-
2 Mbiri 28:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi. Iye anapita kukakumana ndi asilikali omwe anali kubwerera ku Samariya n’kuwauza kuti: “Tamverani! Yehova Mulungu wa makolo anu wapereka Ayuda m’manja mwanu chifukwa chakuti anawakwiyira kwambiri.+ N’chifukwa chake inuyo mwapha anthu pakati pawo mwaukali kwambiri,+ ndipo ukaliwo wafika mpaka kumwamba.+
-