Levitiko
4 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu akachimwa mosadziwa+ pochita zinthu zimene Yehova analamula kuti musachite, muzichita izi:
3 Ngati wansembe wodzozedwa+ wachita tchimo+ ndipo lapangitsa anthu onse kupalamula, azipereka kwa Yehova ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+ 4 Azibweretsa ngʼombe yamphongoyo pamaso pa Yehova pakhomo la chihema chokumanako+ ndipo aziika dzanja lake pamutu wa ngʼombeyo, kenako aziipha pamaso pa Yehova.+ 5 Ndiyeno wansembe wodzozedwayo,+ azitengako pangʼono magazi a ngʼombeyo nʼkulowa nawo mʼchihema chokumanako. 6 Kenako wansembe aziviika chala chake mʼmagaziwo+ nʼkudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7+ pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani ya malo oyera. 7 Wansembeyo azipakanso ena mwa magaziwo panyanga za guwa lansembe la zofukiza zonunkhira,+ limene lili pamaso pa Yehova mʼchihema chokumanako. Magazi ena onse a ngʼombeyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako.
8 Kenako azichotsa mafuta onse a ngʼombe ya nsembe yamachimo, kuphatikizapo mafuta okuta matumbo ndi mafuta onse apamatumbo. 9 Azichotsanso impso ziwiri zomwe zili pafupi ndi chiuno ndi mafuta okuta impsozo. Komanso azichotsa mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 10 Zinthu zimenezi zizikhala zofanana ndi zomwe azichotsa pa ngʼombe ya nsembe yamgwirizano.+ Ndipo wansembe aziziwotcha paguwa lansembe zopsereza.
11 Koma kunena za chikopa cha ngʼombeyo ndi nyama yake yonse pamodzi ndi mutu wake, ziboda zake, matumbo ake ndi ndowe zake,+ 12 kutanthauza ngʼombe yonseyo, aziitenga nʼkupita nayo kunja kwa msasa. Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa* ndipo aziiwotcha pamoto+ wa nkhuni. Aziwotcha ngʼombeyo kumalo otayako phulusa.
13 Tsopano ngati gulu lonse la Isiraeli lapalamula pochita tchimo mosadziwa,+ koma mpingo* sunazindikire kuti iwo achita zimene Yehova anawalamula kuti asachite,+ 14 ndipo kenako tchimolo ladziwika, mpingowo uzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo, ndipo azibwera nayo pakhomo la chihema chokumanako. 15 Akulu a gulu la Isiraeli aziika manja awo pamutu wa ngʼombeyo pamaso pa Yehova, ndipo iziphedwa pamaso pa Yehova.
16 Kenako wansembe wodzozedwa, azibweretsa ena mwa magazi a ngʼombeyo mʼchihema chokumanako. 17 Wansembe aziviika chala chake mʼmagaziwo nʼkudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7 pamaso pa Yehova, patsogolo pa katani.+ 18 Kenako azipaka ena mwa magaziwo panyanga za guwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova, mʼchihema chokumanako. Magazi ena onse aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pakhomo la chihema chokumanako.+ 19 Akatero azichotsa mafuta ake onse ndi kuwawotcha paguwa lansembe.+ 20 Ngʼombeyo azichita nayo ngati mmene anachitira ndi ngʼombe ina ya nsembe yamachimo ija. Azichita zomwezo, ndipo wansembe aziwaphimbira machimo awo+ ndipo adzakhululukidwa. 21 Azitenga ngʼombeyo nʼkupita nayo kunja kwa msasa ndipo aziiwotcha ngati mmene anawotchera ngʼombe yoyamba ija.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo ya mpingo wonse.+
22 Ngati mtsogoleri+ wachimwa mosadziwa pochita chimodzi mwa zinthu zonse zimene Yehova Mulungu wake analamula kuti asachite ndipo wapalamula, 23 kapena ngati wadziwa kuti wachimwa pochita zinthu zosemphana ndi lamulo, azibweretsa mbuzi yaingʼono yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yake. 24 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa mbuzi yaingʼonoyo ndipo aziipha pamaso pa Yehova,+ pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza. Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 25 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimoyo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza.+ 26 Mafuta onse a mbuziyo aziwawotcha paguwa lansembe mofanana ndi mafuta a nsembe yamgwirizano.+ Pamenepo wansembe aziphimba tchimo la mtsogoleriyo, ndipo adzakhululukidwa.
27 Ngati munthu aliyense pakati panu wachimwa mosazindikira pochita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite+ ndipo wapalamula, 28 kapena ngati wadziwa kuti wachimwa, azibweretsa mbuzi yaingʼono yaikazi, yopanda chilema kuti ikhale nsembe chifukwa cha tchimo lakelo. 29 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo azipha nyamayo pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza aja.+ 30 Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza.+ 31 Kenako azichotsa mafuta onse a mbuziyo,+ ngati mmene amachotsera mafuta a nsembe yamgwirizano.+ Akatero wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe kuti akhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo ndipo adzakhululukidwa.
32 Koma ngati akupereka nkhosa monga nsembe yake yamachimo, azibweretsa nkhosa yaingʼono yaikazi yopanda chilema. 33 Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo aziipha kuti ikhale nsembe yamachimo, pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza.+ 34 Wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake nʼkuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza.+ Magazi ena onse a nkhosayo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 35 Ndiyeno azichotsa mafuta onse a nkhosayo, monga mmene amachotsera mafuta a nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yamgwirizano. Akatero wansembe aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova.+ Wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita, ndipo adzakhululukidwa.’”+