2 Samueli
22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamupulumutsa kwa adani ake onse+ ndiponso mʼmanja mwa Sauli.+ 2 Iye anati:
“Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo+ ndiponso Wondipulumutsa.+
3 Mulungu wanga ndi thanthwe langa,+ ine ndimathawira kwa iye,
Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga ya chipulumutso* ndi malo anga achitetezo.*+
Komanso ndi malo anga othawirako,+ mpulumutsi wanga+ amene amandipulumutsa kwa anthu achiwawa.
4 Ndimapempha Yehova, amene ndi woyenera kutamandidwa, kuti andithandize.
Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.
Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,
Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
8 Dziko lapansi linayamba kugwedezeka ndiponso kunjenjemera;+
Maziko akumwamba anagwedezeka.+
Anagwedezeka chifukwa Mulungu anakwiya.+
9 Utsi unatuluka mʼmphuno mwake,
Ndipo moto wowononga unatuluka mʼkamwa mwake;+
Makala oyaka anatuluka mwa iye.
11 Iye anakwera pakerubi+ ndipo anabwera akuuluka.
Anaonekera pamapiko a mngelo.*+
13 Mʼkuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.
14 Kenako Yehova ali kumwamba anayamba kugunda ngati mabingu;+
Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke.+
16 Pansi pa nyanja panaonekera;+
Maziko a dziko lapansi anaonekera chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova,
Chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwake.+
22 Chifukwa ndasunga njira za Yehova,
Ndipo sindinachite chinthu choipa kwambiri, chomwe ndi kusiya Mulungu wanga.
25 Yehova andipatse mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa,+
Komanso chifukwa choti ndine wosalakwa pamaso pake.+
26 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.+
Munthu wamphamvu komanso wosalakwa, mumamuchitira mwachilungamo.+
27 Munthu woyera, mumamusonyeza kuti ndinu woyera,+
Koma munthu wamaganizo opotoka mumamusonyeza kuti ndinu wochenjera.+
30 Ndi thandizo lanu ndingalimbane ndi gulu la achifwamba;
Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+
Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
32 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+
Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+
38 Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapha onse;
Ndipo sindidzabwerera mpaka nditawafafaniza.
42 Amafuula kuti athandizidwe, koma palibe angawapulumutse;
Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.+
43 Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi.
Ndidzawapondaponda ngati matope amumsewu.
44 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga ondipezera zifukwa.+
Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu ya anthu.+
Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
45 Anthu ochokera mʼdziko lina adzandiweramira mwamantha;+
Zimene adzamve zokhudza ine zidzachititsa kuti azindimvera.
46 Anthu ochokera mʼdziko lina adzachita mantha;
Iwo adzatuluka mʼmalo awo otetezeka akunjenjemera.
47 Yehova ndi wamoyo! Litamandike Thanthwe langa!+
Mulungu wanga, yemwe ndi thanthwe limene limandipulumutsa, alemekezeke.+
48 Mulungu woona amabwezera adani anga;+
Iye amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera;+
49 Iye amandipulumutsa kwa adani anga.