Ezara
2 Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ 2 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredikayi, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Bana.
Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+ 3 Ana a Parosi, 2,172. 4 Ana a Sefatiya, 372. 5 Ana a Ara,+ 775. 6 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu, 2,812. 7 Ana a Elamu,+ 1,254. 8 Ana a Zatu,+ 945. 9 Ana a Zakai, 760. 10 Ana a Bani, 642. 11 Ana a Bebai, 623. 12 Ana a Azigadi, 1,222. 13 Ana a Adonikamu, 666. 14 Ana a Bigivai, 2,056. 15 Ana a Adini, 454. 16 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 17 Ana a Bezai, 323. 18 Ana a Yora, 112. 19 Ana a Hasumu,+ 223. 20 Ana a Gibara, 95. 21 Ana a Betelehemu, 123. 22 Amuna a ku Netofa, 56. 23 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24 Ana a Azimaveti, 42. 25 Ana a Kiriyati-yearimu, Kefira ndi Beeroti, 743. 26 Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27 Amuna a ku Mikemasi, 122. 28 Amuna a ku Beteli ndi a ku Ai,+ 223. 29 Ana a Nebo,+ 52. 30 Ana a Magabisi, 156. 31 Ana a Elamu wina, 1,254. 32 Ana a Harimu, 320. 33 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono, 725. 34 Ana a Yeriko, 345. 35 Ana a Senaya, 3,630.
36 Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a mʼbanja la Yesuwa,+ 973. 37 Ana a Imeri,+ 1,052. 38 Ana a Pasuri,+ 1,247. 39 Ana a Harimu,+ 1,017.
40 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya, 74. 41 Oimba,+ ana a Asafu,+ 128. 42 Ana a alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, onse analipo 139.
43 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, 45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, 47 ana a Gideli, ana a Gahara, ana a Reyaya, 48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49 ana a Uziza, ana a Paseya, ana a Besai, 50 ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu, 51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, 53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 54 ana a Neziya ndi ana a Hatifa.
55 Ana a atumiki a Solomo: Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Ami.
58 Atumiki onse apakachisi* pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.
59 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+ 60 ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 652. 61 Ana a ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 63 Choncho, bwanamkubwa* anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+
64 Anthu onse analipo 42,360.+ 65 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200. 66 Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245. 67 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.
68 Atsogoleri ena a nyumba za makolo awo atafika kunyumba ya Yehova imene inali ku Yerusalemu, anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwenso pamalo ake.+ 69 Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka zinthu zoti zithandize pa ntchitoyo. Anapereka madalakima* agolide 61,000, ma mina*+ asiliva 5,000 ndi mikanjo 100 ya ansembe. 70 Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena, oimba, alonda apageti, atumiki apakachisi* ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+