2 Samueli
6 Davide anasonkhanitsanso amuna onse osankhidwa mwapadera mu Isiraeli,+ okwana 30,000. 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+ 3 Koma iwo anakweza likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo,+ ana aamuna a Abinadabu, anali kutsogolera ngolo yatsopanoyo.
4 Choncho ananyamula likasa la Mulungu woona kulichotsa kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri, ndipo Ahiyo anali kuyenda patsogolo pa Likasa. 5 Davide pamodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kusangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Anali kuimbanso zeze,+ zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana. 6 Kenako anafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, ndipo Uza+ anatambasulira dzanja lake pa likasa la Mulungu woona n’kuligwira,+ chifukwa ng’ombe zinatsala pang’ono kuligwetsa. 7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova+ unayakira Uza ndipo Mulungu woona anamukantha+ pomwepo chifukwa cha kuchita chinthu chosalemekeza Mulungu chimenechi. Moti Uza anafera pomwepo, pafupi ndi likasa la Mulungu woona.+ 8 Zitatero, Davide anakwiya chifukwa mkwiyo wa Yehova unaphulikira Uza modzidzimutsa. Chotero malo amenewo amatchedwa dzina lakuti Perezi-uza* kufikira lero.+ 9 Tsiku limenelo, Davide anachita mantha kwambiri chifukwa cha Yehova,+ ndipo anati: “Kodi likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10 Pamenepo Davide sanafunenso kutenga likasa la Yehova kupita nalo kumene iye anali kukhala, ku Mzinda wa Davide.+ Chotero Davide analipatutsira kunyumba ya Obedi-edomu+ Mgiti.+
11 Likasa la Yehova linakhalabe kunyumba ya Obedi-edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anapitiriza kudalitsa+ Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+ 12 Pamapeto pake uthenga unafika kwa Mfumu Davide wonena kuti: “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-edomu ndi zake zonse chifukwa cha likasa la Mulungu woona.” Davide atamva mawu amenewa anapita kukatenga likasa la Mulungu woona kunyumba kwa Obedi-edomu ndi kupita nalo ku Mzinda wa Davide, akusangalala.+ 13 Tsopano onyamula+ likasa la Yehova atangoyenda mapazi 6, nthawi yomweyo Davide anapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi chiweto chonenepa.+
14 Davide ankavina mozungulira pamaso pa Yehova ndi mphamvu zake zonse. Apa n’kuti Davide atavala efodi+ wansalu. 15 Davide ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kupita ndi likasa+ la Yehova, akufuula mokondwera+ ndi kuimba lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 16 Ndiyeno pamene likasa la Yehova linalowa mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kuvina mozungulira pamaso pa Yehova. Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.+ 17 Ndiyeno analowetsa likasa la Yehova muhema limene Davide anamanga n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako Davide anapereka kwa Yehova nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ 18 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova+ wa makamu. 19 Kuwonjezera apo, anthu onse, khamu lonse la Isiraeli, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira yoboola pakati, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi.+ Kenako aliyense wa anthuwo anapita kunyumba yake.
20 Tsopano Davide anabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake.+ Pamenepo Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kukakumana naye ndipo anati: “Lerotu mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake+ mwa kudzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, monga mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi ngakhale pang’ono!”+ 21 Poyankha, Davide anauza Mikala kuti: “Ine ndinali kusangalala pamaso pa Yehova amene anandisankha kuti ndikhale mtsogoleri+ wa anthu a Yehova, Aisiraeli, m’malo mwa bambo ako ndi banja lawo lonse, ndipo ndidzasangalala pamaso pa Yehova.+ 22 Ndipotu ndipitiriza kudzipeputsa kuposa pamenepa,+ moti ndidzichepetsa m’maso mwanga. Ndine wotsimikiza mtima kudzipezera ulemerero pamaso pa akapolo aakazi amene ukunenawo.”+ 23 Choncho Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli sanakhalepo ndi mwana mpaka tsiku la imfa yake.