Ekisodo
2 Pa nthawiyo, mwamuna wina wa fuko la Levi anakwatira mwana wa Levi.+ 2 Mkaziyo anatenga pakati ndi kubereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, anam’bisa+ kwa miyezi itatu.+ 3 Poona kuti sakuthanso kum’bisa,+ anatenga kabokosi kagumbwa* n’kukamata phula.+ Kenako anaikamo mwanayo n’kukasiya kabokosiko pakati pa mabango+ m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo. 4 Ndiyeno mlongo wake wa mwanayo anaima chapatali ndithu kuti aone zimene zingachitikire mwanayo.+
5 Patapita kanthawi, panafika mwana wamkazi wa Farao kudzasamba mumtsinje wa Nailo. Ndipo atsikana omutumikira anali kuyenda m’mphepete mwa mtsinjewo. Kenako iye anaona kabokosi kaja kali pakati pa mabango. Nthawi yomweyo anatuma kapolo wake wamkazi kuti akakatenge.+ 6 Atabweretsa kabokosiko, anakatsegula ndipo anaona kuti muli mwana wamwamuna, ndipo anali kulira. Pamenepo anamumvera chisoni,+ ngakhale kuti anati: “Uyu ndi mmodzi wa ana a Aheberi.” 7 Zitatero, mlongo wake uja anauza mwana wa Farao kuti: “Kodi mungakonde kuti ndikakuitanireni mayi woyamwitsa wachiheberi kuti akulerereni mwanayu?” 8 Pamenepo mwana wa Faraoyo anamuyankha kuti: “Inde pita!” Nthawi yomweyo mtsikanayo anapita kukaitana mayi ake a mwanayo.+ 9 Ndiyeno mwana wa Farao anauza mayiyo kuti: “Tenga mwanayu ukandilerere ndipo ine ndizikulipira.”+ Choncho mayiyo anatenga mwanayo ndipo anamulera. 10 Mwana uja anakula. Kenako anapita naye kwa mwana wa Farao, ndipo anakhala mwana wake.+ Zitatero anam’patsa dzina lakuti Mose* n’kunena kuti: “Chifukwa chakuti ndinamuvuula m’madzi.”+
11 Tsopano m’masiku amenewo pamene Mose anali kukula ndi kukhala wamphamvu, anapita kwa abale ake kuti akaone ntchito imene anali kugwira.+ Kumeneko anaona m’bale wake wachiheberi akumenyedwa ndi Mwiguputo.+ 12 Pamenepo anayang’ana uku ndi uku ndipo anaona kuti palibe amene akumuona. Choncho anapha Mwiguputoyo ndi kum’bisa mumchenga.+
13 Koma tsiku lotsatira atapitanso, anapeza amuna awiri achiheberi akumenyana. Choncho anafunsa wolakwayo kuti: “Ukum’menyeranji mnzako?”+ 14 Poyankha iye anati: “Anakuika iwe ndani kukhala kalonga ndi woweruza wathu?+ Kodi ukufuna kundipha mmene unaphera Mwiguputo uja?”+ Pamenepo Mose anachita mantha ndipo anati mumtima mwake: “Haa! Nkhani ija yadziwika.”+
15 Patapita nthawi, Farao anaimva nkhaniyi ndipo anafuna kupha Mose.+ Koma Mose anam’thawa+ Farao ndipo anapita kukakhala kudziko la Midiyani.+ Atafika kumeneko, anakhala pachitsime. 16 Ndiyeno wansembe+ wa ku Midiyani anali ndi ana aakazi 7. Monga mwa masiku onse, iwo anafika pachitsimepo ndipo anatunga madzi ndi kuwathira m’ngalande kuti ziweto za bambo awo zimwe.+ 17 Monga mwa masiku onse, abusa anafika ndi kuwachotsapo atsikanawo. Zitatero Mose ananyamuka ndi kuthandiza atsikanawo, ndipo iye anamwetsa ziweto zawo.+ 18 Ndiyeno atsikanawo atafika kunyumba kwa bambo wawo Reueli,+ iye anadabwa ndipo anati: “Bwanji mwabwerako mwamsanga chonchi lero?” 19 Ndipo iwo anayankha kuti: “Mwiguputo+ wina watilanditsa kwa abusa, komanso watitungira madzi ndi kutimwetsera ziweto.” 20 Pamenepo iye anauza ana akewo kuti: “Nanga iyeyo ali kuti? Mwamusiyiranji? Pitani mukamuitane kuti adzadye chakudya.”+ 21 Zitatero Mose anavomereza kukhala ndi Reueli, ndipo iye anapereka Zipora+ mwana wake wamkazi kwa Mose. 22 Patapita nthawi Zipora anabereka mwana wamwamuna ndipo Mose anati: “Dzina lake akhale Gerisomu,*+ chifukwa ndine mlendo m’dziko lino.”+
23 Ndiyeno Mose atakhala kumeneko nthawi yaitali, mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma ana a Isiraeli anapitirizabe kuvutika ndi ukapolo ndi kulira modandaula.+ Iwo anapitirizabe kulirira thandizo kwa Mulungu woona chifukwa cha ukapolowo.+ 24 M’kupita kwa nthawi, Mulungu anamva+ kubuula kwawo+ ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ 25 Choncho Mulungu anayang’ana ana a Isiraeli ndipo anaona kuvutika kwawo.