Babulo Wamkulu Kuphedwa Kwake
“Pamphumi pake padalembedwa dzina, chinsinsi, Babulo Wamkulu, Amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.” “Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapsyerera ndi moto; chifukwa [Yehova, “NW”] Mulungu womuweruza ndiye wolimba.”—Chibvumbulutso 17:5; 18:8.
TIRI ndi kuyenera kwa kuzizwa ndi mawu amenewo olembedwa ndi mtumwi Yohane m’zana loyamba la Nyengo yathu Ino. Ndani yemwe ali ‘amayi wa achigololo ameneyu’? Ndimotani mmene iye walakwira Mulungu kotero kuti amuweruze moipa chotero? Palibe kukaikira kuti ziweruzo za Mulungu motsutsana ndi mkazi wachigololo wachinsinsi Babulo Wamkulu ziri zosakaza. Ndipo ichi motsimikizirika chimatipatsa ife chifukwa cha kugamulapo amene ali mkazi wachigololo ameneyu ndi mmene mapeto ake adzatiyambukirira ife.—Chibvumbulutso 18:21.
Ndani kapena nchiyani chimene Babulo Wamkulu anaphiphiritsira? Baibulo limanena kuti olamulira a dziko achita naye chigololo ndi kuti amalonda achita naye malonda. (Chibvumbulutso 18:3) Mwakutero, iye sangaimire ndale zadziko kapena malonda aakulu. Koma ichi chimasiya mbali yachitatu yamphamvu kwenikweni m’dziko monga chandamali chokha kaamba ka dzina la ‘amayi wa achigololo.’ Iye sali wina aliyense kuposa ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga wa Satana!a
Tsopano pakutsala mafunso awa: Nchifukwa ninji, ndimotani, ndipo ndi liti pamene Babulo Wamkulu adzaphedwa? Kapena kuika nkhanizo m’chenicheni: Nchifukwa ninji, ndimotani, ndipo ndi liti pamene chipembedzo chonyenga chidzachokeratu pa dziko iri lapansi?
Cholembera Chosakhala Chachikristu cha Chikristu cha Dziko
Pamene tilingalira cholembera cha chipembedzo chonyenga, tingakumbutsidwe bwino lomwe za mawu a mneneri wakale akuti: “Abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.” (Hoseya 8:7) Ichi chimavomerezana ndi prinsipulo lolongosoledwa ndi mtumwi Wachikristu Paulo: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Chotero, nchiyani chimene chipembedzo chonyenga chafesa pa mlingo wa dziko? Ndipo nchiyani chimene icho chidzatuta?
Yesu Kristu anaphunzitsa kuti otsatira ake ayenera kukonda osati kokha anansi awo komanso adani awo. (Mateyu 5:43, 44) Kugwira mawu kuchokera m’Malemba a Chihebri, Paulo analongosola mmene Akristu akayenera kuchitira adani awo. Iye ananena kuti: “Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzawunjika makala a moto pamutu pake. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.”—Aroma 12:20, 21.
Komabe, mbiri yakale ya zipembedzo za Chikristu cha Dziko iri imodzi ya udani ndi kukhetsa mwazi. Nkhondo za chipembedzo zakale ndi zamakono zophatikiza kufunkha, kugwirira chigololo, ndi imfa zadalitsidwa ndi kulekeleredwa. Mwachitsanzo, kugwirira chigololo kwa ku Abyssinia kochitidwa ndi Italy ya Chifascist (1935) ndi “nkhondo yachipembedzo” ya Franco mu Nkhondo Yachiweniweni ya Chispanish (1936-39) zinadalitsidwa ndi nduna za Tchalitchi cha Katolika.
Kukangana kwa maphunziro a zaumulungu kwakhazikitsidwa mwa kuwotcha anthu pa mlongoti. Wotembenuza Baibulo William Tyndale anapotoledwa khosi pa mlongoti ndipo thupi lake linawotchedwa mu 1536, pambuyo pa kufalitsa kutembenuza kwake kwa “Chipangano Chatsopano” m’Chingelezi. Poyambirirapo, pa kulamula kwa Papa Martin V, maulamuliro a chipembedzo, osonkhezeredwa ndi mzimu wa kubwezera, anafukula mafupa a wotembenuza wa Baibulo Wycliffe zaka 44 pambuyo pa imfa yake kotero kuti akhale ndi chisangalalo cha kuwaotcha iwo. Mkati mwa Kufufuzafufuza kwa Chikatolika, zikwizikwi za Ayuda ndi “opanduka” analandidwa katundu wawo, kuzunzidwa, ndi kuwotchedwa pa mlongoti—zonsezo zoyerekezedwa kuchitidwa m’dzina la Kristu! Katswiri wa zaumulungu wa Chispanish Michael Servetus, yemwe anazunzidwa ndi Aroma Katolika ndi Aprotesitanti mofananamo, anawotchedwa pa mlongoti pa malamulo a John Calvin wa Chiprotesitanti. Mu nkhondo zadziko ziŵiri za zana lino, magulu ankhondo adalitsidwa ndi atsogoleri a chipembedzo “Achikristu,” ndipo asilikali alimbikitsidwa kupha ndi aphungu awo achipembedzo autundu.
Ndi kusiyana kotani nanga ndi Chikristu chowona! Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:12-14.
Kwa Akristu mu Roma, Paulo analemba kuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].” (Aroma 12:17-19) M’chiwunikiro cha maprinsipulo Achikristu, kenaka, Chikristu cha Dziko chalephera. Icho chafesa udani ndi chinyengo ndipo chidzatuta chiwonongeko.
Zipembedzo Zosakhala Zachikristu—Cholembera Chawo
Koma Babulo Wamkulu ali ndi zoposa zipembedzo za Chikristu cha Dziko. Zipembedzo zonse zazikulu zadziko lino zimagawana mu liwongo la mwazi la mkazi wachigololo wa mbiri yoipa ameneyo. Mwachitsanzo, chipembedzo cha Chishinto cha ku Japan chiyenera kukhala ndi mbali ya liwongolo kaamba ka kulingalira kosamvetsetsa ndi kwankhalwe kochitiridwa umboni ndi ankhondo a ku Japan mu Nkhondo ya Dziko ya II. Katswiri wa mbiri yakale Paul Johnson akusungirira kuti “kuti adzilimbitse iwo eni m’dziko lopanda chifundo, ndi lopikisana” olamuliridwa ndi miyezo ya makhalidwe ya ku Europe, iwo anachipeza kukhala choyenerera kupanga “chipembedzo cha boma ndi makhalidwe olamulira, chodziŵika monga Shinto ndi bushido [“njira ya wankhondo”]. . . . Kulambira wolamulira kokhazikika kunakhazikitsidwa, makamaka m’magulu ankhondo, ndipo kuchokera mu ma 1920 kupita mtsogolo mpambo wa mtundu waufuko, kokumin dotoku, unaphunzitsidwa m’sukulu zonse.” Nchiyani chomwe chinali chotulukapo? Podzafika mu 1941, pamene Japan inaphulitsa bomba pa Pearl Harbor ndipo mwakutero kulowa mu Nkhondo ya Dziko ya II, “Shinto . . . inasinthidwa kuchokera ku chiphunzitso chachikale, chamakedzana ndi cha ochepera kupita ku kupangidwa kwa boma lamakono, lodziimira palokha, ndipo mwakutero ndi kunyengezera koipa kwachilendo, chipembedzo, chomwe chikanatumikira kutsutsa zowopsya zakudziko za mbadwowo, chinagwiritsiridwa ntchito kuziyeretsa izo.”
Ponena za kugawidwa kwa India mu 1947, m’kumene kusiyana kwa chipembedzo kunali chochititsa, katswiri wa mbiri yakale Johnson akunena kuti: “Anthu mamiliyoni 5 kufika ku 6 anathaŵa kaamba ka kupulumutsa miyoyo yawo m’malo aliwonse. . . . Kuyerekeza kwa akufa pa nthaŵiyo kunali pakati pa 1 kufika ku 2 miliyoni. Kupenda kwamakono kwenikweni kuli pakati pa 200,000 kufika ku 600,000.” Kufika ku tsiku lino, kupha kosonkhezeredwa ndi chipembedzo ndi kudidikizidwa kumachitika mu chitaganya cha Chihindu. Kaŵirikaŵiri Harijans, kapena okanidwa omwe kalelo ankatchedwa osagwirika, ali minkhole ya magulu a achifwamba olinganizidwa ndi eni dziko olemera.
Chihindu chiri cholunzanitsidwa ndi machitachita a mizimu. (Chibvumbulutso 18:23) Wolemba wa ku India Sudhir Kakar akulankhula za “kusinkhasinkha kwachisawawa kwa Chihindu ndi ulemu kaamba ka kubwebweta ndi okuchita” ndi kuwonjezera kuti: “Openda nyenyezi, onena zamtsogolo, omasulira maloto monganso sadhus [amuna “oyera” onkitsa], oyendayenda [Osanganiza chipembedzo ndi zakunja omwe amachita matsenga] ndi amuna ena opangidwa milungu amatukulidwa mwakuya popeza kuti amalingaliridwa kukhala m’kugwirizana kwathithithi ndi weniweni wopambana.”—India Today, April 30, 1988.
Kuwonjezerapo, pali kukanthana kokhazikika pakati pa Ahindu, Asikh, ndi zipembedzo zina za Kum’mawa. Ku kukanthana kumeneku, chipembedzo chirichonse chimawonjezera kugawana kwake kwa udani, ndewu, ndi kupha. Iyi iri kokha mbali ina ya zipatso za Babulo Wamkulu.
Kuwonjezeraponso, mbiri yamakono ya nkhondo, kupha, ndi kutsendereza imanena zochepera kuyamikira Chiyuda. Chiwawa nthaŵi zina chosonyezedwa ndi ziŵalo za mpatuko wa Hasidic wa Chiyuda kulinga ku omamatira ku mipatuko ina ya Chiyuda ndi zipembedzo zosakhala za Chiyuda kuli kutalitali ndi kuyamikiridwa m’maso mwa Mulungu.
Pamene tiphunzira mbiri yakale ya ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo, tingawone mopepuka chifukwa chimene Woweruza Wamkulu ali ndi maziko a kuphedwa kwa Babulo Wamkulu. “Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.” (Chibvumbulutso 18:24) Kuloŵerera kwa chipembedzo chonyega mu nkhondo za m’dera ndi zadziko kwamupangitsa iye kukhala waliwongo m’maso mwa Mulungu kaamba ka mwazi wa “onse amene anaphedwa padziko.”
Mogwirizana ndi kuweruza kwa Baibulo, Babulo Wamkulu waweruzidwa kukhala woyenerera chiwonongeko chifukwa cha mbiri yake ya chigololo chauzimu ndi olamulira a dziko, liwongo lake la mwazi mu nkhondo, ndi machitachita ake a mizimu. Chotero, Yehova Mulungu wagamulapo mwa chiweruzo kuti ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga wa Satana uyenera kuthetsedwa.—Chibvumbulutso 18:3, 23, 24.
Mmene Chipembedzo Chonyenga Chidzathera
M’chinenero chophiphiritsira chopambana, bukhu la Chibvumbulutso likulongosola chiwonongeko cha Babulo Wamkulu. Pa Chibvumbulutso 17:16 timaŵerenga kuti: “Nyanga khumi udaziwona, ndi chirombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsyereza ndi moto.” “Nyanga khumi” zimaphiphiritsira mphamvu zonse za ndale zadziko tsopano zokhala pa chiwonetsero chadziko ndi zimene zimachilikiza Mitundu Yogwirizana, “chirombo chofiiritsa,” chenichenicho pokhala fano la dongosolo la kachitidwe la ndale zadziko la Mdyerekezi loipitsidwa ndi mwazi.—Chibvumbulutso 16:2; 17:3.b
Mogwirizana ndi ulosi wa Baibulo, mphamvu za ndale zadziko zogwirizana ndi Mitundu Yogwirizana zidzatembenuka motsutsana ndi ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga ndi kuchisakaza icho. Zipembedzo zonyenga zonse zidzayambukiridwa. Madongosolo a kachitidwe ena a ndale zadziko asonyeza kale kusadekha kwawo ndi kuloŵerera kwa chipembedzo chonyenga mu mbali za ndale zadziko ndi zamayanjano. Maiko ena achisosholisiti atenga kaimidwe ka kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu ndipo achepetsa chipembedzo ku chinthu chosakhalako m’chenicheni, monga mmene ziliri mu Albania, kapena ku kapolo wovomera chirichonse, monga mmene ziliri mu Russia ndi China. Kwinakwake, olamulira a ndale zadziko amasonyeza kuipidwa kwamphamvu kaamba ka nthanthi yaumulungu yonena zaufulu ya ansembe ena a Chikatolika m’maiko osauka kwenikweni. Komabe ena akutsendereza zipembedzo zimene zimadziloŵetsa mu nkhani zaufuko. Ngakhale m’maiko otchedwa aufulu, akatswiri a andale zadziko ena amaipidwa ndi kuchita malonda kwa nduna za chipembedzo mu ndale zadziko ndi nkhani zamayanjano.
Chakhalira kudzawonedwa kokha zomwe ziri nkhani zowonjezereka zimene zidzaputa mbali za ndale dziko lonse kuchita molimbana ndi chipembedzo chonyenga. Koma chinthu chimodzi chiri chotsimizirika—kuphedwa kwa Babulo Wamkulu ndi mbali zimenezi sikudzakhala kokha chifuno chawo komanso chifuno cha Mulungu. Chibvumbulutso 17:17 chikulongosola kuti: “Mulungu anapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chirombo, kufikira akwaniridwa mawu a Mulungu.”—Yerekezani ndi Yeremiya 51:12, 13.
Musapange kuphophonya. Kuphedwa kwa Babulo Wamkulu sikudzangokhala kusonyezedwa kwa udani wa ndale zadziko kulinga ku kusamva kwa chipembedzo ndi kuloŵerera. Olamulira a ndale zadziko adzakhala zida zosakhala zaufulu za Mulungu kaamba ka chiwonongeko cha kulambira konyenga dziko lonse. Inde, “machimo ake anawunjikizana kufikira m’mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”—Chibvumbulutso 18:5.
Yehova walamulira kuti chipembedzo chonyenga chonyada chiyenera kuchepetsedwa. Ulosi ukulongosola kuti: “Monga momwe anadzichitira ulemu nadyerera mopanda manyazi, momwemo mumuchitire chozunza ndi choliritsa maliro. Pakuti anena mu mtima mwake kuti, ‘Ndikhala ine mfumukazi, ndipo sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzawona maliro konse.’ Chimenecho ndicho chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa ndi maliro ndi njala, ndipo adzapsyerezedwa kotheratu ndi moto, chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wolimba.”—Chibvumbulutso 18:7, 8, NW.
Kuphedwa Liti?
“Tsiku limodzi” limenelo, kapena nthaŵi yaifupi ya kupha kofulumira, tsopano iri pafupi. M’chenicheni, chiwonongeko cha Babulo Wamkulu chimabweretsa “tsiku la kubwezera chilango ku mbali ya Mulungu wathu.” (Yesaya 61:2, NW) Pambuyo pake, nkhondo yolungama ya Mulungu ya Armagedo idzakhala pa ife. Umboni wonse wa zochitika zadziko chiyambire 1914 umasonyeza kuti nthaŵi ikutha kaamba ka dongosolo la zinthu la Satana. Chotero, kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu kwayandikira.—Luka 21:32-36; Chibvumbulutso 16:14-16.
Ndimotani mmene alambiri owona adzachitira ku chiwonongeko cha Babulo Wamkulu? Chikutero Chibvumbulutso kuti: “Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anaweruzira kuweruzidwa kwanu.” (Chibvumbulutso 18:20) Padzakhala kusangalala kwa chilengedwe cha ponseponse pamene chifuno cha Yehova chidzachitidwa ndipo dzina lake layeretsedwa. Ulosiwo ukulongosola kuti: “Zitatha izi ndinamva ngati mawu akulu a khamu lalikulu m ‘mwamba, liri kunena, [Lemekezani Ya, Anthu inu! NW] Chipulumutso ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali owona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsya dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo.”—Chibvumbulutso 19:1, 2.
Kusakazidwa kwa Babulo Wamkulu, kotsatiridwa ndi kupha kwa Mulungu kwa mbali zotsala za dongosolo la kachitidwe la Satana, kudzatanthauza madalitso osatha kaamba ka alambiri owona a Mulungu, kuphatikizapo ambiri omwe adzawukitsidwa pano padziko lapansi. Monga momwe Yesu analonjezera onse oterowo kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:31, 32; Chibvumbulutso 19:11-21.
Alambiri owona ali kale omasuka ku ziphunzitso za chipembedzo chonyenga zomwe zanyoza Mulungu kupyola m’mibadwo. M’dziko latsopano lolonjezedwa la chilungamo, iwo adzakhala omasuka kukhala popanda mantha a imfa, popeza kuti “Mulungu yekha adzakhala nawo, . . . ; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chibvumbulutso 21:3, 4) Zoyambazo zomwe zidzakhala zitapita zidzaphatikizapo Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko wa Satana wa chipembedzo chonyenga.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka umboni watsatanetsatane wowonjezereka wozindikiritsa Babulo Wamkulu, onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1989.
b Kaamba ka kulongosola kwa zizindikiro izi ndi zina mu Chibvumbulutso, onani bukhu la Revelation--Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
“Ndi kunyengezera kwachilendo koipa, chipembedzo, chomwe chikanatumikira kutsutsa zowopsya zakudziko za mbadwowo, chinagwiritsiridwa ntchito kuziyeretsa izo”
[Chithunzi patsamba 4]
Wycliffe ndi Tyndale anazunzidwa kaamba ka kutembenuza Baibulo
[Mawu a Chithunzi]
From an old engraving in the Bibliothèque Nationale