Ekisodo 20:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+ Levitiko 19:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 “‘Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Deuteronomo 21:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 “Munthu akakhala ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wopanduka,+ amene samvera mawu a bambo ake kapena a mayi ake,+ ndipo amulangiza koma sawamvera,+ Deuteronomo 21:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pamenepo amuna onse a mumzinda wawo azim’ponya miyala ndi kumupha. Muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha kwambiri.+ Miyambo 20:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Aliyense wotemberera bambo ake ndi mayi ake,+ nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ Miyambo 30:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya. Mateyu 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+
12 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.+
3 “‘Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
18 “Munthu akakhala ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wopanduka,+ amene samvera mawu a bambo ake kapena a mayi ake,+ ndipo amulangiza koma sawamvera,+
21 Pamenepo amuna onse a mumzinda wawo azim’ponya miyala ndi kumupha. Muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva ndi kuchita mantha kwambiri.+
17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.
4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+