NKHANI YOPHUNZIRA 40
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
Yehova “Amachiritsa Anthu Osweka Mtima”
“Iye amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga mabala awo.”—SAL. 147:3.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Yehova amasamalira anthu amene asweka mtima chifukwa cha mavuto. Nkhaniyi ifotokoza zimene iye amachita kuti atitonthoze komanso mmene amatithandizira kuti tizilimbikitsa ena.
1. Kodi Yehova amamva bwanji akamaona zimene zikuchitikira atumiki ake?
KODI Yehova amaona zimene zikuchitikira atumiki ake padzikoli? Inde. Iye amadziwa tikamasangalala kapena tikakhumudwa. (Sal. 37:18) Amasangalala akaona kuti tikuyesetsa mmene tingathere kuti tizimutumikira ngakhale pamene tili ndi nkhawa. Kuwonjezera pamenepo, iye amakhalanso wokonzeka kutithandiza komanso kutilimbikitsa.
2. Kodi Yehova amalimbikitsa bwanji anthu a mtima wosweka, nanga tingatani kuti tizipindula ndi zimene amachita potisamalira?
2 Lemba la Salimo 147:3 limati Yehova ‘amamanga mabala’ a anthu osweka mtima. Apa lembali likufotokoza mmene Yehova amasamalirira mwachikondi anthu omwe ali ndi nkhawa. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula ndi zimene Yehova amachita potisamalira? Taganizirani chitsanzo ichi: Dokotala waluso angachite zambiri pothandiza munthu amene wavulala kuti achire. Komabe kuti munthuyo achire, amafunika kutsatira mosamala malangizo a dokotalayo. Munkhaniyi tiona zimene Yehova amauza anthu amene ali ndi nkhawa komanso zimene tingachite kuti tizitsatira malangizo ake achikondi.
YEHOVA AMATITSIMIKIZIRA KUTI NDIFE OFUNIKA
3. N’chifukwa chiyani anthu ena amadziona ngati osafunika kwenikweni?
3 Tikukhala m’dziko limene anthu ake alibe chikondi ndipo n’zomvetsa chisoni kuti izi zimachititsa anthu ambiri kuti azidziona ngati osafunika. Mlongo wina dzina lake Helena anati: “Ndinakulira m’banja lopanda chikondi. Bambo anga anali ankhanza ndipo tsiku lililonse ankandinena kuti ndinali wachabechabe.” N’kutheka kuti mofanana ndi Helen, inunso mwakhala mukuchitiridwa nkhanza, kunyozedwa kapenanso kuchititsidwa kuti muzidziona ngati palibe angakukondeni. Ngati ndi choncho, izi zingachititse kuti zizikuvutani kukhulupirira kuti pali wina yemwe amakukondani.
4. Mogwirizana ndi Salimo 34:18, kodi Yehova akutitsimikizira chiyani?
4 Ngakhale ena akuchitireni zopanda chilungamo, musamakayikire kuti Yehova amakukondani komanso amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. Iye “ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” (Werengani Salimo 34:18.) Ngati ‘mukudzimvera chisoni mumtima’ muzikumbukira kuti Yehova anaona zabwino mumtima mwanu ndipo anakukokerani kwa iye. (Yoh. 6:44) Nthawi zonse iye ndi wokonzeka kukuthandizani chifukwa amakukondani kwambiri.
5. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yesu ankachita ndi anthu omwe ankaonedwa ngati osafunika?
5 Chitsanzo cha Yesu chingatithandize kudziwa mmene Yehova amamvera. Ali padziko lapansi, Yesu ankakomera mtima komanso kuchitira chifundo anthu omwe ankaonedwa ngati osafunika. (Mat. 9:9-12) Mwachitsanzo, mayi wina yemwe ankadwala matenda aakulu atagwira chovala chake pokhulupirira kuti achira, Yesu anamulimbikitsa komanso kumuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Maliko 5:25-34) Yesu anatengera makhalidwe a Atate wake. (Yoh. 14:9) Choncho musamakayikire kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali ndiponso amaona makhalidwe anu abwino kuphatikizapo chikhulupiriro ndi chikondi chanu kwa iye.
6. Kodi munthu angatani ngati akulimbana ndi maganizo odziona kuti ndi wosafunika?
6 Kodi mungatani ngati mukupitirizabe kumadziona kuti ndinu wosafunika? Muziwerenga komanso kuganizira malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali.b (Sal. 94:19) Ngati mwalephera kukwaniritsa cholinga china chake kapenanso kukhumudwa chifukwa chakuti simukuchita zambiri ngati ena, musamadziweruze mopitirira malire. Yehova sayembekezera kuti muzichita zimene simungakwanitse. (Sal. 103:13, 14) Ngati munachitiridwa zinazake zoipa, musamadziimbe mlandu kuti inuyo ndi amene munachititsa. Simumayenera kuchitiridwa zinthu ngati zimenezo. Muzikumbukira kuti Yehova adzaweruza amene amachita zoipa, osati amene amachitiridwa zoipa. (1 Pet. 3:12) Sandra, yemwe anachitiridwa nkhanza ali mwana, ananena kuti: “Nthawi zonse ndimapempha Yehova kuti andithandize kuti ndizidziona moyenera ngati mmene iyeyo amandionera.”
7. Pamene tikutumikira Yehova, kodi tingagwiritse ntchito bwanji zimene zinatichitikira pa moyo wathu?
7 Musamakayikire kuti Yehova angagwiritse ntchito inuyo pothandiza ena. Iye wakupatsani mwayi wogwira naye limodzi ntchito yolalikira. (1 Akor. 3:9) Zimene zinachitika pa moyo wanu zingakuthandizeni kuti muzisonyeza chifundo kwa ena komanso kumvetsa mmene akumvera. Choncho mungachite zambiri powathandiza. Helen yemwe tamutchula kale uja anathandizidwa ndipo panopa nayenso amatha kuthandiza ena. Iye anati: “Yehova wachititsa kuti munthu yemwe ankadziona ngati ‘wachabechabe’ azidziona kuti amakondedwa ndipo angathe kuthandiza ena.” Helen akusangalala kuchita upainiya wokhazikika.
YEHOVA AMAFUNA TIZIVOMEREZA KUTI AMATIKHULULUKIRA
8. Kodi Yehova amatitsimikizira chiyani pa Yesaya 1:18?
8 Atumiki ena a Yehova amadziimbabe mlandu chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyo, kaya asanabatizidwe kapena atabazidwa. Koma tingachite bwino kumakumbukira kuti Yehova anapereka dipo chifukwa chakuti amatikonda kwambiri. Choncho n’zoonekeratu kuti iye amafuna kuti tiziyamikira mphatsoyi. Yehova amatitsimikizira kuti ‘akatithandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi iye,’c satiimbanso mlandu pa zimene tinalakwitsazo. (Werengani Yesaya 1:18.) Timayamikira kuti Yehova sakumbukiranso zimene tinalakwitsa m’mbuyo. Pa nthawi imodzimodziyo amakumbukira zabwino zimene timachita.—Sal. 103:9, 12; Aheb. 6:10.
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizikumbukira zimene tikuchita panopa komanso za m’tsogolo, osati zimene tinachita m’mbuyo?
9 Ngati mukuvutika maganizo chifukwa cha zimene munalakwitsa m’mbuyo, muziyesetsa kuti muziganizira zimene mukuchita panopa komanso zimene mudzachite m’tsogolo m’malo moganizira zomwe munalakwitsa m’mbuyo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Iye ankadzimvera chisoni kuti pa nthawi ina ankazunza kwambiri Akhristu, koma ankadziwa kuti Yehova anamukhululukira. (1 Tim. 1:12-15) Koma kodi iye ankaganizira kwambiri za zimene ankachita m’mbuyozo? Mosakayikira iye sanachite zimenezo monganso mmene sanachitire pomaganizira zimene anachita kuti akhale Mfarisi wolemekezeka. M’malomwake, Paulo ankatumikira Mulungu mwakhama n’kumangoyang’ana zakutsogolo. (Afil. 3:4-8, 13-15) Mofanana ndi Paulo, palibe chimene mungachite kuti musinthe zimene zinachitika m’mbuyo. Koma mukhoza kumalemekeza Yehova mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa n’kumayembekezera mwachidwi zimene Yehova wakulonjezani kutsogolo.
10. Kodi tingatani ngati zimene tinachita m’mbuyomu zinakhumudwitsa ena?
10 Mwina mumakhumudwa ndi zimene munachita m’mbuyo zomwe zinakhumudwitsa ena. Ndiye kodi n’chiyani chomwe chingakuthandizeni? Muzichita zonse zimene mungathe kuti mukonze zinthu komanso kupepesa mochokera pansi pa mtima. (2 Akor. 7:11) Muzipempha Yehova kuti athandize anthu onse amene anakhudzidwa ndi zimene munachita. Iye angathandize inuyo komanso anthu omwe munawakhumudwitsawo kuti mupirire ndiponso muyambirenso kukhala ndi mtendere.
11. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha mneneri Yona? (Onaninso chithunzi chapachikuto.)
11 Muziphunzirapo kanthu pa zimene munalakwitsa ndipo muzilola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito mmene iyeyo akufunira. Taganizirani chitsanzo cha mneneri Yona. M’malo mopita ku Nineve komwe Mulungu anamutuma, Yona analowera kwina. Yehova anamudzudzula ndipo iye anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsa. (Yona 1:1-4, 15-17; 2:7-10) Yehova sanasiye kumugwiritsa ntchito Yona. Anamupatsanso mwayi woti apite ku Nineve ndipo pa nthawiyi Yona anamvera. Iye sanalole kuti kudzimvera chisoni pa zimene analakwitsa kumulepheretse kuchita zimene Mulungu anamutuma.—Yona 3:1-3.
YEHOVA AMAGWIRITSA NTCHITO MZIMU WOYERA POTITONTHOZA
12. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kupeza mtendere tikasokonezeka maganizo? (Afilipi 4:6, 7)
12 Zinthu zoipa zikatichitikira, Yehova amatitonthoza pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. Taganizirani zimene zinachitikira Ron ndi Caro. N’zomvetsa chisoni kuti mwana wawo wamwamuna anadzipha. Iwo anati: “Takhala tikukumana ndi mayesero aakulu, koma awa anali ovuta kwambiri. Nthawi zambiri tinkalephera kugona usiku, choncho tinkapemphera kwa Yehova. Tikatero tinkakhala ndi mtendere wotchulidwa pa Afilipi 4:6, 7.” (Werengani.) Ngati inunso mukulimbana ndi mayesero amene achititsa kuti musweke mtima, muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Muzichita zimenezi nthawi iliyonse komanso kwa nthawi yaitali mmene mukufunira. (Sal. 86:3; 88:1) Muzipempha Yehova mobwerezabwereza kuti akupatseni mzimu wake woyera ndipo nthawi zonse iye adzakuthandizani.—Luka 11:9-13.
13. Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji kuti tipitirize kutumikira Yehova mokhulupirika? (Aefeso 3:16)
13 Kodi mwafooka chifukwa cha zinthu zinazake zoipa zimene zakuchitikirani? Mzimu woyera ungakupatseni mphamvu kuti mupitirize kutumikira Yehova mokhulupirika. (Werengani Aefeso 3:16.) Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Flora. Iye ndi mwamuna wake ankatumikira limodzi monga amishonale. Kenako mwamuna wake anachita zosakhulupirika ndipo ukwati wawo unatha. Flora anati: “Ndinakwiya kwambiri chifukwa cha kusakhulupirika komwe anachitaku. Ndinapempha Yehova kuti andipatse mzimu wake woyera kuti ndithe kupirira. Yehova anandipatsa zimene ndinkafunikira kuti ndichire komanso kuti ndipirire zinthu zomwe poyamba ndinkaona kuti n’zosatheka kuzipirira.” Flora amaona kuti Mulungu wamuthandiza kuti azimudalira kwambiri ndipo sakayikira kuti amamuthandiza pa mayesero ake onse. Iye anawonjezera kuti: “Mawu a pa Salimo 119:32 amafotokoza bwino mmene Yehova anandithandizira. Lembali limati: ‘Ndidzatsatira malamulo anu ndi mtima wonse, chifukwa mwandithandiza kuti ndiwamvetse bwino.’”
14. Kodi tingatani kuti mzimu woyera uzitithandiza?
14 Kodi mungatani kuti muzichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lanu lopempha mzimu woyera? Muzichita nawo zinthu zimene zingachititse kuti mzimu woyera uzikuthandizani. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse kuti muziyendera maganizo a Yehova. (Afil. 4:8, 9) Mukamawerenga, muziona anthu otchulidwa m’Baibulo amene anakumana ndi mavuto osiyanasiyana ndipo muziganizira mmene Yehova anawathandizira kupirira. Sandra yemwe tamutchula kale uja anakumana ndi mavuto aakulu motsatizana. Iye anati: “Nkhani ya Yosefe imandilimbikitsa kwambiri. Iye sanalole kuti mayesero ndi zinthu zopanda chilungamo zomwe zinamuchitikira zimulepheretse kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.”—Gen. 39:21-23.
YEHOVA AMATILIMBIKITSA KUDZERA MWA AKHRISTU ANZATHU
15. Kodi ndi ndani amene angatithandize, nanga angatithandize bwanji? (Onaninso chithunzi.)
15 Tikamakumana ndi mavuto, Akhristu anzathu ‘amatilimbikitsa kwambiri.’ (Akol. 4:11) Zimene abale ndi alongo amachita zimasonyeza kuti Yehova amatikonda. Iwo angatilimbikitse potimvetsera mwachifundo, kapenanso kukhala nafe pa nthawi imene tikukumana ndi mavutoyo. Angatiwerengere vesi linalake lolimbikitsa kapenanso kupemphera nafe.d (Aroma 15:4) Nthawi zina m’bale kapena mlongo angatikumbutse maganizo a Yehova, zomwe zingathandize kuti mtima wathu ukhale m’malo. Akhristu anzathu angatithandizenso m’njira zina monga kutipatsa chakudya pa nthawi imene tili ndi nkhawa.
16. Kodi tingatani kuti ena azitithandiza?
16 Kuti ena atithandize tiyenera kuwafotokozera mavuto athu. Abale ndi alongo athu amatikonda ndipo amafuna kutithandiza. (Miy. 17:17) Koma paokha sangadziwe mmene tikumvera komanso zimene tikufunikira. (Miy. 14:10) Mukakhumudwa muzikhala wokonzeka kufotokozera anzanu amene ndi odalirika. Muziwauza zimene zingakuthandizeni. Mungathe kuuza mkulu mmodzi kapena awiri omwe mumamasuka nawo. Alongo ena amaona kuti zimawathandiza akafotokozera mlongo wina wolimba mwauzimu.
17. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe zingachititse kuti ena alephere kutilimbikitsa, nanga tingatani?
17 Muzipewa mtima womangofuna kukhala panokha. Mtima ukamapweteka simungafune kucheza ndi anthu ena. Ndipo nthawi zina abale ndi alongo sangakumvetseni apo ayi sangalankhule bwino. (Yak. 3:2) Musamalole zinthu ngati zimenezi kukulepheretsani kuti mulimbikitsidwe. Mkulu wina dzina lake Gavin, yemwe amadwala matenda a maganizo ananena kuti: “Nthawi zambiri sindikonda kucheza ndi anthu.” Komabe Gavin amayesetsa kuti azicheza ndi anthu ndipo zimamuthandiza. Mlongo wina dzina lake Amy ananena kuti: “Zomwe zinachitika m’mbuyomu zimachititsa kuti ndizivutika kukhulupirira anthu. Koma ndikuphunzira kukonda komanso kukhulupirira abale ndi alongo ngati mmene Yehova amachitira. Ndimadziwa kuti zimenezi zimasangalatsa Yehova ndipo inenso zimandisangalatsa.”
ZIMENE YEHOVA AMATILONJEZA ZIMATILIMBIKITSA
18. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tikuyembekezera, nanga n’chiyani chomwe tingachite panopa?
18 Timalimba mtima tikaganizira kuti posachedwapa Yehova adzatichiritsa ndipo maganizo ndi thupi lathu zidzakhala bwinobwino. (Chiv. 21:3, 4) Pa nthawi imeneyo zinthu zopweteka zimene timakumana nazo ‘sizidzativutitsanso maganizo.’ (Yes. 65:17) Munkhaniyi taona kuti ngakhale panopa Yehova ‘amamanga mabala athu.’ Muzilola kuti zinthu zambiri zimene Mulungu wakupatsani zizikulimbikitsani komanso kukuthandizani. Musamakayikire ngakhale pang’ono kuti iye “amakufunirani zabwino.”—1 Pet. 5:7.
NYIMBO NA. 7 Yehova Ndi Mphamvu Yathu
a Mayina asinthidwa.
b Onani bokosi lakuti “Yehova Amaona Kuti Ndinu Wofunika.”
c Kuti ‘tikhalenso pa ubwenzi wabwino’ ndi Yehova, tiyenera kusonyeza kuti talapa pomupempha kuti atikhululukire ndiponso kusintha khalidwe lathu. Ngati tachita tchimo lalikulu, tiyeneranso kupempha akulu kuti atithandize.—Yak. 5:14, 15.
d Mwachitsanzo, mungaone malemba amene ali pansi pa mutu wakuti “nkhawa” komanso “chitonthozo” m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu.