Machitidwe a Atumwi
16 Kenako Paulo anafika ku Debe ndiponso ku Lusitara.+ Kumeneko kunali wophunzira wina dzina lake Timoteyo,+ mwana wa mayi wa Chiyuda wokhulupirira, koma bambo ake anali Mgiriki. 2 Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anapereka umboni wabwino wonena za iyeyo. 3 Paulo anasonyeza kuti akufuna kumutenga pa ulendo wake. Choncho anamutenga nʼkumudula chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko,+ popeza onse ankadziwa kuti bambo ake ndi Mgiriki. 4 Mʼmizinda yonse imene ankadutsa, ankapatsa okhulupirira akumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, mogwirizana ndi zimene atumwi ndiponso akulu ku Yerusalemu anagamula.+ 5 Choncho anthu mʼmipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.
6 Kenako iwo anapita ku Fulugiya ndiponso mʼdziko la Galatiya,+ chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu a Mulungu mʼchigawo cha Asia. 7 Atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya,+ koma mzimu wa Yesu sunawalole. 8 Choncho anangodutsa ku Musiya nʼkukafika ku Torowa. 9 Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Anaona munthu wina wa ku Makedoniya ataima nʼkumuuza kuti: “Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.” 10 Atangoona masomphenya amenewo, tinaganiza zopita ku Makedoniya. Tinatsimikiza kuti Mulungu watiitana kuti tikalengeze uthenga wabwino kwa anthu akumeneko.
11 Choncho tinanyamuka ulendo wapanyanja kuchokera ku Torowa kupita ku Samatirake. Koma tsiku lotsatira tinafika ku Neapoli. 12 Titachoka kumeneko tinafika ku Filipi,+ mzinda wolamulidwa ndi Aroma, umenenso ndi likulu la chigawo cha Makedoniya. Tinakhala mumzindawu kwa masiku angapo. 13 Tsiku la sabata tinatuluka pageti nʼkupita mʼmbali mwa mtsinje, kumene tinkaganiza kuti kuli malo opempherera. Kenako tinakhala pansi nʼkuyamba kulankhula ndi azimayi amene anasonkhana kumeneko. 14 Pagululo panali mayi wina dzina lake Lidiya ndipo anali wolambira Mulungu. Iye ankachokera mumzinda wa Tiyatira+ ndipo ankagulitsa nsalu ndi zovala zapepo. Pamene ankamvetsera, Yehova* anatsegula kwambiri mtima wake kuti amvetse zimene Paulo ankalankhula. 15 Iye ndi anthu a mʼbanja lake atabatizidwa+ anatipempha kuti: “Abale anga, ngati mwaona kuti ndine wokhulupirika kwa Yehova,* tiyeni mukakhale kwathu.” Moti anatitenga kuti tipite kwawo.
16 Ndiyeno pamene tinkapita kumalo opempherera, tinakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi mzimu, chiwanda cholosera zamʼtsogolo.+ Iye ankachititsa kuti mabwana ake azipindula kwambiri chifukwa cha zoloserazo. 17 Mtsikana ameneyu ankangotsatira Paulo ndi ifeyo nʼkumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wamʼmwambamwamba+ ndipo akulengeza njira ya chipulumutso kwa inu.” 18 Iye anachita zimenezi kwa masiku ambiri. Kenako Paulo anatopa nazo ndipo anatembenuka nʼkuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.+
19 Koma mabwana ake aja ataona kuti sapindulanso,+ anagwira Paulo ndi Sila nʼkuwakokera mumsika, kubwalo la olamulira.+ 20 Atafika nawo kwa akuluakulu a zamalamulo, ananena kuti: “Anthu awa akusokoneza kwambiri mzinda wathu,+ komanso iwowa ndi Ayuda. 21 Ndipo akufalitsa miyambo imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatira kapena kuichita, popeza ndife Aroma.” 22 Kenako gulu lonselo linanyamuka nʼkuukira atumwiwo. Ndipo akuluakulu a zamalamulowo, anavula atumwiwo malaya awo mochita kuwangʼambira nʼkulamula kuti awakwapule ndi ndodo.+ 23 Atawakwapula zikoti zambiri, anawatsekera mʼndende ndi kulamula woyangʼanira ndende kuti aziwalondera nʼcholinga choti asathawe.+ 24 Popeza kuti anamulamula zimenezi, iye anakawaika mʼchipinda chamkati cha ndendeyo nʼkumanga mapazi awo mʼmatangadza.
25 Koma chapakati pa usiku, Paulo ndi Sila anayamba kupemphera ndiponso kutamanda Mulungu poimba nyimbo,+ moti akaidi ena ankawamva. 26 Mwadzidzidzi panachitika chivomerezi champhamvu, mpaka maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka.+ 27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka nʼkuona kuti zitseko za ndende nʼzotseguka, anasolola lupanga lake kuti adziphe, poganiza kuti akaidiwo athawa.+ 28 Koma Paulo anafuula kuti: “Usadzivulaze, tonse tilipo!” 29 Iye anapempha kuti amupatse nyale ndipo mwamsanga analowa mkatimo. Akunjenjemera ndi mantha, anagwada patsogolo pa Paulo ndi Sila. 30 Kenako anawatulutsa kunja nʼkunena kuti: “Mabwana, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” 31 Iwo anati: “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka limodzi ndi anthu a mʼnyumba yako.”+ 32 Kenako analankhula mawu a Yehova* kwa iye pamodzi ndi onse a mʼnyumba yake. 33 Usiku womwewo, anawatenga nʼkuwatsuka mabala awo. Pasanapite nthawi yaitali, iye ndi anthu onse a mʼbanja lake anabatizidwa.+ 34 Kenako anapita nawo kunyumba kwake nʼkuwaikira chakudya patebulo. Ndipo iye limodzi ndi onse a mʼbanja lake, anasangalala kwambiri chifukwa anakhulupirira Mulungu.
35 Mʼmawa mwake, akuluakulu a zamalamulo anatumiza asilikali kukanena kuti: “Anthu amenewo amasuleni.” 36 Choncho woyangʼanira ndende uja anauza Paulo uthengawo kuti: “Akuluakulu a zamalamulo atumiza anthu kudzanena kuti awirinu mumasulidwe. Choncho tulukani tsopano, ndipo mupite mwamtendere.” 37 Koma Paulo anawauza kuti: “Iwo atikwapula pamaso pa anthu nʼkutitsekera mʼndende popanda kutizenga mlandu, chikhalirecho ndife Aroma.+ Kodi tsopano akutitulutsa mwamseri? Ayi, zimenezo sizitheka! Abwere eniakewo adzatitulutse okha.” 38 Ndiyeno asilikaliwo anakanena zimenezi kwa akuluakulu a zamalamulo aja. Akuluakulu a zamalamulowo anachita mantha atamva kuti anthuwo ndi Aroma.+ 39 Choncho iwo anabwera nʼkuwachonderera, ndipo atawatulutsa anawapempha kuti achoke mumzindawo. 40 Koma iwo atatuluka mʼndendemo anapita kunyumba kwa Lidiya. Ataona abale anawalimbikitsa,+ kenako ananyamuka nʼkumapita.