“Iri Ndi Tsiku la Masiku Onse”
“Ndinagwidwa ndi mzimu m’tsiku la Ambuye.”—CHIVUMBULUTSO 1:10.
1. Ndi “tsiku” lotani limene tikukhalamo, ndipo nchifukwa ninji nsonga imeneyi iri yosangalatsa chotero?
“IRI ndi tsiku la masiku onse. Onani, Mfumu ilamulira!” Mawu opambana amenewa olankhulidwa ndi prezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Bible and Track Society kumbuyoko mu 1922 adakali kuti sangalatsabe lerolino. Iwo akupitirizabe kutikumbutsa ife kuti tikukhala mu nthaŵi yosangalatsa kwambiri ya m’mbiri yonse, nthaŵi yotchedwa mu Baibulo “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10) Ilo ndithudi liri “tsiku la masiku onse,” popeza kuti iri nthaŵi imene Yehova, kupyolera mwa Ufumu wa Kristu, adzabweretsa kukwaniritsidwa kwa zifuno Zake zonse zokulira ndipo adzayeretsa dzina Lake pamaso pa zolengedwa zonse.
2, 3. (a) Kodi tsiku la Ambuye liri la utali wotani? (b) Ndi kuti kumene tingapeze ponena za tsiku limeneli?
2 Tsiku limeneli linayamba mu 1914 pamene Yesu anakhazikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo lidzapitirizabe kupyola kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi, pamene Kristu ‘adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate.’ (1 Akorinto 15:24) Akristu okhulupirika ayang’ana kutsogolo ku tsiku la Ambuye kwa mazana ochuluka. Tsopano, potsiriza pake liri pano! Nchiyani chimene “tsiku la masiku onse” limeneli latanthauza kaamba ka anthu a Mulungu ndi kaamba ka dziko mwachisawawa?
3 Bukhu la Baibulo lomwe limatiuza ife zochulukira ponena za tsiku la Ambuye liri Chivumbulutso. Chifupifupi maulosi onse a bukhu limeneli akukwaniritsidwa mkati mwa tsiku la Ambuye. Koma Chivumbulutso chiri kokha kaindeinde wa mpambo wa mabukhu aulosi amene amatiuza ife ponena za tsiku limenelo. Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, ndi Danieli, pakati pa ena, nawonso amatiuza ife ponena za ilo. Kaŵirikaŵiri, chimene amanena chimatithandiza ife kumvetsetsa bwino kwambiri maulosi a mu Chivumbulutso. Tiyeni tiwone mmene bukhu la Ezekieli mwachindunji limawunikirira pa kukwaniritsidwa kwa Chivumbulutso mkati mwa tsiku la Ambuye.
Amuna Anayi a pa Akavalo
4. Mogwirizana ndi Chivumbulutso, mutu 6, nchiyani chomwe chinachitika pa chiyambi cha tsiku la Ambuye?
4 Mwachitsanzo, m’mutu wachisanu ndi chimodzi wa Chivumbulutso, mtumwi Yohane akulongosola masomphenya okulira: “Ndipo ndinapenya, ndipo, tawonani! kavalo woyera; ndi womkwerayo anali nawo uta; ndipo anampatsa korona, ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” (Chivumbulutso 6:2) Ndani yemwe ali mwamuna wa pa kavalo wolakika ameneyu? Si wina aliyense kuposa Yesu Kristu, wokhazikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi wokwera kukagonjetsa adani ake. (Salmo 45:3-6; 110:2) Kukwera kopambana kwa Yesu kunayambira kumbuyoko mu 1914, pachiyambi penipeni pa tsiku la Ambuye. (Salmo 2:6) Kugonjetsa kwake koyamba kwenikweni kunali kuponya Satana ndi ziwanda zake padziko lapansi. Chotulukapo kaamba ka mtundu wa anthu? “Tsoka mtunda ndi nyanja.”—Chivumbulutso 12: 7-12.
5. Ndi zochitika zowopsya zotani zomwe zimatsatira Wokwera pa kavalo woyera, ndipo ndi ulamuliro wotani umene chochitika chirichose chiri nawo?
5 Panatsatira m’masomphenyawo zinthu zitatu zowopsya: kavalo wofiira wophiphiritsira nkhondo, kavalo wakuda wophiphiritsira njala, ndi kavalo wotumbuluka amene womkwerapo wake anatchedwa “Imfa.” Ponena za kavalo wachinayi ameneyu, timaŵerenga kuti: “Ndipo ndinapenya, ndipo tawonani! kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera dzina lake ndiye Imfa. Ndipo Hade anatsatana naye. Ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinayi la dziko, kukapha ndi lupanga ndi njala ndi imfa ndi zirombo za padziko.”—Chivumbulutso 6:3-8; Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11.
6. Kodi nchiyani chomwe chakhala chotulukapo pa dziko lapansi cha akavalo atatu odzetsa mantha ndi okwerapo amenewa?
6 Zowona ku ulosiwo, mtundu wa anthu wavutika moipa ndi nkhondo, njala, ndi matenda chiyambire 1914. Koma mwamuna wokwera pa kavalo wachinayi amaphanso mwa kugwiritsira ntchito “zirombo za padziko.” Kodi ichi chakhala chochitika chodziŵika chiyambire 1914? Kulingalira kwa ulosi wofananawo kochitidwa ndi Ezekieli kumathandiza kuika mbali imeneyi ya ulosi m’kayang’andiwe kabwino.
7. (a) Ndi ulosi wotani umene Ezekieli ananena ponena za Yerusalemu? (b) Ndimotani mmene ulosi umenewu unakwaniritsidwira?
7 Akumalemba mwinamwake zaka zisanu chiwonongeko cha Yerusalemu chisanachitike mu 607 B.C.E., Ezekieli analosera chilango choipitsitsa kaamba ka Ayuda chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. Iye analemba pansi pa kuwuziridwa kuti: “Ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anyi owawa—lupanga, njala zirombo zoipa, ndi mliri—kuudulira anthu ndi nyama.” (Ezekieli 14:21; 5:17) Kodi chimenechi chinakwaniritsidwa m’chenicheni kumbuyoko? Mosakaikira Yeruslamu anavutika ndi njala ndi mkhalidwe wa nkhondo pamene mapeto ake anayandikira. Ndipo njala kaŵirikaŵiri imadzetsa matenda. (2 Mbiri 36:1-3, 6, 13, 17-21; Yeremiya 52:4-7; Maliro 4:9, 10) Kodi panalinso mliri weniweni wa zirombo za mthengo pa nthaŵi imeneyo? Mwachidziŵikire panali nkhani za kugwidwa kwa anthu kapena ngakhale kuphedwa ndi zinyama, popeza Yeremiya ananeneratunso chimenechi.—Levitiko 26:22-33; Yeremiya 15:2, 3.
8. Ndi mbali yotani imene zirombo zakuthengo zachita mkati mwa tsiku la Ambuye pakali pano?
8 Bwanji ponena za lerolino? M’maiko otukuka, nyama za kuthengo siziri vuto lowopsya limene zinali panthaŵi imodzi. M’maiko ena, ngakhale kuli tero, nyama za kuthengo zikupitirizabe kutenga minkhole, makamaka ngati tiphatikizapo njoka ndi ng’ona pakati pa “zirombo za pa dziko lapansi.” Imfa zowopsya zoterozo sizimachitiridwa ripoti kaŵirikaŵiri m’nkhani za mitundu yonse, koma ziri zodziŵika. Bukhu lakuti Planet Earth—Flood limalankhula za ambiri mu India ndi Pakistan omwe “amwalira mu ululu kaamba ka kulumidwa ndi njoka zaululu” pamene akuyesera kuthaŵa kusefukira kwa madzi. India Today inchitira ripoti mudzi umodzi mu West Bengal kumene kuyerekezera kwa akazi 60 ataikiridwa amuna awo chifukwa cha kuwukira kwa kambuku. Matsoka oterowo angakhoze kukhala ngakhale ofala mowonjezereka mtsogolo pamene chitaganya cha anthu chikunyonyotsoka ndi pamene njala iwonjezeka.
9. Ndi mtundu wina uti wa “nyama” womwe wapangitsa tsoka ndi kuvutika pakati pa mtundu wa anthu mkati mwa zana lino?
9 Koma Ezekieli analankhula mwachindunji ku mtundu wina wa “nyama” pamene iye ananena kuti: “Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula, womwetula nyama. Analusira miyoyo . . . Akalonga ake mkati mwake akunga afisi akumwetula nyama.” (Ezekieli 22:25, 27) Chotero anthu angakhoze kuchita mofanana ndi nyama nawonso, ndipo ndimotani nanga mmene mtundu wa anthu wavutikira kuchokera ku owukira oterowo mkati mwa zana lathu! Ambiri afa pa manja a aupandu ndi achifwamba a uchinyama. Inde, m’njira yoposa imodzi imfa yapeza kututa kwake kokulira kwa minkhole kuchokera ku “zirombo za pa dziko lapansi.”
10. Nchiyani chimene kundandalitsa kwa Yohane kwa nkhondo, njala, matenda, ndi zirombo zakuthengo monga zochititsa imfa kumatithandiza ife kuwona?
10 Kundandalitsidwa kwa nkhondo, njala, matenda, ndi zirombo m’masomphenya a Yohane kumatithandiza kuwona kuti kuvutika kopiriridwa ndi Yerusalmeu mu 607 B.C.E. kunayenera kulinganizidwa m’zochitika zambiri mkati mwa tsiku lathu. Tsiku la Ambuye chotero latanthauza kale kuvutika kaamba ka dziko, kwakukulukulu chifukwa chakuti kulamulira kwa mtundu wa anthu kwakana kugonjera ku mwamuna wokwera pa Kavalo woyambirirayo, Mfumu yoikidwa, Yesu Kristu. (Salmo 2:1-3) Bwanji, ngakhale ndi tero, ponena za anthu a Mulungu? Nchiyani chomwe tsiku la Ambuye latanthauza kwa iwo?
Kuyesa Kachisi
11. Pa Chivumbulutso 11:1, nchiyani chomwe Yohane analamulidwa kuchita, ndipo ichi chinalozera ku kachisi uti?
11 Pa Chivumbulutso 11:1, mtumwi Yohane akunena kuti: “Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo ndi kuti: ‘Tanyamuka nuyese kachisi wa Mulungu ndi guwa la nsembe ndi iwo akulambiramo.’” Kuyesa kwa masomphenya kwa kachisi kumeneku kunali kwa tanthauzo kwenikweni kaamba ka anthu a Mulungu. Ndi mabwalo a kachisi ati amene Yohane anayesa? Osati kachisi wa Chiyuda weniweni kumene Yohane analambirirako asanakhale Mkristu. Kachisi ameneyo anakanidwa ndi Yehova, ndipo anawonongedwa mu 70 C.E. (Mateyu 23:37–24:2) M’malomwake, anali makonzedwe okulira a kachisi wauzimu wa Yehova. M’kachisi wophiphiritsira ameneyu, Akristu odzozedwa amatumikira monga ansembe ang’ono m’mabwalo a padziko lapansi.—Ahebri 9:11, 12, 24; 10:19-22; Chivumbulutso 5:10.
12. Ndi liti pamene kachisi ameneyu anakhalako, ndipo ndi zochitika zotani zomwe zinachitika ponena za iye m’zana loyamba?
12 Kachisi ameneyo anakhalako mu 29 C.E. pamene Yesu anadzozedwa monga wansembe wamkulu. (Ahebri 3:1; 10:5) Iye anafunikira kukhala ndi ansembe ang’ono 144,000, ndipo m’zana loyamba ambiri a amenewa anasankhidwa, kusindikizidwa chizindikiro, ndipo kenaka anamwalira okhulupirika. (Chivumbulutso 7:4; 14:1) Koma pamene Akristu a m’zana loyamba amenewo anamwalira, iwo anagona m’manda, osaukitsidwa mwamsanga kupita kumwamba. (1 Atesalonika 4:15) Ndiponso, pambuyo pa zana loyamba mpatuko wokulira unalowerera, ndipo Akristu aunsembe odzozedwa anazingidwa ndi “anamsongole” omakulakula, ampatuko. (Mateyu 13:24-30) Kupyola m’mazana onse chiyambire pamenepo, chikanakhala bwino lomwe kufunsidwa kuti: ‘Kodi ansembe ang’ono onse 144,000 adzasindikizidwa chizindikiro?’ ‘Kodi onse omwe anafa mokhulupirika adzawukitsidwa kutumikira m’mabwalo akumwamba?’ Kuyesa kwa kachisi kwa masomphenya kunasonyeza kuti yankho ku lirilonse la mafunso amenewa liri inde. Nchifukwa ninji?
13. Kodi nchiyani chimene kuyesa mabwalo a kachisi kwa Yohane kunatsimikizira, ndipo nchiyani chomwe chinachitika kumayambiriro m’tsiku la Ambuye?
13 Chifukwa chakuti mu ulosi wa Baibulo kuyesa kwa chinachake kaŵirikaŵiri kumasonyeza kuti chifuno cha Yehova kaamba ka chinthu chimencho chiri chotsimikizirika kugwiriridwapo ntchito kotheratu. (2 Mafumu 21:13; Yeremiya 31:39; Maliro 2:8) Chotero, masomphenya a kuyesa kwa Yohane kwa mabwalo a kachisi anali chitsimikiziro chakuti mkati mwa tsiku la Ambuye, zifuno zonse za Yehova zonena za kachisi zikakwaniritsidwa. M’chigwirizano ndi ichi ndipo molingana ndi umboni wonse, awo a odzozedwa omwe anali atafa kale mokhulupirika anayamba kuwukitsidwa ku malo awo olonjezedwa m’mabwalo akumwamba kuyambira mu 1918. (1 Atesalonika 4:16; Chivumbulutso 6:9-11) Koma bwanji ponena za otsala a 144,000?
14. Nchiyani chomwe chinachitika kwa Akristu odzozedwa nkhondo yoyamba ya dziko isanachitike ndi mkati mwake?
14 Ngakhale lisanayambe tsiku la Ambuye, Akristu odzozedwa omwe anatuluka m’Chikristu cha Dziko chopatuka anayamba kusonkhanitsidwa m’gulu losiyana. Iwo anali atamanga mbiri yabwino ya kukhulupirika m’kulengeza kufunika kwa chaka cha 1914, koma m’chaka chosankha chimenecho, pamene nkhondo yoyamba ya dziko inali kuchitika, iwo anayamba kuvutika ndi kupsyinjidwa, ‘kutswanya.’ Ichi chinafikira pa kaindeinde mu 1918 pamene otsogolera a Watch Tower Sosaite anaikidwa m’ndende, ndipo ntchito yolalikira yolinganizidwa inali pafupi kulekeka. Panthaŵi imeneyo, iwo anali ‘ophedwa’ kotheratu. (Chivumbulutso 11:2-7) Kodi nchiyani chimene chinali tanthauzo la kuyesa mabwalo a kachisi kaamba ka Akristu amenewa?
15. Nchiyani chomwe kuyesa kwa kachisi wa m’masomphenya kuntanthauza kaamba ka anthu a Mulungu a m’tsiku la Ezekieli?
15 M’chaka cha 593 B.C.E., zaka 14 pambuyo pa kuwonongedwa kwa kachisi wa Yehova m’Yerusalemu, Ezekieli anawona nyumba ya Yehova m’masomphenya. Iye anapatsidwa kuchezera kokulira kwa kachisi ameneyu ndipo anayang’anira pamene iriyonse ya mbali zake inali kuyesedwa mosamalitsa. (Ezekieli, mitu 40-42) Kodi ichi chinatanthauzanji? Yehova iyemwini analongosola: Kuyesedwa kwa kachisi kunatanthauza chiyeso kaamba ka anthu a Ezekieli. Ngati iwo akanadzichepetsa iwo eni, kulapa machimo awo, ndi kulinga ku malamulo a Yehova, iwo akawuzidwa muyeso wa kachisiyo. Ichi mwachiwonekere chikawalimbikitsa iwo m’chiyembekezo chakuti tsiku lina anthu a Yehova akamasulidwa kuchoka m’Babulo ndipo kachiŵirinso kulambira Yehova m’kachisi wake weniweni.—Ezekieli 43:10, 11.
16. (a) Kodi kuyesa kwa Yohane kwa bwalo la kachisi kunatsimikizira anthu a Mulungu za chiyani kumbuyoko mu 1918? (b) Ndimotani mmene ichi chinakwaniritsidwira?
16 Mofananamo, ngati Akristu okhumudwitsidwa amenewo kumbuyoko mu 1918 akadzichepetsa iwo eni ndi kulapa machimo alionse omwe anachita, iwo akamasulidwa kukhala ndi dalitso la Yehova ndi kuchita mbali yokulira m’makonzedwe ake a kachisi. Ndipo ichi ndi chimene chinachitika. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 11:11, iwo ‘anaima,’ kapena mophiphiritsira anawukitsidwa. Kuwukitsidwa kofananako kwa mu ulosi wa Ezekieli kunaimira kubwezeretsedwa kwa Ayuda ku dziko lawo. (Ezekieli 37:1-14) ‘Kuwukitsidwa’ kwamakono kumeneku kunatembenuka kukhala kubwezeretsedwa kwa anthu a Mulungu kuchoka ku mkhalidwe wawo wokhumudwitsidwa, chifupifupi wosagwira ntchito, kupita ku waumoyo, mkhalidwe wokangalika mu umene akachita mbali yokulira mu utumiki wa Yehova. ‘Kuwukitsidwa’ koteroko kunachitika mu 1919.
Mpukutu Waung’ono
17. (a) Longosolani masomphenya a Yohane pa Chivumulutso 10:1. (b) Ndani yemwe anali mngelo amene Yohane anawona, ndipo ndi mkati mwa tsiku lotani pamene masomphenyawo anali pafupi kukwaniritsidwa?
17 Pa Chivumbulutso 10:1, Yohane anawona “mngelo wina wolimba alikutsika kumwamba, wovala mtambo, ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuŵa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto.” Ichi mwanjira ina yake chimafanana ndi masomphenya a Yehova owonedwa papitapo ndi Ezekieli ndipo ndi Yohane iyemwini. (Ezekieli 8:2; Chivumbulutso 4:3) Koma Yohane pano anawona mngelo, osati Yehova. Chotero, afunikira kukhala anali Mwana wamkulu waungelo wa Yehova, Yesu Kristu, amene “ali chifanefane cha Mulungu.” (Akolose 1:15) Ndiponso, Chivumbulutso 10:2 chimaika Yesu kukhala kuimirira m’malo aulamuliro waukulu, wokhala ndi “phazi lake la kulamanja pa nyanja, koma la kulamanzere pa dziko lapansi.” Chotero mngelo amaimira Yesu mkati mwa tsiku la Ambuye.—Onani Salmo 8:4-8; Ahebri 2:5-9.
18. (a) Nchiyani chomwe Yohane analamuliridwa kudya? (b) Mu masomphenya ofananawo, nchiyani chomwe Ezekieli analamuliridwa kudya, ndipo ndi chotulukapo chotani?
18 Yesu, mumkhalidwe wake wokulira wa m’masomphenya, ali ndi mpukutu wang’ono m’dzanja lake, ndipo Yohane akulangizidwa kutenga mpukutuwo ndi kuwudya. (Chivumbulutso 10:8, 9) Mwanjirayi, Yohane ali ndi chokumana nacho chofanana kwenikweni ndi chija cha Ezekieli, yemwe analamuliridwanso kudya mpukutu wa m’masomphenya. M’nkhani ya Ezekieli, Yehova iyemwini anapereka mpukutuwo kwa mneneriyo, ndipo Ezekieli anawona kuti “munalembedwa momwemo nyimbo za maliro ndi chisoni ndi tsoka.” (Ezekieli 2:8-10) Ezekieli akusimba kuti: “Momwemo ndinaudya, ndi m’kamwa mwanga munazuna ngati uchi.” (Ezekieli 3:3) Kodi kudya kwa mpukutuwo kuntanthauzanji kwa Ezekieli?
19. (a) Nchiyani chomwe chinaimiridwa ndi kudya mpukutuwo kwa Ezekieli? (b) Ndani yemwe anafunikira kulandira mauthenga owawa omwe Ezekieli analamuliridwa kulalikira?
19 Mwanchiwonekere, mpukutuwo unali ndi chidziŵitso cha ulosi chouziridwa. Pamene Ezekieli anadya mpukutuwo, iye analandira ntchito ya kulengeza chidziŵitso chimenechi kumlingo wakuti chinakhala mbali ya iye. (Yerekezani ndi Yeremiya 15:16.) Koma zamkati mwa mpukutuwo sizinali zozuna kwa ena. Mpukutuwo unali wodzala ndi “nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.” Kodi uthenga wowawa umenewo unali wa yani? M’malo oyambirira, Ezekieli anauzidwa kuti: “Wobadwa ndi munthu iwe, muka nufike kunyumba ya Israyeli, nunene nawo mawu anga.” (Ezekieli 3:4) Pambuyo pake, uthenga wa Ezekieli unafalikira kuphatikiza mitundu ya kunja yowazungulira.—Ezekieli, mitu 25-32.
20. Nchiyani chomwe chinachitika pamene Yohane anadya mpukutu waung’ono, ndipo nchiyani chomwe chinatulukapo kuchokera ku kuchita kwake tero?
20 M’nkhani ya Yohane, zotulukapo za kudya kwake mpukutuwo zinali zofananako. Iye akusimba kuti: “Ndipo ndinatenga [mpukutu waung’ono, NW] m’dzanja la mngelo ndipo ndinaudya ndipo unali m’kamwa mwanga wozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinaudya, m’mimba mwanga mudawawa.” (Chivumbulutso 10:10) Kudya mpukutu kunali kozuna kaamba ka Yohane nayenso. Chinali chosangalatsa kukhala ndi mawu a Yehova kukhala mbali ya iye. Komabe uthengawo unali ndi nosonga zowawa kwa iwo. Zowawa kwa yani? Yohane anauzidwa kuti: “uyenera kuneneranso pa anthu ndi mitundu ndi manenedwe ndi mafumu ambiri.”—Chivumbulutso 10:11.
21. (a) Nchiyani chomwe Akristu odzozedwa anachita mu 1919 chomwe chinafanana ndi kudya mpukutu wang’ono kwa Yohane, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Nchiyani chomwe chinali chotulukapo cha Chikristu cha Dziko ndi dziko mwachisawawa?
21 Ndimotani mmene zonsezi zakwaniritsidwira mkati mwa tsiku la Ambuye? Mogwirizana ndi nsonga za m’mbiri, kumbuyoko mu 1919 Akristu okhulupirika anatenga thayo la kutumikira Yehova kotheratu kotero kuti inakhala mbali ya iwo, ndipo ichi chinali chozuna kwenikweni. Koma dalitso lawo ndi thayo zinatsimikizira kukhala zowawa kwa ena—makamaka kwa atsogoleri a Chikristu cha Dziko. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti Akristu odzozedwa okhulupirika amenewa molimba mtima analengeza uthenga wa Yehova wonse kaamba ka mtundu wa anthu. Osati kokha kuti iwo analalikira “mbiri yabwino ya ufumu” koma anavumbulanso mkhalidwe wakufa mwauzimu wa Chikristu cha Dziko ndi dziko mwachisawawa.—Mateyu 24:14; Chivumbulutso 8:1-9:21; 16:1-21.
22. (a) Ndi mwanjira yokulira yotani mmene odzozedwa akhala akugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova mkati mwa tsiku la Ambuye pakali pano? (b) Nchiyani chomwe tsiku la Ambuye latanthauza kwa dziko la Satana ndi kaamba ka anthu a Mulungu?
22 Khamu lokhulupirika limeneli la Akristu linagwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kusonkhanitsa otsirizira a 144,000 kaamba ka kusindikizidwa chizindikiro, ndipo anatsogolera kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu, omwe ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. (Chivumbulutso 7:1-4, 9, 10) Khamu lalikulu limeneli limachita mbali yofunika m’chifuniro cha Yehova kulinga ku dziko iri lapansi, ndipo kuwonekera kwake kwapangitsa chimwemwe chokulira ponse paŵiri kumwamba ndi padziko lapansi. (Chivumbulutso 7:11-17; Ezekieli 9:1-7) Chotero, “tsiku la masiku onse” limenli latanthauza kale kuvutika kaamba ka dziko la Satana koma madalitso olemerera kaamba ka anthu a Yehova. Tiyeni tiwone, tsopano, mmene ichi chidzapitirizira kukhala chowona pamene tsiku la Ambuye lipitiriza.
Kodi Mungalongosole?
◻ Nchiyani chomwe chiri tsiku la Ambuye?
◻ Kodi ndi mbali yowononga yotani yomwe “zirombo zadziko lapansi” zikuchita mkati mwa tsiku la Ambuye?
◻ Ndi chitsimikiziro chotani chimene Yehova anapereka mwa kugwiritsira ntchito kuyesa kwa Yohane kwa bwalo la kachisi?
◻ Nchiyani chomwe kudya mpukutu waung’ono kwa Yohane kunatanthauza kaamba ka otsalira odzozedwa mu 1919?
◻ Kudzafika pano, nchiyani chomwe tsiku la Ambuye latanthauza kaamba ka anthu a Mulungu ndi kaamba ka dziko mwachisawawa?
[Chithunzi patsamba 13]
Kuyesa kachisi kwa Yohane kunapereka chitsimikiziro cholimba kwa odzozedwa m’tsiku la Ambuye