Yeremiya
4 Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli, ubwerere kwa ine.+ Ndipo ngati ungachotse zinthu zako zonyansazo chifukwa cha ine,+ sudzakhalanso wothawathawa. 2 Ndipo ngati udzalumbira+ kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wachoonadi+ ndi chilungamo,’+ pamenepo mitundu ya anthu idzapeza madalitso* kudzera mwa iye ndipo idzadzitama m’dzina lake.”+
3 Zimene Yehova wanena kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu ndi izi: “Limani minda panthaka yabwino, ndipo musabzale mbewu pakati pa minga.+ 4 Chitani mdulidwe wa mitima yanu pamaso pa Yehova,+ inu anthu a ku Yuda ndi okhala mu Yerusalemu. Chitani zimenezi kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto, pakuti ukatero udzayaka popanda munthu wozimitsa, chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+
5 Nenani zimenezi mu Yuda anthu inu, ndipo zilengezeni ngakhale mu Yerusalemu.+ Fuulani ndi kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa m’dziko lonse.+ Fuulani kuti: “Sonkhanani pamodzi, ndipo tiyeni tilowe m’mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu. 7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+ 8 Pachifukwa chimenechi valani ziguduli,* anthu inu.+ Dzigugudeni pachifuwa ndi kulira mofuula,+ chifukwa mkwiyo woyaka moto wa Yehova sunatichokere.+
9 Yehova wanena kuti: “Zidzachitika pa tsikulo kuti mfumu sidzalimba mtima,+ chimodzimodzinso akalonga ake. Ansembe adzagwidwa ndi mantha ndipo aneneri adzadabwa.”+
10 Pamenepo ndinanena kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa anthu awa+ ndiponso Yerusalemu mwa kunena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ koma lupanga lawabaya* mpaka mumtima.”
11 Pa nthawiyo adzauza anthu awa ndi Yerusalemu kuti: “M’njira zodutsidwadutsidwa za m’chipululu zopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga+ mukutuluka mphepo yotentha.+ Mphepo imeneyi si youluzira mankhusu* kapena yoyeretsera tirigu. 12 Mphepo yamphamvu ikuchokera m’njirazo kubwera kwa ine. Ine ndidzawauza ziweruzo zanga.+ 13 Taonani! Mdani adzabwera ngati mitambo yamvula ndipo magaleta* ake ali ngati mphepo yamkuntho.+ Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+ Tsoka ife chifukwa tafunkhidwa. 14 Tsuka mtima wako ndi kuchotsa zoipa zonse, iwe Yerusalemu, kuti upulumuke.+ Kodi maganizo ako oipawo udzakhala nawo mpaka liti?+ 15 Pakuti mawu akumveka kuchokera ku Dani+ ndipo akulengeza uthenga wopweteka kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu.+ 16 Nenani zimenezi anthu inu. Nenani zimenezi kwa anthu a mitundu ina. Lengezani zimene zidzagwera Yerusalemu.”
“Alonda akubwera kuchokera kudziko lakutali+ ndipo adzalengeza uthenga wa zimene zidzagwera mizinda ya Yuda. 17 Iwo akhala ngati alonda a kunja kwa mzinda ndipo azungulira Yerusalemu kumbali zonse+ kuti amuukire chifukwa chakuti wandipandukira,”+ watero Yehova. 18 “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+ Limeneli ndilo tsoka lako chifukwa zidzakhala zowawa. Zidzatero chifukwa kupanduka kwako kwalowerera mpaka mumtima.”
19 M’mimba mwanga ine, m’mimba mwanga! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.+ Mtima wanga ukuvutika.+ Sindingathe kukhala chete pakuti ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.+ 20 Alengeza za kuphwanya kosakaziratu pakuti dziko lonse lafunkhidwa.+ Mwadzidzidzi, mahema anga ndi nsalu za mahema angawo zafunkhidwa+ m’kanthawi kochepa. 21 Kodi ndiona chizindikirocho ndi kumva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kufikira liti?+ 22 Anthu anga ndi opusa.+ Iwo sanaganizire za ine.+ Iwo ndi ana opanda nzeru ndipo sazindikira kalikonse.+ Iwo ndi anzeru pa kuchita zoipa koma sadziwa kuchita zabwino.+
23 Ndinaliona dzikolo, ndipo linali lopanda kanthu ndi lachabechabe.+ Ndinayang’ana kumwamba ndipo sikunali kuwala.+ 24 Ndinaona mapiri ndipo anali kugwedezeka. Zitunda zonse zinali kunjenjemera.+ 25 Ndinayang’anitsitsa koma sindinaone munthu aliyense. Ndipo zolengedwa zonse zouluka zinali zitathawa.+ 26 Ndinayang’anitsitsa ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo. Mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+ Zimenezi zinachitika ndi dzanja la Yehova chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.
27 Yehova wanena kuti: “Dziko lonseli lidzakhala bwinja+ ndipo ndidzawafafaniza.+ 28 Pachifukwa chimenechi dziko lidzalira+ ndipo kumwamba kudzachita mdima.+ Izi zili choncho chifukwa ndanena, ndaganiza zimenezi mozama, sindinadziimbe mlandu ndipo sindisintha maganizo anga.+ 29 Chifukwa cha phokoso la asilikali okwera pamahatchi ndiponso oponya mivi ndi uta, mzinda wonse ukuthawa.+ Alowa paziyangoyango ndi kuthawira m’matanthwe.+ Mumzinda uliwonse anthu athawamo ndipo palibe munthu amene akukhalamo.”
30 Iwe unali kuvala zovala zamtengo wapatali,* unali kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide ndipo unali kudzikongoletsa m’maso mwako ndi utoto wakuda.+ Tsopano utani popeza wafunkhidwa? Unali kutaya nthawi ndi kudzikongoletsa.+ Amene anali kukukhumba tsopano akukukana ndipo akufunafuna moyo wako.+ 31 Ine ndamva mawu ngati a mkazi amene akumva ululu. Ndamva ngati kubuula kwa mkazi amene akubereka mwana wake woyamba,+ koma ndi mawu a mwana wamkazi wa Ziyoni amene akupuma movutikira. Iye akutambasula manja ake+ ndi kulira kuti: “Tsoka ine, chifukwa ndatopa ndi anthu amene akufuna kundipha!”+