Ekisodo
28 “Pakati pa Aisiraeli, usankhe Aroni+ mʼbale wako pamodzi ndi ana ake+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara komanso Itamara+ kuti atumikire monga ansembe anga. 2 Aroni mʼbale wako umupangire zovala zopatulika kuti zimupatse ulemerero ndi kumʼkongoletsa.+ 3 Ulankhule ndi anthu onse aluso* amene ndinawapatsa mzimu wa nzeru.+ Anthuwo amupangire Aroni zovala zomwe zizisonyeza kuti wayeretsedwa, kuti atumikire monga wansembe wanga.
4 Zovala zoti apange ndi izi: chovala pachifuwa,+ efodi,+ malaya akunja odula manja,+ mkanjo wamandalasi, nduwira+ ndi lamba wapamimba.+ Aroni mʼbale wako ndi ana ake awapangire zovala zopatulikazi, kuti atumikire monga ansembe anga. 5 Anthu alusowo agwiritse ntchito golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.
6 Apange efodi wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 7 Efodiyo akhale ndi nsalu ziwiri za mʼmapewa ndipo azilumikize kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 8 Lamba woluka*+ womangira efodi, wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.
9 Utenge miyala iwiri ya onekisi+ nʼkulembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba.+ 10 Mayina 6 uwalembe pamwala umodzi ndipo mayina 6 otsalawo uwalembe pamwala winawo potsatira mmene anabadwira. 11 Mmisiri wogoba agobe mayina a ana a Isiraeli pamiyala iwiriyo ngati mmene amagobera chidindo.+ Kenako miyalayo idzaikidwe mʼzoikamo zake zagolide. 12 Udzalowetse miyala iwiriyo pansalu zamʼmapewa za efodi kuti ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Isiraeli.+ Poonekera kwa Yehova, Aroni azidzanyamula mayina awo pansalu ziwiri zamʼmapewa ake kuti chikhale chikumbutso. 13 Upange zoikamo miyala zagolide, 14 ndi matcheni awiri agolide woyenga bwino. Uwapange ngati zingwe zopota+ mwaluso, ndipo ulumikize matcheni okhala ngati zingwewo ku zoikamo miyala.+
15 Uuze munthu waluso lopeta kuti apange chovala pachifuwa chachiweruzo+ ndipo achipange mwaluso mofanana ndi efodi. Achipange ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 16 Ukachipinda pakati mbali zake zonse 4 zizifanana, mulitali mwake chikhale masentimita 22* ndipo mulifupi mwake masentimita 22. 17 Uikepo miyala ndipo ikhale mʼmizere 4. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi. 18 Mzere wachiwiri ukhale ndi miyala ya nofeki, safiro ndi yasipi. 19 Mzere wachitatu ukhale ndi miyala ya lesemu,* agate ndi ametusito. 20 Mzere wa 4 ukhale ndi miyala ya kulusolito, onekisi ndi yade. Ndipo iikidwe mʼzoikamo miyala zagolide. 21 Miyalayo uiike malinga ndi mayina a ana 12 a Isiraeli. Mwala uliwonse aulembe mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo ndipo mwala uliwonse ukhale ndi dzina limodzi mwa mayina a mafuko 12.
22 Pachovala pachifuwa upangepo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+ 23 Upange mphete ziwiri zagolide nʼkuziika pachovala pachifuwa. Mphete ziwirizo uziike mʼmakona awiri a chovala pachifuwacho. 24 Ulowetse zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zomwe zili mʼmakona a chovala pachifuwa. 25 Ulowetse zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri zimene zili pansalu zamʼmapewa za efodi chakutsogolo. 26 Upange mphete ziwiri zagolide nʼkuziika mʼmakona awiri a chovala pachifuwa kumbali yamkati yokhudzana ndi efodi.+ 27 Upangenso mphete zina ziwiri zagolide nʼkuziika kutsogolo kwa efodi, mʼmunsi mwa nsalu ziwiri zamʼmapewa, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba woluka* wa efodi.+ 28 Chovala pachifuwacho achimange ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chilowe mumphete za chovala pachifuwa komanso mphete za efodi. Zimenezi zidzathandiza kuti chovala pachifuwacho chisasunthe koma chizikhala pamwamba pa lamba woluka* wa efodi.
29 Aroni azinyamula mayina a ana a Isiraeli pamtima pake, pachovala pachifuwa chachiweruzo, akamalowa mʼMalo Oyera kuti chikhale chikumbutso pamaso pa Yehova nthawi zonse. 30 Udzaike Urimu ndi Tumimu*+ mʼchovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamakaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula pamtima pake zinthu zogwiritsa ntchito poweruza Aisiraeli akamaonekera kwa Yehova nthawi zonse.
31 Upange malaya odula manja ovala mkati mwa efodi. Uwapange ndi ulusi wabuluu wokhawokha.+ 32 Malayawo akhale otsegula pamwamba pake, pakatikati. Potsegulapo pakhale popenderera mʼmphepete mwake ndi nsalu yowomba. Pakhale potsegula ngati chovala chakunkhondo chamamba achitsulo, kuti chisangʼambike. 33 Mumpendero wake wamʼmunsi upangemo zinthu zooneka ngati makangaza* za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri kuzungulira mpenderowo. Upangenso mabelu agolide pakati pa makangazawo kuzungulira mpenderowo. 34 Uziika belu lagolide kenako khangaza, belu lagolide kenako khangaza kuzungulira mpendero wamʼmunsi mwa malaya odula manjawo. 35 Aroni azivala malayawo kuti atumikire, ndipo mabeluwo azimveka iye akamalowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova komanso akamatuluka, kuti asafe.+
36 Upangenso kachitsulo konyezimira kagolide woyenga bwino ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti: ‘Yehova ndi Woyera.’+ 37 Kachitsulo kameneko ukamangirire panduwira+ ndi chingwe chabuluu. Kazikhala patsogolo pa nduwirayo. 38 Kachitsuloko kazikhala pamphumi pa Aroni. Munthu akachimwira zinthu zopatulika+ zimene Aisiraeli amaziyeretsa akamazipereka ngati mphatso zopatulika, Aroni aziyankha mlandu wa tchimo limenelo. Kachitsuloko kazikhala pamphumi pake nthawi zonse, kuti azichititsa anthuwo kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova.
39 Uwombe mkanjo wamandalasi ndi ulusi wabwino kwambiri. Upangenso nduwira ya nsalu yabwino kwambiri ndiponso uluke lamba wa mkanjo.+
40 Ana a Aroni uwapangirenso mikanjo, malamba ndi mipango* yokulunga kumutu+ kuti iwapatse ulemerero ndi kuwakongoletsa.+ 41 Uveke Aroni mʼbale wako pamodzi ndi ana ake zinthu zimenezi. Ukatero uwadzoze,+ uwayeretse nʼkuwaika*+ kuti atumikire monga ansembe anga. 42 Uwapangirenso makabudula ansalu ofika* mʼntchafu kuti azibisa maliseche awo.+ 43 Aroni ndi ana ake azivala makabudula amenewa polowa mʼchihema chokumanako kapena popita kuguwa lansembe kukatumikira pamalo oyera kuti asapalamule mlandu nʼkufa. Limeneli ndi lamulo kwa iye ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.”