Tifunika Kukhala Maso Kwambiri Tsopano
“Chifukwa chake dikirani [“nthaŵi zonse,” NW], pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”—MATEYU 24:42.
1, 2. N’chiyani chikusonyeza kuti tikukhala kumapeto kwa dongosolo lino la zinthu?
“ZOCHITIKA m’zaka za m’ma 1900 zinakhudzidwa kwambiri ndi nkhondo,” anatero mwamuna wina wolemba mabuku dzina lake Bill Emmott. Ngakhale kuti anavomereza kuti m’mbuyo monsemu anthu akhala akuvutika chifukwa cha nkhondo ndi ziwawa, iye ananenanso kuti: “Ndi mmenenso zinakhalira m’zaka za m’ma 1900, chomwe chinasintha m’zakazi ndicho kuopsa kwake kwa zinthu zimenezi. Nkhondo yoyambirira yomwe inakhudzadi dziko lonse inamenyedwa m’zaka zimenezi . . . Ndipo, ndiye ngati kuti kunali kuphera mphongo mfundoyi, m’zaka zimenezi simunamenyedwe nkhondo yotero imodzi yokha, koma nkhondo ziŵiri.”
2 Yesu Kristu analosera nkhondo za pakati pa ‘mtundu ndi mtundu wina ndiponso ufumu ndi ufumu wina.’ Koma iyi ndi mbali imodzi chabe ya ‘chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwa Kristu ndiponso cha mapeto a dongosolo lino la zinthu.’ Mu ulosi waukulu umenewu, Yesu anatchulanso njala, milili, ndi zivomezi. (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:6, 7, 10, 11) M’njira zambiri, mavuto ameneŵa tsopano akukhudza madera akuluakulu komanso akuvutitsa kwambiri. Kuipa kwa anthu kwafala kwambiri, monga momwe timaonera pa zomwe iwo amachitira Mulungu ndiponso anthu anzawo. Tikuona kutha kwa makhalidwe abwino ndiponso kuwonjezeka kwa upandu ndi ziwawa. Anthu tsopano akukonda ndalama m’malo mokonda Mulungu, atanganidwa ndi zosangalatsa. Zonsezi ndi umboni wakuti tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa.’—2 Timoteo 3:1-5.
3. Kodi “zizindikiro za nyengo ino” ziyenera kutikhudza motani?
3 Kodi kuipiraipira kwa kachitidwe ka zinthu ka anthu mumakaona motani? Anthu ambiri alibe nazo ntchito kapena kumva chisoni ndi zinthu zoipa zimene zikuchitika masiku ano. Anthu otchuka ndiponso anzeru a dzikoli sazindikira “zizindikiro za nyengo ino”; ndipo nawonso atsogoleri achipembedzo sakuwaphunzitsa bwino anthu awo za nkhaniyi. (Mateyu 16:1-3) Koma Yesu analimbikitsa om’tsatira ake kuti: “Chifukwa chake dikirani nthaŵi zonse, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:42) Pano Yesu sikuti akungotilimbikitsa kukhala odikira, koma ‘kudikira nthaŵi zonse.’ Kuti tikhale odikira nthaŵi zonse, tiyenera kukhala atcheru ndi ogalamuka. Kuti tichite zimenezi pamafunika zambiri osati kungovomereza chabe kuti tikukhala m’masiku otsiriza kapenanso kungozindikira kuti tili m’nthaŵi zoŵaŵitsa. Tifunika kutsimikizadi kuti “chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” (1 Petro 4:7) Tikatero m’pamene tidzaone kufunika kokhala maso kwambiri. Motero funso lofunika kuti tiliganizire ndi lakuti: ‘N’chiyani chingatithandize kukhala otsimikiza kwambiri kuti mapeto ali pafupi?’
4, 5. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala otsimikiza kwambiri kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ali pafupi, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi chinthu chimodzi chomwe chikufanana pakati pa masiku a Nowa ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu n’chiti?
4 Taonani mmene zinthu zinalili patangotsala pang’ono kuchitika chinthu chachilendo kwambiri m’mbiri ya anthu—Chigumula chachikulu cha m’masiku a Nowa. Anthu anali oipa kwambiri moti Yehova “anavutika m’mtima mwake.” Analengeza kuti: “Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi.” (Genesis 6:6, 7) Ndipo anaterodi. Pofotokoza kufanana kwa nthaŵiyo ndi masiku athu ano, Yesu anati: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika [“kukhalapo,”] kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:37.
5 N’zomveka kunena kuti Yehova akuvutika mumtima ndi dzikoli ngati momwe anavutikira ndi dziko la m’nthaŵi ya Chigumula chisanadze. Popeza kuti anawononga dziko losapembedza la m’masiku a Nowa, mosakayikira adzawononganso dziko loipa la masiku ano. Kumvetsa kufanana komwe kulipo pakati pa nthaŵi imeneyo ndi masiku athu ano, kuyenera kutithandiza kukhala otsimikiza kwambiri kuti mapeto a dzikoli ali pafupi. Ndiyeno, kodi ndi zinthu ziti zomwe zikufanana? Pali zinthu zokwana zisanu. Choyamba n’chakuti chenjezo la chiwonongeko chomwe chikubwera likuperekedwa mosapita m’mbali.
Anachenjezedwa za “Zinthu Zisanapenyeke”
6. Kodi n’chiyani chimene Yehova anafuna kuchita m’masiku a Nowa?
6 M’masiku a Nowa, Yehova analengeza kuti: “Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthaŵi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi aŵiri.” (Genesis 6:3) Kulengezedwa kwa lamulo la Mulungu limeneli m’chaka cha 2490 B.C.E. kunali chiyambi cha mapeto a dziko losapembedza limenelo. Tangoganizani tanthauzo la zimenezi kwa anthu a m’nthaŵi imeneyo! Panangotsala zaka 120 zokha ndipo kenako Yehova anali kudzabweretsa “chigumula cha madzi pa dziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, mmene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo.”—Genesis 6:17.
7. (a) Kodi Nowa anachitanji ndi chenjezo la Chigumula? (b) Kodi tiyenera kuchitanji ndi machenjezo a mapeto a dongosolo lino la zinthu?
7 Nowa analandira chenjezo la chiwonongeko kudakali zaka makumi angapo chiwonongekocho chisanafike, ndipo anagwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi imeneyo kukonza za chipulumutso. Mtumwi Paulo anati: ‘Pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, [Nowa] pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.’ (Ahebri 11:7) Nanga ife? Patha zaka pafupifupi 90 kuchokera pamene masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu anayamba mu 1914. Tilidi ‘m’nthaŵi ya chimaliziro.’ (Danieli 12:4) Kodi tiyenera kuchitanji ndi machenjezo amene akhala akuperekedwa? “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse,” limatero Baibulo. (1 Yohane 2:17) Motero ino ndiyo nthaŵi yochita chifuniro cha Yehova mwachangu kwambiri.
8, 9. Kodi ndi machenjezo otani amene akuperekedwa m’nthaŵi zathu zino, ndipo akulengezedwa motani?
8 Masiku ano, omwe akuphunzira Baibulo moona mtima adziŵa kuchokera m’Malemba ouziridwa kuti dongosolo lino la zinthu likupita kuchiwonongeko. Kodi ife timakhulupirira zimenezi? Taonani zomwe Yesu Kristu ananena momveka bwino: “Padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Yesu ananenanso kuti adzabwera monga Woweruza woikidwa ndi Mulungu ndipo adzalekanitsa anthu monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Omwe adzapezeke kuti ngosayenerera ‘adzamka ku chilango cha nthaŵi zonse; koma olungama kumoyo wa nthaŵi zonse.’—Mateyu 25:31-33, 46.
9 Yehova wakhala akulengeza machenjezo ameneŵa mwa kuwakumbutsa anthu panthaŵi yake kudzera m’chakudya chauzimu choperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Komanso, anthu aliwonse, mtundu uliwonse, fuko lililonse, ndiponso lilime lililonse akupemphedwa kuti ‘aope Mulungu, ndi kum’patsa ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruzo chake.’ (Chivumbulutso 14:6, 7) Mbali yaikulu ya uthenga wa Ufumu womwe ukulalikidwa padziko lonse ndi Mboni za Yehova ndi chenjezo lakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzachotsa maulamuliro a anthu. (Danieli 2:44) Chenjezo limeneli silofunika kuliona mwachibwanabwana. Mulungu Wamphamvuyonse amakwaniritsa mawu ake nthaŵi zonse. (Yesaya 55:10, 11) Anakwaniritsa mawu ake m’masiku a Nowa, ndipo achitanso chimodzimodzi masiku athu ano.—2 Petro 3:3-7.
Chiwerewere Chinachuluka Kwambiri
10. Kodi m’masiku a Nowa chiwerewere chinafika pati?
10 Nthaŵi yathu ino ikufanana ndi masiku a Nowa pankhani inanso. Yehova analamula mwamuna ndi mkazi woyambirira kuti ‘adzaze dziko lapansi’ ndi anthu, pogwiritsa ntchito moyenera mphamvu zawo za kugonana zomwe Mulungu anawapatsa m’makonzedwe abanja. (Genesis 1:28) M’masiku a Nowa, angelo osamvera anapatsira anthu chilakolako chosayenera cha kugonana. Anabwera padziko lapansi, m’matupi a anthu, nagona ndi akazi okongola, n’kubala ana omwe anali mbali ina anthu, mbali ina ziwanda—Anefili. (Genesis 6:2, 4) Tchimo la angelo okonda chiwerewere ameneŵa analifananitsa ndi makhalidwe onyansa a mu Sodomu ndi Gomora. (Yuda 6, 7) Motero, chiwerewere chinafala m’masiku amenewo.
11. Kodi ndi makhalidwe otani omwe akupangitsa kuti nthaŵi zathu zino zifanane ndi masiku a Nowa?
11 Nanga bwanji za makhalidwe a masiku ano? M’masiku otsiriza ano, moyo wa anthu ambiri ndi wokonda kugonana. Paulo anawafotokoza bwino anthu otereŵa kuti “sazindikiranso kanthu konse”; ambiri adzipereka kuti “akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.” (Aefeso 4:19) Zinthu zolaula, anthu kugonana asanakwatirane, kugwirira ana, ndiponso kugonana amuna kapena akazi okhaokha n’zofala kwambiri. Ena ayamba kale ‘kulandira mwa iwo okha mphoto yakuyenera kulakwa kwawo’ kudzera m’matenda opatsirana mwa kugonana, kutha kwa mabanja, ndiponso mavuto ena ndi ena.—Aroma 1:26, 27.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kudana ndi chiopa?
12 M’masiku a Nowa, Yehova anadzetsa Chigumula chachikulu ndi kuwononga dziko lokonda kugonana la masiku amenewo. Tisaiwale mfundo yakuti masiku ano ndi ofanana ndendende ndi mmene masiku a Nowa analili. ‘Chisautso chachikulu’ chomwe chikubwera chidzasesa padziko lapansi pano anthu ‘adama, achigololo, olobodoka ndi zoipa, ndi odziipsa ndi amuna.’ (Mateyu 24:21; 1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Ndiyetu m’pofunika kwambiri kuti tiphunzire kudana ndi choipa ndi kupeŵa malo amene angatichititse chiwerewere.—Salmo 97:10; 1 Akorinto 6:18.
Dziko Lapansi “Linadzala ndi Chiwawa”
13. Kodi n’chifukwa chiyani dziko ‘linadzala ndi chiwawa’ m’masiku a Nowa?
13 Pofotokoza khalidwe linanso la m’masiku a Nowa, Baibulo limati: “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” (Genesis 6:11) Sikuti chiwawa chinali chachilendo kwenikweni. Mwana wa Adamu Kaini anapha mbale wake wolungama. (Genesis 4:8) Posonyeza mzimu wachiwawa wa m’masiku ake, Lameke analemba ndakatulo yosonyeza mmene iye anaphera mnyamata wina, mwina pofuna kudziteteza. (Genesis 4:23, 24) Chomwe chinali chachilendo m’masiku a Nowa chinali kuchuluka kwa ziwawazo. Ana osamvera a Mulungu omwe anali angelo atakwatira akazi padziko lapansi ndi kubala ana, Anefili, chiwawa chinachuluka kuposa kale lonse. Baibulo la New World Translation limasonyeza kuti m’chinenero choyambirira cha Chihebri dzina la zimphona zachiwawazi limatanthauza “Ogwetsa”—“anthu omwe anali kugwetsa anzawo.” (Genesis 6:4) Motero, dziko ‘linadzala ndi chiwawa.’ (Genesis 6:13) Tangoganizirani mavuto omwe Nowa ayenera kuti anakumana nawo polera ana ake m’dziko lotero. Komabe, Nowa anasonyeza kuti anali ‘wolungama pamaso pa Yehova m’mbadwo umenewo.’—Genesis 7:1.
14. Kodi dziko “ladzala ndi chiwawa” motani?
14 Ziwawa zakhala zikuchitika m’mbiri yonse ya anthu. Koma mofanana ndi mmene zinalili m’masiku a Nowa, m’masiku athu ano mukuchitikanso ziwawa kwambiri kusiyana ndi n’kale lonse. Nthaŵi zonse timamva za ziwawa zochitika panyumba, zauchigaŵenga, kupulula mafuko a anthu, ndiponso kupha anthu ambiri popanda zifukwa zenizeni. Komanso miyoyo miyandamiyanda ya anthu yatayika chifukwa cha nkhondo. Dziko ladzalanso ndi chiwawa. Chifukwa chiyani? Kodi n’chiyani chachititsa kuti ziwawa ziwonjezeke? Yankho lake likusonyezanso kufanana kwina kwa masiku athu ano ndi masiku a Nowa.
15. (a) Kodi n’chiyani chachititsa kuti ziwawa zichuluke m’masiku otsiriza ano? (b) Kodi tili ndi chikhulupiriro chakuti zotsatira zake zikhala zotani?
15 Ufumu wa Mulungu Waumesiya utakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, Mfumu yomwe inaikidwa, Yesu Kristu, inagwira ntchito ina yapadera kwambiri. Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba kubwera padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9-12) Chigumula chisanadze, angelo osamvera anasiya okha malo awo kumwamba; koma nthaŵi yathu ino, iwo anachita kuthamangitsidwa. Komanso, tsopano sangathe kukhala ndi matupi a anthu padziko lapansi pano kuti asangalale ndi zokhumba zawo zonyansa zakuthupi. Motero, chifukwa chothedwa nzeru, ukali, komanso mantha ndi chiwonongeko chomwe chikubwera, iwo akulimbikitsa anthu ndi mabungwe kuchita zinthu zauchigaŵenga ndiponso ziwawa zomwe sitingayembekezere munthu kuchita ndipo akuchita zimenezi kuposanso mmene zinkachitikira m’masiku a Nowa. Yehova anawononga dziko lomwe linalipo Chigumula chisanadze angelo osamvera pamodzi ndi ana awo atalidzaza ndi zoipa. Sitikukayikira m’pang’ono pomwe kuti achitanso chimodzimodzi m’masiku athu ano. (Salmo 37:10) Koma anthu omwe ali maso masiku ano akudziŵa kuti kuwomboledwa kwawo kwayandikira.
Uthenga Ukulalikidwa
16, 17. Kodi chinthu chachinayi chomwe chikufananitsa masiku athu ano ndi masiku a Nowa n’chiyani?
16 Mfundo yachinayi yomwe ikufananitsa masiku ano ndi dziko lomwe linalipo Chigumula chisanadze ikuoneka m’ntchito yomwe Nowa anapatsidwa. Nowa anakhoma chingalawa chachikulu kwambiri. Analinso “mlaliki.” (2 Petro 2:5) Kodi ankalalikira uthenga wotani? Mwachionekere, mfundo zina zaulaliki wa Nowa zinali zolimbikitsa anthu kuti atembenuke mitima ndiponso zowachenjeza za chiwonongeko chomwe chinali kubwera. Yesu anati anthu a m’masiku a Nowa ‘sanadziŵe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, nichipululutsa iwo onse.’—Mateyu 24:38, 39.
17 Mofanana ndi zimenezi, pamene Mboni za Yehova zikuyesetsa kugwira ntchito yawo yolalikira, uthenga wa Ufumu wa Mulungu ukulengezedwa padziko lonse. Anthu, pafupifupi kulikonse padziko lapansili, angathe kumva ndi kuŵerenga uthenga wa Ufumu m’chinenero chawo. Magazini ya Nsanja ya Olonda yolengeza Ufumu wa Yehova, tsopano ikusindikizidwa makope oposa 25,000,000 m’zinenero zoposa 140. Inde, uthenga wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa “padziko lonse lapansi, [kuti] ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” Ntchito imeneyi ikadzagwiridwa kufika pamene Mulungu akufuna, chimaliziro chidzafikadi.—Mateyu 24:14.
18. Kodi zomwe anthu ambiri akuchita ndi ntchito yathu yolalikira zikufanana motani ndi zomwe anthu ankachita m’masiku a Nowa?
18 Tikalingalira mmene anthu analili opanda chidwi ndi zinthu zauzimu ndiponso makhalidwe oipa omwe analipo Chigumula chitayandikira, n’zosavuta kuona mmene anthu osamvera ankasekera ndiponso kuchitira chipongwe banja la Nowa. Koma chimaliziro chinafikabe. Chimodzimodzinso masiku otsiriza ano, “onyoza ndi kuchita zonyoza” afala kwambiri. “Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala,” limatero Baibulo. (2 Petro 3:3, 4, 10) Lidzafika ndithu panthaŵi yomwe inakonzedwa. Silidzachedwa. (Habakuku 2:3) N’chanzeru kwambiri kukhala odikira nthaŵi zonse.
Anthu Ochepa Okha Anapulumuka
19, 20. Kodi tingafananitse motani Chigumula ndi chiwonongeko cha dongosolo lino la zinthu?
19 Kufanana kwa masiku a Nowa ndi masiku athu ano sikuti kukuthera pa kuipa kwa anthu ndi kuwonongedwa kwawo ayi. Mofanana ndi kuti panali anthu opulumuka Chigumula, padzakhalanso opulumuka mapeto a dongosolo lino la zinthu. Anthu omwe anapulumuka Chigumula anali anthu ofatsa omwe moyo wawo unasiyana ndi moyo wa anthu ena ambiri. Anamvera chenjezo la Mulungu, n’kudzilekanitsa ndi dziko loipa lapanthaŵiyo. Baibulo limati: “Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova. . . . Anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake.” (Genesis 6:8, 9) Pa anthu onse, banja limodzi lokha, “[anthu] oŵerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.” (1 Petro 3:20) Ndipo Yehova Mulungu analamula anthu amenewo kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.”—Genesis 9:1.
20 Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti padzakhala “khamu lalikulu” limene ‘lidzatuluka m’chisautso chachikulu.’ (Chivumbulutso 7:9, 14) Kodi m’khamu lalikulu mudzakhala anthu angati? Yesu mwiniyo ananena kuti: “Chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Poyerekeza ndi anthu sikisi biliyoni omwe alipo padziko lapansi pano, opulumuka chisautso chachikulu chomwe chikubweracho adzakhala ochepa. Koma iwo angadzapatsidwenso mwayi wofanana ndi umene unaperekedwa kwa opulumuka Chigumula. Opulumukawo angadzapatsidwe mwayi kwa kanthaŵi ndithu woti abereke ana monga mbali ya dziko lapansi latsopano.—Yesaya 65:23.
“Dikirani Nthaŵi Zonse”
21, 22. (a) Kodi mwapindula motani ndi kuphunzira nkhani ya Chigumula? (b) Kodi lemba la chaka cha 2004 ndi liti, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo omwe likupereka?
21 Ngakhale kuti Chigumula chingaoneke kuti chinachitika kale kwambiri, koma chikutipatsa chenjezo lomwe sitiyenera kulinyalanyaza. (Aroma 15:4) Kufanana komwe kulipo pakati pa masiku a Nowa ndi masiku athu ano kuyenera kutithandiza kuzindikira bwino tanthauzo la zimene zikuchitikazi ndi kutithandiza kukhala tcheru ndi kudza monga mbala kwa Yesu kudzaweruza oipa.
22 Masiku ano, Yesu Kristu akutsogolera ntchito yaikulu yomanga mwauzimu. Pofuna kuti olambira oona adzatetezedwe ndi kupulumuka, pali paradaiso wauzimu yemwe ali ngati chingalawa. (2 Akorinto 12:3, 4) Kuti tidzapulumutsidwe pa chisautso chachikulu, tiyenera kupitiriza kukhala m’paradaiso ameneyu. Kunja kwa paradaiso wauzimuyu kuli dziko la Satana, lomwe lili tcheru kuti litenge aliyense yemwe akugona mwauzimu. M’pofunika kwambiri kuti ‘tidikire nthaŵi zonse’ ndi kukhala okonzekeratu tsiku la Yehova.—Mateyu 24:42, 44.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Yesu analimbikitsa kuchitanji ponena za kubwera kwake?
• Kodi Yesu anayerekezera nthaŵi ya kukhalapo kwake ndi chiyani?
• Kodi nthaŵi zathu zino ndi zofanana motani ndi masiku a Nowa?
• Kodi tikaona kufanana komwe kulipo pakati pa masiku a Nowa ndi masiku athu ano kuyenera kukhudza motani changu chathu?
[Mawu Otsindika patsamba 18]
Lemba la chaka cha 2004 likhala lakuti: ‘Dikirani . . . Khalani okonzekeratu.’—Mateyu 24:42, 44.
[Chithunzi patsamba 15]
Nowa anamvera chenjezo la Mulungu. Kodi ife timachita mofananamo?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
“Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kukhalapo kwake kwa Mwana wa munthu”