Mutu 9
Gwiranibe Mwamphamvu Dzina la Yesu
PEGAMO
1. Kodi uthenga wotsatira wa Yesu unapita kumpingo uti, ndipo Akhristu a mumpingo umenewo ankakhala mumzinda wotani?
KALE munthu akayenda mtunda wa makilomita 80 kuchokera mumzinda wa Simuna, kudutsa msewu wa m’mphepete mwa nyanja, kupita chakumpoto kenako n’kuyenda mtunda wa makilomita 25 kudutsa chigwa cha mtsinje wa Caicus, ankafika ku Pegamo, mzinda umene panopa umatchedwa kuti Bergama. Mzinda umenewu unali wotchuka chifukwa cha kachisi wa Zeu, kapena kuti Jupita. M’zaka za m’ma 1800, akatswiri ofukula zinthu za m’mabwinja anasamutsa guwa la nsembe la kachisi ameneyu kupita nalo ku Germany. Kumeneko analiika m’nyumba yosungiramo zinthu zakale yotchedwa Pergamon imene ili mumzinda wa Berlin, kumene anthu amapita kukaliona. M’nyumba imeneyi mulinso mafano ambiri ndi zithunzi za milungu yonyenga. Kodi Ambuye Yesu anapereka uthenga wotani kwa Akhristu a ku Pegamo, mzinda umene anthu ankalambira kwambiri mafano?
2. Kodi Yesu anadzifotokoza bwanji, ndipo ‘lupanga lakuthwa konsekonse’ limene likutuluka m’kamwa mwake likuimira chiyani?
2 Yesu anayamba ndi kudzifotokoza yekha kuti: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Pegamo lemba kuti: Izi ndi zimene akunena amene ali ndi lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.” (Chivumbulutso 2:12) Apa Yesu anabwereza mawu omufotokoza amene ali pa Chivumbulutso 1:16. Popeza kuti iye ndi Woweruza ndiponso Wopereka chilango, adzapha anthu amene amazunza ophunzira ake. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri. Koma ponena za chiweruzo, anthu amene ali mumpingo amvere chenjezo lakuti Yehova, kudzera mwa “mthenga wa pangano,” Yesu Khristu, ‘sadzazengereza kupereka umboni’ wotsutsa anthu onse amene amati ndi Akhristu koma amalambira mafano, amachita chigololo, amanama, amachita chinyengo ndiponso safuna kusamalira anthu aumphawi. (Malaki 3:1, 5; Aheberi 13:1-3) Tonse tiyenera kutsatira malangizo ndi uphungu umene Mulungu anapereka kudzera mwa Yesu.
3. Kodi anthu a mumzinda wa Pegamo ankachita zinthu ziti zosonyeza kulambira konyenga, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti “mpando wachifumu” wa Satana unali kumeneko?
3 Kenako Yesu anauza mpingowo kuti: “Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana.” (Chivumbulutso 2:13a) Zoonadi, Akhristuwo ankakhala mumzinda umene anthu ambiri ankalambira Satana. Kuwonjezera pa kachisi wa Zeu, mumzindawo munalinso kachisi wa Esikulapia, mulungu wa mphamvu zochiritsa. Mzinda wa Pegamo unalinso wotchuka ndi kulambira mfumu. Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “Satana” amatanthauza “Wotsutsa,” ndipo ‘mpando wake wachifumu’ ukuimira ulamuliro wake wa padziko lonse umene Mulungu waulola kuti ukhalepo kwa kanthawi. Anthu olambira mafano mumzinda wa Pegamo anali ochuluka kwambiri. Zimenezi zikusonyeza kuti “mpando wachifumu” wa Satana unakhazikika mumzindawo. Satana ayenera kuti anakwiya kwambiri chifukwa chakuti Akhristu a kumeneko anakana kumulambira pokana kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo.
4. (a) Kodi Yesu anawayamikira motani Akhristu a ku Pegamo? (b) Kodi Pliny amene anali nthumwi ya Mfumu Trajan ya Roma analembera mfumuyo chiyani chokhudza zimene iyeyo ankachita ndi Akhristu? (c) Ngakhale kuti moyo wa Akhristu a ku Pegamo unali pangozi, kodi iwo anasankha kuchita chiyani?
4 N’zoonadi, “mpando wachifumu wa Satana” unali ku Pegamo. Komabe Yesu anapitiriza kuuza Akhristu a mpingo wa ku Pegamo kuti: “Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa, ndipo sunakane kuti umakhulupirira ine. Sunakane ngakhale m’masiku a Antipa mboni yanga, wokhulupirika wanga uja, amene anaphedwa pambali panu, kumene Satana akukhala.” (Chivumbulutso 2:13b) Mawu amenewatu analimbikitsa kwambiri Akhristuwo. N’zosakayikitsa kuti Antipa anaphedwa chifukwa chokana kuchita nawo zinthu zogwirizana ndi ziwanda ndiponso kulambira mfumu ya Roma. Yohane atangolandira ulosi umenewu, Pliny Wamng’ono, yemwe anali nthumwi ya Trajan, mfumu ya Roma, analembera kalata mfumuyo. M’kalatayo, iye anafotokoza mmene ankachitira ndi anthu amene ankapezeka ndi mlandu wokhala Akhristu ndipo mfumuyo inavomereza. Pliny anafotokoza kuti anthu amene anakana kuti si Akhristu ankawamasula. Iye anati: “Ndinkawauza kuti azilankhula motsatira pemphero lopita kwa milungu limene ndinkanena. Ndinkawauzanso kuti apereke nsembe zofukiza ndiponso vinyo kwa fano lanu [la Trajan] . . . komanso kuti atukwane Khristu.” Aliyense amene ankapezeka kuti ndi Mkhristu ankaphedwa. Ngakhale kuti Akhristu a ku Pegamo ankakumana ndi zoopsa zoterezi, sanasiye chikhulupiriro chawo. Akhristu amenewa ‘anagwirabe mwamphamvu dzina la Yesu’ popitiriza kulemekeza udindo wapamwamba umene Yesu ali nawo monga Woweruza ndiponso Wokweza Dzina la Yehova. Iwo anatsatira mokhulupirika chitsanzo cha Yesu chochitira umboni za Ufumu.
5. (a) Kodi masiku ano anthu akuchita zinthu ziti zofanana ndi kulambira mfumu zimene zabweretsa mayesero ovuta kwambiri kwa Akhristu? (b) Kodi magazini a Nsanja ya Olonda athandiza bwanji Akhristu pa nkhani imeneyi?
5 Pa nthawi zosiyanasiyana, Yesu ananena kuti Satana ndi amene akulamulira dziko loipali. Koma chifukwa chakuti Yesu ankatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, Satana analibe mphamvu pa iye. (Mateyu 4:8-11; Yohane 14:30) Masiku ano, mayiko amphamvu, makamaka “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kum’mwera” akulimbana kwambiri chifukwa chakuti aliyense akufuna azilamulira dziko lonse. (Danieli 11:40) Mofanana ndi zimene anthu a ku Pegamo ankachita posonyeza kukonda kwambiri dziko lawo ndiponso kulambira mfumu, masiku anonso anthu ambiri padziko lonse amakonda kuchita zinthu zosonyeza kukonda dziko lawo. M’magazini a Nsanja ya Olonda ya November 1, 1939, ya November 1, 1979, ya September 1, 1986, komanso ya November 1, 2002, munali nkhani zomveka bwino za m’Baibulo zimene zinathandiza Akhristu pa nkhani yokhudza kusachita nawo zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko. Nkhani zimenezi zinapereka malangizo kwa Akhristu amene akufuna kuyendabe m’dzina la Yehova ndi kugonjetsa dziko monga mmene Yesu analigonjetsera molimba mtima.—Mika 4:1, 3, 5; Yohane 16:33; 17:4, 6, 26; 18:36, 37; Machitidwe 5:29.
6. Kodi Mboni za Yehova masiku ano zasonyeza bwanji chikhulupiriro cholimba ngati cha Antipa?
6 Malangizo amenewo anali ofunika kwambiri pa nthawiyo. Pa nthawi imene anthu ankachita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo, Akhristu a Mboni za Yehova odzozedwa komanso anzawo a nkhosa zina, anafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Mwachitsanzo, m’dziko la United States, ana a sukulu ambirimbiri anachotsedwa sukulu ndiponso aphunzitsi ambiri anachotsedwa ntchito chifukwa chokana kulambira mbendera. Ndiponso m’dziko la Germany Mboni za Yehova zinazunzidwa koopsa chifukwa chokana kulambira chizindikiro cha chipani cha Nazi. Monga mmene taonera kale, chipani cha Nazi, chomwe mtsogoleri wake anali Hitler, chinapha atumiki a Yehova okhulupirika masauzande ambiri chifukwa anakana kuchita zinthu zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo, komwe ndi kulambira mafano. M’chaka cha 1930, pa nthawi imene anthu a chipembedzo cha Shinto ku Japan ankalambira kwambiri mfumu, apainiya awiri anafesa kwambiri mbewu ya Ufumu m’dziko la Taiwan limene linkalamuliridwa ndi dziko la Japan. Asilikali amene ankalamulira dzikoli anatsekera apainiyawo m’ndende ndipo mmodzi anafera kundende komweko chifukwa chochitidwa nkhanza kwambiri. Mpainiya winayo anamutulutsa, koma kenako anamuwombera kumsana ndipo anaphedwa ngati Antipa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Mpaka pano, pali mayiko amene amakakamiza anthu awo kuti azilambira zizindikiro za dziko monga mbendera komanso kuti azichita chilichonse chimene boma lawo likufuna. Achinyamata ambiri a Mboni amangidwa ndipo ambiri aphedwa chifukwa chokana molimba mtima kuchita nawo zinthu zimenezi. Ngati ndinu wachinyamata amene mukukumana ndi mavuto ngati amenewa, muziphunzira Mawu a Mulungu tsiku lililonse kuti ‘mukhale ndi chikhulupiriro chosunga moyo’ chimene chingakuthandizeni kudzapeza moyo wosatha.—Aheberi 10:39–11:1; Mateyu 10:28-31.
7. Kodi ana ena a sukulu m’dziko la India anatani pa nkhani yoimba nyimbo ya fuko, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
7 Nawonso ana a sukulu akumana ndi mavuto ofanana ndi amenewa. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1985, mumzinda wa Kerala m’dziko la India, ana atatu a Mboni za Yehova anakana kuimba nyimbo yafuko chifukwa cha chikhulupiriro chawo cha m’Baibulo. Pamene anzawo ankaimba nyimbo yafuko, iwo anangoima mwaulemu, komabe anawachotsa sukulu. Bambo a anawo anapititsa nkhaniyi ku Khoti Lalikulu Kwambiri la ku India. Kumeneko oweruza milandu awiri anagamula mlanduwo mokomera anawo. Oweruzawo ananena molimba mtima kuti: “Chikhalidwe chathu chimatiphunzitsa kuti tizikhala ololera, zikhulupiriro zathu zimatiphunzitsa kuti tizikhala ololera, malamulo athu amatilimbikitsa kuti tizikhala ololera, choncho tisachite zinthu zosemphana ndi zimenezi.” Manyuzipepala anafalitsa nkhani imeneyi m’dziko lonse la India, limene pa nthawiyo chiwerengero cha anthu ake chinali gawo limodzi mwa magawo asanu a chiwerengero cha anthu padziko lonse. Manyuzipepalawo ananena kuti m’dzikolo muli Akhristu amene amalambira Mulungu woona Yehova, ndipo amatsatira mfundo za m’Baibulo mokhulupirika.
Misampha ya Satana
8. Kodi Yesu anapatsa Akhristu a ku Pegamo uphungu woyenerera wotani?
8 Akhristu a ku Pegamo ankatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Koma Yesu anawauza kuti: “Ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo.” Kodi Akhristuwo analakwa chiyani kuti Yesu awapatse uphungu? Iye ananena kuti: “Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.”—Chivumbulutso 2:14.
9. Kodi Balamu anali ndani, ndipo malangizo ake ‘anaikira bwanji ana a Isiraeli chopunthwitsa’?
9 M’nthawi ya Mose, Mfumu Balaki ya ku Mowabu inatuma Balamu, mneneri yemwe sanali Mwisiraeli koma ankadziwa zinthu zina zokhudza Yehova, kuti akatemberere Aisiraeli. Yehova analetsa Balamu kuchita zimenezi, ndipo anamuchititsa kuti adalitse Aisiraeliwo ndi kutemberera adani awo. Pofuna kusangalatsa Balaki amene anali atakwiya, Balamu anaganizira njira ina yobisika yogonjetsera Aisiraeliwo mosavuta. Njirayo inali yakuti akazi achimowabu akope amuna achiisiraeli kuti achite nawo chiwerewere ndiponso kuti alambire nawo fano la mulungu wonyenga, Baala wa ku Peori. Zimenezi zinathekadi. Kenako mkwiyo wolungama wa Yehova unayakira Aisiraeliwo ndipo anawagwetsera mliri umene unapha anthu 24,000 achiwerewerewo. Mliriwo unasiya pamene wansembe Pinihasi anapha ena mwa anthu achiwerewerewo kuti achotse zoipa pakati pa Aisiraeli.—Numeri 24:10, 11; 25:1-3, 6-9; 31:16.
10. Kodi mumpingo wa ku Pegamo munalowa zopunthwitsa ziti, ndipo mwina n’chifukwa chiyani Akhristu a mumpingowo ankaganiza kuti Mulungu sangawaimbe mlandu chifukwa cha machimo awo?
10 Ndiyeno kodi m’masiku a Yohane, ku Pegamo kunalinso zopunthwitsa zofanana ndi zimenezo? Inde zinaliko. Makhalidwe oipa monga chiwerewere ndiponso kulambira mafano anali atalowerera mumpingo. Akhristu amenewo sanamvere machenjezo amene Mulungu anawapatsa kudzera mwa mtumwi Paulo. (1 Akorinto 10:6-11) Popeza kuti anapirira pamene ankazunzidwa, mwina ankaganiza kuti Yehova sawaimba mlandu akamachita zachiwerewere. Choncho Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti apeweretu kuchita zoipazo.
11. (a) Kodi Akhristu ayenera kusamala ndi chiyani, ndipo ayenera kupewa maganizo otani? (b) Kwa zaka zambiri, kodi ndi anthu ochuluka bwanji amene akhala akuchotsedwa mumpingo wachikhristu, ndipo ambiri a iwo anachotsedwa pa chifukwa chiti?
11 Masiku anonso Akhristu ayenera kupewa chizolowezi ‘chotenga kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lotayirira.’ (Yuda 4) Tiyenera kudana ndi zoipa ndipo tiyeneranso ‘kumenya matupi athu’ kuti tipitirize kusonyeza makhalidwe abwino achikhristu. (1 Akorinto 9:27; Salimo 97:10; Aroma 8:6) Tisamaganize kuti tikamatumikira Mulungu mwakhama ndiponso ndi mtima wosagawanika pamene tikuzunzidwa, ndiye kuti tili ndi ufulu wochita zachiwerewere. Kwa zaka zambiri, anthu masauzande ambirimbiri achotsedwa mumpingo wachikhristu padziko lonse, ndipo ambiri mwa anthu amenewa achotsedwa chifukwa cha chiwerewere. M’zaka zina, chiwerengero cha ochotsedwawo chakhala chachikulu kwambiri kuposa cha Aisiraeli amene anafa chifukwa cholambira Baala wa ku Peori. Choncho tiyenera kusamala kwambiri kuti tisakhale m’gulu la anthu amenewa.—Aroma 11:20; 1 Akorinto 10:12.
12. Kodi ndi mfundo ziti zimene zinkagwira ntchito kwa atumiki a Mulungu akale zimenenso zikugwira ntchito kwa Akhristu masiku ano?
12 Yesu anadzudzulanso Akhristu a ku Pegamo chifukwa ‘ankadya zoperekedwa nsembe kwa mafano.’ Kodi ankachita bwanji zimenezi? Tikaona mawu amene Paulo analembera Akhristu a mumpingo wa ku Korinto, mwina ena ankagwiritsira ntchito ufulu wawo molakwika pochita mwadala zinthu zimene zinkavutitsa chikumbumtima cha ena. Koma zikuoneka kuti mwina ankachita nawo miyambo yokhudza kulambira mafano. (1 Akorinto 8:4-13; 10:25-30) Akhristu okhulupirika masiku ano ayenera kusonyeza chikondi chenicheni kuti asakhumudwitse ena pamene akugwiritsira ntchito ufulu wawo wachikhristu. Iwo ayenera kupewa kulambira zinthu zomwe zili ngati mafano masiku ano monga anthu otchuka a pa TV, a m’mafilimu ndiponso anthu otchuka ochita masewera. Komanso ayenera kupewa kuona ndalama ndi mimba zawo ngati milungu yawo.—Mateyu 6:24; Afilipi 1:9, 10; 3:17-19.
Pewani Mpatuko
13. Kodi Yesu anadzudzulanso bwanji Akhristu a ku Pegamo, ndipo n’chifukwa chiyani mpingowo unafunikira kudzudzulidwa?
13 Yesu anapitiriza kudzudzula Akhristu a ku Pegamo kuti: “Ndiponso uli ndi olimbikira chiphunzitso cha mpatuko wa Nikolao.” (Chivumbulutso 2:15) M’mbuyomu Yesu anayamikira Akhristu a ku Efeso chifukwa chodana ndi zochita za anthu ampatuko umenewu. Koma Akhristu a mpingo wa ku Pegamo anafunika kupatsidwa uphungu kuti mumpingomo musakhale mpatuko. Akhristuwo ankafunika kukhala olimba kwambiri potsatira mfundo zachikhristu n’cholinga choti mgwirizano umene Yesu anaupempherera pa Yohane 17:20-23 usathe. Iwo ankafunika “kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola ndiponso kudzudzula otsutsa.”—Tito 1:9.
14. (a) Kuyambira kale, kodi mpingo wachikhristu wakhala ukulimbana ndi anthu otani, ndipo kodi mtumwi Paulo anawafotokoza bwanji anthu amenewa? (b) Kodi aliyense amene anatengeka n’kutsatira gulu lampatuko, ayenera kumvera mawu ati a Yesu?
14 Kuyambira kale, mpingo wachikhristu wakhala ukulimbana ndi anthu onyada ampatuko, amene amalankhula mawu okopa komanso achinyengo n’cholinga choti ‘ayambitse magawano ndi kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. Zimenezi ndi zosemphana ndi chiphunzitso chimene timaphunzira’ kudzera m’njira imene Yehova amatiphunzitsira. (Aroma 16:17, 18) Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu kuti apewe mpatuko pafupifupi m’makalata ake onse.a Masiku ano, ngakhale kuti Yesu wakonzanso mpingo wachikhristu kuti ukhale woyera ndi wogwirizana, mpatuko umathabe kuyamba. Chotero aliyense amene anatengeka n’kutsatira gulu lampatuko, ayenera kumvera mawu a Yesu akuti: “Choncho ulape. Ngati sulapa, ndikubwera kwa iwe msanga, ndipo ndidzamenyana nawo ndi lupanga lalitali la m’kamwa mwanga.”—Chivumbulutso 2:16.
15. Kodi mpatuko umayamba bwanji?
15 Kodi mpatuko umayamba bwanji? Mwina munthu wina amayamba kuphunzitsa za m’mutu mwake n’kupangitsa anthu ena kuti azikayikira ndi kutsutsa mfundo zina za choonadi cha m’Baibulo (monga mfundo yakuti tikukhala m’masiku otsiriza). Zikatero gulu la anthu limachoka mumpingo n’kutsatira munthuyo. (2 Timoteyo 3:1; 2 Petulo 3:3, 4) Kapena wina angayambe kutsutsa mmene ntchito ya Yehova ikuchitikira ndipo angamalimbikitse anthu kuti asamagwire ntchitoyo mwakhama ponena kuti ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu kunyumba ndi nyumba ndi yosagwirizana ndi Malemba komanso ndi yosafunikira. Anthu amenewa akanamvera Yesu ndi atumwi ake n’kumalalikira kunyumba ndi nyumba, zikanawathandiza kuti akhale odzichepetsa. Koma iwo amasankha kuchoka m’chipembedzo choona kuti asamatanganidwe ndi chipembedzocho, ndipo mwina anthuwo amasonkhana mwa apo ndi apo n’kumangowerengera limodzi Baibulo. (Mateyu 10:7, 11-13; Machitidwe 5:42; 20:20, 21) Anthu amenewa amapeka ziphunzitso zawozawo pa nkhani ya Chikumbutso cha imfa ya Yesu, lamulo la m’Malemba lokhudza kupewa magazi, kukondwerera maholide osiyanasiyana ndi kusuta fodya. Komanso amasiya kulemekeza dzina la Yehova ndipo posakhalitsa amayamba kuchita zinthu zoipa zimene Babulo Wamkulu amachita. Ndipo ena amafika poipa kwambiri moti Satana amawachititsa kuyamba ‘kumenya akapolo anzawo’ amene poyamba anali abale awo.—Mateyu 24:49; Machitidwe 15:29; Chivumbulutso 17:5.
16. (a) N’chifukwa chiyani anthu amene akopeka ndi anthu ampatuko ayenera kulapa mwamsanga? (b) Kodi anthu amene akukana kulapa chidzawachitikire n’chiyani?
16 Aliyense amene wayamba kukopeka ndi anthu ampatuko ayenera kumvera mwachangu malangizo a Yesu akuti alape. Tiyenera kupeweratu ziphunzitso zampatuko chifukwa chakuti zili ngati poizoni. Anthu ampatuko amayambitsa ziphunzitso zoipa chifukwa cha nsanje ndi chidani. Izi n’zosiyana kwambiri ndi choonadi chimene Yesu amaphunzitsa mu mpingo wake, chomwe ndi cholungama, choyera komanso cholimbikitsa chikondi. (Luka 12:42; Afilipi 1:15, 16; 4:8, 9) Koma anthu amene sakufuna kulapa, Ambuye Yesu ‘akumenyana nawo ndi lupanga lalitali la m’kamwa mwake.’ Iye akupeta anthu ake kuti ateteze mgwirizano umene anaupempherera usiku womaliza pamene anali ndi ophunzira ake padziko lapansi. (Yohane 17:20-23, 26) Popeza kuti anthu ampatuko amakana kulangizidwa mwachikondi ndiponso kuthandizidwa ndi nyenyezi zimene zili m’dzanja lamanja la Yesu, iye amawaweruza ndiponso kuwapatsa “chilango choopsa” ndipo amawaponya “kunja kumdima.” Zimenezi zikutanthauza kuti iwo amachotsedwa mumpingo kuti asakhalenso chofufumitsa chosokoneza anthu a Mulungu.—Mateyu 24:48-51; 25:30; 1 Akorinto 5:6, 9, 13; Chivumbulutso 1:16.
‘Mana Obisika Komanso Mwala Woyera’
17. Kodi Akhristu odzozedwa amene ‘amapambana pa nkhondo’ amalandira chiyani, ndipo kodi Akhristu a ku Pegamo anayenera kupewa chiyani?
17 Anthu amene amamvera malangizo a Yesu, amene anawapereka kudzera mwa mzimu woyera wa Yehova, adzalandira mphoto yaikulu. Tamvani zimene Yesu ananena. Iye anati: “Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo ndidzamupatsa ena mwa mana obisika. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwa dzina latsopano limene wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.” (Chivumbulutso 2:17) Choncho Akhristu a ku Pegamo, mofanana ndi Akhristu a ku Simuna, analimbikitsidwa kuti ‘apambane pa nkhondo.’ Kuti zinthu ziwayendere bwino, Akhristu a ku Pegamo, kumene kunali mpando wachifumu wa Satana, anayenera kupewa kulambira mafano. Iwo anayeneranso kupewa chiwerewere, kupanga magulu ampatuko ogwirizana ndi zochita za Balaki ndi Balamu ndiponso mpatuko wa Nikolao. Akanapewa zimenezi, Akhristu odzozedwawo akanaitanidwa kudzadya nawo ena mwa “mana obisika.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?
18, 19. (a) Kodi mana amene Yehova anapatsa Aisiraeli anali chiyani? (b) Kodi ndi mana ati amene anali m’malo obisika? (c) Kodi kudya mana obisika kukuimira chiyani?
18 M’nthawi ya Mose, Yehova anapereka mana kwa Aisiraeli kuti azidya pamene anali pa ulendo wodutsa m’chipululu. Mana amenewo sanali obisika chifukwa chakuti m’mawa uliwonse, kupatulapo tsiku la Sabata, ankagwa modabwitsa kuchokera kumwamba ndipo ankaoneka ngati tinthu tolimba koma topyapyala ndi tosalala ngati mame amene aundana panthaka. Mulungu anapereka mana amenewa kwa Aisiraeli kuti asafe ndi njala. Yehova analamula Mose kuti asunge ena mwa mana amenewa mumtsuko wa golide n’kukausunga mulikasa la pangano kuti ‘mibadwo yonse ya Aisiraeli’ izikumbukira.—Ekisodo 16:14, 15, 23, 26, 33; Aheberi 9:3, 4.
19 M’pake kuti Yesu ananena za mana obisika. Mana amenewa ankakhala m’malo obisika, m’Malo Oyera Koposa a m’chihema, mmene munkaoneka kuwala kodabwitsa pamwamba pa Likasa. Kuwalako kunali chizindikiro chakuti Yehova ali m’Malo Oyera Koposawo. (Ekisodo 26:34) Palibe amene ankaloledwa kulowa m’malo oyerawo kuti akadye mana obisikawo. Komabe, Yesu ananena kuti otsatira ake odzozedwa amene akupambana pa nkhondo adzadya “mana obisika.” Monga mmene Yesu anachitira, odzozedwawo salowa “m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu, amene ndi chithunzi cha malo enieniwo, koma [amalowa] kumwamba kwenikweniko.” (Aheberi 9:12, 24) Pamene akuukitsidwa, iwo amavala matupi omwe sangawonongeke ndiponso amapatsidwa moyo womwe sungafe. Yehova ndi amene amawapatsa zimenezi, zomwe zikuimira kupatsidwa “mana obisika” omwe sangawonongeke. Kagulu kameneka ka anthu opambana pa nkhondo kali ndi mwayi waukulu kwambiri.—1 Akorinto 15:53-57.
20, 21. (a) Kodi kupereka mwala woyera kwa Akhristu odzozedwa kukuimira chiyani? (b) Popeza kuti pali miyala yoyera 144,000 yokha, kodi a khamu lalikulu ali ndi chiyembekezo chotani?
20 Akhristu amenewa amalandiranso “mwala woyera.” Kale m’makhoti a Aroma, miyala yotere ankaigwiritsa ntchito popereka chiweruzo.b Mwala woyera unkatanthauza kuti munthu sanamupeze ndi mlandu, koma mwala wakuda unkatanthauza kuti amupeza ndi mlandu, ndipo kawirikawiri ankaphedwa. Mfundo yakuti Yesu akupereka “mwala woyera” kwa Akhristu a ku Pegamo ikusonyeza kuti iye sanawapeze ndi mlandu ndiponso kuti iwo ndi oyera. Koma mawu a Yesu amenewa ayenera kuti ali ndi tanthauzo linanso. M’nthawi ya Aroma, miyala imeneyi ankaigwiritsanso ntchito ngati matikiti olowera pakhomo kumalo amene kukuchitika zinthu zinazake zofunika kwambiri. Choncho mwala woyera ungasonyeze chinthu china chapadera kwambiri chimene Mkhristu wodzozedwa aliyense amene akupambana pa nkhondo akusangalala nacho. Iye amaloledwa kulowa kumalo olemekezeka kumwamba, kuti akakhale nawo pa ukwati wa Mwanawankhosa. Miyala yoyerayi ilipo 144,000 yokha basi.—Chivumbulutso 14:1; 19:7-9.
21 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti inuyo a khamu lalikulu amene mumalambira limodzi ndi odzozedwawo, simudzalandira madalitso alionse? Ayi, sichoncho. Ngakhale kuti simudzalandira mwala woyera wokuthandizani kuti mukalowe kumwamba, ngati mutapirira, mungathe kudzapulumuka pa chisautso chachikulu n’kudzagwira nawo ntchito yosangalatsa yobwezeretsa Paradaiso padziko lapansi. Anthu okhulupirika amene anakhalapo kale Chikhristu chisanayambe adzaukitsidwa n’kugwira nawo ntchito imeneyi. Enanso amene adzaukitsidwe ndi a nkhosa zina amene amwalira posachedwapa. Kenako, anthu onse owomboledwa amene anamwalira adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.—Salimo 45:16; Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9, 14.
22, 23. Kodi dzina lolembedwa pamwala woyera umene umaperekedwa kwa Akhristu odzozedwa likuimira chiyani, nanga kodi zimenezi n’zolimbikitsa bwanji?
22 Kodi ndi dzina latsopano liti limene lalembedwa pamwala woyerawo? Dzina ndi njira yodziwira munthu komanso yomusiyanitsira ndi anthu ena. Akhristu odzozedwa amenewa amalandira mwala woyera akapambana pa nkhondo ndi kumwalira ali okhulupirika padziko lapansi. N’zoonekeratu kuti dzina la Mkhristu limene lalembedwa pamwala woyerawo likutanthauza kuti mwini wakeyo adzapatsidwa mwayi wapadera wokakhala ndi Yesu kumwamba. Anthu amene dzina lawo lalembedwa pamwalawo ndi okhawo amene adzapatsidwe mwayi wapadera wokhala mafumu mu Ufumu wa kumwamba. Choncho dzinali likuimira udindo kapena ntchito imene azidzagwira, ndipo “wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.”—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:12.
23 Kudziwa zimenezi kumalimbikitsa kwambiri Akhristu odzozedwa kuti ‘amve zimene mzimu ukunena ku mipingo’ ndi kuzigwiritsa ntchito. Zimalimbikitsanso kwambiri anzawo a khamu lalikulu, kuti azitumikira nawo Mulungu mokhulupirika pa nthawi imene odzozedwawo ali padziko lapansi. Iwo amasangalala kutumikira nawo limodzi polalikira za Ufumu wa Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a Onaninso 1 Akorinto 3:3, 4, 18, 19; 2 Akorinto 11:13; Agalatiya 4:9; Aefeso 4:14, 15; Afilipi 3:18, 19; Akolose 2:8; 1 Atesalonika 3:5; 2 Atesalonika 2:1-3; 1 Timoteyo 6:3-5; 2 Timoteyo 2:17; 4:3, 4; Tito 1:13, 14; 3:10; Aheberi 10:26, 27.
b Onani Machitidwe 26:10. Mawu akuti “ine ndinali kuvomereza” anachokera ku mawu achigiriki amene amatanthauza kuti “ndinaponya mwala [kapena kuti ndinaponya voti] motsutsana nawo.”
[Zithunzi patsamba 43]
Kumalo osungirako zinthu zakale otchedwa Pergamon ku Berlin kuli zithunzi zosonyeza kuti anthu a ku Pegamo ankalambira kwambiri mafano
[Chithunzi patsamba 45]
Mana ena ankawabisa mulikasa la pangano. Mfundo yakuti Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo amapatsidwa mana obisika, ikutanthauza kuti Akhristu amenewa amapatsidwa moyo umene sungafe
[Chithunzi patsamba 45]
Mwala woyera umaperekedwa kwa anthu amene aloledwa kukakhala nawo pa ukwati wa Mwanawankhosa