Genesis
2 Motero, kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse za mmenemo zinamalizidwa kulengedwa.+ 2 Pofika tsiku la 7, Mulungu anali atamaliza ntchito yake imene anali kuchita. Pa tsiku la 7 limenelo, iye anayamba kupuma pa ntchito yake yonse imene anali kuchita.+ 3 Kenako Mulungu anadalitsa tsiku la 7. Analipatula kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli, iye wakhala akupuma pa ntchito yake yonse yolenga ndi yopanga zimene anafuna.+
4 Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera, m’tsiku limene Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.+
5 Nthaka ya padziko lapansi inali isanayambe kumera zitsamba ndi zomera zina, chifukwa Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula+ padziko lapansi. Panalibenso munthu woti n’kulima nthakayo. 6 Koma nkhungu+ inali kukwera m’mwamba kuchokera padziko lapansi, ndipo inali kunyowetsa nthaka yonse.+
7 Kenako, Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi,+ ndipo anauzira mpweya wa moyo+ m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala wamoyo.+ 8 Yehova Mulungu atatero, anakonza munda ku Edeni,+ chakum’mawa, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo.+ 9 Motero Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya. Anameretsanso mtengo wa moyo+ pakati pa mundawo, komanso mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.+
10 Panalinso mtsinje wochokera mu Edeni umene unali kuthirira mundawo. Potuluka mmenemo, mtsinjewo unayamba kugawikana n’kukhala mitsinje inayi. 11 Mtsinje woyamba dzina lake ndi Pisoni, umene umazungulira dziko lonse la Havila+ kumene kuli golide. 12 Golide wa dziko limenelo ndi wabwino.+ Kulinso mafuta onunkhira a bedola+ ndi miyala yamtengo wapatali ya onekisi.+ 13 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni, umene umazungulira dziko lonse la Kusi. 14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidekeli,+ umene umalowera kum’mawa kwa Asuri.+ Ndipo mtsinje wachinayi ndi Firate.+
15 Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni+ kuti aziulima ndi kuusamalira.+ 16 Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu.+ 17 Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.”+
18 Kenako Yehova Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.”+ 19 Yehova Mulungu anali kuumba ndi dothi nyama iliyonse yakutchire, ndi cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga. Ndipo anayamba kuzibweretsa kwa munthuyo, kuti chilichonse achitche dzina. Dzina lililonse limene munthuyo anatchula chamoyo chilichonse,+ limenelo linakhaladi dzina lake.+ 20 Choncho munthuyo anali kutcha mayina nyama zonse zoweta, ndiponso zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga, komanso nyama iliyonse yakutchire. Koma munthuyo analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera. 21 Motero Yehova Mulungu anagoneka munthuyo tulo tofa nato.+ Munthuyo ali chigonere choncho, Mulungu anamuchotsa nthiti imodzi n’kutseka pamalopo ndi mnofu. 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anapanga mkazi kuchokera kunthiti imene anaichotsa kwa mwamunayo. Atatero, anamubweretsa kwa iye.+
23 Ndiyeno mwamunayo anati:
“Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga
Ndi mnofu wa mnofu wanga.+
Ameneyutu adzatchedwa Mkazi,
Chifukwa iyeyu watengedwa kwa mwamuna.”+
24 Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake,+ n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.+ 25 Ndipo onsewo, mwamuna ndi mkazi wakeyo, anali kukhala maliseche.+ Koma sankachita manyazi.+