-
Mlaliki 3:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso kuti azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+ 13 komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa nʼkumasangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa cha ntchito yake yonse imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+
-
-
Mlaliki 5:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso choyenera chimene ine ndaona nʼchakuti: Munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala+ chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku ochepa a moyo wake amene Mulungu woona wamupatsa. Chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.*+ 19 Komanso Mulungu woona akapatsa munthu chuma ndiponso zinthu zambiri+ zimene angathe kusangalala nazo, ayenera kulandira mphoto yake* ndi kusangalala chifukwa cha ntchito imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+
-