2 Mafumu
22 Yosiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 8 ndipo analamulira zaka 31 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Bozikati.+ Dzina lawo linali Yedida mwana wa Adaya. 2 Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire kumanja kapena kumanzere.
3 Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, mfumuyo inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu yemwe anali mlembi, kuti apite kunyumba ya Yehova.+ Inamuuza kuti: 4 “Pita kwa Hilikiya+ mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti asonkhanitse ndalama zonse zimene zikubwera kunyumba ya Yehova,+ zimene alonda a pakhomo atolera kwa anthu.+ 5 Azipereke kwa omwe asankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova, kuti akazipereke kwa amene akugwira ntchitoyo mʼnyumba ya Yehova, kuti akonze* nyumbayo.+ 6 Akazipereke kwa amisiri, kwa omanga nyumba ndiponso kwa amisiri omanga ndi miyala. Agulirenso matabwa ndi miyala yosema kuti akonzere nyumbayo.+ 7 Koma anthu amene akupatsidwa ndalamazo asafunsidwe mmene akuziyendetsera chifukwa ndi anthu odalirika.”+
8 Kenako Hilikiya mkulu wa ansembe anauza Safani mlembi+ kuti: “Ndapeza buku la Chilamulo+ mʼnyumba ya Yehova!” Choncho Hilikiya anapereka bukulo kwa Safani ndipo iye anayamba kuliwerenga.+ 9 Ndiyeno Safani mlembi anapita kwa mfumu kukanena kuti: “Atumiki anu akhuthula ndalama zimene anazipeza mʼnyumbayo ndipo azipereka kwa omwe anasankhidwa kuti aziyangʼanira ntchito panyumba ya Yehova.”+ 10 Safani mlembi anauzanso mfumuyo kuti: “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku+ linalake.” Ndiyeno Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.
11 Mfumuyo itangomva mawu a mʼbuku la Chilamulo, inangʼamba zovala zake.+ 12 Kenako mfumuyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu+ mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti: 13 “Pitani mukafunse kwa Yehova mʼmalo mwa ineyo, anthuwa ndiponso mʼmalo mwa Ayuda onse. Mukafunse zokhudza mawu a mʼbuku limene lapezekali, chifukwa Yehova watikwiyira kwambiri,+ popeza makolo athu sanamvere mawu a mʼbukuli. Iwo sanachite zonse zimene zalembedwamo zokhudza ife.”
14 Choncho wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya anapita kwa Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe ankayangʼanira mosungira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi. Hulidayo ankakhala Kumbali Yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+ 15 Iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Munthu amene wakutumaniyo mukamuuze kuti: 16 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake pokwaniritsa mawu onse amʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.+ 17 Chifukwa chakuti andisiya nʼkumapereka nsembe zautsi kwa milungu+ ina kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo,+ mkwiyo wanga udzayakira malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’”+ 18 Mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova, mukaiuze kuti, “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: ‘Ponena za mawu amene wamvawo, 19 chifukwa chakuti mtima wako unali womvera* ndipo unadzichepetsa+ pamaso pa Yehova utamva zimene ndanena zokhudza malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chinthu chodabwitsa ndi temberero ndipo unangʼamba zovala zako+ nʼkuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva, watero Yehova. 20 Nʼchifukwa chake ndidzakuika mʼmanda a makolo ako ndipo udzaikidwa mʼmanda ako mwamtendere. Maso ako sadzaona tsoka lonse limene ndidzabweretse pamalo ano.’”’” Kenako iwo anakauza mfumuyo zimenezi.