Chikhulupiriro Chimatipanga Kukhala Oleza Mtima ndi Olimbikira Kupemphera
‘Lezani mtima, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye kuyandikira.’—YAKOBO 5:8.
1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira za Yakobo 5:7, 8?
“KUKHALAPO” kwa Yesu Kristu koyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali kwachitikadi tsopano. (Mateyu 24:3-14) Kuposa kale, onse amene amati amakhulupirira Mulungu ndi Kristu ali ndi chifukwa cholingalirira mawu a wophunzira Yakobo akuti: “Lezani mtima, abale, kufikira kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya myundo ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza [“kukhalapo,” NW] kwake kwa Ambuye kuyandikira.”—Yakobo 5:7, 8.
2. Kodi awo amene Yakobo analembera kalata anali ndi mavuto ena otani?
2 Awo amene Yakobo analembera kalata yake youziridwa anafunikira kuleza mtima ndi kuthetsa mavuto osiyanasiyana. Ambiri sanali kuchita zinthu monga momwe onena kuti amakhulupirira Mulungu ayenera kuchitira. Mwachitsanzo, anafunikira kuchitapo kanthu pa zikhumbo zina zimene zinali kukula m’mitima ya anthu ena. Bata linayenera kubwezeretsedwa pakati pa Akristu oyambirira amenewo. Anafunikanso uphungu wonena za kuleza mtima ndi kulimbikira kupemphera. Pamene tikambitsirana zimene Yakobo anawauza, tiyeni tione mmene tingagwiritsirire ntchito mawu ake m’miyoyo yathu.
Zikhumbo Zoipa Nzowononga
3. Kodi nchiyani chinachititsa kusagwirizana mumpingo, ndipo zimenezi zingatiphunzitsenji?
3 Pakati pa ena odzinenera kukhala Akristu panalibe mtendere, ndipo zikhumbo zoipa ndizo zinali muzu wa vutoli. (Yakobo 4:1-3) Kusagwirizana kunali kusokoneza zinthu, ndipo ena anali kuweruza abale awo mopanda chikondi. Zimenezi zinali kuchitika chifukwa chakuti zikhumbo zawo za zokondweretsa zinali kulimbana m’ziŵalo zawo za m’thupi. Ifeyo tifunikira kupempherera thandizo kuti tikane zikhumbo zakuthupi zofuna malo apamwamba, ulamuliro, ndi katundu kuti tisasokoneze mtendere wa mumpingo m’njira ina iliyonse. (Aroma 7:21-25; 1 Petro 2:11) Pakati pa Akristu ena a m’zaka za zana loyamba, chisiriro chinakula mpaka kukhala mzimu waudani ndi wambanda. Popeza Mulungu sanawathandize kuti akwaniritse zikhumbo zawo zoipa, iwo anapitirizabe kuyesetsa kuti akwaniritse zolinga zawo. Ngati ifenso tili ndi zikhumbo zoipa zoterozo, tingapemphe koma sitidzalandira, popeza kuti Mulungu wathu woyera samayankha mapemphero oterowo.—Maliro 3:44; 3 Yohane 9, 10.
4. Kodi nchifukwa ninji Yakobo akutcha ena kuti “akazi achigololo,” ndipo mawu ameneŵa ayenera kutikhudza motani?
4 Akristu ena oyambirira anali ndi malingaliro akudziko, nsanje, ndipo anali onyada. (Yakobo 4:4-6) Yakobo akutcha ena kuti “akazi achigololo” chifukwa chakuti anali mabwenzi a dziko lapansi ndipo chifukwa cha zimenezo anali ndi mlandu wa chigololo chauzimu. (Ezekieli 16:15-19, 25-45) Ndithudi, sitiyenera kukhala ndi malingaliro, kalankhulidwe, ndi kachitidwe ka zinthu kakudziko, popeza zimenezo zingatipange adani a Mulungu. Mawu ake akutisonyeza kuti “kuchita nsanje” kuli mbali ya malingaliro oipa, kapena kuti “mzimu,” umene uli mwa anthu ochimwa. (Genesis 8:21; Numeri 16:1-3; Salmo 106:16, 17; Mlaliki 4:4) Choncho titadziŵa kuti tiyenera kuyesetsa kuti tigonjetse nsanje, kunyada, kapena malingaliro ena oipa, tiyeni tipemphe thandizo la Mulungu la mzimu woyera. Mphamvu imeneyo, yoperekedwa mwachisomo cha Mulungu, njaikulu kuposa “kuchita nsanje.” Ndipo pamene kuli kwakuti Yehova amatsutsa onyada, iye adzatipatsa chisomo ngati tiyesetsa kukana malingaliro auchimo.
5. Kuti tikhale ndi chisomo cha Mulungu, kodi tiyenera kukwaniritsa zoyenera zotani?
5 Kodi tingachilandire motani chisomo cha Mulungu? (Yakobo 4:7-10) Kuti tikhale ndi chisomo chochokera kwa Yehova, tiyenera kumumvera iye, kulandira zogaŵira zake, ndi kugonjera ku chifuniro chake chilichonse. (Aroma 8:28) Tiyeneranso ‘kukaniza,’ kapena ‘kutsutsana,’ ndi Mdyerekezi. Iye ‘adzatithaŵa’ ngati tilimbikira kukhala ochirikiza ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova. Tili ndi thandizo la Yesu, amene amaletsa zinthu zoipa za dziko kotero kuti palibe chimene chingativulaze kotheratu. Ndipo tisaiŵale nkomwe kuti: Mwa pemphero, kumvera, ndi chikhulupiriro, timayandikira kwa Mulungu, ndipo amakhaladi pafupi nafe.—2 Mbiri 15:2.
6. Kodi nchifukwa ninji Yakobo akutcha Akristu ena kuti “ochimwa”?
6 Kodi nchifukwa ninji Yakobo akugwiritsira ntchito liwu lakuti “ochimwa” kunena ena amene amati amakhulupirira Mulungu? Chifukwa chakuti anali ndi mlandu wa “nkhondo” ndi udani wambanda—mzimu wosaloledwa kwa Akristu. (Tito 3:3) “Manja” awo, odzaza zochita zoipa, anafunikira kuyeretsedwa. Anafunikiranso kuyeretsa “mitima” yawo, chimake cha zolingalira. (Mateyu 15:18, 19) “A mitima iŵiri” amenewo ankalephera kusankha pakati pa ubwenzi ndi Mulungu ndi ubwenzi ndi dziko lapansi. Pokhala tachenjezedwa mwa chitsanzo chawo choipa, tiyeni tikhalebe osamala kuti zinthu zimenezi zisawononge chikhulupiriro chathu.—Aroma 7:18-20.
7. Kodi nchifukwa ninji Yakobo akuuza ena kuti ‘alire, alire misozi’?
7 Yakobo akuuza oŵerenga ake kuti ‘akhale osautsidwa, alire, alire misozi.’ Ngati anasonyeza chisoni chaumulungu, zingakhale umboni wakuti analapa. (2 Akorinto 7:10, 11) Lerolino, ena amene amati ali ndi chikhulupiriro akufuna kupalana ubwenzi ndi dziko. Ngati ena a ife akulondola njira imeneyo, kodi sitiyenera kulira chifukwa cha mkhalidwe wathu wauzimu wofooka ndi kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tiwongolere zinthu? Kuwongolera zinthu moyenerera ndi kulandira chikhululukiro cha Mulungu kudzatipatsa chimwemwe chifukwa chokhala ndi chikumbumtima choyera ndi chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha.—Salmo 51:10-17; 1 Yohane 2:15-17.
Musaweruzane
8, 9. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kunenezana kapena kuweruzana?
8 Kuneneza wokhulupirira mnzako ndi tchimo. (Yakobo 4:11, 12, NW) Komabe ena amakonda kudzudzula Akristu anzawo, mwinamwake chifukwa cha mzimu wawo wodzilungamitsa kapena chifukwa chakuti amafuna kudzikweza mwa kunyoza ena. (Salmo 50:20; Miyambo 3:29) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘neneza’ limapereka lingaliro la chidani ndipo limatanthauza kukokomeza mlandu kapena kunamizira. Kumeneku kumakhala kuweruza mbale moŵaŵa. Kodi ndi motani mmene kumeneku kulili ‘kuneneza kapena kuweruza lamulo la Mulungu’? Eya, alembi ndi Afarisi ‘anakaniza mochenjera lamulo la Mulungu’ naweruza mwa malamulo awoawo. (Marko 7:1-13, NW) Mofananamo, ngati taweruza mbale amene Yehova sanamuweruze, kodi sindiye kuti ‘taweruza lamulo la Mulungu’ ndipo mochimwa tatanthauza kuti nlopereŵera? Ndipo mwa kudzudzula mbale wathu popanda chifukwa, tingakhale tikulephera kukwaniritsa lamulo la chikondi.—Aroma 13:8-10.
9 Tiyeni tikumbukire kuti: “Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi”—Yehova. ‘Malamulo ake ali angwiro,’ osati opereŵera. (Salmo 19:7; Yesaya 33:22) Mulungu yekha ndiye ali ndi mphamvu yoika malangizo ndi malamulo kaamba ka chipulumutso. (Luka 12:5) Choncho Yakobo akufunsa kuti: “Iwe woweruza mnzako ndiwe yani?” Kuweruza ndi kutsutsa ena sikwathu ayi. (Mateyu 7:1-5; Aroma 14:4, 10) Kukumbukira za uchifumu wa Mulungu ndi kupanda tsankhu kwake ndiponso kuchimwa kwathu kuyenera kutiletsa kuweruza ena modziona ngati olungama.
Peŵani Kudzidalira Modzitama
10. Kodi nchifukwa ninji timayenera kudalira Yehova m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku?
10 Nthaŵi zonse tiyenera kulingalira za Yehova ndi malamulo ake. (Yakobo 4:13-17) Monyalanyaza Mulungu, odzidalira okha amati: “Lero kapena maŵa tidzapita kuloŵa ku mudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kusatsa malonda, ndi kupindula nawo.” Ngati ‘tidziunjikira chuma chathu osakhala nacho chuma cha kwa Mulungu,’ moyo wathu ukhoza kutha maŵa ndipo sitidzakhala ndi mwaŵi wa kutumikira Yehova. (Luka 12:16-21) Monga momwe Yakobo akunenera, tili monga utsi wammamaŵa “wakuonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka.” (1 Mbiri 29:15) Tingayembekezere chimwemwe chosatha ndi moyo wosatha kokha mwa kukhulupirira Yehova.
11. Kodi kunena kuti, “Akalola Mulungu” kumatanthauzanji?
11 M’malo monyalanyaza Mulungu modzitama, tiyenera kumati: “Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.” Kunena kuti, “Akalola Mulungu” kumasonyeza kuti tikuyesa kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake. Tingafunikire kuchita malonda kuti tichirikize banja lathu, kuyenda maulendo pantchito ya Ufumu, ndi zina zotero. Koma tisadzitamandire. “Kudzitamandira kuli konse kotero nkoipa” chifukwa chakuti kumanyalanyaza kudalira Mulungu.—Salmo 37:5; Miyambo 21:4; Yeremiya 9:23, 24.
12. Kodi mawu a pa Yakobo 4:17 amatanthauzanji?
12 Mwachionekere kuti amalize ndemanga zake ponena za kudzidalira ndi kudzitama, Yakobo akuti: “Kwa iye amene adziŵa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.” Mkristu aliyense modzichepetsa ayenera kusonyeza kudalira kwake Mulungu. Ngati satero, “kwa iye kuli tchimo.” Zoonadi, pulinsipulo limodzimodzili limagwiranso ntchito ponena za kulephera kuchita zimene kukhulupirira Mulungu kumafuna kwa ife.—Luka 12:47, 48.
Chenjezo kwa Achuma
13. Kodi Yakobo akuti bwanji ponena za ogwiritsira ntchito chuma chawo molakwa?
13 Popeza kuti Akristu ena oyambirira anayamba kukondetsa chuma kapena anali kukhumbira achuma, Yakobo akunena mawu amphamvu okhudza achuma ena. (Yakobo 5:1-6) Anthu akudziko ogwiritsira ntchito chuma chawo molakwa ‘analira ndi kuchema chifukwa cha masautso amene anali kudza pa iwo’ pamene Mulungu anawabwezera malinga ndi zochita zawo. M’masikuwo, chuma cha anthu ambiri chinali kwenikweni zinthu monga zovala, tirigu, ndi vinyo. (Yoweli 2:19; Mateyu 11:8) Zina mwa zimenezi zimatha kuwola kapena ‘kujiwa ndi njenjete,’ koma Yakobo akugogomezera kupanda pake kwa chuma, osati kuwonongeka kwake. Ngakhale kuti golidi ndi siliva sizichita dzimbiri, ngati tazibisa, zingakhale zopanda pake monga zinthu zimene zachita dzimbiri. “Dzimbiri” limasonyeza kuti chuma chakuthupi sichinagwiritsiridwe ntchito bwino. Choncho, tonsefe tiyenera kukumbukira kuti “chinthu chonga moto, [NW]” nchimene awo odalira katundu wawo wakuthupi ‘akundika m’masiku otsiriza’ pamene mkwiyo wa Mulungu udzadza pa iwo. Popeza tikukhala mu “nthaŵi ya chimariziro,” mawu ameneŵa ali ndi tanthauzo lapadera kwa ife.—Danieli 12:4; Aroma 2:5.
14. Kodi nthaŵi zambiri achuma amachitanji, ndipo tiyenera kuchita chiyani ndi zimenezo?
14 Achuma nthaŵi zambiri amanyenga antchito yosenga m’minda yawo ndipo samawapatsa malipiro awo. Malipirowa ‘afuula’ kaamba ka chilango chobwezera. (Yerekezerani ndi Genesis 4:9, 10.) Anthu achuma akudziko ‘adyerera padziko.’ Pomwerekera ndi zokondweretsa, iwo amakhala ndi mitima yonenepa, yosamva kalikonse ndipo adzapitirizabe kuchita zimenezi pa “tsiku” loikidwira kuphedwa kwawo. Iwo ‘amatsutsa ndi kupha wolungama.’ Yakobo akuti: “Wolungamayo, sakaniza inu.” Koma katembenuzidwe kena kamati, “kodi satsutsa inu?” Mulimonse mmene zilili, sitiyenera kukondera achuma. Tiyenera kuika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo.—Mateyu 6:25-33.
Chikhulupiriro Chimatithandiza Kuleza Mtima
15, 16. Kodi nchifukwa ninji kuleza mtima kuli kofunika kwambiri?
15 Pokhala atanenapo za anthu achuma akudziko opondereza anzawo, Yakobo kenako akulimbikitsa Akristu oponderezedwa kuti akhale oleza mtima. (Yakobo 5:7, 8) Ngati okhulupirira anapirira mavuto awo moleza mtima, chikhulupiriro chawo chinali kuyembekezera kufupidwa panthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu, pamene owapondereza adzalandira chiweruzo. (Mateyu 24:37-41) Akristu oyambirira amenewo anafunikira kukhala ngati mlimi amene amayembekezera mvula ya myundo moleza mtima, pamene amabzala, ndi mvula ya masika yobalitsa zipatso. (Yoweli 2:23) Ifenso tiyenera kuleza mtima ndi kulimbitsa mitima yathu, makamaka popeza kuti “kukhalapo kwake kwa Ambuye” Yesu Kristu kwachitika!
16 Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuleza mtima? (Yakobo 5:9-12) Kuleza mtima kumatithandiza kuti tisamabuule kapena kuipidwa pamene okhulupirira anzathu atiputa. Ngati ‘tiipidwa wina ndi mnzake’ mwa mzimu woipa, Woweruza Yesu Kristu adzatitsutsa. (Yohane 5:22) Tsopano pamene “kukhalapo” kwake kwayamba ndipo “aima pakhomo,” tiyeni tichirikize mtendere mwa kuleza mtima ndi abale athu, amene chikhulupiriro chawo chikuyesedwa kwambiri. Chikhulupiriro chathu chimalimbitsidwa tikakumbukira kuti Mulungu anafupa Yobu chifukwa chakuti anapirira ziyeso zake moleza mtima. (Yobu 42:10-17) Ngati tili ndi chikhulupiriro ndipo tileza mtima, tidzaona kuti “Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.”—Mika 7:18, 19.
17. Kodi nchifukwa ninji Yakobo akunena kuti, “Musalumbire”?
17 Ngati sitileza mtima, tingagwiritsire ntchito lilime molakwa pamene tili pavuto. Mwachitsanzo, tingafulumire kulumbira. “Musalumbire,” akutero Yakobo, pochenjeza za kulumbira kwachizoloŵezi. Kutsimikiza mawu mwa kulumbira nthaŵi zonse kumaonekanso kukhala kwachinyengo. Choncho, tizingolankhula choonadi basi, inde wathu kukhaladi inde, ndi iyayi wathu kukhaladi iyayi. (Mateyu 5:33-37) Inde, Yakobo sakunena kuti nkulakwa kulumbira m’khoti ponena choonadi.
Chikhulupiriro ndi Mapemphero Athu
18. Kodi ndi m’mikhalidwe yotani mmene tiyenera ‘kupemphera’ ndi ‘kuimba’?
18 Pemphero liyenera kukhala lofunika kwambiri pamoyo wathu ngati tikufuna kulamulira kalankhulidwe kathu, kukhala woleza mtima, ndi kukhala ndi chikhulupiriro chokwanira mwa Mulungu. (Yakobo 5:13-20) Kwenikweni tikakhala pachiyeso, tiyenera ‘kupemphera.’ Ngati takondwa, tiyeni ‘tiimbe,’ monga momwe Yesu ndi atumwi ake anachitira pamene iye anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake. (Marko 14:26) Nthaŵi zina, timamthokoza kwambiri Mulungu kotero kuti timaimba zitamando ngakhale mumtima. (1 Akorinto 14:15; Aefeso 5:19) Ndipo nkosangalatsa chotani nanga kutama Yehova ndi nyimbo pamisonkhano yachikristu!
19. Kodi tiyenera kuchitanji ngati tadwala mwauzimu, ndipo nkuchitiranji zimenezi?
19 Sitingakonde kuimba ngati tikudwala mwauzimu, mwinamwake chifukwa cha khalidwe loipa kapena kulephera kudya nthaŵi zonse pagome la Yehova. Ngati zili choncho kwa ife, modzichepetsa tiyeni tiitane akulu kuti ‘atipempherere.’ (Miyambo 15:29) Ndiponso iwo ‘adzatidzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye.’ Monga mafuta oletsa kuŵaŵa kwa bala, mawu awo otonthoza ndi uphungu wawo wa m’Malemba zidzathandiza kuthetsa kuchita tondovi, kukayikira, ndi mantha. ‘Pemphero lachikhulupiriro lidzatipulumutsa’ ngati talichirikiza ndi chikhulupiriro chathu. Ngati akulu apeza kuti matenda athu auzimu achititsidwa ndi tchimo lalikulu, iwo mwachikondi adzatisonyeza kulakwa kwathu ndi kuyesetsa kutithandiza. (Salmo 141:5) Ndipo ngati talapa, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu adzamva mapemphero awo ndi kutikhululukira.
20. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuvomerezana machimo athu wina ndi mnzake ndi kupemphererana?
20 ‘Kuvomerezana wina ndi mnzake machimo athu’ kuyenera kukhala chotitetezera kuti tisachimwenso. Kuyenera kusonkhezera kumverana chifundo, mkhalidwe umene udzatisonkhezera ‘kupemphererana wina ndi mnzake.’ Tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti zimenezi zidzakhala zopindulitsa chifukwa chakuti pemphero la “munthu wolungama”—munthu wachikhulupiriro ndiponso woonedwa ndi Mulungu kukhala wolungama—limachita zambiri kwa Yehova. (1 Petro 3:12) Mneneri Eliya anali ndi zofooka monga zathu, koma mapemphero ake anali ogwira ntchito. Anapemphera, ndipo mvula siinagwe zaka zitatu ndi theka. Pamene anapempheranso, mvula inagwa.—1 Mafumu 17:1; 18:1, 42-45; Luka 4:25.
21. Kodi tingachitenji ngati Mkristu mnzathu ‘wasochera posiyana nacho choonadi’?
21 Bwanji ngati wina mumpingo ‘wasochera posiyana ndi choonadi,’ kusiya chiphunzitso chabwino ndi khalidwe loyenera? Tikhoza kumbweza kuchoka pacholakwa chake mwa uphungu wa m’Baibulo, pemphero, ndi zothandiza zina. Ngati tamthandiza, zimenezi zidzampangitsa kukhala wotetezereka ndi dipo la Kristu ndipo adzapulumuka ku imfa yauzimu ndi kuponyedwa kuchiwonongeko. Mwa kuthandiza wolakwa, timakwirira machimo ake ambiri. Wolakwa wodzudzulidwa atachoka pa cholakwa chake, ndipo walapa, ndi kupempha chikhululukiro, tidzakondwera kuti tinachitapo kanthu kuti machimo ake akwiriridwe.—Salmo 32:1, 2; Yuda 22, 23.
Kanthu Kena kwa Tonsefe
22, 23. Kodi mawu a Yakobo ayenera kutikhudza motani?
22 Ndithudi, kalata ya Yakobo ili ndi kanthu kena kopindulitsa kwa tonsefe. Imatisonyeza mmene tingalimbanirane ndi ziyeso, imatipatsa uphungu wotsutsa tsankhu, ndiponso imatilimbikitsa kuchita ntchito zowongoka. Yakobo akutilimbikitsa kulamulira lilime, kukana chisonkhezero cha dziko, ndi kuchirikiza mtendere. Mawu ake ayeneranso kutichititsa kukhala oleza mtima ndi olimbikira kupemphera.
23 Zoonadi, kalata ya Yakobo poyamba inatumizidwa kwa Akristu oyambirira odzozedwa. Komabe, tonsefe tiyenera kulola uphungu wake kutithandiza kumamatira ku chikhulupiriro chathu. Mawu a Yakobo angalimbitse chikhulupiriro chimene chimatisonkhezera kuchitapo kanthu motsimikiza mtima mu utumiki wa Mulungu. Ndipo kalata youziridwa ndi Mulungu imeneyi imamanga chikhulupiriro chokhalitsa chimene chimatipanga kukhala Mboni za Yehova zoleza mtima, ndi zolimbikira kupemphera lerolino, mkati mwa “kukhalapo kwa Ambuye” Yesu Kristu.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu ena oyambirira anafunikira kusintha mzimu wawo ndi khalidwe lawo?
◻ Kodi Yakobo akuwachenjeza za chiyani achuma?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala oleza mtima?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupemphera nthaŵi zonse?
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 23]
Akristu ena oyambirira anafunikira kukhala oleza mtima kwambiri kwa okhulupirira anzawo
[Chithunzi patsamba 24]
Akristu ayenera kukhala oleza mtima, achikondi, ndi olimbikira kupemphera