Tumikirani Yehova Mokhulupirika
“Ndi munthu wokhulupirika inu [Yehova] mudzachita mokhulupirika.”—2 SAMUELI 22:26, NW.
1. Kodi Yehova amachita motani ndi okhulupirika kwa iye?
YEHOVA sangalipiridwe pazonse zimene amachitira anthu ake. (Salmo 116:12) Mphatso zake zauzimu ndi zakuthupi ndi chifundo chake nzabwino kwambiri chotani nanga! Mfumu Davide wa Israyeli wakale anadziŵa kuti Mulungu amachitanso mokhulupirika kwa okhulupirika kwa iye. Davide anatero m’nyimbo imene anapeka ‘m’tsiku limene Yehova anampulumutsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la [Mfumu] Sauli.’—2 Samueli 22:1.
2. Kodi ndimfundo zina ziti zotchulidwa m’nyimbo ya Davide yolembedwa mu 2 Samueli chaputala 22?
2 Davide anayamba nyimbo yake (mogwirizana ndi Salmo 18) mwakutamanda Yehova monga “Mpulumutsi” m’kuyankha pemphero. (2 Samueli 22:2-7) Ali m’kachisi wake wakumwamba, Yehova anachitapo kanthu kupulumutsa mtumiki wake wokhulupirikayo kwa adani amphamvu. (Mavesi 8-19) Chotero, Davide anafupidwa kaamba ka kulondola njira yolungama ndi kuyenda m’mabande a Yehova. (Mavesi 20-27) Zondandalitsidwa motsatira ndizo ntchito zochitidwa mwa mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu. (Mavesi 28-43) Potsiriza, Davide anatchula kupulumutsidwa kwa anthu ofuna kumpeza mlandu m’banja ndi kwa adani akunja ndi kuyamika Yehova monga amene “apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; Nawonetsera chifundo wodzozedwa wake.” (Mavesi 44-51) Yehova akhoza kutipulumutsa nafenso ngati tilondola njira yolungama ndi kudalira iye kaamba ka nyonga.
Chimene Kukhala Wokhulupirika Kumatanthauza
3. Malinga ndi lingaliro la Malemba, kodi kukhala wokhulupirika kumatanthauzanji?
3 Nyimbo ya Davide ya chipulumutso imatipatsa chitsimikizo chotonthoza ichi: “Ndi munthu wokhulupirika inu [Yehova] mudzachita mokhulupirika.” (2 Samueli 22:26) Ali mfotokozi Wachihebri wakuti cha·sidhʹ amene amatanthauza kuti “munthu wokhulupirika,” kapena “munthu wakukoma mtima kwachikondi.” (Salmo 18:25, NW mawu am’tsinde) Liwu la dzina lakuti cheʹsedh liri ndi lingaliro la kukoma mtima kumene kumamamatira ku chinthucho kufikira cholinga chakecho chikwaniritsidwa. Yehova amasonyeza mtundu wa kukoma mtima koteroko kwa atumiki ake, mongadi momwe iwonso amakusonyezera kwa iye. Kukhulupirika kolungama ndi kopatulika kumeneku kumamasuliridwa ‘kukoma mtima kwachikondi’ ndi ‘chikondi chokhulupirika.’ (Genesis 20:13; 21:23) M’malemba Achigiriki, “kukhulupirika” kuli ndi lingaliro la kupatulika ndi kulemekezeka, kosonyezedwa m’dzina lakuti ho·si·oʹtes ndi mfotokozi wakuti hoʹsi·os. Kukhulupirika koteroko kumaphatikizapo umphumphu ndi kudzipereka ndipo kumatanthauza kukhala wakhama ndi kuchita mosamalitsa ntchito zonse za kwa Mulungu. Kukhala wokhulupirika kwa Yehova kumatanthauza kumamatira kwa iye ndi kudzipereka molimba kotero kuti kumachita monga glu wamphamvu.
4. Kodi kukhulupirika kwake Yehova kumasonyezedwa motani?
4 Kukhulupirika kwa Yehova iye mwiniyo kumasonyezedwa m’njira zambiri. Mwachitsanzo, iye amaweruza oipa chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika kwa anthu ake ndi kukhulupirika kwake ku chiweruzo cholungama ndi chilungamo. (Chivumbulutso 15:3, 4; 16:5) Kukhulupirika kwake ku pangano lake ndi Abrahamu kunamsonkhezera kukhala woleza mtima kwa Aisrayeli. (2 Mafumu 13:23) Okhulupirika kwa Mulungu angadalire pachithandizo chake kufikira mapeto a njira yawo yakukhulupirika ndipo akhoza kukhala otsimikiza kuti iye adzawakumbukira. (Salmo 37:27, 28; 97:10) Yesu analimbikitsidwa ndi chidziŵitso chakuti monga ‘wokhulupirika’ wamkulu wa Mulungu, moyo wake sukasiyidwa m’Sheol.—Salmo 16:10; Machitidwe 2:25, 27.
5. Popeza kuti Yehova ngwokhulupirika, kodi iye amafunanji kwa atumiki ake, ndipo ndifunso lotani limene lidzalingaliridwa?
5 Popeza kuti Yehova Mulungu ngwokhulupirika, amafuna atumiki ake kukhala okhulupirika. (Aefeso 4:24) Mwachitsanzo, amuna ayenera kukhala okhulupirika kuti ayeneretsedwe kuikidwa monga akulu a mpingo. (Tito 1:8) Kodi ndizinthu ziti zimene ziyenera kusonkhezera anthu a Mulungu kumtumikira mokhulupirika?
Chiyamikiro cha Zinthu Zophunziridwa
6. Kodi tiyenera kumva motani ponena za zinthu za m’Malemba zimene taphunzira, ndipo kodi tiyenera kukumbukiranji ponena za chidziŵitso choterocho?
6 Chiyamikiro cha zinthu za m’Malemba zimene taphunzira chiyenera kutisonkhezera kutumikira Yehova mokhulupirika. Mtumwi Paulo anafulumiza Timoteo kuti: “Ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa; ndikuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (2 Timoteo 3:14, 15) Kumbukirani kuti chidziŵitso choterocho chinachokera kwa Mulungu kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
7. Kodi akulu ayenera kumva bwanji ponena za chakudya chauzimu chogaŵiridwa kupyolera mwa kapolo wokhulupirika?
7 Makamaka akulu oikidwa ayenera kuyamikira chakudya chauzimu chopatsa nyonga chogaŵiridwa ndi Mulungu kupyolera mwa kapolo wokhulupirika. Zaka zingapo zapitazo akulu ochepekera analibe chiyamikiro choterocho. Wowona wina anati amunaŵa “anali kusuliza nkhani za mu Nsanja ya Olonda, osafuna kuivomereza monga . . . ngalande ya Mulungu ya chowonadi, nthaŵi zonse akumayesa kusonkhezera ena m’njira yawo yakulingalira.” Komabe, akulu okhulupirika samayesa konse kusonkhezera ena kukana chakudya chauzimu chirichonse choperekedwa ndi Mulungu kupyolera mwa kapolo wokhulupirikayo.
8. Bwanji ngati sitimvetsetsa mfundo ina ya m’Malemba yoperekedwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?
8 Monga Mboni za Yehova zokhulupirika, tonsefe tiyenera kukhala okhulupirika kwa iye ndi gulu lake. Sitiyenera ngakhale kulingalira zakupambuka pa kuunika kwabwino koposa kwa Yehova kulondola njira yampatuko imene ingatitsogolere ku imfa yauzimu tsopano ndi chiwonongeko potsirizira pake. (Yeremiya 17:13) Koma bwanji ngati kukhala kovuta kwa ife kuvomereza kapena kumvetsetsa mokwanira mfundo ya m’Malemba yoperekedwa ndi kapolo wokhulupirika? Pamenepo tiyenera kuzindikira modzichepetsa kumene tinaphunzira chowonadi ndi kupempherera nzeru yakuti tigonjetse chiyeso chimenechi kufikira pamene chitha mwakumveketsedwa kolembedwa m’zofalitsidwa.—Yakobo 1:5-8.
Yamikirani Ubale Wachikristu
9. Kodi ndimotani mmene 1 Yohane 1:3-6 amasonyezera kuti Akristu ayenera kukhala ndi mzimu wamayanjano?
9 Chiyamikiro chochokera mumtima cha mzimu wa mayanjano okhalapo paubale wathu Wachikristu chimapereka chifukwa china chotumikirira Yehova mokhulupirika. Kwenikweni, unansi wathu ndi Mulungu ndi Kristu sungakhale wabwino mwauzimu popanda mzimu umenewu. Mtumwi Yohane anauza Akristu odzozedwa kuti: “Chimene tidachiwona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso, mukayanjane [“kucheza,” Diaglott] pamodzi ndi ife. Ndipo chiyanjano chathu chirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Kristu. . . . Tikati kuti tiyanjana ndi iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi.” (1 Yohane 1:3-6) Lamulo lakachitidwe limeneli limagwira ntchito kwa Akristu onse, kaya chiyembekezo chawo nchakumwamba kapena chapadziko lapansi.
10. Ngakhale kuti Euodiya ndi Suntuke mwachiwonekere kunawavuta kuthetsa vuto pakati pawo, kodi ndimotani mmene Paul anawonera akaziŵa?
10 Kuyesayesa nkofunika kuti tisunge mzimu wa mayanjano. Mwachitsanzo, mkazi Wachikristu Euodiya ndi Suntuke mwachiwonekere kunawavuta kuthetsa vuto pakati pawo. Motero Paulo anawafulumiza kukhala “amtima umodzi mwa Ambuye.” Anawonjezera kuti: “Ndikupemphaninso, m’nzanga wa m’goli wowona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu uthenga wabwino, pamodzi ndi Klementonso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina awo ali m’bukhu la moyo.” (Afilipi 4:2, 3) Amuna aumulungu amenewo anakangalika pamodzi ndi Paulo ndi ena “mu uthenga wabwino,” ndipo iye anali wotsimikiza kuti iwo anali pakati pa awo ‘amene maina awo analembedwa m’bukhu la moyo.’
11. Ngati Mkristu wokhulupirika ayang’anizana ndi vuto lauzimu, kodi kukakhala koyenera kukumbukira chiyani?
11 Akristu samavala baji yaulemu yosonyeza mathayo amene akhala akutumikira m’gulu la Yehova ndi mmene atumikirira mokhulupirika. Ngati ali ndi vuto lauzimu, kukakhala kupanda chikondi motani nanga kunyalanyaza zaka zawo za utumiki wokhulupirika kwa Yehova! Mwachiwonekere, wotchedwayo “m’nzanga wa m’goli wowona” anali mbale wokhulupirika wachangu kuthandiza ena. Ngati inu muli mkulu, kodi ndinu ‘m’nzawo wa m’goli wowona,’ woyembekezera kupereka chithandizo mokoma mtima? Tonsefe tilingalire zabwino zochitidwa ndi okhulupirira anzathu, monga momwe Mulungu amachitira, ndi kuwathandiza mwachikondi kunyamula zothodwetsa zawo.—Agalatiya 6:2; Ahebri 6:10.
Kulibenso Kwina Kopita
12. Pamene mawu a Yesu anachititsa ‘ophunzira ambiri kubwerera kuzinthu zakumbuyo,’ kodi Petro ananenanji?
12 Tidzakakamizika kutumikira Yehova mokhulupirika ndi gulu lake ngati tikumbukira kuti kulibenso kwina kokapeza moyo wamuyaya. Pamene mawu a Yesu anachititsa ‘ophunzira ambiri kubwerera kuzinthu zakumbuyo,’ iye anafunsa atumwi ake kuti: “Nanga inunso mufuna kuchoka,” Petro anayankha nati: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziŵa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.”—Yohane 6:66-69.
13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji Chiyuda cha m’zaka za zana loyamba chinalibe chiyanjo chaumulungu? (b) Kodi nchiyani chimene Mboni ya Yehova yanthaŵi yaitali inanena za gulu la Mulungu lowoneka?
13 “Mawu a moyo wosatha” munalibemo m’Chiyuda cha m’zaka za zana loyamba C.E. Tchimo lake lalikulu linali kukana Yesu monga Mesiya. Chiyuda, m’mipangidwe yake yonse, sichinazikidwe kotheratu pa Malemba Achihebri. Asaduki anakana kukhalako kwa angelo ndipo sanakhulupirire chiukiriro. Ngakhale kuti Afarisi sanavomerezane nawo m’mbali zimenezi, iwo mochimwa anapeputsa Mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yawo yosagwirizana ndi Malemba. (Mateyu 15:1-11; Machitidwe 23:6-9) Miyambo imeneyi inaika Ayuda muukapolo ndi kuchititsa kukhala kovuta kwa ambiri kuvomereza Yesu Kristu. (Akolose 2:8) Changu cha pa ‘miyambo ya makolo ake’ chinachititsa Saulo (Paulo) m’kusadziŵa kwake kukhala wozunza otsatira Kristu wankhanza.—Agalatiya 1:13, 14, 23.
14 Chiyuda chinalibe chiyanjo cha Mulungu, koma Yehova anadalitsa gulu la otsatira a Mwana wake—“anthu achangu pantchito zokoma.” (Tito 2:14) Gulu limenelo lidakalipo, ndipo Mboni ina ya Yehova kwa nthaŵi yaitali inati ponena za ilo: “Ngati pali kanthu kamene kakhala kofunika koposa kwa ine, kanthuko ndiko kumamatira ku gulu la Yehova lowoneka. Zochitika zanga zoyambirira zinandiphunzitsa mmene kuliri kopanda pake kudalira pakulingalira kwaumunthu. Pamene maganizo anga anakhutiritsidwa pamfundo imeneyi, ndinatsimikiza mtima kumamatira kugulu lokhulupirika la Yehova. Kodi ndimotaninso mmene munthu angapezere chiyanjo cha Yehova ndi madalitso?” Kulibenso kwina kulikonse kumene munthu angapezeko chiyanjo chaumulungu ndi moyo wamuyaya.
15. Kodi nkugwirizaniranji ndi gulu la Yehova lowoneka ndipo ndi awo osenza mathayo m’menemo?
15 Mitima yathu iyenera kutisonkhezera kugwirizana ndi gulu la Yehova chifukwa chakuti timadziŵa kuti ilo ndilo lokhalo limene likutsogozedwa ndi mzimu wake ndipo likudziŵikitsa dzina lake ndi zifuno zake. Ndithudi, osenza mathayo m’menemo ali opanda ungwiro. (Aroma 5:12) Koma “Mulungu anawapsera mtima” Aroni ndi Miriamu pamene anaimba mlandu Mose naiŵala kuti iye, osati iwo, ndiye anali ndi thayo lopatsidwa ndi Mulungu. (Numeri 12:7-9) Lerolino, Akristu okhulupirika amagwirizana ndi “atsogoleri” chifukwa chakuti nchimene Yehova amafuna. (Ahebri 13:7, 17) Umboni wa kukhulupirika kwathu umaphatikizapo kufika pamisonkhano mokhazikika ndi kupereka ndemanga ‘zimene zimafulumiza ena kuchikondi ndi ntchito zabwino.’—Ahebri 10:24, 25.
Khalani Omangirira
16. Kodi nchikhumbo chakuchitira ena chiyani chimene chiyenera kutisonkhezeranso kutumikira Yehova mokhulupirika?
16 Chikhumbo chakukhala womangirira ena chiyeneranso kutisonkhezera kutumikira Yehova mokhulupirika. Paulo analemba kuti: “Chidziŵitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.” (1 Akorinto 8:1) Popeza kuti mtundu wina wa chidziŵitso unatukumula okhala nacho, Paulo ayenera kukhala anatanthauza kuti chikondi chimamangiriranso awo osonyeza mkhalidwewo. Bukhu lolembedwa ndi Aprofesa aŵiri Weiss ndi English limati: “Munthu amene ali wokhoza kukonda, kaŵirikaŵiri amakondedwa nayenso. Kukhoza kwa kufunira zabwino ndi kulingalira ena m’mbali iriyonse ya moyo . . . kuli ndi chiyambukiro chapadera chomangirira pa munthu amene amasonyeza kulingalira ena koteroko limodzinso ndi pa munthu amene amachitiridwa zimenezo ndipo motero kumadzetsa chisangalalo kwa onse aŵiri.” Mwakusonyeza chikondi, timamangirira ena ndi ife eni, monga kwasonyezedwa ndi mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
17. Kodi chikondi chimamangirira motani, ndipo chidzatiletsa kuchitanji?
17 Pa 1 Akorinto 8:1, Paulo anagwiritsira ntchito liwu Lachigiriki lakuti a·gaʹpe, lotanthauza chikondi chozikidwa m’malemba. Chimamangirira, popeza kuti chikhala chilezere ndi chokoma mtima, chikwirira ndi kupirira zinthu zonse, ndipo sichilephera konse. Chikondi chimenechi chimachotsa malingaliro ovulaza, monga ngati kunyada ndi kaduka. (1 Akorinto 13:4-8) Chikondi choterocho chidzatithandiza kupeŵa kung’ung’udza za abale athu, amene ali opanda ungwiro monga momwe tiriri. Chidzatiletsa kufanana ndi “anthu osapembedza” amene “anakwaŵira m’tseri” pakati pa Akristu owona a m’zaka za zana loyamba. Anthu ameneŵa ‘anapeputsa ufumu nachitira mwano aulemerero,’ mwachiwonekere akung’ung’udza za anthu onga oyang’anira odzozedwa Achikristu amene anali ndi ulemerero winawake woikidwa pa iwo. (Yuda 3, 4, 8) Mokhulupirika kwa Yehova, tisagonjere konse kuchiyeso chakuchita chirichonse chofanana ndi zimenezo.
Kanizani Mdyerekezi!
18. Kodi Satana amakhumba kuchitanji kwa anthu a Yehova, koma kodi nchifukwa ninji sangakhoze kutero?
18 Chidziŵitso chakuti Satana amafuna kuwononga kugwirizana kwathu monga anthu a Mulungu chiyenera kuwonjezera kutsimikiza kwathu kutumikira Yehova mokhulupirika. Satana amakhumbadi kufafaniza anthu a Mulungu onse, ndipo atumiki a Mdyerekezi apadziko lapansi nthaŵi zina amapha alambiri owona. Koma Mulungu sadzalola Satana kufafaniza onse psiti. Yesu anafa kuti “akamuwononge iye amene ali nayo mphamvu ya imfa, ndiye Mdyerekezi.” (Ahebri 2:14) Malo a Satana akuchitirako mphamvu yake achepetsedwa kwambiri makamaka chiyambire kugwetsedwa kwake kuchokera kumwamba pambuyo pakulongedwa ufumu kwa Kristu mu 1914. Ndipo panthaŵi yoikidwiratu ya Yehova, Yesu adzawononga Satana ndi gulu lake.
19. (a) Kodi ndichenjezo lotani lonena za zoyesayesa za Satana limene magazini ano anapereka zaka zambiri zapitazo? (b) Kuti tipeŵe misampha ya Satana, kodi tiyenera kupereka chisamaliro chotani pochita ndi okhulupirira anzathu?
19 Magazini ano panthaŵi ina anachenjeza kuti: “Ngati Satana, mdyerekeziyo, angachititse chisokonezo pakati pa anthu a Mulungu, kuwachititsa kukangana ndi kumenyana pakati pawo, kapena kusonyeza ndi kukulitsa maganizo adyera amene akawonongetsa chikondi chaubale, pamenepo akakhoza kupeza chipambano m’kuwalikwira.” (The Watch Tower ya May 1, 1921, tsamba 134) Tisamulole konse Mdyerekezi kuwononga kugwirizana kwathu, mwinamwake mwakutiloŵetsa m’kusinjirira, kapena kumenyana. (Levitiko 19:16) Tisalole konse Satana kutigonjetsa mwanjira yakuti ife enife tivulaze otumikira Yehova mokhulupirika kapena kuvutitsa kwambiri moyo wawo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:10, 11.) Mmalomwake, tiyeni tigwiritsire ntchito mawu a Petro akuti: “Khalani odzisungira, dikirani, mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: Ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Petro 5:8, 9) Mwakuima nji motsutsana ndi Satana, tikhoza kusunga kugwirizana kwathu kodalitsidwa monga anthu a Yehova.—Salmo 133:1-3.
Dalirani Mulungu Mwapemphero
20, 21. Kodi kudalira Yehova mwapemphero kumagwirizana motani ndi kumtumikira mokhulupirika?
20 Kudalira Mulungu mwapemphero kudzatithandiza kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Pamene tiwona kuti akuyankha mapemphero athu, timakokeredwa pafupi naye. Paulo anafulumiza kudalira Yehova Mulungu mwapemphero pamene analemba kuti: “Ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.” (1 Timoteo 2:8) Mwachitsanzo, nkofunika chotani nanga kuti akulu adalire Mulungu mwapemphero! Chisonyezero chotero cha kukhulupirika kwa Yehova pamene akumana kukambitsirana nkhani za mpingo chidzathandiza kupeŵa makani osatha ndi kupsetsana mtima kothekera kubukapo.
21 Kudalira Yehova Mulungu mwapemphero kumatithandiza kusamalira mathayo athu muutumiki wake. Mwamuna wina amene anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka makumi ambiri anati: “Kufunitsitsa kwathu kulandira gawo lirilonse lopatsidwa kwa ife m’gulu la Mulungu lapadziko lonse, ndi kukhalabe kwathu pagawo lathulo, osagwedezeka, kumadzetsa chiyanjo cha Yehova pazoyesayesa zathu zowona mtima. Ngakhale ngati ntchito imene tagaŵiridwa iwonekera kukhala yochepa, kaŵirikaŵiri zimachitika kuti popanda kuichita mokhulupirika, mautumiki ena ambiri ofunika sakanachitidwa. Chifukwa chake ngati tikhala odzichepetsa ndi okondweretsedwa m’kulemekeza dzina la Yehova ndipo osati lathu, pamenepo tikhoza kukhala otsimikizira kuti nthaŵi zonse tidzakhala “okhazikika, osasunthika, akuchuluka m’ntchito ya [Yehova, NW]”—1 Akorinto 15:58.
22. Kodi madalitso ochuluka a Yehova ayenera kuyambukira motani kukhulupirika kwathu?
22 Mosasamala kanthu ndi zimene timachita muutumiki wa Yehova, ndithudi, sitingathe kumlipira zimene watichitira. Tiri osungika chotani nanga m’gulu la Mulungu, tiri ozingidwa ndi mabwenzi ake! (Yakobo 2:23) Yehova watidalitsa ndi kugwirizana kochokera m’chikondi chaubale chozama kwambiri kwakuti Satana iye mwiniyo sangathe kuchizula. Chifukwa chake timamatiretu kwa Atate wathu wakumwamba ndi kugwirira ntchito pamodzi monga anthu ake. Tsopano ndi m’nthaŵi zomka muyaya, titumikiretu Yehova mokhulupirika.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kukhulupirika kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndizinthu ziti zimene ziyenera kutifulumiza kutumikira Yehova mokhulupirika?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kumkaniza Mdyerekezi?
◻ Kodi ndimotani mmene pemphero lingatithandizire kukhala atumiki okhulupirika a Yehova?
[Chithunzi patsamba 23]
Atumiki okhulupirika a Yehova samalola Mdani wawo wonga mkango, Mdyerekeziyo, kuswa kugwirizana kwawo