Mutu 21
Tsiku Lachiweruza ndi Pambuyo Pake
1. Kodi lingaliro lofala la Tsik Lachiweruzo nlotani?
KODI TSIKU LACHIWERUZO limapereka chithunzithuzi chotani ku maganizo anu? Ena amaganizira mpando wachifumu waukulu, ndipo pamaso pake mzere wautali wa anthu amene aukitsidwa kwa akufa. Pamene munthu aliyense akudutsa pamaso pa mpando wachifumuwo, iye akuweruzidwa mwa ntchito zake zakale, zonse zimene zalembedwa m’bukhu la Woweruzayo. Mwa zinthu zimene anachita, munthuyo akutumizidwa mwina kumwamba kapena kuhelo wamoto.
2. (a) Kodi ndani amene walinganiza Tsiku Lachiweruzo? (b) Kodi iye anaika yani kukhala woweruza?
2 Komabe, Baibulo limapereka chithunzithunzi chosiyana kwambiri cha Tsiku Lachiweruzo. Siliri tsiku lonthunthumiridwa kapena kuwopedwa. Wonani zimene Baibulo limanena ponena za Mulungu: “Anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu.” (Machitidwe 17:31) Ndithudi, woweruza woikidwa ndi Mulungu ameneyu ndiye Yesu Kristu.
3. (a) Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti Kristu adzakhala wopanda tsankho m’kuweruza kwake? (b) Kodi anthu adzaweruzidwa pa maziko otani?
3 Tingatsimikizire kuti Kristu adzakhala wopanda tsankho ndi wolungama m’kuweruza kwake. Ulosi wonena za iye pa Yesaya 11:3, 4 umatitsimikiziritsa zimenezi. Motero, mosemphana ndi lingaliro lofala, iye sadzaweruza anthu pa maziko a machimo awo akale, ambiri ake amene angakhale atachitidwa mosadziwa. Baibulo limafotokoza kuti pa imfa munthu amamasuka kapena kumasulidwa ku machimo alionse amene wachita. Limati: “Iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.” (Aroma 6:7) Zimenezi zikutanthauza kuti pamene munthu aukitsidwa iye adzaweruzidwa pa maziko a zimene akuchita mkati mwa Tsiku Lachiweruzo, osati pa zimene anachita asanafe.
4. (a) Kodi Tsiku Lachiweruzo lidzakhala la utali wotani? (b) Kodi ndani amene adzakhala oweruza limodzi ndi Kristu?
4 Chifukwa cha chimenecho, Tsiku Lachiweruzo siliri tsiku lenileni la maola 24. Baibulo limamveketsa zimenezi pamene limatchula awo amene adzakhala ndi Yesu Kristu m’kuchita kuweruzako. (1 Akorinto 6:1-3) “Ndinawona mipando yachifumu,” akutero wolemba Baibuloyo, “ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro.” Oweruza amenewa ndiwo atsatiri odzozedwa okhulupirika a Kristu amene, monga momwe Baibulo likupitirizira kunena, “anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi.” Motero Tsiku Lachiweruzo lidzakhala zaka 1,000 kutalika kwake. Ndilo nyengo imodzimodziyo ya zaka 1,000 mkati mwa imene Kristu ndi atsatiri ake odzodzedwa okhulupirika 144,000 adzalamulira monga “miyamba yatsopano” pa “dziko [lapansi] latsopano.”—Chivumbulutso 20:4, 6; 2 Petro 3:13.
5, 6. (a) Kodi wamasalmo Wabaibulo anafotokoza motani Tsiku Lachiweruzo? (b) Kodi moyo udzakhala wotani padziko lapansi mkati mwa Tsiku Lachiweruzo?
5 Yang’anani pamasamba ano. Iwo akupereka lingaliro lina la mmene Tsiku lachiweruzo lidzakhalira labwino kwambiri kwa anthu. Wamasalmo Wabaibulo analemba za nthawi yabwino kwambiri imeneyo: “Munda ukondwerere ndi zonse ziri m’mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera; pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi: adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi chowonadi.”—Salmo 96:12, 13.
6 Mkati mwa Tsiku Lachiweruzo awo amene akupyola Harmagedo adzagwira ntchito kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Akufa adzalandiridwa m’paradaiso ameneyu. (Luka 23:43) Kudzakhala chimwemwe chotani nanga pamene mabanja olekanitsidwa kwa nthawi yaitali ndi imfa akugwirizanitsidwanso! Inde, nkokondweretsa chotani nanga kukhala mu mtendere, kukhala ndi thanzi labwino ndi kulandira chilangizo ponena za zifuno za Mulungu! Baibulo limati: “Pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9) Mkati mwa Tsiku Lachiweruzo anthu onse adzaphunzira ponena za Yehova, ndipo iwo adzapatsidwa mpata uliwonse kuti amumvere ndi kumtumikira.
7. Mkati mwa Tsiku Lachiweruzo, kodi nchiyani chimene chidzachitikira awo amene akusankha kutumikira Mulungu ndi awo amene akukana kutero?
7 Ndimo m’mikhalidwe yaparadaiso yoteroyo m’mene Yesu Kristu nd mafumu anzake 144,000 adzaweruza anthu. Anthu amene akusankha kutumikira Yehova adzakhala okhoza kulandira moyo wosatha. Koma, ngakhale mkati mwa mikhalidwe yabwino koposa imeneyi, ena adzakana kutumikira Mulungu. Monga momwe Malemba akunenera: “Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m’dziko la machitidwe owongoka, iye adzangochimwa.” (Yesaya 26:10) Motero atapatsidwa mpata wokwanira wa kusintha njira zawo ndi kuphunzira chilungamo, oipa oterowo adzaphedwa. Ena adzaphedwa ngakhale Tsiku Lachiweruzo lisanathe. (Yesaya 65:20) Iwo sadzaloledwa kukhalapobe kuti awononge kapena aipitse dziko lapansi laparadaiso.
8. Kodi mkhalidwe wa kudzisungira wa anthu a ku Sodomu unali wotani?
8 Ndithudi udzakhala mwawi waukulu kwambiri wa kuukitsidwira padziko lapanso mkati mwa Tsiku Lachiweruzo lalikulu la Yehova. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti udzakhala mwawi umene saali onse amene adzasangalala nawo. Mwachitsanzo, talingalirani za anthu a Sodomu wakale. Baibulo limanena kuti anthu a Sodomu anafunafuna kukhala ndi maunansi akugonana ndi “amuna” amene anali kuchezera Loti. Kudzisungira kwawo kwachisembwere kunali kopambanitsa kwambiri kotero kuti ngakhale pamene iwo mozizwitsa anakanthidwa ndi khungu, “anavutika kufufuza pakhomo” la nyumba kuti alowe kukagonana ndi alendo a Loti.—Genesis 19:4-11.
9, 10. Kodi nchiyani chimene Malemba amasonyeza ponena za chiyembekezo chachiukiriro cha anthu oipa a ku Sodomu?
9 Kodi anthu oipa kwambiri chotero adzaukitsidwa mkati mwa Tsiku Lachiweruzo? Malemba amasonyeza kuti iwo mwachiwonekere sadzatero. Mwachitsanzo, mmodzi wa ophunzira ouziridwa a Yesu, Yuda, analemba choyamba ponena za angelo amene anasiya malo awo kumwamba kuti adzagonane ndi ana aakazi a anthu. Pamenepo iye anawonjezera kuti: “Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.” (Yuda 6, 7; Genesis 6:1, 2) Inde, kaamba ka chisembwere chawo chopambanitsa anthu a Sodomu ndi a m’mizinda yoizungulira anakanthidwa ndi chiwonongeko chimene iwo mwachiwonekere sadzaukitsidwako.—2 Petro 2:4-6, 9, 10a.
10 Yesu nayeso anasonyeza kuti Asodomu sangadzaukitsidwe. Pamene analankhula za Kapernao, umodzi wa mizinda kumene anachitira zozizwitsa, iye anati: “Ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe [Kapernao] zikanachitidwa m’Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero. Komanso ndinena kwa inu kuti dzuwa lakuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.” (Mateyu 11:22-24) Yesu panopa anali kugogomezera liwongo la anthu a ku Kapernao mwa kunena kuti kukakhala kofewerapo kwa Asodomu akalewo amene, m’maganizo mwa omvetsera ake Achiisrayeli, anali osayenerera kotheratu ndi chiukiriro pa Tsiku Lachiweruzo.
11. Kodi nchifukwa ninji kudzakhala kofewerapo pa Tsiku Lachiweruzo kwa “olungama koposa kwa ena alionse a “osalungama”?
11 Ndithudi, pamenepo, tiyenera kuchita zirizonse zimene tingathe kukhala ndi moyo kotero kuti tiyenerere chiukiriro. Koma kungafunsidwebe kuti: Kodi kudzakhala kovuta kwambiri kwa ena a akufa oukitsidwawo kuphunzira ndi kuchitachita chilungamo koposa mmene kudzakhalira kwa enanso? Eya talingalirani: Anthu “olungama” oterowo onga Abrahamu, Isake, Yobu, Debora, Rute ndi Danieli asanafe, onsewo anayang’anira mtsogolo kukudza kwa Mesiya. Ha mmene iwo adzakhalira achimwemwe nanga mkati mwa Tsiku Lachiweruzo kuphunzira za iye, ndi kuti iye akulamulira kumwamba! Chotero kudzakhala kofewerapo kwambiri kwa anthu “olungama” kuchitachita chilungamo panthawiyo koposa kwa “osalungama” ena alionse amene akuukitsidwa kuti atero.—Machitidwe 24:15.
KUUKA KWA “MOYO NDI KUUKA KWA “KUWERUZA”
12. Malinga ndi kunena kwa Yohane 5:28-30, kodi ndani amene akulandira “kuuka kwa moyo,” ndi amene akulandira “kuuka kwa kuweruza”?
12 M’kufotokoza mkhalidwe pa Tsiku Lachiweruzo, Yesu anati: “Onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza . . . monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.” (Yohane 5:28-30) Kodi “kukuuka kwa moyo” kumeneku nchiyani, ndipo kodi “kukuuka kwa kuweruza” nchiyani? Ndipo kodi ndani amene akukulandira?
13. Kodi kukutanthauzanji kwa munthu kulandira “kuuka kwa moyo”?
13 Tawona bwino lomwe kuti pamene akufa atulukira kuchokera kumanda, iwo sakuweruzidwa ndi ntchito zawo zakale. M’malo mwake, iwo akuweruzidwa pamaziko a zimene iwo akuchita mkati mwa Tsiku Lachiweruzo. Chotero pamene Yesu anatchula “amene adachita zabwino” ndi “amene adachita zoipa,” iye anatanthauza zinthu zabwino ndi zinthu zoipa zimene iwo akachita mkati mwa Tsiku Lachiweruzo. Chifukwa cha zinthu zabwino zimene akuchita, ambiri a awo oukitsidwa adzafikira ungwiro waumunthu pofika mapeto a Tsiku Lachiweruzo lazaka 1,000. Motero kubwera kwawo kuchokera kwa akufa kudzatsimikizira kukhala “kuuka kwa moyo,” pakuti iwo adzapeza moyo wangwiro wopanda tchimo.
14. Kodi kukutanthauzanji kwa munthu kulandira “kuuka kwa kuweruza”?
14 Ndiponso, bwanji ponena za awo ‘ameene adachita zoipa kapena zinthu zoipa’ mkati mwa Tsiku Lachiweruzo? Kubwera kwawo kuchokera kwa akufa kudzatsimikizira kukhala “kuuka kwa kuweruza.” Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Zikutanthauza chiweruzo kapena chitsutso cha kuimfa. Motero anthu amenewa adzaphedwa mwina mkati kapena pofika mapeto a Tsiku Lachiweruzo. Chifukwa ndicho chakuti iwo akuchita zinthu zoipa; iwo akukana mouma khosi kuphunzira ndi kutsatira chilungamo.
PAMENE TSIKU LACHIWERUZO LIYAMBA
15. Kodi nchiyani chimene chikuchitika Tsiku Lachiweruzo liri pafupi kuyamba?
15 Mtumwi Yohane anawona m’masomphenya chimene chikuchitika mwamsanga Tsiku Lachiweruzo lisanayambe. Iye analemba kuti: “Ndinawona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m’mwamba zinathawa pamaso pake, . . . Ndipo ndinawona akufa, akulu ndi ang’ono alinkuima ku mpando wachifumu . . . ndipo akufa anaweruzidwa.” (Chivumbulutso 20:11, 12) Motero Tsiku Lachiweruzo lisanayambe, dongosolo la zinthu liripoli lopangika ndi ‘dziko lapansi ndi kumwamba’ lidzachoka. Awo okha otumikira Mulungu adzatsala, pamene oipa onse akuwonongedwa pa Harmagedo.—1 Yohane 2:17.
16. (a) Kodi ndani kuphatikiza pa akufa amene adzaweruzidwa mkati mwa Tsiku Lachiweruzo? (b) Kodi iwo adzaweruzidwa kuchokera m’chiyani?
16 Motero, sindiwo “akufa” oukitsidwa okha amene adzaweruzidwa mkati mwa Tsiku Lachiweruzo. “Amoyo” amene akupyola Harmagedo, kuphatikizapo ana alionse amene iwo angakhale nawo, adzaweruzidwanso. (2 Timoteo 4:1) M’masomphenya Yohane anawona mmene iwo akuweruzidwira. “Ndipo mabukhu anatsegulidwa,” iye anatero kulemba. “Ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabukhu, monga mwa ntchito zawo. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m’menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.”—Chivumbulutso 20:12, 13.
17. Kodi “mabukhu” amene “amoyo” ndi “akufa” adzaweruzidwamo nchiyani?
17 Kodi “mabukhu” amene akutsegulidwa mwa amene “akufa” kuphatikizapo “amoyo” akuweruzidwa nchiyani? Mwachiwonekere adzakhala kanthu kena kowonjezera ku Bukhu lathu Lopatulika liripoli. Iwo ndiwo zolembedwa zouziridwa kapena mabukhu amene ali ndi malamulo ndi zilangizo za Yehova. Mwa kuwerenga amenewa anthu onse padziko lapansi adzakhala okhoza kudziwa chifuniro cha Mulungu. Ndiyeno, pa maziko a malamulo ndi zilangizo “mabukhu” amenewa, aliyense padziko lapansi adzaweruzidwa. Awo amene akumvera zinthu zolembedwamo adzalandira mapindu a nsembe yadipo ya Kristu, ndipo iwo mwapang’onopang’ono adzafikira ku ungwiro waumunthu.
18. (a) Kodi mkhalidwe udzakhala wotani pa mapeto a Tsiku Lachiweruzo? (b) Kodi “akufa” akukhala ndi moyo m’njira yotani pa mapeto a zaka 1,000?
18 Pofika mapeto a Tsiku Lachiweruzo la zaka 1,000 palibe aliyense padziko lapansi adzakhala mu mkhalidwe wakufa chifukwa cha tchimo la Adamu. Zowonadi, m’lingaliro lotheratu aliyense adzakhala atafika ku moyo. Izi ndizo zimene Baibulo limatchula pamene limati: “Otsala a akufa [osaphatikizapo a144,000 amene akupita kumwamba] sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:5) Kutchulako pano “otsala a akufa” sikumatanthauza kuti enanso akuukitsidwa pa mapeto a Tsiku Lachiweruzo la zaka 1,000. M’malo mwake kumatanthauza kuti anthu onse akukhala ndi moyo m’chakuti iwo potsirizira pake amafika ungwiro waumunthu. Iwo adzakhala mu mkhalidwe wangwiro umodzimodziwo monga momwe analiri Adamu ndi Hava m’munda wa Edene. Kodi nchiyani chimene chidzachitika pa nthawi imeneyo?
PAMBUYO PA TSIKU LACHIWERUZO
19. Kodi Kristu akuchitanji pa mapeto a Tsiku Lachiweruzo?
19 Atachita zonse zimene Mulungu wampatsa kuti achite, Yesu Kristu “akupereka ufumu kwa Mulungu ndi Atate wake.” Zimenezi ziri pa mapeto a Tsiku Lachiweruzo la zaka 1,000. Pofika pa nthawi imeneyo adani onse adzakhala atachotsedwa. Wotsirizira wa amenewa ndiye imfa yolandiridwa kwa Adamu. Idzachotsedwa! Pamenepo Ufumuwo ukukhala chuma cha Yehova Mulungu. Iye akuulamulira mwachindunji monga Mfumu.—1 Akorinto 15:24-28.
20. (a) Kodi Yehova adzachitanji kuti adziwe maina a anthu amene ayenera kulembedwa “m’bukhu la moyo”? (b) Kodi nchifukwa ninji chiyeso chotsiriza cha anthu chiri choyenerera?
20 Kodi Yehova adzadziwa motani maina a anthu amene ayenera kulembedwa mu “mpukutu wa moyo,” kapena “bukhu la moyo”? (Chivumbulutso 20:12, 15) Kudzakhala mwa chiyeso pa anthu. Kumbukirani mmene Adamu ndi Hava analepherera pansi pa chiyeso choterocho, ndi mmene Yobu, poyesedwa, anasungira umphumphu. Koma anthu ochuluka amene akukhala ndi moyo kufikira mapeto a zaka 1,000 adzakhala chikhulupiriro chawo chisanayesedwe. Iwo asanaukitsidwe anali osadziwa zifuno za Yehova. Iwo anali mbali ya dongosolo la zinthu loipa la Satana; ndipo anali “osalungama.” Ndiyeno, ataukitsidwa, kunali kosavuta kwa iwo kutumikira Yehova chifukwa cha kukhala m’Paradaiso popanda chitsutso chirichonse chochokera kwa Mdyerekezi. Koma kodi mabiliyoni a anthu amenewa, amene pa nthawi imeneyo ali angwiro, adzatumikira Yehova ngati Satana atapatsidwa mwayi wa kuyesa kuwaletsa kuchita motero mowonjezereka? Kodi Satana angawachitire zimene anachitira Adamu ndi Hava angwirowo?
21. (a) Kodi Yehova adzachititsa anthu kuyesedwa motani? (b) Pamene chiyesocho chitsirizidwa, kodi nchiyani chimene chidzachitikira awo onse olowetsedwamo?
21 Kuti athetse mafunso oterowo, Yehova akumasula Satana ndi ziwanda zake m’phompho kumene iwo akhala anali kwa zaka 1,000. Kodi chotulukapo nchiyani? Baibulo likusonyeza kuti Satana akupambana m’kuleketsa anthu ena kutumikira Yehova. Amenewa adzakhala ngati “mchenga wa kunyanja,” kutanthauza kuti chiwerengero chawo nchosadziwika. Chiyeso chimenechi chitachitidwa, Satana ndi ziwanda zake, ndiponso awo amene sakupambana chiyesocho, akuponyedwa “m’nyanja ya moto” yophiphiritsira, imene iri imfa yachiwiri (yamuyaya). (Chivumbulutso 20:7-10, 15) Koma awo amene maina awo akupezedwa atalembedwa “m’bukhu la moyo” adzakhalabe m’paradaiso wapadziko lapansi waulemereroyo. Kukhala kwa maina awo atalembedwa “m’bukhu la moyo” kumatanthauza kuti Yehova amawawona kukhala olungama kotheratu mu mtima, maganizo ndi thupi ndipo motero oyenerera kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi.
TSIKU LA CHIWERUZO LIRIPOLI
22. Kuti tipitirizebe kukhala ndi moyo kuwona Tsiku Lachiweruzo ndi chiyeso chotsiriza cha anthu, kodi nchiyani chimene ife tsopano tiyenera kupyola?
22 Motero Baibulo limapereka chidziwitso chonena za zochitika koposa zaka 1,000 kulowa mtsogolo. Ndipo limasonyeza kuti palibe chifukwa chowopera zimene ziri mtsogolo. Koma funso ndilo: Kodi mudzakhalako kuti musangalale ndi zinthu zabwino zimene Yehova Mulungu wakundika? Zimenezi zidzadalira pakuti kaya mukupyola tsiku lachiweruzo loyambirira, ndiko kuti, “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza” liripoli—2 Petro 3:7.
23. (a) Kodi tsopano anthu alinkulekanitsidwira m’magulu awiri otani? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira gulu lirilonse, ndipo chifukwa ninji?
23 Inde, kuyambira pamene Kristu anabwerera ndi kukhala pansi pampando wake wachifumu wakumwamba, anthu onse akhala pa chiweruzo. “Tsiku la chiweruzo” liripoli limadza Tsiku Lachiweruzo la zaka 1,000 lisanayambe. Mkati mwa chiweruzo chiripochi anthu alinkulekanitsidwa monga “mbuzi” kudzanja lamanzere la Kristu kapena monga “nkhosa” kudzanja lake lamanja. “Mbuzi” zidzaphedwa chifukwa chakuti izo zikulephera kuthandiza “abale” odzozedwa a Kristu mu utumiki wawo kwa Mulungu. M’kupita kwa nthawi, “mbuzi” zimenezi zimadzisonyeza kukhala ochimwa osalapa, oipa, otindiwala m’kuchita kwawo chosalungama. “Nkhosa,” nazonso, zidzapatsidwa moyo mu ulamuliro Waufumu chifukwa chakuti izo zimachirikiza “abale” a Kristu m’njira iriyonse.—Mateyu 25:31-46.
[Zithunzi patsamba 178]
Kodi nchifukwa ninji Yesu adanena kuti kukakhala kofewerapo kwa Sodomu pa Tsiku Lachiweruzo?