Salimo
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe potsatira kaimbidwe ka Mahalati* ndipo iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa mʼbanja la Zera.
88 Inu Yehova, Mulungu amene amandipulumutsa,+
Masana ndimafuulira inu,
Ndipo usiku ndimabwera pamaso panu.+
2 Pemphero langa lifike kwa inu.+
Tcherani khutu lanu kuti mumve* kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+
4 Anandiika kale mʼgulu la anthu amene akutsikira kudzenje.*+
5 Amene wasiyidwa pakati pa anthu akufa
Ngati anthu ophedwa amene agona mʼmanda,
Amene simukuwakumbukiranso
Komanso amene sakuthandizidwa ndi inu.*
6 Mwandiika mʼdzenje lakuya kwambiri,
Mʼmalo amdima, mʼphompho lalikulu.
7 Mkwiyo wanu ukundilemera kwambiri,+
Ndipo ndikumva ngati mukundipanikiza ndi mafunde anu amphamvu. (Selah)
8 Anzanga mwawathamangitsira kutali ndi ine.+
Mwandipangitsa kuti ndikhale chinthu chonyansa kwa iwo.
Ndakodwa ndipo sindingathe kuthawa.
9 Diso langa lachita mdima chifukwa cha kuvutika kwanga.+
Ndimaitana inu Yehova tsiku lonse.+
Ndimapemphera kwa inu nditakweza manja anga.
10 Kodi mungachitire zinthu zodabwitsa anthu akufa?
Kodi anthu akufa amene sangathe kuchita kanthu angadzuke nʼkukutamandani?+ (Selah)
11 Kodi chikondi chanu chokhulupirika chingalengezedwe kumanda?
Kodi kukhulupirika kwanu kungalengezedwe mʼmalo a chiwonongeko?*
12 Kodi ntchito zanu zodabwitsa zingadziwike mu mdima?
Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika mʼdziko la anthu oiwalika?+
13 Koma ine ndimafuulirabe kwa inu Yehova kuti mundithandize,+
Mʼmawa uliwonse pemphero langa limafika kwa inu.+
14 Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani mukundikana?+
Nʼchifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+
15 Kuyambira ndili mnyamata,
Ndakhala ndikuzunzika komanso kutsala pangʼono kufa.+
Ndafooka kwambiri chifukwa cha zinthu zoopsa zimene mwalola kuti ndikumane nazo.
16 Ndafooka chifukwa cha mkwiyo wanu woyaka moto.+
Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandiwononga.
17 Zinthu zimene mumachita zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.
Zanditsekera kuzungulira mbali zonse.