Ezekieli
44 Kenako munthu uja ananditengeranso kuchipata chakunja cha malo opatulika, chimene chinayang’ana kum’mawa,+ ndipo tinapeza kuti chinali chotseka.+ 2 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Chipata ichi chizikhalabe chotseka. Sichidzatsegulidwa, ndipo munthu wamba sadzalowa kudzera pachipata chimenechi chifukwa chakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli,+ walowa kudzera pachipata chimenechi. Choncho chidzapitirizabe kukhala chotseka. 3 Koma mtsogoleri+ wa anthu azidzakhala m’chipata chimenechi kuti azidzadya chakudya pamaso pa Yehova.+ Azidzalowa mmenemo kudzera kukhonde la kanyumba ka pachipata ndipo azidzatulukiranso komweko.”+
4 Kenako ananditengera kutsogolo kwa Nyumba ija kudzera pachipata cha kumpoto kuti ndikaone zimene zinali kumeneko. Kumeneko ndinaona ulemerero wa Yehova utadzaza m’nyumba ya Yehova.+ Pamenepo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ 5 Tsopano Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, khala tcheru+ ndipo uone ndi maso ako. Umve ndi makutu ako zonse zimene ndikukuuza zokhudza malangizo ndi malamulo onse a nyumba ya Yehova. Uonetsetse khomo la Nyumbayi ndi zipata zonse zotulukira m’malo opatulikawa. 6 Uuze anthu opandukawo,+ inde uuze a nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mwanyanya kuchita zinthu zonyansa, inu a nyumba ya Isiraeli.+ 7 Mumatenga alendo osachita mdulidwe wa mtima ndi mdulidwe wa khungu lawo+ kuti alowe m’malo anga opatulika ndi kuwadetsa. Ndithu iwo amadetsa nyumba yanga. Pamene mukupereka chakudya+ changa chomwe ndi mafuta+ ndi magazi,+ pangano langa limaphwanyidwa chifukwa cha zonyansa zanu zonse.+ 8 Inu simunakwaniritse utumiki wanu wosamalira zinthu zanga zopatulika,+ ndipo simunasankhe ena kuti azinditumikira pamalo anga opatulika m’malo mwa inu.”’+
9 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mlendo aliyense amene ali pakati pa ana a Isiraeli, wosachita mdulidwe wa mtima ndi mdulidwe wa khungu, asalowe m’malo anga opatulika.”’+
10 “‘Koma Alevi amene anachoka kwa ine n’kupita kutali+ adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo. Iwo anachoka kwa ine pamene Aisiraeli anandisiya n’kutsatira mafano awo onyansa.+ 11 Kenako Aleviwo adzakhala atumiki m’malo anga opatulika. Adzakhala ndi maudindo oyang’anira zipata za Nyumba ino ndipo adzakhala atumiki a pa Nyumbayi.+ Iwo azidzapha nyama za nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zina za anthu+ ndipo adzaimirira pamaso pa anthuwo ndi kuwatumikira.+ 12 Ine ndatambasula dzanja langa kuti ndiwalange+ chifukwa chakuti anali kutumikira anthu pamaso pa mafano awo onyansa.+ Iwo anakhala chopunthwitsa kwa anthu a nyumba ya Isiraeli ndipo anawachititsa zinthu zoipa,+ choncho adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 13 ‘Sadzayandikira kwa ine kuti anditumikire monga ansembe kapena kuyandikira zinthu zanga zilizonse zopatulika, zomwe ndi zoyera koposa.+ Iwo adzanyozeka ndi kukumana ndi zotsatira za zonyansa zimene anachita.+ 14 Ine ndidzawaika kuti azidzachita utumiki wa pa Nyumbayi wokhudza ntchito zake zonse ndi zonse zoyenera kuchitika mmenemo.’+
15 “‘Ansembe achilevi,+ ana a Zadoki,+ amene anali kugwira ntchito za pamalo anga opatulika pamene ana a Isiraeli anachoka kwa ine n’kupita kutali,+ amenewa adzandiyandikira ndi kunditumikira. Iwo adzaima pamaso panga+ ndi kundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 ‘Iwo ndi amene adzalowe m’malo anga opatulika,+ ndipo adzayandikira tebulo* langa ndi kunditumikira.+ Amenewa adzachita utumiki wawo kwa ine.+
17 “‘Iwo akafuna kulowa m’tinyumba ta zipata za bwalo lamkati, azivala zovala zansalu. Asamavale zovala zaubweya wa nkhosa pamene akutumikira m’tinyumba ta zipata za bwalo lamkati komanso mkati mwenimwenimo.+ 18 Iwo azivala zovala za kumutu zansalu+ ndi makabudula ansalu.+ Asamavale zovala zochititsa thukuta. 19 Akafuna kupita kubwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zawo zimene anavala potumikira.+ Aziika zovalazo m’zipinda zopatulika zodyeramo+ ndipo azivala zovala zina kuti asayeretse anthu ndi zovala zawozo.+ 20 Asamamete tsitsi la kumutu kwawo,+ komanso tsitsilo lisamatalike kwambiri, chotero tsitsilo azilidulira.+ 21 Ansembe asamamwe vinyo ngati akukalowa m’bwalo lamkati.+ 22 Iwo asamatenge mkazi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati kuti akhale mkazi wawo,+ koma azitenga anamwali omwe ndi ana ochokera m’nyumba ya Isiraeli+ kapena azitenga mkazi wamasiye amene anali mkazi wa wansembe.’
23 “‘Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu choipitsidwa. Aziwaphunzitsa kuti adziwe kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi choyera.+ 24 Iwo aziimirira pa mlandu ndi kuweruza.+ Aziweruza motsatira zigamulo zanga.+ Azisunga malamulo ndi malangizo anga okhudza zikondwerero zanga zonse,+ ndipo aziyeretsa masabata anga.+ 25 Asamapite kumene kuli munthu wakufa kuti angakhale odetsedwa. Koma wansembe akhoza kudzidetsa chifukwa cha bambo ake, mayi ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, m’bale wake kapena mlongo wake amene sanakwatiwepo.+ 26 Akamaliza kudziyeretsa, azimuwerengera masiku 7.+ 27 Pa tsiku limene adzalowe m’malo oyera, m’bwalo lamkati, kuti adzatumikire m’malo oyerawo, adzapereke nsembe yake yamachimo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
28 “‘Ponena za cholowa chawo, ineyo ndiye cholowa chawo.+ Anthu inu musawapatse chilichonse kuti chikhale chuma chawo mu Isiraeli, chuma chawo ndine. 29 Iwowa ndi amene azidzadya nsembe yambewu, nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula.+ Chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mu Isiraeli chidzakhala chawo.+ 30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira za mtundu uliwonse ndi zopereka zanu zonse za mtundu uliwonse zabwino kwambiri zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wochokera ku mbewu zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe+ kuti madalitso abwere panyumba yanu.+ 31 Ansembe asamadye nyama iliyonse imene aipeza yakufa, asamadye chouluka chilichonse kapena nyama iliyonse imene yakhadzulidwa ndi chilombo.’+