Ekisodo
3 Tsopano Mose anakhala m’busa wa ziweto za Yetero,*+ wansembe wa ku Midiyani, amene anali apongozi ake.+ Pamene anali kuweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona,+ ku Horebe.+ 2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinali kuyaka moto. Atachiyang’anitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikupsa. 3 Pamenepo Mose anati: “Ndipatuke kuti ndikaonetsetse chodabwitsa chachikulu chimenechi, kuti ndione chifukwa chake chitsamba chamingachi chikuyaka koma osapsa.”+ 4 Yehova ataona kuti Mose wapatuka kuti akaonetsetse, nthawi yomweyo Mulungu anamuitana kuchokera pakatikati pa chitsamba chamingacho, kuti: “Mose! Mose!” ndipo iye anayankha kuti: “Ndili pano.”+ 5 Ndiyeno Mulungu anati: “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, chifukwa malo waimawo ndi malo oyera.”+
6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa atate ako, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Pamenepo Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona. 7 Yehova anawonjezeranso kuti: “Ndaona nsautso ya anthu anga amene ali ku Iguputo, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Zoonadi, ndikudziwa bwino zowawa zawo.+ 8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ 9 Taona, ndamva kulira kwa ana a Isiraeli, komanso ndaona kupondereza kumene Aiguputo akuwapondereza.+ 10 Tsopano, tamvera. Ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga ana a Isiraeli ku Iguputo.”+
11 Koma Mose anayankha Mulungu woona kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?”+ 12 Pamenepo Mulungu anati: “Chifukwa ndidzakhala nawe.+ Ndipo chizindikiro chako chakuti ine ndi amene ndakutuma ndi ichi:+ Pambuyo powatulutsa anthuwo mu Iguputo, anthu inu mudzatumikira Mulungu woona paphiri lino.”+
13 Koma Mose anafunsa Mulungu woona kuti: “Nditati ndakafika kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’+ Ndikawayankhe kuti chiyani?” 14 Mulungu anamuyankha Mose kuti: “NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA.”+ Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ana a Isiraeli ukawauze kuti, ‘NDIDZAKHALA AMENE NDIDZAFUNE KUKHALA ndiye wandituma kwa inu.’”+ 15 Kenako Mulungu anauzanso Mose kuti:
“Zimene ukauze ana a Isiraeli ndi izi, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ wandituma kwa inu.’ Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale,*+ ndipo ndicho chondikumbukirira ku mibadwomibadwo.+ 16 Pita, ukasonkhanitse akulu a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, anaonekera kwa ine+ n’kundiuza kuti: “Ndithu, ndidzakulanditsani ndi kuchitapo kanthu+ pa zonse zimene akukuchitirani mu Iguputo. 17 Ndikunenetsa kuti, ndidzakuchotsani mu nsautso+ ya Aiguputo ndi kukulowetsani m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori,+ Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.”’+
18 “Ukadzatero adzamvera mawu ako.+ Pamenepo, iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo ndi kuiuza kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tiyende ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+ 19 Koma ine ndikudziwa bwino kuti mfumu ya Iguputo sidzakulolani kupita kufikira nditaisonyeza mphamvu zanga.+ 20 Ndidzatambasula dzanja langa+ ndi kukantha Iguputo ndi ntchito zanga zonse zodabwitsa zimene ndidzazichita m’dzikolo. Pamenepo adzakulolani kuchoka.+ 21 Chotero ndidzachititsa Aiguputo kukomera mtima anthu anga, moti pochoka simudzachoka chimanjamanja.+ 22 Mkazi aliyense adzapemphe zinthu zasiliva, zagolide, ndi zovala kwa munthu wokhala naye pafupi ndi kwa mlendo wamkazi wokhala m’nyumba mwake. Zinthu zimenezi mudzaveke ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mudzatenge zinthu zambiri za Aiguputo.”+