MAWU AKUMAPETO
1 YEHOVA
Dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo dzinali limatanthauza kuti iye akhoza kukwaniritsa lonjezo lililonse komanso akhoza kukwaniritsa cholinga chilichonse chomwe angakhale nacho. Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo ndi amene analenga zinthu zonse. Iye ali ndi mphamvu zotha kuchita chilichonse chimene akufuna.
M’Chiheberi, dzina la Mulungu linkalembedwa ndi zilembo 4. Koma m’Chingelezi zilembo zimenezi ndi YHWH kapena JHVH. Dzina la Mulungu limapezeka pafupifupi nthawi zokwana 7,000 m’mipukutu yoyambirira yachiheberi. Anthu padziko lonse lapansi amatchula dzina la Yehova m’njira zosiyanasiyana mogwirizana ndi chiyankhulo chawo.
2 BAIBULO ‘LINAUZIRIDWA NDI MULUNGU’
Mulungu ndi amene analemba Baibulo koma anagwiritsira ntchito anthu. Zimene zinachitika polemba Baibulo n’zofanana ndi zimene zimachitika ngati gogo atapempha mdzukulu wake kuti amulembere kalata. Maganizo a m’kalatayo amakhala a gogoyo. Nayenso Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera potsogolera anthu amene analemba Baibulo kuti alembe maganizo ake. Mzimu woyera unkatsogolera anthuwo m’njira zosiyanasiyana ndipo nthawi zina unkawachititsa kuona masomphenya kapena kulota maloto a zinthu zimene ankafunika kulemba.
3 MFUNDO ZA M’BAIBULO
Mfundo za m’Baibulo ndi zinthu zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana ndipo sizisintha. Mwachitsanzo, mfundo yoti “kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino” imatiphunzitsa kuti anthufe timatengera makhalidwe a anthu amene timakonda kucheza nawo, kaya akhale abwino kapena oipa. (1 Akorinto 15:33) Ndipo mfundo yoti “chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho” imatiphunzitsa kuti sitingathe kupewa zotsatira za zinthu zimene timachita.—Agalatiya 6:7.
4 ULOSI
Ulosi ndi uthenga wochokera kwa Mulungu. Ulosi ukhoza kukhala wofotokoza zimene Mulungu akufuna kuchita, wophunzitsa anthu makhalidwe abwino, wolamula anthu kuti achite zinazake kapena wokhudza kuweruza anthu. Ukhozanso kukhala uthenga wofotokoza zimene zidzachitike m’tsogolo. M’Baibulo muli maulosi ambirimbiri amene anakwaniritsidwa kale.
5 MAULOSI ONENA ZA MESIYA
Maulosi onse a m’Baibulo onena za Mesiya anakwaniritsidwa pa Yesu. Onani bokosi lakuti, “Maulosi Onena za Mesiya.”
▸ Mutu 2, ndime 17, mawu am’munsi
6 CHOLINGA CHA MULUNGU POLENGA DZIKO LAPANSI
Yehova analenga dzikoli kuti anthu amene amamukonda azikhalamo mosangalala. Cholinga chakechi sichinasinthe. Posachedwapa, Mulungu adzachotsa zoipa zonse padzikoli ndipo adzapereka moyo wosatha kwa atumiki ake.
7 SATANA MDYEREKEZI
Satana ndi mngelo amene anayambitsa kagulu koukira ulamuliro wa Mulungu. Iye amatchedwa Satana, kutanthauza “Wotsutsa” chifukwa amachita zinthu zotsutsana ndi Mulungu. Amatchedwanso Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza.” Satana anapatsidwa dzina limeneli chifukwa amanena zinthu zabodza zokhudza Mulungu komanso amanamiza anthu.
8 ANGELO
Yehova anayamba kulenga angelo asanalenge dziko lapansili. Iwo analengedwa kuti azikhala kumwamba ndipo alipo mamiliyoni ambirimbiri. (Danieli 7:10) Angelo ali ndi mayina komanso makhalidwe osiyanasiyana. Ndipo angelo okhulupirika salola kuti anthu aziwalambira. Iwo ali ndi maudindo osiyanasiyana ndiponso amagwira ntchito zosiyanasiyana. Zina mwa ntchitozi ndi monga kutumikira kumpando wachifumu wa Yehova, kupereka mauthenga ochokera kwa Mulungu, kuteteza komanso kutsogolera atumiki a Mulungu padziko lapansi, kupereka ziweruzo za Mulungu, ndiponso kuthandiza anthu pa ntchito yolalikira. (Salimo 34:7; Chivumbulutso 14:6; 22:8, 9) Posachedwapa, angelo adzathandiza Yesu pomenya nkhondo ya Aramagedo.—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:14, 15.
9 UCHIMO
Tchimo ndi chilichonse chimene munthu amaganiza kapena kuchita chomwe ndi chosemphana ndi zimene Yehova amafuna. Popeza tchimo lingachititse kuti tisakhale pa ubwenzi ndi Mulungu, iye anatipatsa mfundo ndi malamulo amene amatithandiza kuti tisamachimwe mwadala. Poyamba, Yehova analenga zinthu zabwino zokhazokha. Koma pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera, anachimwa ndipo zimenezi zinachititsa kuti asakhalenso angwiro. Iwo anakalamba ndipo kenako anafa. Chifukwa chakuti tinatengera uchimo wawowo, ifenso timakalamba ndiponso kufa.
10 ARAMAGEDO
Aramagedo ndi nkhondo imene Mulungu adzamenye pofuna kuwononga dziko la Satanali komanso kuthetsa zoipa zonse.
11 UFUMU WA MULUNGU
Ufumu wa Mulungu ndi boma limene Yehova anakhazikitsa kumwamba ndipo Yesu Khristu ndi amene akulamulira monga Mfumu. M’tsogolomu, Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuchotsa zoipa zonse padzikoli ndipo udzalamulira dziko lonse lapansi.
12 YESU KHRISTU
Mulungu anayamba kulenga Yesu asanalenge china chilichonse. Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzafere anthu. Yesu ataphedwa, Yehova anamuukitsa. Panopa Yesu akulamulira kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.
13 ULOSI WONENA ZA MILUNGU 70
Baibulo linaneneratu za nthawi imene Mesiya adzaonekere. Linanena kuti iye adzaonekera pamapeto pa milungu 69, yomwe inayamba m’chaka cha 455 B.C.E. n’kudzatha m’chaka cha 29 C.E.
Kodi tikudziwa bwanji kuti milungu 69 inatha m’chaka cha 29 C.E.? Milungu 69 inayamba m’chaka cha 455 B.C.E. pamene Nehemiya anafika ku Yerusalemu n’kuyamba kumanganso mzindawo. (Danieli 9:25; Nehemiya 2:1, 5-8) Nthawi zambiri tikamva mawu akuti “mlungu” timaganizira za masiku 7. Koma milungu yotchulidwa mu ulosiwu si milungu ya masiku 7 koma ndi milungu ya zaka, “tsiku limodzi kuimira chaka.” (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Zimenezi zikutanthauza kuti mlungu uliwonse unkakhala ndi zaka 7 zomwe zikusonyeza kuti milungu 69 ndi zaka zokwanira 483 (69 x 7). Tikawerengetsera zaka 483 kuchokera m’chaka cha 455 B.C.E., zikutifikitsa mu 29 C.E. Chaka chimenechi ndi chimene Yesu anabatizidwa n’kukhala Mesiya.—Luka 3:1, 2, 21, 22.
Ulosiwu umanenanso za mlungu wina wowonjezera, zomwe ndi zaka 7 zinanso. Ulosiwu unaneneratu kuti mkati mwa nthawi imeneyi, m’chaka cha 33 C.E., Mesiya adzaphedwa, ndipo kuyambira m’chaka cha 36 C.E., uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa kwa anthu a mitundu yonse osati kwa Ayuda okha.—Danieli 9:24-27.
14 BODZA LAKUTI PALI MILUNGU ITATU MWA MULUNGU MMODZI
Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova Mulungu ndi Mlengi ndipo iye asanalenge zinthu zina zonse analenga Yesu. (Akolose 1:15, 16) Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse. Iye sananenepo kuti ndi wofanana ndi Mulungu. M’malomwake, iye anati: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28; 1 Akorinto 15:28) Koma zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi: Atate, Mwana ndi mzimu woyera. Zimenezi n’zabodza chifukwa sizipezeka m’Baibulo.
Mzimu woyera ndi mphamvu yosaoneka imene Mulungu amaigwiritsira ntchito pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Mzimu woyera si munthu. Mwachitsanzo, Akhristu oyambirira “anadzazidwa ndi mzimu woyera,” komanso Yehova ananena kuti: “Ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana.”—Machitidwe 2:1-4, 17.
15 MTANDA
N’chifukwa chiyani Akhristu oona sagwiritsa ntchito mtanda polambira Mulungu?
Kwa nthawi yaitali, mtanda wakhala ukugwiritsidwa ntchito m’zipembedzo zonyenga. Kale, mtanda unkagwiritsidwa ntchito ndi anthu amene ankalambira zinthu zachilengedwe ndiponso kuchita miyambo yachikunja yokhudza kugonana. Kwa zaka 300 kuchokera pamene Yesu anaphedwa, palibe Mkhristu aliyense amene ankagwiritsa ntchito mtanda polambira. Koma kenako, mfumu yachiroma dzina lake Constantine inalowa Chikhristu cha anthu ampatuko ndipo inalimbikitsa Akhristuwo kuti azigwiritsa ntchito mtanda ngati chizindikiro chawo. Akhristu ampatukowa ankagwiritsa ntchito chizindikirochi n’cholinga choti chipembedzo chawo chifalikire. Koma palibe kugwirizana kulikonse pakati pa mtanda ndi Yesu Khristu. Buku lina la Akatolika limanena kuti: “Anthu omwe sanali Akhristu komanso amene anakhalapo Chikhristu chisanayambe ndi amene ankagwiritsa ntchito mtanda pochita miyambo yawo.”—New Catholic Encyclopedia.
Yesu sanafere pamtanda. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “mtanda” amatanthauza “mtengo woongoka,” “thabwa” kapenanso amangotanthauza “mtengo” basi. Baibulo lina limafotokoza kuti: “M’Baibulo lachigiriki [la Chipangano Chatsopano] mulibe mawu alionse onena za mitengo iwiri yopingasa ngati mmene mtanda wamasiku ano umaonekera.” (The Companion Bible) Choncho Yesu anafera pamtengo woongoka.
Yehova safuna kuti tizigwiritsa ntchito mafano kapena zizindikiro pomulambira.—Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14.
16 MWAMBO WOKUMBUKIRA IMFA YA YESU
Yesu analamula ophunzira ake kuti azichita mwambo wokumbukira imfa yake. Iwo amachita mwambowu chaka chilichonse pa tsiku la 14 la mwezi umene Ayuda ankautchula kuti Nisani. Tsikuli ndi limenenso Aisiraeli ankachita mwambo wa Pasika. Pamwambowu pamayendetsedwa mkate ndi vinyo, zimene zimaimira thupi komanso magazi a Yesu. Anthu omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba ndi amene amadya mkate komanso kumwa vinyoyo. Koma amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansili, amangoonerera mwaulemu ndipo sadya nawo mkate kapena kumwa vinyo.
17 MOYO
Mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi mawu akuti “moyo” amagwiritsidwa ntchito pofotokoza za (1) munthu, (2) nyama, komanso (3) moyo wa munthu kapena wa nyama. Onani zitsanzo izi:
Munthu. “M’masiku a Nowa . . . chingalawa . . . chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, miyoyo 8 yokha.” (1 Petulo 3:20) Palembali mawu akuti “miyoyo” akuimira anthu. Anthu ake anali Nowa ndi mkazi wake komanso ana awo aamuna atatu ndi akazi awo.
Nyama. “Mulungu anati: ‘M’madzi mukhale zamoyo zambirimbiri, ndiponso zolengedwa zouluka ziuluke m’mlengalenga mwa dziko lapansi.’ Tsopano Mulungu anati: ‘Dziko lapansi likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta, nyama zokwawa, [“zamoyo”] komanso nyama zakutchire monga mwa mitundu yake.’ Ndipo zinaterodi.”—Genesis 1:20, 24.
Moyo wa munthu kapena wa nyama. Yehova anauza Mose kuti: “Onse amene anali kufuna moyo wako anafa.” (Ekisodo 4:19) Yesu ali padziko lapansi pano ananena kuti: “Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.”—Yohane 10:11.
Kuwonjezera pamenepa, munthu akamachita zinazake ndi ‘moyo wake wonse’ zimatanthauza kuti akuchita zinthuzo mofunitsitsa komanso modzipereka. (Mateyu 22:37; Deuteronomo 6:5) Mawu akuti “moyo” amagwiritsidwanso ntchito pofotokoza zokhumba ndi zolakalaka za munthu.
18 MZIMU
Mawu achiheberi ndi achigiriki amene anamasuliridwa kuti “mzimu” mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi angatanthauze zinthu zosiyanasiyana. Koma nthawi zonse amatanthauza mphamvu yosaoneka, ngati mmene ilili mphepo komanso mpweya umene anthufe ndi zinyama timapuma. Mawuwa amanenanso za Mulungu, zolengedwa monga angelo ndi ziwanda komanso za mzimu woyera umene ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. Baibulo siliphunzitsa kuti mzimu ndi chinthu chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo munthu akamwalira.—Ekisodo 35:21; Salimo 104:29; Mateyu 12:43; Luka 11:13.
19 GEHENA
Gehena ndi dzina la malo enaake omwe anali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Kumalo amenewa ndi komwe ankawotcherako zinyalala. Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti m’nthawi ya Yesu zinyama komanso anthu ankawotchedwa ku Gehena ali amoyo. Choncho Gehena sakutanthauza malo enieni kumene anthu akafa amakazunzidwa komanso kuwotchedwa mpaka kalekale. Pamene Yesu ananena kuti anthu ena adzapita ku Gehena, ankatanthauza kuti anthuwo adzawonongedwa moti sadzakhalanso ndi moyo mpaka kalekale.—Mateyu 5:22; 10:28.
20 PEMPHERO LA AMBUYE
Limeneli ndi pemphero limene Yesu anapereka pophunzitsa ophunzira ake kupemphera. Pempheroli limadziwikanso kuti pemphero la Atate Wathu kapena pemphero lachitsanzo. Zina mwa zinthu zimene Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera ndi izi:
“Dzina lanu liyeretsedwe”
Tikamanena zimenezi timakhala tikupempha Yehova kuti ayeretse dzina lake kuti lisadetsedwe ndi zinthu zilizonse zabodza, n’cholinga choti aliyense kaya kumwamba kapena padziko lapansi azilemekeza dzina lake.
“Ufumu wanu ubwere”
Tikamanena zimenezi timakhala tikupempha kuti Ufumu wa Mulungu uwononge dziko la Satanali n’kuyamba kulamulira dziko lonse lapansi komanso kulikonza kuti likhale paradaiso.
“Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano”
Tikamanena zimenezi timakhala tikupempha kuti cholinga cha Mulungu choti anthu omvera komanso angwiro adzakhale m’Paradaiso mpaka kalekale chikwaniritsidwe, monga mmene iye ankafunira polenga anthu.
21 DIPO
Yehova anapereka dipo la Yesu pofuna kupulumutsa anthu ku uchimo ndi imfa. Pankafunika dipo lolipirira moyo wangwiro umene Adamu anataya komanso lothandiza kuti anthu akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. Kuti zimenezi zitheke, Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzafere anthu ochimwafe. Chifukwa choti Yesu anatifera, tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha tili angwiro.
22 N’CHIFUKWA CHIYANI CHAKA CHA 1914 CHILI CHOFUNIKA KWAMBIRI?
Chaputala 4 cha buku la Danieli chinaneneratu kuti Mulungu adzakhazikitsa Ufumu wake m’chaka cha 1914.
Ulosi: Yehova anachititsa Mfumu Nebukadinezara kulota maloto a zinthu zimene zinali kudzachitika m’tsogolo. Iye analota mtengo wautali umene unadulidwa ndipo chitsa chake sichinkaphukira mpaka panadutsa “nthawi zokwanira 7” chifukwa anali atachikulunga ndi zinthu zachitsulo. Kenako mtengowo unayambiranso kuphukira.—Danieli 4:1, 10-16.
Kodi ulosi umenewu ukutanthauza chiyani?: Mtengowo ukuimira ulamuliro wa Mulungu. Kwa zaka zambiri, Yehova ankagwiritsira ntchito mafumu a ku Yerusalemu kuti azitsogolera mtundu wa Isiraeli. (1 Mbiri 29:23) Koma mafumu amenewa anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Mulungu, choncho iye sanawalole kuti apitirize kulamulira. Kenako Yerusalemu anawonongedwa m’chaka cha 607 B.C.E. Pamenepa ndi pomwe panayambira “nthawi zokwanira 7.” (2 Mafumu 25:1, 8-10; Ezekieli 21:25-27) Pamene Yesu ananena kuti: “Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira,” ankanena za “nthawi zokwanira 7” zimenezi. (Luka 21:24) “Nthawi zokwanira 7” zimenezi sizinathe Yesu ali padziko lapansi pano. Yehova analonjeza kuti adzasankha Mfumu yatsopano kumapeto kwa “nthawi zokwanira 7.” Ulamuliro wa Mfumu yatsopano imeneyi ndi umene udzabweretse madalitso kwa anthu padziko lonse lapansi.—Luka 1:30-33.
Kodi “nthawi zokwanira 7” zimenezi ndi nthawi yaitali bwanji?: “Nthawi zokwanira 7” zinali zaka 2,520. Tikawerengetsera zaka 2,520 kuchokera m’chaka cha 607 B.C.E., zikutifikitsa m’chaka cha 1914. Chaka chimenechi ndi chimene Yehova anasankha Yesu, yemwe ndi Mesiya kukhala Mfumu ya Ufumu wake wakumwamba.
Kodi tadziwa bwanji kuti “nthawi zokwanira 7” ndi zaka 2,520? Baibulo limanena kuti nthawi zitatu ndi hafu, ndi masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Choncho “nthawi zitatu ndi hafu” kuwirikiza kawiri ndi masiku 2,520 zomwe ndi “nthawi zokwanira 7.” Koma masiku 2,520 amenewa ndi zaka 2,520 chifukwa Baibulo limanena kuti ‘tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi.’—Numeri 14:34; Ezekieli 4:6.
23 MIKAYELI MKULU WA ANGELO
Baibulo limatchula za “mkulu wa angelo” mmodzi yekha, yemwe dzina lake ndi Mikayeli.—Danieli 12:1; Yuda 9.
Mikayeli ndi Mtsogoleri wa angelo a Mulungu okhulupirika. Lemba la Chivumbulutso 12:7, limati: “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka . . . ndi angelo ake.” Buku la Chivumbulutso limanena kuti Yesu ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la Mulungu, choncho Mikayeli ndi dzina lina la Yesu.—Chivumbulutso 19:14-16.
24 MASIKU OTSIRIZA
Mawu akuti masiku otsiriza amanena za nthawi imene padziko lapansi padzachitike zinthu zikuluzikulu, Ufumu wa Mulungu ukadzatsala pang’ono kuwononga dziko la Satanali. Mawu ena angati amenewa, monga akuti “mapeto a nthawi ino” ndiponso akuti “kukhalapo kwa Mwana wa munthu,” amagwiritsidwanso ntchito m’Baibulo ponena za nthawi imeneyi. (Mateyu 24:3, 27, 37) “Masiku otsiriza” anayamba pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba m’chaka cha 1914 ndipo adzatha dziko la Satanali likadzawonongedwa pa nkhondo ya Aramagedo.—2 Timoteyo 3:1; 2 Petulo 3:3.
25 KUUKITSIDWA KWA AKUFA
Baibulo limanena kuti Mulungu adzaukitsa akufa. Ndipo limatchula anthu okwana 9 omwe anaukitsidwa ndi Eliya, Elisa, Yesu, Petulo komanso Paulo. Anthuwa anaukitsa anthu akufa pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anawapatsa. Yehova akulonjeza kuti adzaukitsa anthu “olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Baibulo limatchulanso za anthu ena amene amaukitsidwa n’kukakhala kumwamba. Anthu amenewa ndi amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti akalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba.—Yohane 5:28, 29; 11:25; Afilipi 3:11; Chivumbulutso 20:5, 6.
26 KUKHULUPIRIRA MIZIMU
Kukhulupirira mizimu ndi khalidwe loipa limene anthu amachita poyesa kugwirizana ndi ziwanda, kaya polankhula nazo okha kapena kugwiritsa ntchito anthu monga asing’anga kapena amatsenga. Anthu amene amakhulupirira mizimu amachita zimenezi chifukwa anauzidwa zinthu zabodza zoti munthu akafa, mzimu wake suufa ndipo ungavulaze anthu amoyo kapena kuwathandiza. Mizimu yoipa imachititsanso kuti anthu asamamvere Mulungu. Mitundu ina ya kukhulupirira mizimu ndi monga kukhulupirira nyenyezi, kuona pagalasi lamatsenga, kutanthauzira mizere ya m’manja, kutanthauzira kulira kwa mbalame, kumasulira maloto komanso kuchita zamatsenga. Palinso zinthu zina zambiri ngati mabuku, magazini, mafilimu, zithunzi, ndiponso nyimbo zimene zimalimbikitsa anthu kukhulupirira mizimu kapena kuganiza kuti kukhulupirira mizimu n’kwabwino. Miyambo yambiri yokhudzana ndi maliro monga kukonza phwando pa tsiku lamaliro, kuchita mwambo wokumbukira tsiku limene munthu winawake anamwalira, kupereka nsembe kwa akufa, kulondera maliro ndiponso miyambo ya mmene munthu ayenera kulirira maliro a mwamuna kapena mkazi wake, ndi yogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Ndipotu, nthawi zambiri anthu amagwiritsa ntchito mankhwala pochita zamizimu.—Agalatiya 5:20; Chivumbulutso 21:8.
27 ULAMULIRO WA YEHOVA
Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo ndi amene analenga zinthu zonse. (Chivumbulutso 15:3) N’chifukwa chake iye ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Salimo 24:1; Yesaya 40:21-23; Chivumbulutso 4:11) Iye anapereka malamulo oti zinthu zimene analenga zizitsatira. Yehova alinso ndi mphamvu zosankha ena kuti akhale olamulira. Tikamamukonda komanso kumumvera timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake.—1 Mbiri 29:11.
28 KUCHOTSA MIMBA
Kuchotsa mimba n’kupha dala mwana amene sanabadwe. Ndipo sikuchitika mwangozi kapena chifukwa cha mavuto ena a m’thupi la mayiyo ayi. Mayi akangotenga pakati, m’pamene moyo wa mwana umayambika. Choncho mwanayo ndi munthunso payekha.
29 KUIKIDWA MAGAZI
Kuika magazi ndi njira imene achipatala amagwiritsa ntchito magazi kapena chigawo china pa zigawo 4 za magazi n’kumupatsa munthu wina. Zigawo 4 zikuluzikulu zimenezi ndi madzi a m’magazi, maselo ofiira, maselo oyera ndi maselo othandiza magazi kuundana.
30 CHILANGO
M’Baibulo mawu akuti “chilango” sikuti amangotanthauza kulanga munthu chifukwa choti walakwa. Amatanthauzanso kupatsidwa malangizo, kuphunzitsidwa komanso kudzudzulidwa. Yehova salanga anthu mwankhanza. (Miyambo 4:1, 2) Iye amapereka chitsanzo chabwino kwa makolo. Malangizo ake amawapereka mwachikondi moti munthu amene akulangizidwayo amayamba kuwakonda. (Miyambo 12:1) Yehova amakonda anthu ndipo amawaphunzitsa. Amawapatsa malangizo owathandiza kupewa kuchita zinthu zoipa komanso amawaphunzitsa kuti aziganiza ndi kuchita zinthu zimene iyeyo amasangalala nazo. Makolo akamalanga ana awo, ayenera kuwathandiza kudziwa kuti kumvera n’kofunika kwambiri. Ayeneranso kuwaphunzitsa kukonda Yehova, Mawu ake komanso kumvetsa mfundo za m’Baibulo.
31 ZIWANDA
Ziwanda ndi angelo oipa ndipo ndi zamphamvu kuposa anthufe. Angelo oipawa anadzipanga kukhala adani a Mulungu pamene anasankha kusamumvera. (Genesis 6:2; Yuda 6) Iwo anagwirizana ndi Satana poukira ulamuliro wa Yehova.—Deuteronomo 32:17; Luka 8:30; Machitidwe 16:16; Yakobo 2:19.