Wolembedwa ndi Maliko
12 Kenako anayamba kulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ nʼkumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa nʼkumanga nsanja.+ Atatero anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina.+ 2 Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. 3 Koma iwo anamugwira nʼkumumenya ndipo anamubweza chimanjamanja. 4 Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema mʼmutu komanso kumuchitira zachipongwe.+ 5 Anatumizanso wina koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha. 6 Iye anatsala ndi mmodzi yekha woti amutumize, mwana wake wokondedwa.+ Choncho anamutumizadi nʼkunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 7 Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa! uyu ndi amene adzalandire cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8 Choncho anamugwira nʼkumupha ndipo anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo.+ 9 Kodi mwiniwake wa mundawo adzachita chiyani? Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.+ 10 Kodi simunawerengepo zimene lemba limanena? Paja limanena kuti: ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.*+ 11 Umenewu wachokera kwa Yehova* ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.’”+
12 Atamva zimenezo ankafuna kumugwira,* koma anaopa gulu la anthu, chifukwa iwo anadziwa kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya nʼkuchokapo.+
13 Pambuyo pake anamutumizira ena mwa Afarisi ndi anthu amene ankatsatira Herode kuti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule.+ 14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi nʼzololeka* kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi tizipereka kapena tisamapereke?” Yesu anazindikira chinyengo chawo ndipo anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari* kuno ndilione.” 16 Iwo anamubweretsera ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi komanso mawu akewa nʼzandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 17 Choncho Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.
18 Kenako Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma osasiya mwana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.+ 20 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira alibe ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu. 22 Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 23 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.” 24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25 Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26 Koma pa mfundo yakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge mʼbuku la Mose munkhani yokhudza chitsamba chaminga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+ 27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+
28 Mmodzi wa alembi amene anafika nʼkuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino. Choncho anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba* ndi liti pa malamulo onse?”+ 29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba ndi lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova* mmodzi. 30 Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.’+ 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32 Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi ndipo palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.’+ 33 Ndipo kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, nʼzofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+ 34 Yesu atazindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru, anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Koma panalibe amene analimba mtima kuti amufunsenso.+
35 Komabe, pamene Yesu ankaphunzitsa mʼkachisi, ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 36 Kudzera mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako.”’+ 37 Davideyo anamutchula kuti Ambuye, ndiye zingatheke bwanji kuti akhale mwana wake?”+
Ndipo gulu lalikulu la anthu linkamumvetsera mosangalala. 38 Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika.+ 39 Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+ 40 Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*
41 Ndiyeno anakhala pansi pamalo amene ankatha kuona moponyeramo zopereka*+ ndipo anayamba kuona mmene gulu la anthu linkaponyera ndalama moponyera zoperekamo. Anaona anthu ambiri olemera akuponyamo makobidi ambiri.+ 42 Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+ 43 Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.+ 44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+