 Davide anasonkhanitsanso asilikali amphamvu mu Isiraeli, okwana 30,000. 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka nʼkupita ku Baale-yuda kuti akatenge Likasa la Mulungu woona.+ Pa likasa limeneli anthu amaitanirapo dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ 3 Koma iwo ananyamulira Likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo, ana aamuna a Abinadabu, ndi amene ankatsogolera ngolo yatsopanoyo.
4 Choncho ananyamula Likasa la Mulungu woona kuchokera kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri ndipo Ahiyo ankayenda patsogolo pa Likasa. 5 Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankasangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Ankaimbanso zeze, zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana. 6 Koma atafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, Uza anagwira Likasa la Mulungu woona,+ chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa. 7 Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo Mulungu woona anamuphera+ pomwepo chifukwa chochita zinthu mopanda ulemu.+ Moti Uza anafera pompo, pafupi ndi Likasa la Mulungu woona. 8 Koma Davide anakwiya* chifukwa Yehova anakwiyira kwambiri Uza. Malo amenewa amadziwika ndi dzina lakuti Perezi-uza* mpaka lero. 9 Choncho Davide anachita mantha kwambiri ndi Yehova+ tsiku limenelo, ndipo anati: “Kodi Likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10 Davide sanafunenso kutenga Likasa la Yehova kupita nalo kumene ankakhala, ku Mzinda wa Davide.+ Mʼmalomwake Davide analamula kuti lipite kunyumba ya Obedi-edomu+ wa ku Gati.*
11 Likasa la Yehova linakhala kunyumba ya Obedi-edomu wa ku Gati kwa miyezi itatu, ndipo Yehova ankadalitsa Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+ 12 Mfumu Davide inauzidwa kuti: “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-edomu ndi zinthu zake zonse chifukwa cha Likasa la Mulungu woona.” Choncho Davide anapita kukatenga Likasa la Mulungu woona kunyumba kwa Obedi-edomu nʼkupita nalo ku Mzinda wa Davide, akusangalala.+ 13 Anthu amene ananyamula+ Likasa la Yehova atangoyenda mapazi 6, Davide anapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi chiweto chonenepa.
14 Davide ankavina mozungulira pamaso pa Yehova ndi mphamvu zake zonse. Apa nʼkuti atavala efodi wansalu.+ 15 Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankayenda ndi Likasa+ la Yehova akufuula mokondwera+ ndiponso akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 16 Likasa la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ anasuzumira pawindo ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha nʼkumavina mozungulira pamaso pa Yehova. Ndipo Mikala anayamba kumunyoza mumtima mwake.+ 17 Kenako anaika Likasa la Yehova pamalo ake mutenti imene Davide anamanga.+ Ndiyeno Davide anapereka kwa Yehova+ nsembe zopsereza+ ndi nsembe zamgwirizano.+ 18 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano, anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 19 Komanso anapatsa anthu onse mikate yozungulira yoboola pakati, makeke a zipatso za kanjedza ndi makeke a mphesa. Anapereka zimenezi ku gulu lonse la Isiraeli, mwamuna ndiponso mkazi. Kenako aliyense anapita kunyumba kwake.
20 Davide atabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ anatuluka kukakumana naye. Mikala anati: “Lero mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake podzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, ngati mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi.”+ 21 Davide anauza Mikala kuti: “Inetu pamene paja ndimasangalala pamaso pa Yehova amene anandisankha mʼmalo mwa bambo ako ndi banja lawo lonse kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, Aisiraeli.+ Choncho ndidzasangalala pamaso pa Yehova. 22 Ndipitiriza kudzichepetsa kuposa pamenepa ndipo ndipitiriza kudziona ngati wotsika. Koma akapolo aakazi amene ukunenawo azindilemekeza.” 23 Choncho Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ sanakhalepo ndi mwana mpaka tsiku limene anafa.