-
1 Petulo 2:4-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pamene mukubwera kwa Ambuye, amene ndi mwala wamoyo umene anthu anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso ndi wamtengo wapatali kwa Mulunguyo,+ 5 inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera. Monga ansembe oyera muzidzapereka nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+ 6 Paja Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala wosankhidwa mwapadera mu Ziyoni. Umenewu ndi mwala wapakona ya maziko, womwe ndi wamtengo wapatali, ndipo aliyense wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”*+
7 Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa mumamukhulupirira. Koma kwa amene samukhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.”+
-