MUTU 6
Atumiki Othandiza Amagwira Ntchito Yofunika Kwambiri
POLEMBERA kalata mpingo wa ku Filipi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ine Paulo ndili pamodzi ndi Timoteyo monga akapolo a Khristu Yesu. Ndikulembera oyera onse ogwirizana ndi Khristu Yesu amene ali ku Filipi, komanso oyang’anira ndi atumiki othandiza.” (Afil. 1:1) Onani kuti m’kalatayi Paulo anatchula za atumiki othandiza. N’zoonekeratu kuti amuna amenewa ankagwira ntchito yofunika kwambiri pothandiza akulu mu mpingo pa nthawiyo. Ndi mmenenso zilili masiku ano. Atumiki othandiza amagwira ntchito zosiyanasiyana pothandiza oyang’anira ndipo zimenezi zimachititsa kuti mpingo uziyenda bwino.
2 Kodi mumadziwa atumiki othandiza a mu mpingo mwanu? Nanga kodi mumadziwa ntchito zimene amagwira zokuthandizani komanso zothandiza mpingo wonse? Yehova amayamikira kwambiri ntchito imene amunawa amagwira. Ponena za amuna amenewa, Paulo analemba kuti: “Amuna otumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndi ufulu waukulu wa kulankhula za chikhulupiriro, mwa Khristu Yesu.”—1 Tim. 3:13.
ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AYENERERE KUKHALA MTUMIKI WOTHANDIZA
3 Atumiki othandiza ayenera kutsatira mfundo zachikhristu pa moyo wawo, ayenera kukhala odalirika komanso osamalira bwino maudindo awo. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu amene Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Timoteyo, onena za zimene munthu ayenera kuchita kuti ayenerere kukhala mtumiki wothandiza. Iye anati: “Nawonso atumiki othandiza akhale opanda chibwana, osanena pawiri, osakonda kumwa vinyo wambiri, ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo. Akhale ogwira chikhulupiriro mwamphamvu, chimene ndi chinsinsi chopatulika cha Mulungu, ali ndi chikumbumtima choyera. Ndiponso, amenewa ayesedwe kaye ngati ali oyenerera, ndiyeno atumikire monga atumiki, popeza ndi opanda chifukwa chowanenezera. Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi, oyang’anira bwino ana awo ndi mabanja awo.” (1 Tim. 3:8-10, 12) Kutsatira mfundo zapamwamba zachikhristu zimenezi kumateteza mpingo kuti usaneneredwe zoipa chifukwa cha anthu amene asankhidwa kuti akhale pa maudindo.
4 Atumiki othandiza ayenera kukhala akhama mu utumiki mwezi uliwonse kaya akhale achinyamata kapena achikulire. Akamachita zimenezi, amakhala akutsanzira Yesu. Amasonyezanso kuti amafunitsitsa kuti anthu adzapulumuke ngati mmene Yehova amafunira.—Yes. 9:7.
5 Amuna amene akutumikira monga atumiki othandiza amasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani ya kavalidwe, kudzikongoletsa, kalankhulidwe komanso makhalidwe. Amakhalanso oganiza bwino zimene zimachititsa kuti azilemekezedwa ndi ena. Ndiponso amaona kuti mwayi wotumikira mu mpingo komanso ubwenzi wawo ndi Yehova ndi wamtengo wapatali.—Tito 2:2, 6-8.
6 Amuna amenewa asanakhale atumiki othandiza, ‘amayesedwa kaye ngati ali oyenerera,’ ndipo amakhala atasonyeza kale kuti ndi okhulupirika komanso odzipereka. Amakhalanso atasonyeza kuti amaika patsogolo zinthu za Ufumu ndipo akuyesetsa kuti ayenerere utumiki uliwonse umene angapatsidwe. Zoonadi, amuna amenewa ndi zitsanzo zimene ena mu mpingo angatsanzire.—1 Tim. 3:10.
NTCHITO ZA ATUMIKI OTHANDIZA
7 Atumiki othandiza amagwira ntchito zosiyanasiyana zothandiza abale ndi alongo, zomwe zimathandiza kuti oyang’anira azikhala ndi nthawi yokwanira yophunzitsa ndi kuweta nkhosa. Bungwe la akulu likamapereka ntchito zosiyanasiyana zoti atumiki othandiza azigwira, limaganizira za luso la mtumiki aliyense komanso zimene zikufunikira pampingopo.
Atumiki othandiza amagwira ntchito zosiyanasiyana zomwe zimathandiza kuti oyang’anira azikhala ndi nthawi yokwanira yophunzitsa ndi kuweta nkhosa
8 Mwachitsanzo, angasankhe mtumiki wothandiza wina kuti azisamalira mabuku n’cholinga choti tizipeza mabuku ophunzira komanso ogwiritsa ntchito mu utumiki. Ena angamasamalire maakaunti a mpingo kapena magawo. Enanso angapatsidwe ntchito yosamalira maikofoni, zokuzira mawu, kulandira alendo komanso kuthandiza akulu m’njira zina. Pamakhala ntchito yaikulu posamalira Nyumba ya Ufumu kuti izioneka bwino, choncho nthawi zambiri atumiki othandiza amapatsidwa udindo wosamalira ntchito zimenezi.
9 M’mipingo ina muli atumiki othandiza okwanira moti zimakhala zotheka kuti mtumiki wothandiza aliyense apatsidwe ntchito imodzi yokha. Pamene m’mipingo ina mtumiki wothandiza mmodzi angapatsidwe ntchito zambiri. Nthawi zina ntchito imodzi ingamagwiridwe ndi atumiki othandiza angapo. Ngati pa mpingo palibe atumiki othandiza okwanira oti azisamalira ntchito zofunika zimenezi, bungwe la akulu lingasankhe abale ena obatizidwa achitsanzo chabwino kuti azisamalira ntchitozo. Izi zimathandiza abalewa kudziwa mmene angagwirire ntchito zina za pa mpingo ndipo zimenezi zimadzawathandiza akadzakhala atumiki othandiza. Ngati palibe abale oyenerera, akulu angapemphe mlongo wachitsanzo chabwino kuti azisamalira ntchito zina, ngakhale kuti sangaikidwe kukhala mtumiki wothandiza. Munthu wachitsanzo chabwino ndi amene anthu ena angatsanzire khalidwe lake komanso zochita zake. Ayenera kukhala woti amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kusonkhana nthawi zonse, kulalikira, kusamalira banja, kusankha bwino zosangalatsa, kavalidwe, kudzikongoletsa ndi zina zotero.
10 M’mipingo imene muli akulu ochepa kwambiri, atumiki othandiza oyenerera angapatsidwe ntchito yopenda anthu amene akufuna kubatizidwa ndipo angakambirane nawo mafunso okhudza ziphunzitso za m’Baibulo. Mafunso amenewa amapezeka m’chigawo choyamba cha Zakumapeto cha mutu wakuti, “Zimene Akhristu Amakhulupirira.” Popeza chigawo chachiwiri cha mutu wakuti, “Moyo Wachikhristu” chimafuna kuti munthu afotokoze za moyo wake, m’pofunika kuti chigawo chimenechi akambirane ndi mkulu.
11 Bungwe la akulu likhoza kuona kuti ndi bwino kuti pakapita nthawi azisintha ntchito zimene atumiki othandiza ena amagwira. Komabe zimakhala bwino kwambiri ngati munthu atagwira ntchito yomweyomweyo kwa nthawi yaitali kuti aizolowere.
12 Malinga ndi mmene zinthu zilili pa mpingopo, ntchito zina zikhoza kuperekedwa kwa atumiki othandiza omwe kupita kwawo patsogolo kukuonekera kwa “anthu onse.” (1 Tim. 4:15) Ngati pa mpingo palibe akulu okwanira, mtumiki wothandiza akhoza kuikidwa kukhala wothandiza wa woyang’anira kagulu kapena nthawi zina akhoza kuikidwa kukhala mtumiki wa kagulu. Ngati mtumiki wothandiza waikidwa kukhala mtumiki wa kagulu, ayenera kugwira ntchito moyang’aniridwa ndi akulu. Atumiki othandiza akhoza kupatsidwa nkhani zina za mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu ndiponso kuchititsa Phunziro la Baibulo la Mpingo ngati pangafunike kutero, kapenanso kukamba nkhani za onse. Atumiki othandiza akhoza kupatsidwanso ntchito zina ngati pa mpingopo palibe akulu okwanira. Angapatsidwe ntchitozi ngati ali oyenerera komanso ngati akuoneka kuti azikwanitsa. (1 Pet. 4:10) Popeza udindo wawo ndi kuthandiza akulu, atumiki othandiza ayenera kudzipereka kwambiri pogwira ntchito zawo.
13 Ngakhale kuti ntchito zawo n’zosiyana ndi zimene akulu amagwira, sikuti Mulungu amaona kuti utumiki wawo ndi wotsikirapo poyerekezera ndi wa akulu. Amaona kuti udindo wawo ndi wofunika kwambiri kuti mpingo uziyenda bwino. Pakapita nthawi, atumiki othandiza amene amasamalira bwino maudindo awo ndipo akhoza kuweta komanso kuphunzitsa, angavomerezedwe kutumikira monga akulu.
14 Ngati ndinu m’bale wachinyamata kapena mwangobatizidwa kumene, kodi mukuyesetsa kuti muyenerere kukhala mtumiki wothandiza? (1 Tim. 3:1) Masiku ano pakufunika amuna ambiri oyenerera oti azitumikira mumpingo chifukwa anthu ambiri akubwera m’gulu la Yehova. Kuti muyenerere kukhala ndi udindo, muyenera kuyesetsa kuti mukhale ndi mtima wofuna kuthandiza ena. Chimene chingakuthandizeni kukhala ndi mtima umenewu ndi kuganizira chitsanzo cha Yesu. (Mat. 20:28; Yoh. 4:6, 7; 13:4, 5) Chidwi chanu chofuna kuthandiza ena chidzawonjezereka mukamaona chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chokhala wopatsa. (Mac. 20:35) Choncho, muzidzipereka pothandiza ena, pokonza ndi kusamalira Nyumba ya Ufumu kapena pochita mbali ya mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu imene mwiniwake sanabwere. Ngati mukufuna kukhala ndi udindo muyeneranso kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Makhalidwe amenewa mungakhale nawo ngati muli ndi pulogalamu yophunzira Baibulo panokha. (Sal. 1:1, 2; Agal. 5:22, 23) Kuwonjezera pamenepa, m’bale amene akuyesetsa kuti ayenerere udindo, angasonyeze kuti ndi wodalirika komanso wokhulupirika ngati akusamalira bwino ntchito zimene wapatsidwa pampingo.—1 Akor. 4:2.
15 Atumiki othandiza amaikidwa ndi mzimu woyera n’cholinga choti azigwira ntchito zothandiza mpingo. Onse mu mpingo angasonyeze kuti amayamikira ntchito yaikulu imene atumiki othandiza amagwira pochita zinthu mogwirizana nawo pamene akugwira ntchito yawo. Mpingo ukamachita zimenezi, umasonyezanso kuti umayamikira zimene Yehova anakonza n’cholinga choti zinthu zizichitika mwadongosolo m’gulu lake.—Agal. 6:10.