Nahumu
1 Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu* wa ku Elikosi:
2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.
Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake.+
Yehova amabwezera adani ake,
Ndipo adani ake amawasungira mkwiyo.
3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+
Koma Yehova salephera kulanga munthu woyenera kulangidwa.+
Njira yake ili mumphepo yowononga ndiponso yamkuntho.
Ndipo mitambo ili ngati fumbi lopondapo mapazi ake.+
Zomera za ku Basana ndi za ku Karimeli zimafota,+
Nawonso maluwa a ku Lebanoni amafota.
Dziko lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha nkhope yake
Pamodzi ndi nthaka komanso zinthu zonse zokhala mʼdzikomo.+
6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+
Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+
Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto,
Ndipo miyala idzaphwanyidwa chifukwa cha iye.
7 Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo pa nthawi yamavuto.+
Amadziwa* amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+
9 Kodi Yehova mungamukonzere chiwembu chotani?
Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso.
Sipadzakhalanso masautso.+
10 Iwo alukanalukana ngati minga,
Ndipo ali ngati anthu oledzera.
Koma adzawotchedwa ngati mapesi ouma.
11 Mwa iwe mudzatuluka winawake amene adzakonzera Yehova chiwembu,
Ndiponso kupereka malangizo achabechabe.
12 Yehova wanena kuti:
“Ngakhale kuti iwo anali ndi mphamvu zambiri komanso anali ambiri,
Adzadulidwa ndipo sadzakhalaponso.*
Ndakusautsa,* koma sindidzakusautsanso.
13 Tsopano ndidzathyola goli lake nʼkulichotsa pa iwe,+
Ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo.
Ndidzachotsa zifaniziro zosema ndi zifaniziro zachitsulo mʼnyumba* za milungu yako.
Ndidzakukonzera manda chifukwa uli ngati chinthu chonyansa.’
15 Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.
Iye akulengeza za mtendere.+
Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza,
Chifukwa munthu aliyense wopanda pake sadzadutsa pakati pako.
Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”