Miyambo
2 Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+
Koma pakamwa pa zitsiru pamangolankhula mawu opusa.
4 Lilime lodekha* lili ngati mtengo wa moyo,+
Koma mawu achinyengo amachititsa kuti anthu ataye mtima.
5 Munthu wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+
Koma munthu wochenjera amamvera ena akamudzudzula.+
6 Mʼnyumba ya munthu wolungama muli chuma chambiri,
Koma zokolola za munthu woipa zimamubweretsera mavuto.+
7 Milomo ya munthu wanzeru imafalitsa zimene akudziwa,+
Koma mtima wa munthu wopusa suchita zimenezo.+
8 Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa kwa Yehova,+
Koma pemphero la munthu wowongoka mtima limamusangalatsa.+
10 Chilango chimaoneka choipa* kwa munthu amene wasiya njira yabwino,+
Koma aliyense amene amadana ndi kudzudzulidwa adzafa.+
11 Ngati Yehova amaona bwinobwino amene ali mʼManda* ndiponso malo achiwonongeko,*+
Ndiye kuli bwanji zimene zili mʼmitima ya anthu?+
12 Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akumudzudzula.+
Iye sadzapempha malangizo kwa anthu anzeru.+
13 Mtima wachimwemwe umapangitsa kuti nkhope izioneka yosangalala,
Koma munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.+
14 Anthu anzeru* amayesetsa kuti adziwe zinthu,+
Koma pakamwa pa anthu opusa pamasangalala ndi zinthu zopusa.+
15 Masiku onse a munthu amene akukumana ndi mavuto amakhala oipa,+
Koma munthu amene ali ndi mtima wosangalala* amachita phwando nthawi zonse.+
16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+
Kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri koma uli ndi nkhawa.*+
17 Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+
Kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa* koma pali chidani.+
18 Munthu wosachedwa kupsa mtima amayambitsa mkangano,+
Koma munthu amene sakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+
19 Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+
Koma njira ya munthu wowongoka mtima ili ngati msewu wosalazidwa bwino.+
21 Munthu wopanda nzeru amasangalala ndi uchitsiru,+
Koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+
22 Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana,*
Koma alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.+
23 Munthu amasangalala akapereka yankho labwino,*+
Ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+
27 Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake,+
Koma amene amadana ndi ziphuphu adzakhalabe ndi moyo.+
28 Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+
Koma pakamwa pa anthu oipa pamangolankhula zoipa.