Chikondi Chimagonjetsa Nsanje Yoipa
“Chikondi chilibe nsanje.”—1 AKORINTO 13:4, NW.
1, 2. (a) Kodi Yesu anauzanji ophunzira ake ponena za chikondi? (b) Kodi nkotheka kukhala wachikondi ndi wansanje panthaŵi imodzimodzi, ndipo nchifukwa ninji mwayankha motero?
CHIKONDI ndicho chizindikiro chodziŵira Chikristu choona. Yesu Kristu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Mtumwi Paulo anauziridwa kulongosola mmene chikondi chiyenera kuyambukirira maunansi a Akristu. Pakati pa zinthu zina, analemba kuti: “Chikondi chilibe nsanje.”—1 Akorinto 13:4.
2 Pamene Paulo analemba mawu amenewo, anali kunena za nsanje yoipa. Chifukwa sakanauza mpingo umodzimodziwo kuti: “Ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu.” (2 Akorinto 11:2) “Nsanje ya Mulungu” yakeyo inauka chifukwa cha amuna amene anali oipitsa mpingo. Chimenechi chinasonkhezera Paulo kulembera Akristu a ku Korinto kalata youziridwa yachiŵiri yodzala ndi uphungu wachikondi.—2 Akorinto 11:3-5.
Nsanje Pakati pa Akristu
3. Kodi vuto la nsanje linakula motani pakati pa Akristu a ku Korinto?
3 M’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, Paulo anawathandiza za vuto lina limene linali kulepheretsa Akristu atsopano ameneŵa kumvana pakati pawo. Iwo anali kukweza amuna ena, ‘akumadzitukumulira mnzake ndi kukana wina.’ Zimenezi zinachititsa magaŵano mkati mwa mpingo, pamene osiyanasiyana anali kumati: “Ine ndine wa Paulo,” “Koma ine wa Apolo,” “Koma ine wa Kefa.” (1 Akorinto 1:12; 4:6) Mwa chitsogozo cha mzimu woyera, mtumwi Paulo anakhoza kufika pamuzu penipeni pa vutolo. Akorintowo anali kuchita monga anthu amaganizo akuthupi, osati monga “auzimu.” Chifukwa chake, Paulo analemba kuti: “Mulinso athupi; pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndewu pakati pa inu simuli a thupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?”—1 Akorinto 3:1-3.
4. Kodi Paulo anagwiritsira ntchito fanizo lotani pothandiza abale ake kukhala ndi kaonedwe kabwino ka wina ndi mnzake, ndipo kodi tingatengepo phunziro lanji?
4 Paulo anathandiza Akorinto kukhala ndi kaonedwe koyenera ka mphatso ndi maluso a anthu osiyanasiyana mumpingo. Iye anafunsa kuti: “Akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” (1 Akorinto 4:7) Mu 1 Akorinto chaputala 12, Paulo analongosola kuti aja amene anali mbali ya mpingowo anali monga ziŵalo zosiyanasiyana za thupi la munthu, monga dzanja, diso, ndi khutu. Iye anasonyeza kuti Mulungu anapanga ziŵalo zosiyanasiyana za thupi mwa njira yakuti zisamalirane china ndi chinzake. Paulo analembanso kuti: “Chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziŵalo zonse zikondwera nacho pamodzi.” (1 Akorinto 12:26) Atumiki a Mulungu onse lerolino ayenera kugwiritsira ntchito chilangizo chimenechi kwa wina ndi mnzake. M’malo mochitira nsanje munthu wina chifukwa cha thayo lake kapena zipambano zake mu utumiki wa Mulungu, tiyenera kukondwera limodzi naye.
5. Kodi nchiyani chimene chavumbulidwa pa Yakobo 4:5, ndipo kodi Malemba amasonyeza motani choonadi cha mawu ameneŵa?
5 Kunena zoona, zimenezi nzofeŵa kunena kuposa kuchita. Mlembi wa Baibulo Yakobo akutikumbutsa kuti “nsanje” ikhala mwa munthu wochimwa aliyense. (Yakobo 4:5) Imfa yoyamba ya munthu inachitika chifukwa chakuti Kaini anagonja ku nsanje yoipa imeneyi. Afilisti anazunza Isake chifukwa chakuti anachitira nsanje kuchuluka kwa chuma chake. Rakele anachitira nsanje kubala ana kwa mbale wake. Ana aamuna a Yakobo anachitira nsanje chikondi chosonyezedwa kwa mphwawo Yosefe. Miriamu mwachionekere anachitira nsanje mlamu wake wosakhala Mwisrayeli. Kora, Datani, ndi Abiramu mwanjiru anachitira chiŵembu Mose ndi Aroni. Mfumu Sauli inachitira nsanje chipambano cha Davide m’nkhondo. Mosakayika, nsanje ndiyonso inachititsa ophunzira a Yesu kumakangana ponena za amene anali wamkulu pakati pawo. Choona nchakuti, palibe munthu wopanda ungwiro amene alibiretu mkhalidwe woipa umenewu wa “nsanje.”—Genesis 4:4-8; 26:14; 30:1; 37:11; Numeri 12:1, 2; 16:1-3; Salmo 106:16; 1 Samueli 18:7-9; Mateyu 20:21, 24; Marko 9:33, 34; Luka 22:24.
Mumpingo
6. Kodi ndimotani mmene akulu angalamulirire nsanje?
6 Akristu onse ayenera kupeŵa kaduka ndi nsanje yoipa. Zimenezi zimaphatikizapo mabungwe a akulu oikidwa kusamalira mipingo ya anthu a Mulungu. Ngati mkulu ali wofatsa, sadzayesa kuchita zinthu moonetsera kuti amaposa ena. Ndiponso, ngati mkulu wina ali ndi maluso apadera monga wodziŵa kulinganiza zinthu kapena mlankhuli wapoyera waluso, enawo ayenera kukondwera naye, akumamuona kukhala dalitso pampingo. (Aroma 12:15, 16) Mbale wina angakhale akupita patsogolo bwino, akumaonetsa umboni wa kubala zipatso za mzimu wa Mulungu m’moyo wake. Pokambitsirana za ziyeneretso zake, akulu ayenera kusamala kuti asakulitse zophophonya zazing’ono kuti alungamitse kusavomerezedwa kwake kukhala mtumiki wotumikira kapena mkulu. Kuchita motero kudzasonyeza mzimu wopanda chikondi ndi wosalolera.
7. Kodi ndi vuto lanji limene lingabukepo pamene Mkristu wina apatsidwa thayo lateokrase?
7 Ngati munthu wina alandira thayo lateokrase kapena dalitso lauzimu, ena mumpingo ayenera kupeŵa kumchitira kaduka. Mwachitsanzo, mlongo wina waluso angamagwiritsiridwe ntchito kaŵirikaŵiri kuposa wina m’zitsanzo pamisonkhano Yachikristu. Zimenezi zingachititse nsanje kwa alongo ena. Mwinamwake mkhalidwe umodzimodzi ndiwo unali pakati pa Euodiya ndi Suntuke a mpingo wa Filipi. Akazi amakono oterowo angafunikire chilimbikitso chachifundo cha akulu kuti akhale odzichepetsa ndi kuti akhale ndi “mtima umodzi mwa Ambuye.”—Afilipi 2:2, 3; 4:2, 3.
8. Kodi nsanje ingatsogolere ku machitidwe oipa ati?
8 Mkristu angakhale akudziŵa za cholakwa chinachake chakumbuyo cha munthu amene tsopano wadalitsidwa ndi mathayo mumpingo. (Yakobo 3:2) Chifukwa cha nsanje, angayambe kumauza ena za chimenecho ndi kukayikira za thayo la munthuyo mumpingo. Zimenezi nzowombana ndi chikondi, chimene “chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) Nkhani za nsanje zingasokoneze mtendere wa mpingo. Wophunzira Yakobo anachenjeza kuti: “Mukakhala nako kaduka koŵaŵa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi. Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziŵanda.”—Yakobo 3:14, 15.
M’Banja Lanu
9. Kodi okwatirana angachepetse motani malingaliro ansanje?
9 Maukwati ambiri amalephera chifukwa cha nsanje yoipa. Munthu wosakhulupirira mnzake wa mu ukwati alibe chikondi. (1 Akorinto 13:7) Ndiponso, wina wa mu ukwati angasonyeze kusasamala za nsanje ya mnzakeyo. Mwachitsanzo, mkazi angachite nsanje chifukwa cha chisamaliro chimene mwamuna wake amasonyeza kwa mkazi wina. Kapena mwamuna angachite nsanje chifukwa cha nthaŵi yochuluka imene mkazi wake amaiwonongera pa kusamalira wachibale wake wovutika. Pochita manyazi ndi malingaliro oterowo, a mu ukwati angakhale chete ndi kusonyeza mkwiyo wawo mwa njira zina zimene zimacholoŵanitsa vutolo. M’malo mwake, mwamuna kapena mkazi amene wachita nsanjeyo ayenera kukambitsirana moona mtima ndi mnzakeyo ponena za malingaliro ake. Ndiyeno, mnzake nayenso ayenera kusonyeza kuti akumvetsetsa ndipo ayenera kumuuza motsimikiza kuti amamkondadi. (Aefeso 5:28, 29) Onse aŵiri ayenera kupeŵa kuchititsana nsanje mwa kupeŵa mikhalidwe imene ingaibutse. Nthaŵi zina woyang’anira Wachikristu angafunikire kuthandiza mkazi wake kuzindikira kuti akungopereka chithandizo chochepa ndi choyenera kwa akazi ena kuti akwaniritse thayo lake monga mbusa wa nkhosa za Mulungu. (Yesaya 32:2) Ndithudi, mkulu ayenera kusamala kuti asapereke chifukwa chilichonse choputa nsanje mwa wina. Zimenezi zimafuna uchikatikati, akumatsimikiza kuti amatayiranso nthaŵi pa kulimbitsa ukwati wake.—1 Timoteo 3:5; 5:1, 2.
10. Kodi makolo angathandize motani ana awo kuletsa malingaliro a nsanje?
10 Makolo ayeneranso kuthandiza ana awo kudziŵa nsanje yoipa. Ana kaŵirikaŵiri amayamba kukangana kumene kumathera m’kumenyana. Kaŵirikaŵiri chochititsa chimakhala nsanje. Pakuti zosoŵa za mwana aliyense nzosiyana, ana sayenera kuchitidwa molingana. Ndiponso, ana ayenera kudziŵa kuti aliyense wa iwo ali ndi zimene amachita bwino ndi zimene samachita bwino kwambiri. Ngati mwana wina nthaŵi zonse amalimbikitsidwa kuchita bwino molingana ndi wina, zimenezo zidzakulitsa nsanje mwa iye ndi kunyada mwa winayo. Chifukwa chake, makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kupima kupita patsogolo kwawo mwa kupenda zitsanzo za m’Mawu a Mulungu, osati mwa kupikisana ndi wina. Baibulo limati: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” M’malo mwake, “yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.” (Agalatiya 5:26; 6:4) Chofunika koposa nchakuti makolo Achikristu athandize ana awo mwa kukhala ndi phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse, akumasonyeza zitsanzo zabwino ndi zoipa m’Mawu a Mulungu.—2 Timoteo 3:15.
Zitsanzo za Kulamulira Nsanje
11. Kodi Mose anali motani chitsanzo chabwino cha kuletsa nsanje?
11 Mosiyana ndi olamulira a dzikoli osusukira ulamuliro mwadyera, “Mose [anali] wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Pamene kutsogolera Aisrayeli kunafika pakukhala mtolo kwa Mose yekha, Yehova anachititsa mzimu Wake kugwira ntchito pa Aisrayeli ena 70, ukumawapatsa mphamvu kuti athandize Mose. Pamene aŵiri mwa ameneŵa anayamba kuchita ngati aneneri, Yoswa anaona kuti zimenezi zinali kusokoneza utsogoleri wa Mose. Yoswa anafuna kuletsa amunawo, koma Mose modzichepetsa anati: “Kodi uchita nsanje nawo chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!” (Numeri 11:29) Inde, Mose anali wokondwa pamene ena analandira mwaŵi wa mathayo. Sanadzifunire ulemerero wake mwansanje.
12. Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Jonatani kupeŵa malingaliro a nsanje?
12 Chitsanzo chabwino cha mmene chikondi chimagonjetsera malingaliro a nsanje yoipa chinaperekedwa ndi Jonatani, mwana wa Sauli Mfumu ya Israyeli. Jonatani ndiye anali wotsatirapo kuloŵa ufumu wa atate wake, koma Yehova anali atasankha Davide, mwana wa Jese, kuti akhale mfumu yotsatirapo. Ambiri amene akanakhala mumkhalidwe wa Jonatani akanachitira nsanje Davide, akumamuona kukhala mdani. Komabe, chikondi cha Jonatani pa Davide chinaletsa malingaliro otero kukula mwa iye. Atamva za imfa ya Jonatani, Davide anati: “Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.”—2 Samueli 1:26.
Zitsanzo Zabwino Koposa
13. Kodi ndani amene ali chitsanzo chabwino koposa pa nkhani ya nsanje, ndipo nchifukwa ninji?
13 Yehova Mulungu ali chitsanzo chabwino koposa cha kukhala ndi ulamuliro ngakhale pa nsanje yabwino. Iye amalamulira bwino lomwe malingaliro oterowo. Mchitidwe wamphamvu uliwonse wosonyeza nsanje ya Mulungu, nthaŵi zonse umakhala wogwirizana ndi chikondi chake, chilungamo, ndi nzeru yake.—Yesaya 42:13, 14.
14. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani mosiyana ndi Satana?
14 Chitsanzo chachiŵiri chabwino koposa cha kukhala mbuye wa nsanje ndicho cha Mwana wokondedwa wa Mulungu, Yesu Kristu. “Pokhala nawo maonekedwe a Mulungu,” Yesu “sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu.” (Afilipi 2:6) Ha, ndi kusiyana kotani nanga ndi njira yotengedwa ndi mngelo wachikhumbo chadyera amene anadzakhala Satana Mdyerekezi! Monga “mfumu ya ku Babulo,” Satana anakhumba mwansanje ‘kufanana ndi Wam’mwambamwamba,’ mwa kudzikweza kukhala mulungu wopikisana ndi Yehova. (Yesaya 14:4, 14; 2 Akorinto 4:4) Satana anayesa ngakhale kuchititsa Yesu ‘kumgwadira’ iye. (Mateyu 4:9) Koma palibe chimene chikanapambutsa Yesu panjira ya kudzichepetsa kwake ndi kugonjera kwake ku ulamuliro wa Yehova. Mosiyana ndi Satana, Yesu “anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].” Yesu anachirikiza kuyenera kwa ulamuliro wa Atate wake, akumakaniratu njira ya Mdyerekezi ya kunyada ndi nsanje. Chifukwa cha kukhulupirika kwa Yesu, “Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m’dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afilipi 2:7-11.
Kulamulira Nsanje Yanu
15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala osamala kotero kuti tiletse malingaliro a nsanje?
15 Mosiyana ndi Mulungu ndi Kristu, Akristu ali opanda ungwiro. Pokhala ochimwa, nthaŵi zina angachite zinthu mwa nsanje yoipa. M’malo mwa kulola nsanje kutisonkhezera kusuliza wokhulupirira mnzathu ponena za cholakwa chaching’ono kapena tchimo longoganizira, nkofunika kuti tisinkhesinkhe pa mawu ouziridwa aŵa: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?”—Mlaliki 7:16.
16. Kodi ndi uphungu wabwino wotani wonena za nsanje umene unaperekedwa m’kope lakale la magazini ano?
16 Pankhani ya nsanje, The Watch Tower ya March 15, 1911, inachenjeza kuti: “Pamene kuli kwakuti tiyenera kukhala achangu kwambiri, ansanje kwambiri pachifuniro cha Ambuye, tiyenera kuona kuti siili nkhani yaumwini; ndipo tisamale kuti tisakhale ‘wodudukira.’ Ndiyenonso, tione ngati kungakhale koyenera kuisiira m’manja mwa akulu kapena ngati lili thayo lathu kuti tipite kwa akulu. Tonse tiyenera kukhala ndi nsanje yaikulu ya pa chifuniro cha Ambuye ndi ya pa ntchito ya Ambuye, koma tisamale kuti isakhale ya mtundu woipa . . . m’mawu ena, tiyenera kukhala otsimikiza kwenikweni kuti siili nsanje yochitirana kaduka, koma nsanje yosamalirana, kaamba ka zabwino za wina ndi mkhalidwe wake wabwino koposa.”—1 Petro 4:15.
17. Kodi tingapeŵe motani machitidwe oipa a nsanje?
17 Kodi ndimotani mmene ife monga Akristu tingapeŵere kunyada, nsanje, ndi kaduka? Yankho lili mwa kulola mzimu woyera wa Mulungu kuyenda mwatawatawa m’moyo wathu. Mwachitsanzo, tiyenera kupempherera mzimu wa Mulungu ndi chithandizo chake kuti tisonyeze zipatso zake zabwino. (Luka 11:13) Tiyenera kupezeka pamisonkhano Yachikristu, imene imayamba ndi pemphero ndipo imakhala ndi mzimu wa Mulungu ndi dalitso lake. Ndiponso, tiyenera kuphunzira Baibulo, limene linauziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Ndipo tiyenera kutenga mbali m’ntchito yolalikira Ufumu imene ikuchitidwa ndi mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova. (Machitidwe 1:8) Kuthandiza Akristu anzathu osweka mtima chifukwa cha chinthu choipa chowachitikira kuli njira ina yotsatirira chisonkhezero chabwino cha mzimu wa Mulungu. (Yesaya 57:15; 1 Yohane 3:15-17) Kukwaniritsa mwachangu mathayo Achikristu onseŵa kudzathandiza kutitetezera ku machitachita oipa a nsanje, pakuti Mawu a Mulungu amati: “Muyendeyende ndi mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.”—Agalatiya 5:16.
18. Kodi nchifukwa ninji sitidzapitiriza nthaŵi zonse kulimbana ndi malingaliro a nsanje yoipa?
18 Chikondi chaikidwa pamalo oyamba pa mndandanda wa zipatso za mzimu woyera wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Kusonyeza chikondi kudzatithandiza kulamulira zikhoterero zauchimo tsopano. Koma bwanji ponena zamtsogolo? Mamiliyoni a atumiki a Yehova ali ndi chiyembekezo cha moyo m’Paradaiso alinkudzayo wa pa dziko lapansi, mmene adzayembekezera kulandira ungwiro wa anthu. M’dziko latsopano limenelo, chikondi chidzasefukira ndipo palibe amene adzagonja ku malingaliro oipa a nsanje, pakuti “cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
Mfundo Zofuna Kusinkhasinkha
◻ Kodi Paulo anagwiritsira ntchito fanizo lotani kuthandiza kuletsa nsanje?
◻ Kodi nsanje ingasokoneze motani mtendere wa mpingo?
◻ Kodi makolo angaphunzitse motani ana awo kuletsa nsanje?
◻ Kodi tingapeŵe motani machitidwe oipa a nsanje?
[Chithunzi patsamba 16]
Musalole nsanje kusokoneza mtendere wa mpingo
[Chithunzi patsamba 17]
Makolo angaphunzitse ana awo kuletsa malingaliro a nsanje