1 Mbiri
9 Aisiraeli onse analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo mʼBuku la Mafumu a Isiraeli. Ndipo Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.+ 2 Oyamba kubwerera nʼkukakhala kucholowa chawo mʼmizinda yawo anali Aisiraeli ena, ansembe, Alevi ndi atumiki apakachisi.*+ 3 Ndipo mbadwa zina za Yuda,+ za Benjamini,+ za Efuraimu ndi za Manase zinkakhala ku Yerusalemu. 4 Pa mbadwazi panali Utai mwana wa Amihudi. Amihudi anali mwana wa Omuri, Omuri anali mwana wa Imiri ndipo Imiri anali mwana wa Bani. Amenewa anali mbadwa za Perezi+ mwana wa Yuda. 5 Pa mbadwa za Shela, panali Asaya woyamba kubadwa ndiponso ana ake. 6 Pa mbadwa za Zera+ panali Yeweli ndi abale awo okwana 690.
7 Pa mbadwa za Benjamini panali Salelu mwana wa Mesulamu. Mesulamu anali mwana wa Hodaviya ndipo Hodaviya anali mwana wa Hasenuwa. 8 Panalinso Ibineya mwana wa Yerohamu ndi Ela mwana wa Uzi ndipo Uzi anali mwana wa Mikiri. Komanso panali Mesulamu mwana wa Sefatiya. Sefatiya anali mwana wa Reueli ndipo Reueli anali mwana wa Ibiniya. 9 Abale awo potsatira mibadwo yawo analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.
10 Pagulu la ansembe panali Yedaya, Yehoyaribu, Yakini+ 11 ndi Azariya mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Merayoti ndipo Merayoti anali mwana wa Ahitubu. Ahitubu anali mtsogoleri wa nyumba* ya Mulungu woona. 12 Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu. Yerohamu anali mwana wa Pasuri ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya. Komanso panali Maasai mwana wa Adieli. Adieli anali mwana wa Yahazera, Yahazera anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Mesilemiti ndipo Mesilemiti anali mwana wa Imeri. 13 Panalinso abale awo. Onse anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo ndipo analipo 1,760. Iwo anali amuna amphamvu ndiponso oyenerera, omwe ankatumikira panyumba ya Mulungu woona.
14 Pagulu la Alevi panali Semaya+ mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu ndipo Azirikamu anali mwana wa Hasabiya. Amenewa anali mbadwa za Merari. 15 Panalinso Bakabakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika. Mika anali mwana wa Zikiri ndipo Zikiri anali mwana wa Asafu. 16 Komanso panali Obadiya mwana wa Semaya. Semaya anali mwana wa Galali, Galali anali mwana wa Yedutuni. Ndiye panalinso Berekiya mwana wa Asa mwana wa Elikana, amene ankakhala mʼmidzi ya Anetofa.+
17 Alonda apageti+ anali Salumu, Akubu, Talimoni ndi Ahimani ndipo mʼbale wawo Salumu ndi amene anali mtsogoleri. 18 Mpaka nthawi imeneyo, iye ankakhala pageti la mfumu la mbali yakumʼmawa.+ Amenewa anali alonda a pamageti a misasa ya Alevi. 19 Panalinso Salumu mwana wa Kore. Kore anali mwana wa Ebiasafu ndipo Ebiasafu anali mwana wa Kora. Salumu ndi abale ake a kwa bambo ake, mbadwa za Kora, anali oyangʼanira ntchito pochita utumiki wawo ngati alonda apachihema. Makolo awo ankayangʼanira pamsasa wa Yehova ngati alonda apageti. 20 Pinihasi+ mwana wa Eliezara+ ndi amene anali mtsogoleri wawo kalekale ndipo Yehova anali naye. 21 Zekariya+ mwana wa Meselemiya anali mlonda wapageti lolowera kuchihema chokumanako.
22 Onse amene anasankhidwa kuti akhale alonda apamakomo analipo 212. Iwo ankakhala mʼmidzi yawo mogwirizana ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.+ Davide ndi Samueli wamasomphenya+ anaika anthuwa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 23 Iwo ndi ana awo ankayangʼanira anthu amene ankachita utumiki wolondera mageti a nyumba ya Yehova kapena kuti chihema chopatulika.+ 24 Alonda apagetiwo ankakhala mbali zonse 4, kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera.+ 25 Nthawi ndi nthawi abale awo amene ankakhala mʼmidzi yawo, ankabwera kudzagwira nawo ntchito kwa masiku 7. 26 Pamagetiwo panali akuluakulu 4 oyangʼanira amene anaikidwa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iwo anali Alevi ndipo ankayangʼanira zipinda zodyera ndi chuma chamʼnyumba ya Mulungu woona.+ 27 Usiku ankakhala mʼmalo awo mozungulira nyumba yonse ya Mulungu woona chifukwa ankachita utumiki wawo waulonda. Iwowa ndi amene ankasunga makiyi nʼkumatsegula nyumbayo mʼmawa uliwonse.
28 Ena a iwo ankayangʼanira ziwiya+ zogwiritsa ntchito pa utumiki ndipo ankaziwerenga pozitulutsa ndi pozilowetsa. 29 Ena anasankhidwa kuti aziyangʼanira ufa wosalala,+ vinyo,+ mafuta,+ lubani,*+ mafuta a basamu,+ ziwiya zonse zopatulika+ komanso ziwiya zina. 30 Ena mwa ana a ansembe ankasakaniza mafuta onunkhira a basamu. 31 Matitiya Mlevi, yemwe anali mwana woyamba wa Salumu mbadwa ya Kora, anali ndi udindo woyangʼanira zinthu zophikidwa mʼziwaya,+ umene anapatsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake. 32 Abale awo ena, mbadwa za Kohati, ankayangʼanira mikate yosanjikiza,*+ kuti aziikonza pa tsiku lililonse la Sabata.+
33 Amenewa anali oimba, atsogoleri a nyumba za makolo a Alevi mʼzipinda zodyera. Iwo sankapatsidwa ntchito zina chifukwa ankagwira ntchito yawo masana komanso usiku. 34 Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a Alevi potsatira mibadwo yawo ndipo ankakhala ku Yerusalemu.
35 Yeyeli bambo wa Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni+ ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka. 36 Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nera, Nadabu, 37 Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti. 38 Mikiloti anabereka Simeamu. Onsewa ankakhala pafupi ndi abale awo ku Yerusalemu pamodzi ndi abale awo ena. 39 Nera+ anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli+ ndipo Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu+ ndi Esibaala. 40 Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+ 41 Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi. 42 Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza. 43 Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Refaya, Refaya anabereka Eleasa ndipo Eleasa anabereka Azeli. 44 Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Amenewa anali ana a Azeli.