Genesis 39:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+ 1 Mafumu 15:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo sanapatuke pa chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake,+ kupatulapo pa nkhani ya Uriya Mhiti.+ 1 Mbiri 21:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Zinthu zimenezi zinali zoipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo anapha Aisiraeli. Salimo 5:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mudzawononga olankhula bodza.+Munthu wokhetsa magazi+ ndi wachinyengo,+ Yehova amaipidwa naye. Salimo 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu. Yeremiya 32:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+ Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ Aheberi 13:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+
9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+
5 Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo sanapatuke pa chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake,+ kupatulapo pa nkhani ya Uriya Mhiti.+
4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.
19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+