Yoswa
1 Mose mtumiki wa Yehova atamwalira, Yehova anauza Yoswa*+ mwana wa Nuni, mtumiki+ wa Mose, kuti: 2 “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodano ndi kulowa mʼdziko limene ndikulipereka kwa Aisiraeli.+ 3 Malo alionse amene phazi lanu lidzapondapo ndidzakupatsani, mogwirizana ndi zimene ndinalonjeza Mose.+ 4 Dziko lanu lidzayambira kuchipululu kufika ku Lebanoni mpaka kumtsinje waukulu wa Firate, dziko lonse la Ahiti+ mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu* kumadzulo.+ 5 Palibe amene adzakugonjetse masiku onse a moyo wako.+ Ndidzakhala nawe ngati mmene ndinakhalira ndi Mose+ ndipo sindidzakutaya kapena kukusiya.+ 6 Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iweyo ndi amene utsogolere anthuwa kuti akatenge dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndidzawapatsa.+
7 Ukhale wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatira malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula. Usapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere,+ kuti uzichita zinthu mwanzeru kulikonse kumene ungapite.+ 8 Buku la Chilamulo ili lisachoke pakamwa pako.+ Uziliwerenga ndi kuganizira mozama* masana ndi usiku, kuti uzitsatira bwinobwino zonse zimene zalembedwamo.+ Ukamatero, zizikuyendera bwino ndipo uzichita zinthu mwanzeru.+ 9 Ndakulamula kale kuti ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, chifukwa Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene ungapite.”+
10 Kenako Yoswa analamula akapitawo a anthuwo kuti: 11 “Pitani mumsasa wonsewu, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani ndipo mupezeretu zinthu zonse zofunikira, chifukwa pakapita masiku atatu muwoloka Yorodano nʼkulowa mʼdzikolo kuti mukalitenge, dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.’”+
12 Ndiyeno Yoswa anauza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase kuti: 13 “Kumbukirani mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani+ akuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndipo wakupatsani dziko ili. 14 Akazi anu ndi ana anu atsale limodzi ndi ziweto zanu kutsidya lino la Yorodano,+ pamalo amene Mose wakupatsani. Koma asilikali amphamvu nonsenu,+ muwoloke ndipo muzikayenda patsogolo pa abale anu,+ mutakonzeka kumenya nkhondo. Muyenera kuwathandiza. 15 Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakatenga malo amene Yehova Mulungu akuwapatsa, mʼpamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kumalo anu amene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani, tsidya lino la Yorodano, kumʼmawa kuno.’”+
16 Iwo anayankha Yoswa kuti: “Zonse zimene mwatilamula tichita, ndipo kulikonse kumene mungatitumize tipita.+ 17 Tidzamvera chilichonse chimene mungatiuze ngati mmene tinkachitira ndi Mose. Yehova Mulungu wanu akhale nanu ngati mmene anakhalira ndi Mose.+ 18 Munthu aliyense wophwanya dala malamulo anu, ndi wosamvera mawu anu pa chilichonse chimene mungamulamule, aphedwe.+ Inuyo mukhale wolimba mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.”+