12 Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani?+ Akufuna kuti muzichita izi: muziopa Yehova Mulungu wanu,+ muziyenda mʼnjira zake zonse,+ muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse,+