Mutu 11
Angelo a Mulungu Amatithandiza
ANTHU ena amanena kuti amakhulupirira zimene angaone basi. Koma kuganiza motero ndi kupusa. Pali zinthu zambiri zimene sitinazionepo ndi maso athuŵa koma timakhulupirira kuti ziliko. Kodi ungatchuleko chimodzi?—
Bwanji nanga mpweya umene timapuma? Kodi timaumva pathupi lathu?— Kweza dzanja lako ndi kuliuzira. Kodi wamva chilichonse?— Inde wamva, koma sunauone mpweyayo, kodi wauona ngati?—
Takambirana kale kuti mizimu sioneka. Tinaphunzira kuti ina ndi yabwino koma ina ndi yoipa. Tandiuza mayina a mizimu ina yabwino imene sitingaione.— Eya, pali Yehova Mulungu, Yesu, ndi angelo abwino. Kodi ukuganiza kuti kulinso angelo oipa?— Baibulo limanena kuti aliko. Tandiuza zimene waphunzira za iwo.—
Zimene tikudziŵa n’zakuti angelo onse, abwino ndi oipa, ali ndi mphamvu kuposa ife. Mphunzitsi Waluso anali kudziŵa zambiri za angelo. Chifukwa chake n’chakuti anali mngelo asanabadwe ngati khanda padziko lapansi. Anali kukhala ndi angelo ena kumwamba. Iye anali kudziŵa angelo ambirimbiri. Kodi angelo onseŵa ali ndi mayina?—
Eya, tinaphunzira kuti Mulungu anapatsa nyenyezi mayina. Chifukwa cha zimenezi tikutsimikiza kuti angelo onse ali ndi mayina awo. Ndipo tikudziŵa kuti iwo amalankhulana chifukwa Baibulo limatiuza kuti pali ‘chinenero cha angelo.’ (1 Akorinto 13:1) Kodi ukuganiza kuti angelowo amalankhulana za chiyani? Kodi amanena za ife padziko lapansi pano?—
Tikudziŵa kuti angelo a Satana, kapena kuti ziwanda, akuyesetsa kutikakamiza kuti tisamvere Yehova. Choncho iwo ayenera kuti akamalankhulana, amanena za zimene angachite kuti atisokoneze. Iwo amafuna kuti ife tifanane nawo kuti Yehova asiye kutikonda. Nanga bwanji angelo okhulupirika a Mulungu? Kodi ukuganiza kuti iwonso amalankhula za ife?— Inde, amatero. Iwo amafuna kutithandiza. Leka ndikuuze mmene angelo ena a Mulungu anathandizira anthu amene anali kukonda Yehova ndi kumutumikira.
Mwachitsanzo, panali munthu wina dzina lake Danieli. Iye anali kukhala ku Babulo. Anthu ambiri kumeneko sanali kukonda Yehova. Anthuwo anakhazikitsa lamulo lolangira munthu aliyense amene anapemphera kwa Yehova Mulungu. Koma Danieli sanasiye kupemphera kwa Yehova. Kodi ukudziŵa zimene iwo anamuchita Danieli?—
Inde, anthu oipa amenewo anaponya Danieli m’dzenje la mikango. Danieli anali yekhayekha m’dzenjemo ndi mikango yanjala. Kodi ukudziŵa chimene chinachitika mmenemo?— ‘Mulungu anatuma mngelo wake ndipo anaitseka pakamwa mikango,’ anatero Danieli. Mikangoyo sinamupweteke m’pang’ono pomwe! Angelo angachitire anthu amene amatumikira Yehova zinthu zabwino kwambiri.—Danieli 6:18-22.
Nthaŵi inanso Petro anali m’ndende. Ngati ukukumbukira, Petro anali bwenzi la Mphunzitsi Waluso, Yesu Kristu. Anthu ena sanakondwere pamene Petro anawauza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Choncho iwo anaika Petro m’ndende. Asilikali anali kudikirira Petro kuti asathaŵe. Kodi panali wina amene akanamuthandiza?—
Petro anali kugona pakati pa alonda aŵiri, ndipo manja ake anamangidwa unyolo. Koma Baibulo limanena kuti: ‘Taonani, mngelo wa Yehova anafika, ndipo kuunika kunawala m’ndendemo; ndipo anakhudza Petro m’nthiti, ndi kumuutsa iye kuti, Tauka msanga’!
Pamenepo maunyolo amene anali m’manja mwa Petro anamasuka ndi kugwera pansi! Ndiyeno mngeloyo anauza Petro kuti: ‘Vala zovala zako ndi nsapato zako, ndipo unditsate.’ Alondawo sanathe kuletsa zimenezi chifukwa mngelo ndiye anali kuthandiza Petro. Kenako anafika pachitseko chachitsulo, ndipo panachitika zodabwitsa. Chitsekocho chinatseguka chokha! Mngelo ameneyo anamasula Petro kuti apitirize kulalikira.—Machitidwe 12:3-11.
Kodi ukuganiza kuti angelo angatithandize ifenso?— Inde, angatithandize. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iwo adzatiteteza kuti tisavulale?— Ngati tichita dala zinthu zimene tikudziŵa kuti zingatipweteke, angelo sadzatiteteza. Ngakhale ngati sitichita zoterozo, tingavulalebe. Angelo sanalamulidwe kuletsa zimenezi. Koma Mulungu wawapatsa ntchito yapadera kuti achite.
Baibulo limanena kuti mngelo wina amauza anthu kulikonse kuti alambire Mulungu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Kodi mngelo ameneyo amawauza bwanji anthu zimenezo? Kodi amafuula ali kumwamba kuti aliyense amve?— Ayi. M’malo mwake, anthu amene amakhulupirira Yesu padziko lapansi amauza ena za Mulungu, ndipo angelo amatsogolera ntchito yawoyo. Angelowo amaonetsetsa kuti munthu amene akufuna kwambiri kudziŵa Mulungu apeze mpata wa kumva za iye. Ifenso tiyenera kuchita ntchito imeneyi, ndipo angelo adzatithandiza.
Koma bwanji ngati anthu amene sakonda Mulungu akutivutitsa? Bwanji atatiika m’ndende? Kodi angelowo angatimasule?— Iwo ali nayo mphamvu yotimasula, koma sikuti amatero nthaŵi zonse.
Paulo, amene anali kukhulupirira Yesu, anali m’ndende nthaŵi inayake. Anali paulendo m’boti ndipo kunali chimphepo. Koma angelo sanamumasule nthaŵi yomweyo. Chifukwa chake chinali chakuti panali anthu ena amene anafunika kumva za Mulungu. Mngelo ananena kuti: ‘Usaope Paulo; udzaimirira pamaso pa Kaisara.’ Inde, Paulo anafunika kupita kwa wolamulira dziko lonse, Kaisara, kuti akamulalikire. Nthaŵi zonse angelo anali kudziŵa kumene Paulo anali, ndipo anamuthandiza. Ifenso adzatithandiza ngati titumikira Mulungu ndi mtima wonse.—Machitidwe 27:23-25.
Palinso ntchito ina yaikulu imene angelo adzachita, ndipo adzachita ntchito imeneyo posachedwapa. Nthaŵi yakuti Mulungu awononge anthu oipa ili pafupi kwambiri. Onse amene salambira Mulungu woona adzawonongedwa. Aja amene amanena kuti sakhulupirira angelo chifukwa chakuti angelowo sawaona adzadziŵa kuti ndi olakwa.—2 Atesalonika 1:6-8.
Nanga ife zidzatikhalira bwanji panthaŵiyo?— Ngati tili kumbali imodzi ndi angelo a Mulungu, iwo adzatithandiza. Koma kodi ife tili kumbali yawodi?— Tili kumbali yawo ngati tikutumikira Yehova. Ndipo ngati tikutumikira Yehova, tiyenera kuuza anthu kuti iwonso azimutumikira.
Kuti mudziŵe zambiri za mmene angelo amathandizira anthu, ŵerengani Salmo 34:7; Mateyu 4:11; 18:10; Luka 22:43; ndi Machitidwe 8:26-31.